CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EZEKIELI 42-45
Kubwezeletsa Kulambila Koyela
Masomphenya a Ezekieli a kacisi anatsimikizila Ayuda otsalila ku ukapolo kuti kulambila koyela kudzabwezeletsedwa. Ndiponso, anawakumbutsa za miyezo ya Yehova yapamwamba ya kulambila koyela.
Ansembe anali kudzaphunzitsa anthu miyezo ya Yehova
44:23
Fotokozani zitsanzo za mmene kapolo wokhulupilika ndi wanzelu watiphunzitsila kusiyana pakati pa cinthu copatulika na cinthu codetsedwa. (kr peji 110-117)
• Anthu azidzacilikiza owatsogolela
45:16
Kodi tingaonetse bwanji kuti timacilikiza akulu a mumpingo wathu?