CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EZEKIELI 46-48
Madalitso Amene Isiraeli Wobwezeletsedwa Anali Kudzalandila
Masomphenya a Ezekieli analimbikitsa Aisiraeli a ku ukapolo, ndipo anawatsimikizila kuti maulosi a kubwezeletsedwa kwa kulambila koona adzakwanilitsika. Kulambila koyela kunali kudzabwezeletsedwa pa malo ake okwezeka, kwa anthu odalitsidwa na Yehova.
Masomphenyawo anaonetsa dongosolo, mgwilizano, na citetezo
47:7-14
Nthaka yaconde
Banja lililonse linalandila coloŵa cake
Anthu asanagaŵilidwe malo, “gawo” lina lapadela linali kupatulidwa kuti likhale “copeleka” kwa Yehova
48:9, 10
Ningawonetse bwanji kuti niimaika patsogolo kulambila Yehova mu umoyo wanga? (w06 4/15 peji 27-28 pala. 13-14)