October 16-22
HOSEYA 1-7
Nyimbo 18 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Cikondi Cokhulupilika Cimam’kondweletsa Yehova —Nanga Imwe?”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Hoseya.]
Hos. 6:4, 5—Yehova anakhumudwa pamene Aisiraeli analephela kuonetsa cikondi cokhulupilika kwa iye (w10 8/15 peji 25 pala. 18)
Hos. 6:6—Yehova amakondwela tikaonetsa cikondi cokhulupilika (w07 9/15 peji 16 pala. 8; w07 6/15 peji 27 pala. 7)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Hos. 1:7—Ni liti pamene nyumba ya Yuda inacitilidwa cifundo na kupulumutsidwa? (w07 9/15 peji 14 pala. 7)
Hos. 2:18—Kodi vesiyi inakwanilitsidwa bwanji? Nanga idzakwanilitsidwa bwanji m’tsogolo? w05 11/15 peji 20 pala. 16; g05 9/8 peji 12 pala. 2)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Hos. 7:1-16
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) 1 Yoh. 5:3—Phunzitsani Coonadi—Itanilani munthuyo ku misonkhano.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) Deut. 30:11-14; Yes. 48:17, 18—Phunzitsani Coonadi—Muuzeni za webusaiti yathu ya jw.org. (Onani mwb16.08 peji 8 pala. 2.)
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) lv peji 12-13 mapa. 16-18—Onetsani mmene tingam’fikile pamtima wophunzila.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (15 min.) Nkhani ya mkulu. Kwa mamineti 5, ŵelengani na kufotokoza lemba loyenelela lopezeka mu Nsanja ya Mlonda ya November 15, 2015 peji 15. Ndiyeno tambitsani vidiyo yakuti Malangizo Opangila Zopeleka pa Intaneti. Pambuyo pake, aunikileni za peji ya pa jw.org yakuti, “Mmene Mungapelekele Ndalama Zothandizila pa Nchito ya Padziko Lonse” na kufotokoza njila zotumizila pa intaneti m’dziko lanu.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 20 mapa. 1-6, mabokosi “Nchito Yathu Yaikulu Yoyamba Yopeleka Thandizo Masiku Ano” na “Kukonzekela Zakugwa Mwadzidzidzi”
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 50 na Pemphelo