LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 March tsa. 7
  • “Khalanibe Maso”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Khalanibe Maso”
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mumamvela Macenjezo?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Wosamvela Malamulo Aonekela
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 March tsa. 7
Anamwali 10 a m’fanizo la Yesu

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 25

“Khalanibe Maso”

25:1-12

Ngakhale kuti fanizo la Yesu la anamwali 10 linali kupita kwa otsatila ake odzozedwa, uthenga wake ungagwilenso nchito kwa Akhristu onse. (w15 3/15 mape. 12-16) “Cotelo khalanibe maso cifukwa simukudziŵa tsiku kapena ola lake.” (Mat. 25:13) Kodi imwe mungalifotokoze fanizo la Yesu limeneli?

  • Mkwati (vesi 1)—Yesu

  • Anamwali ocenjela ndiponso okonzeka (vesi 2)—Akhristu odzozedwa amene ni okonzeka kukwanilitsa nchito yawo mokhulupilika, na amene amawala ngati zounikila mpaka ku mapeto (Afil. 2:15)

  • Mau ofuula akuti: “Mkwati uja wafika!” (vesi 6)—Cizindikilo ca kukhalapo kwa Yesu

  • Anamwali opusa (vesi 8)—Akhristu odzozedwa amene adzapita kukakumana na Mkwati koma sanakhale maso ndiponso sanakhulupilike

  • Anamwali ocenjela anakana kupatsako anzawo mafuta (vesi 9)—Akhristu odzozedwa okhulupilika akadzaikiwa cidindo comaliza, sadzathandizanso aliyense wosakhulupilika

  • “Mkwati Anafika” (vesi 10)—Yesu adzabwela kudzapeleka ciweluzo pamene cisautso cacikulu catsala pang’ono kutha

  • Anamwali ocenjela analoŵa limodzi na mkwati m’nyumba imene munali phwando lacikwati, ndipo citseko cinatsekewa (vesi 10)—Yesu adzasonkhanitsila odzozedwa ake okhulupilika kumwamba, koma osakhulupilika sadzalandila mphoto yawo ya kumwamba

Fanizo limeneli siliphunzitsa kuti odzozedwa ambili adzakhala osakhulupilika cakuti padzafunika ena owaloŵa m’malo. M’malomwake, ni cenjezo kwa Mkhristu wodzozedwa aliyense kuti ali na ufulu kaya wosankha kukhala maso ndi wokonzeka kapena kukhala wopusa ndi wosakhulupilika. Yesu anati: “Khalani okonzeka.” (Mat. 24:44) Mosasamala kanthu za ciyembekezo cathu, Yesu amafuna kuti tonse tikonzekeletse mitima yathu pa nchito zabwino na kuti tizitsatila miyezo ya kukhalabe maso.

Nimaonetsa bwanji kuti ndine wogalamuka?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani