LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr18 January masa. 1-5
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
  • Tumitu
  • JANUARY 1-7
  • JANUARY 8-14
  • JANUARY 15-21
  • JANUARY 22-28
  • JANUARY 29–FEBRUARY 4
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
mwbr18 January masa. 1-5

Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

JANUARY 1-7

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 1-3

“Ufumu Wakumwamba Wayandikila”

nwtsty mfundo zounikila pa Mat. 3:1, 2

kulalikila: M’cigiriki, liu limeneli litanthauza “kulengeza poyela monga mthenga.” Limatsindika kumene akulengezela: nthawi zambili pabwalo, ndi pamaso pa anthu ambili osati pa kagulu kocepa.

Ufumu: Liu lake la Cigiriki lakuti ba·si·leiʹa loyambilila kuonekela, litanthauza boma komanso malo na anthu amene akulamulidwa na mfumu. Liu la Cigiriki limeneli limaonekela maulendo okwana 162 M’malemba Acigiriki Acikhristu. Koma maulendo 55, lipezeka m’buku la Mateyu, ndipo kaŵili-kaŵili likutanthauza ulamulilo wakumwamba wa Mulungu. Mateyu anawaseŵenzetsa kwambili liu limeneli cakuti buku lake tingaliche kuti Uthenga Wabwino wa Ufumu.

Ufumu wakumwamba: Mau awa amapezeka nthawi zokwana 30, ndipo apezeka cabe mu Uthenga Wabwino wa Mateyu. Mu Uthenga Wabwino wa Maliko na wa Luka, muli mau ofananako akuti “Ufumu wa Mulungu,” kuonetsa kuti “Ufumu wa Mulungu” uli kumwamba ndipo udzalamulila kucokela kumwamba kosaonekako.—Mat. 21:43; Maliko 1:15; Luka 4:43; Dan. 2:44; 2 Tim. 4:18.

wayandikila: M’lingalilo lakuti Mfumu ya m’tsogolo ya Ufumu wakumwamba anali atatsala pafupi kuonekela.

nwtsty zithunzi

Covala ca Yohane M’batizi na Maonekedwe Ake

Yohane anali kuvala covala caubweya wa ngamila na lamba wacikumba m’ciuno mwake, umene anali kunyamulilamo tunthu tung’ono-tung’ono. Mneneli Eliya analinso kuvala covala cofanana ndi ca Yohane. (2 Maf. 1:8) Covala ca ubweya wa ngamila cinali cokakala, ndipo cinali ca anthu osauka. Koma zovala zofewa zapamwamba zopangiwa na nsalu zinali za anthu olemela. (Mat. 11:7-9) Popeza kuti Yohane anali Mnaziri cibadwile, n’kutheka kuti sanagelapo tsitsi lake. Conco, covala cake na mmene iye anali kuonekela ziyenela kuti zinaonetsa poyela kuti anali na umoyo wosalila zambili, ndipo anali wodzipeleka kothelatu kucita cifunilo ca Mulungu.

Dzombe

M’Baibo, liu lakuti “dzombe” lingatanthauze mitundu yosiyana-siyana ya ziwala zokhala na tunyanga twatufupi, maka-maka ziwala zimene zimauluka m’magulu. Malinga na kafuku-fuku amene anacitika ku Yerusalemu, ziwala za m’cipululu zimakhala na mapuloteni 75 pelesenti m’thupi. Masiku ano, anthu akafuna kudya dzombe amacotsa mutu, miyendo, mapiko, na cimimba cake. Ndiye mbali yotsala imene ni cifuwa cake, amaidya yaiŵisi kapena yophika. Ena amakamba kuti dzombe ukamalidya limamveka monga nkhanu ndipo lili na mapuloteni ambili.

Uci

Cithunzi coonetsa nthenje imene njuchi zinamanga (1) ndi cisa ca uci (2). Uci umene Yohane anali kudya uyenela kuti unali kupangiwa na njuci zosacita kusunga zochedwa kuti Apis mellifera syriaca, zimene zinali kukhala ku delalo. Njuci zimenezi zinazoloŵela kukhala kumalo otentha m’cipululu ca Yudeya koma sizisungiwa na anthu cifukwa n’zazikali zimaluma. Komabe, kuciyambi kwa m’ma 800 B.C.E., anthu a ku Isiraeli anali kusunga njuci m’mitsuko yadothi. Mapale a mitsuko yosungilamo njuci zimenezo anapezeka pakati pa tauni inayake yakale (lomba imachedwa Tel Rehov), imene ili ku cigwa ca Yorodani. Uci wa m’mitsuko imeneyi, unali kupangiwa na mtundu wa njuci zimene zioneka kuti zinatengewa ku dziko limene lomba timati Turkey.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 1:3

