Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
AUGUST 6-12
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 17-18
“Muzionetsa Kuyamikila”
nwtsty mfundo zounikila pa Luka 17:12, 14
amuna 10 akhate: M’nthawi za Baibo, anthu odwala khate anali kukhala moyandikana ambili kapena m’tumagulu. Anali kucita izi kuti azithandizana mosavuta. (2 Maf. 7:3-5) Koma Cilamulo ca Mulungu cinali kufuna kuti akhate azikhala kwa okha. Wakhate anafunikilanso kucenjeza anthu akafika pafupi nawo, mwa kufuula kuti: “Wodetsedwa, wodetsedwa!” (Lev. 13:45, 46) Potsatila Cilamulo, akhatewo anaima capatali na Yesu.—Onani Mat. 8:2.
mukadzionetse kwa ansembe: Pokhala pansi pa Cilamulo, Yesu Khristu ali padziko lapansi anali kulemekeza unsembe wa Aroni. Ndiye cifukwa cake anauza akhate amene anawacilitsa kuti akaonane na wansembe. (Mat. 8:4; Maliko 1:44) Malinga na Cilamulo ca Mose, wansembe ndiye anali kutsimikizila kuti munthu wakhate wapola. Conco, wakhate wocilitsidwayo anali kuyenda ku kacisi kukapeleka nsembe kapena mphatso. Mphatsozo zinali mbalame zamoyo ziŵili zosadetsedwa, nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiila kwambili, na kamtengo ka hisope.—Lev. 14:2-32.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Luka 17:10
opanda pake: Mau ake eni-eni ni, “opanda nchito; osafunika.” M’fanizo lake, Yesu sanatanthauze kuti akapolo, amene ni ophunzila ake, azidziona kuti ni opanda nchito kapena osafunika iyai. Pa vesiyi, mau akuti “opanda pake” mu nkhaniyi atanthauza kuti akapolo ayenela kudziona moyenela, mosaona kuti afunika kupatsidwa ulemu wapadela kapena kutamandidwa mwapadela. Akatswili ena amati lingalilo lake la mauwa n’lakuti “ndise akapolo wamba osafunika kupatsidwa ulemu wapadela.”
nwtsty mfundo younikila pa Luka 18:8
cikhulupililo: Kapena kuti “mtundu wa cikhulupililo ici.” Cikhulupililo cimene Yesu anali kukamba pa vesiyi si cikhulupililo wamba, koma ceni-ceni, monga cija ca mkazi wamasiye wochulidwa m’fanizo la Yesu. (Luka 18:1-8) Cikhulupililo cimeneci cingaphatikizepo kukhulupilila mphamvu ya pemphelo, komanso kukhulupilila kuti Mulungu adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa anthu ake osankhidwa. Yesu sanapeleke yankho pa funso limene iye anafunsa kotelo kuti ophunzila ake aganizilepo pa cikhulupililo cawo. Fanizo lokamba za pemphelo na cikhulupililo linali la panthawi yake. Zili zonco cifukwa Yesu anali atangochula za mayeselo amene ophunzila ake anali kudzakumana nawo.—Luka 17:22-37.
AUGUST 13-19
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Luka 19:43
mpanda wazisonga: Kapena kuti “Mpanda wa mitengo yosongoka.” Liu la Cigiriki lakuti khaʹrax limapezeka cabe pa vesiyi m’Malemba Acigiriki Acikhristu. Liuli limatanthauza “mtengo wosongoka kapena umene amaseŵenzetsa pomanga mpanda; mtengo woongoka.” Lingatanthauzenso “mpanda wa asilikali wa mitengo yosongoka.” Mau a Yesu anakwanilitsika mu 70 C.E. pamene Aroma motsogoleledwa na Tito anamanga mpanda wa zisonga, mozungulila Yerusalemu. Panali zifukwa zitatu zimene Tito anamangila mpandawo. Anali kufuna kuti Ayuda alephele kuthaŵa, avomeleze kuti agonja, ndiponso kuti asatuluke kukafu-nafuna cakudya. Kuti asilikali aciroma apeze zomangila mpanda wozungulila Yerusalemu, anali kudula mitengo yonse yozungulila mzindawo.
nwtsty mfundo younikila pa Luka 20:38
pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo: Kapena kuti “pakuti m’maso mwake, onsewo ndi amoyo.” Baibo imaonetsa kuti onse amene ali moyo koma ni otalikilana na Mulungu, ni akufa m’maso mwake. (Aef. 2:1; 1 Tim. 5:6) Mofananamo, colinga ca Yehova coukitsa atumiki ake okondedwa n’cotsimikizilika cakuti iye amawaona ngati kuti ni amoyo.—Aroma 4:16, 17.
AUGUST 20-26
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 21-22
nwtsty mfundo zounikila pa Luka 21:33
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzacoka: Malemba ena amaonetsa kuti kumwamba na dziko lapansi zidzakhalako mpaka kale-kale. (Gen. 9:16; Sal. 104:5; Mlal. 1:4) Conco, tingaone kuti mau a Yesu apa ni okokomeza, kutanthauza kuti ngakhale zinthu zosatheka zitacitika, ndipo kumwamba na dziko lapansi zacoka, mau a Yesu adzakwanilitsikabe. (Yelekezelani na Mat. 5:8.) Komabe, pa vesiyi, kumwamba na dziko lapansi zingatanthauze kumwamba kophiphilitsa na dziko lapansi lophiphilitsa, zimene zimachedwa “kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale” pa Chiv. 21:1.
mau anga sadzacoka ayi: Kapena kuti “ndithudi mau anga sadzacoka ayi.” Mau aŵili a Cigiriki oonetsa kukana amene anawaseŵenzetsa, amatanthauza kukana kwa mtu wagalu. Mau amenewa amaonetsa kuti zimene Yesu anakamba zinali zotsimikizika.
AUGUST 27–SEPTEMBER 2
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 23-24
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Luka 23:31
pamene mtengo uli wauŵisi, . . . mtengowo ukadzauma: Yesu ayenela kuti anali kukamba mtundu wa Ayuda. Mtunduwu unali monga mtengo umene ni wakufa koma ukali wauŵisi, cifukwa pa nthawi imene Yesu anali moyo Ayuda ena anali kukhulupilila mwa iye. Komabe, posapita nthawi Yesu anali kudzaphedwa, ndipo Ayuda okhulupilika anali kudzadzozedwa na mzimu woyela kuti akhale mbali ya Isiraeli wauzimu. (Aroma 2:28, 29; Agal. 6:16) Panthawiyo, Isiraeli wakuthupi anali atafa mwauzimu, n’kukhala ngati mtengo wouma.—Mat. 21:43.
nwtsty zithunzi
Msomali mu fupa la kadendene
Ici ni cithunzi ca fupa la kadendene ka munthu kokhomeleledwa msomali wotalika 11.5 cm. Fupali linafukulidwa mu 1968 ca kum’poto kwa Yeresalemu, ndipo ni lakale m’nthawi za Aroma. Limapeleka umboni wakuti misomali anali kuiseŵenzetsa pakupha munthu mwa kum’khomelela pamtengo. Msomaliwu ungafanane na misomali imene asilikali aciroma anaseŵenzetsa pokhomelela Yesu Khristu pa mtengo. Fupa limeneli analipeza m’bokosi lamwala. M’bokosimo anali kusungilamo mafupa ouma a anthu akufa pambuyo pakuti mnofu wawo unawola. Izi zionetsa kuti munthu amene anali kufela pa mtengo anali kuikiwa m’manda.