UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Ǹ’cifukwa Ciani Kulambila Koyela Kuli Kofunika?
Ayuda amene anali ku ukapolo analimbikitsidwa na masomphenya a kacisi amene Ezekieli anaona. Masomphenyawo anawapatsa ciyembekezo cakuti kulambila koyela kudzabwezeletsedwa. M’masiku otsiliza ano, kulambila koyela ‘kwakhazikika pamwamba pa nsonga za mapili,’ ndipo ise tili pakati pa anthu amene akhamukila ku phili limenelo. (Yes. 2:2) Kodi mumayamikila mwayi wodziŵa Yehova na kum’tumikila?
MADALITSO A KULAMBILA KOYELA:
Cakudya cauzimu coculuka cimene cimapeleka mayankho pa mafunso ofunika ngako onena za umoyo. Cimatithandizanso kukhala na makhalidwe abwino ndi ciyembekezo cotsimikizika.—Yes. 48:17, 18; 65:13; Aroma 15:4
Ubale wa padziko lonse.—Sal. 133:1; Yoh. 13:35
Mwayi wokhala anchito anzake a Mulungu pa nchito yokhutilitsa.—Mac. 20:35; 1 Akor. 3:9
“Mtendele wa Mulungu” umene umatilimbitsa pa nthawi ya mavuto.—Afil. 4:6, 7
Cikumbumtima coyela.—2 Tim. 1:3
“Ubwenzi wolimba ndi Yehova.”—Sal. 25:14.
Ningaonetse bwanji kuti nimaona kulambila koyela kukhala kofunika ngako?