Tamara: Ni mzimayi woyamba pa azimayi asanu ochulidwa mu mzela wobadwila wa Mesiya m’buku la Mateyu. Ena anayi ni Rahabi na Rute, onse sanali akazi aciisiraeli (vesi 5); Batiseba, “mkazi wa Uriya” (vesi 6); na Mariya (vesi 16). Azimayiwa ayenela kuti akuchulidwa cifukwa cakuti pali zinazake zapadela zimene zinapangitsa kuti aliyense wa iwo akhale mumzela wa makolo a Yesu.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 3:11

ndidzakubatizani: Kapena “kukumizani.” Liu lacigiriki lakuti ba·ptiʹzo litanthauza “kuviika kapena kumiza.” Malifalensi ena a m’Baibo amaonetsa kuti ubatizo ni kumiza thupi lonse m’madzi. Panthawi ina, Yohane anali kubatiza anthu pa malo ena m’Cigwa ca Yorodano pafupi na Salimu “cifukwa kunali madzi ambili kumeneko.” (Yoh. 3:23) Pamene Filipo anali kubatiza nduna ya ku Itiyopiya, ‘onse aŵili . . . analoŵa m’madzimo.’ (Mac. 8:38) Liu lacigiriki limodzi-modzi linagwilitsidwanso nchito mu Baibo yochedwa Septuagint pa 2 Maf. 5:14 pokamba zakuti Namani ‘anamila maulendo 7.’

JANUARY 8-14

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 4-5

“Zimene Tiphunzilapo pa Ulaliki wa Yesu wa Paphili”

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 5:3

Odala: Osati cabe kumva bwino mu mtima pamene akusangalala ayi. Koma ngati ni kwa anthu, liuli limatanthauza munthu wodalitsidwa ndi woyanjidwa na Mulungu . Liuli ligwilitsidwanso nchito pofotokoza za Mulungu na ulemelelo wakumwamba wa Yesu.—1 Tim. 1:11; 6:15

anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu: Mau a Cigiriki amene anawamasulila kuti “amene amazindikila,” kapena kuti, “amene ni osauka (osoŵa; amphawi; opempha-pempha),” pa lembali akutanthauza aja amene ni osoŵa ndipo akudziŵa zimenezo. Liu limodzi-modzili linaseŵenzetsewa pa Luka 16:20, 22, pokamba za Lazaro “wopemphapempha.” M’ma Baibo ena, mau a Cigiriki amene anawamasulila kuti amene ni “osauka mu mzimu,” amapeleka lingalilo la anthu amene amazindikila umphawi wawo wauzimu na kuti afunikila Mulungu.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 5:7

acifundo: M’Baibo mau akuti “acifundo” ndi “cifundo” akaseŵenzetsewa satanthauza cabe kukhululukila kapena kusakhwimitsa zinthu. Nthawi zambili amakamba za kukoma mtima na kumvelela ena cisoni kumene kumapangitsa munthu kuthandiza ofunikila thandizo.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 5:9

amene amabweletsa mtendele: Ni amene amasunga mtendele komanso amene amaubweletsa ngati ukusoŵeka.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 4:9

kuŵelama kamodzi kokha: Liu la Cigiriki limene linamasulidwa kuti “kuŵelama” limapeleka lingalilo locita cinthu mwacidule. Pokamba kuti “n’kundiwelamila kamodzi kokha,” Mdyelekezi anaonetsa kuti sanapemphe Yesu kuti amuŵelamile kapena kumulambila kwa nthawi yaitali; kunali kumulambila kamodzi cabe.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 4:23

kuphunzitsa . . . kulalikila: Kuphunzitsa kumasiyana na kulalikila cifukwa mphunzitsi samalengeza cabe; iye amalangiza, kufotokoza, kuseŵenzetsa mfundo zokopa na kupeleka umboni.

