CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | HOSEYA 1-7
Cikondi Cokhulupilika Cimam’kondweletsa Yehova—Nanga Imwe?
Mau akuti cikondi cokhulupilika amatanthauza kukonda munthu mokhulupilika, modzipeleka, na kumamatila kwa iye zivute zitani. Pofuna kuphunzitsa tanthauzo la cikondi cokhulupilika na kukhululuka, Yehova anaseŵenzetsa Hoseya na mkazi wake wosakhulupilika, Gomeri.—Hos. 1:2; 2:7; 3:1-5.
Kodi Gomeri anaonetsa bwanji kuti analibe cikondi cokhulupilika?
Kodi Aisiraeli anaonetsa bwanji kusoŵa cikondi cokhulupilika?
Kodi Hoseya anaonetsa bwanji cikondi cokhulupilika?
Nanga Yehova anaonetsa bwanji cikondi cokhulupilika?
ZOFUNIKA KUSINKHA-SINKHA: Nanga ine, ningaonetse bwanji cikondi cokhulupilika kwa Yehova?