NYIMBO 124
Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse
Yopulinta
(Salimo 18:25)
1. Kwa Yehova M’lungu wathu,
Tikhulupilikedi.
Tim’lambile, tim’tamande,
Niwokhulupilika.
Timvele uphungu wake
Na mtima wathu wonse.
Tim’dalile, timukonde,
Ndipo tisamusiye.
2. Kwa abale tionetse
Cikondi na cifundo.
Akakhala pa mavuto
Tiziŵasamalila.
Ndipo tiŵalemekeze;
Tisaŵakaikile.
Nthawi zonse tisungane
Inde tisasiyane.
3. Kwa akulu a mumpingo,
Tikhulupilikedi.
Titsatile malangizo
Amene atipatsa.
Ngati tikhulupilika
Tidzadalitsidwadi.
Tidzakhala a Yehova
Iye adzatikonda.
(Onaninso Sal. 149:1; 1 Tim. 2:8; Aheb. 13:17.)