JANUARY 15-21

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 6-7

“Pitilizani Kufuna-funa Ufumu Coyamba”

nwtsty mfundo younikila Mat. 6:24

kapolo: Liu lake m’Cigiriki litanthauza kugwila nchito monga kapolo, kuonetsa kuti ni munthu amene ni wa mbuye mmodzi cabe. Apa Yesu anali kuonetsa kuti n’zosatheka Mkhristu kukhala wodzipeleka kwa Mulungu monga mmene Mulunguyo afunila, koma panthawi imodzimodzi n’kukhala wodzipeleka ku cuma.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 6:33

pitilizani kufunafuna: Velebu yacigiriki ya mau amenewa imaonetsa cinthu cocitika mopitiliza ndipo m’mau ena tingakambe kuti “Kufuna-funa kosalekeza.” Otsatila oona a Yesu sangafune-fune Ufumu kwa kanthawi cabe basi n’kupita kukacita zinthu zina ayi. M’malomwake, nthawi zonse Ufumu umakhala cinthu coyamba mu umoyo wawo.

Ufumu: M’mipukutu ina yakale yacigiriki analemba kuti “Ufumu wa Mulungu.”

cake: Kutanthauza Mulungu, ‘Atate wakumwamba’ wochulidwa pa Mat. 6:32.

cilungamo: Anthu amene amafuna-funa cilungamo ca Mulungu amakhala okonzeka kucita cifunilo cake na kutsatila miyezo yake yolungama. Ciphunzitso cimeneci cinali kusiyana kwambili na ciphunzitso ca Afarisi, amene anakhazikitsa cilungamo cawo.—Mat. 5:20.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo zounikila pa Mat. 7:28, 29

linadabwa: Velebu ya Cigiriki imene anaseŵenzetsa apa ingatanthauze “kudabwa kwambili mpaka kukhala kakasi.” Velebu imeneyi ionetsa kuti mau amene Yesu anakamba anakhudza kwambili khamu la anthuwo.

kaphunzitsidwe kake: Mau awa amakamba za mmene Yesu anali kuphunzitsila, njila zake zophunzitsila, zimene zinaphatikizapo ziphunzitso zake, na malangizo onse amene anapeleka pa Ulaliki wake wa Paphili.

osati monga alembi awo: Mmalo mogwila mau a arabi monga anthu aulamulilo, malinga na cikhalidwe ca alembi, Yesu anali kukamba monga woimilako Yehova, amene ali monga munthu wokhala na ulamulilo. Anacita izi mwa kutenga ziphunzitso zake M’mau a Mulungu.—Yoh. 7:16.

JANUARY 22-28

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 8-9

“Yesu Anali Kukonda Anthu”

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 8:3

n’kumukhudza: Cilamulo ca Mose cinakamba kuti odwala khate afunika kukhala kwaokha kuti ena asayambukilidwe. (Lev. 13:45, 46; Num. 5:1-4) Koma atsogoleli a cipembedzo aciyuda anawonjezelapo malamulo ena. Mwacitsanzo, munthu sanali kufunika kuyandikana na wodwala khate na mamita pafupi-fupi 1.8, ngati kuli cimphepo, anali kufunika kutalikilana naye na mamita pafupi-fupi 45. Malamulo amenewa anapangitsa kuti anthu azicitila nkhanza odwala khate. Zolembedwa zina zakale imaonetsa kuti m’rabi amene anali kubisala odwala khate, na wina amene anali kuponya miyala anthu akhate kuti akhale kutali, anali kucita bwino. Mosiyana na zimenezi, Yesu anakhudzidwa kwambili ataona mmene wodwala khate anali kuvutikila cakuti anacita zimene Ayuda ena akanaona kuti ni kusaganiza bwino—anakhudza munthuyo. Anacita zimenezo olo kuti akanacilitsa wakhateyo na mau cabe.—Mat. 8:5-12.

Ndikufuna: Yesu sanangomvela pempho cabe, koma anaonetsa kuti ni wofunitsitsa kucitapo kanthu. Izi zionetsa kuti anasonkhezeledwa na zambili osati cabe kuona kuti ni udindo wake kucita zimenezo.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 9:10

kudya patebulo: Kudyela pamodzi na munthu pathebulo cinali cizindikilo cakuti pali ubwenzi wathithithi pakati pawo. Conco, Ayuda a m’nthawi ya Yesu sanali kukhala na munthu amene si Myuda pathebulo kapena kuti kudya naye pamodzi.

okhometsa msonkho: Ayuda ambili anali kukhometsa misonkho ya olamulila aciroma. Anthu anali kuzonda Ayudawo cifukwa anali kugwilizana na olamulila odedwa acikunja komanso cifukwa anali kukakamiza anthu kulipila zambili kuposa zimene anali kufunikila kulipila. Okhometsa msonkho anali kupewedwa na Ayuda anzawo, ndipo anali kuonedwa cimodzimodzi na ocimwa ndi mahule.—Mat. 11:19; 21:32.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 9:36

anawamvela cisoni: Velebu yacigiriki yakuti splag·khniʹzo·mai imene anaseŵenzetsa apa ilinganako na liu lakuti “matumbo” (splagʹkhna), kuonetsa mmene munthu amamvelela m’thupi akakhudzika kwambili. Ili ni limodzi mwa mau amphamvu ngako m’Cigiriki oonetsa cifundo.

JANUARY 29–FEBRUARY 4

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 10-11

“Yesu Anali Kutsitsimula Anthu”

nwtsty mfundo zounikila pa Mat. 10:29, 30

mpheta: Liu la Cigiriki lakuti strou·thiʹon ni liu la mbalame iliyonse yaing’ono, koma nthawi zambili limatanthauza mpheta, mbalame yochipa kwambili pa mbalame zonse zimene anthu amagula monga cakudya.

kakhobidi kamodzi kocepa mphamvu: Kapena kuti “asariyoni.” Ni malipilo a munthu amene waseŵenza kwa maminetsi 45. (Onani Buku Lothandiza pohunzila Mau a Mulungu Cigawo 18.) Yesu ali paulendo wake wacitatu wopita ku Galileya, anakamba kuti mpheta ziŵili zinali kuguliwa na ndalama imodzi ya asariyoni. Panthawi ina, mwina patapita caka cimodzi, pamene Yesu anali kucita utumiki wake ku Yudeya, anakamba kuti mpheta zisanu zinali kuguliwa na ndalama ziŵili. (Luka 12:6) Mfundo zimenezi zionetsa kuti mpheta zinali zochipa ngako kwa amalonda cakuti mpheta yacisanu anali kuipeleka mahala.

tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliŵelenga: Tsitsi la m’mutu wa munthu nthawi zambili limaposa pa 100,000. Nzelu zozama za Yehova zofika pa kudziŵa tunthu twatung’ono conco, zionetsa kuti amacita cidwi ngako na wotsatila aliyense wa Khristu.

nwtsty zithunzi

Mpheta

Mpheta zinali mbalame zochipa kuposa mbalame zonse zimene anthu anali kugula monga cakudya. Ziŵili zinali kuguliwa na ndalama imene munthu angaseŵenzele kwa maminetsi 45. Liu lake la Cigiriki liphatikizapo mbalame zinanso zing’ono-zing’ono, ngakhale zija zodziŵika zimene zimabwela panyumba (Passer domesticus biblicus) na mpheta za ku Spain (Passer hispaniolensis), zimene zikali kupezeka kwambili ku Israel.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 11:28

olemedwa: Anthu amene Yesu anali kuwaitana kuti abwele, anali “olemedwa” na nkhawa komanso nchito. Kulambila kwawo Yehova kunakhala colemetsa cifukwa ca miyambo ya anthu imene anawonjezela pa Cilamulo ca Mose. (Mat. 23:4) Ngakhale Sabata, imene colinga cake cinali kutsitsimula, inakhala colemetsa.—Eks. 23:12; Maliko 2:23-28; Luka 6:1-11.

ndidzakutsitsimutsani: Liu la Cigiriki la “kutsitsimula” lingatanthauze zonse ziŵili kupumula (Mat. 26:45; Maliko 6:31) na kulekeza kugwila nchito kuti upezenso mphamvu (2 Akor. 7:13; Filim. 7). Mau a vesiyi komanso oizungulila aonetsa kuti kusenza “goli” (Mat. 11:29) la Yesu kuphatikizapo kugwila nchito osati kupumula. Velebu ya Cigiriki pokamba za Yesu, limapeleka lingalilo lakuti adzapelekanso mphamvu kwa ofooka kuti athe kunyamula goli lake lopepuka komanso lofewa.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 11:29

Senzani goli langa: Yesu apa anaseŵenzetsa liu lakuti “goli” mophiphilitsa pokamba za kugonjela ulamulilo na citsogozo. Ngati anali kuganizila za goli limene Mulungu anam’senzetsa, ndiye kuti anali kuitana ophunzila ake kuti asenze goli limene iye akusenza na kuti iye adzawathandiza. Ngati n’conco, mauwo tingawakambe kuti: “Bwelani musenze goli langa limodzi na ine.” Koma ngati Yesu akusenzetsa ena goli limenelo, ndiye kuti zikutanthauza kuti monga ophunzila ake, tifunika kugonjela ulamulilo wa Khristu na citsogozo cake.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani