LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr18 October masa. 1-6
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
  • Tumitu
  • OCTOBER 1-7
  • OCTOBER 8-14
  • OCTOBER 15-21
  • OCTOBER 22-28
  • OCTOBER 29–NOVEMBER 4
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
mwbr18 October masa. 1-6

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

OCTOBER 1-7

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 9-10

“Yesu Amasamalila Nkhosa Zake”

nwtsty zithunzi

Khola la Nkhosa

Khola la nkhosa linali mpanda umene unali kumangidwa n’colinga cofuna kuteteza nkhosa kwa akawalala na nyama zolusa. Usiku, abusa anali kusungila m’khola nkhosa zawo pofuna kuziteteza. Nthawi za m’Baibo, makola a nkhosa anali kukhala osiyana maonekedwe na kukula kwake, ndipo sanali kukhala na mtenje. Nthawi zambili anali kumangidwa na miyala ndipo anali kukhala na khomo limodzi. (Num. 32:16; 1 Sam. 24:3; Zef. 2:6) Yohane anakamba za kuloŵa m’khola la nkhosa “kudzela pakhomo,” limene panali kukhala “mlonda wa pakhomo.” (Yoh. 10:1, 3) Anthu ambili akaika nkhosa zawo m’khola limodzi, m’kholamo munali kukhala magulu ambili a nkhosa usiku, ndipo mlonda wa pakhomo anali kufunika kukhala maso kuti ateteze nkhosazo. Kukaca m’maŵa, mlonda wa pakhomo anali kuwatsegulila khomo abusa. M’busa aliyense anali kutenga gulu lake la nkhosa mwa kuitana maina a nkhosazo, ndipo nkhosazo zinali kuyadziŵa bwino mawu ya m’busa wawo ndipo zinali kum’londola. (Yoh. 10:3-5) Yesu anakamba za cizoloŵezi cimeneci pofuna kufotokoza mmene iye amasamalilila ophunzila ake.—Yoh. 10:7-14.

w11 5/15 mape. 7-8 pala. 5

Mabanja Acikhristu Ayenela ‘Kukhalabe Maso’

5 Tiyeni tione zimene mutu wa banja ungaphunzile kwa Khristu. M’busa amakhala pa ubwenzi wabwino na nkhosa zake cifukwa ca kudziŵana komanso kukhulupililana. M’busa amadziŵa bwino kwambili nkhosa zake zonse ndipo nkhosa zimam’dziŵa m’busayo na kum’khulupilila. Zimamvela mawu ake na kuwazindikila. Yesu anati: “Nkhosa zanga ndimazidziŵa, izonso zimandidziŵa.” Iye samangodziŵa zinthu zocepa cabe zokhudza mpingo. Palembali, mawu acigiriki amene anawamasulila kuti “kudziŵa” atanthauza “kudziŵa bwino-bwino aliyense payekha.” Conco M’busa Wabwino amadziŵa bwino-bwino nkhosa iliyonse payokha. Iye amadziŵa zimene nkhosa iliyonse ikufuna, zimene ingacite bwino, komanso zofooka zake. Palibe ciliconse cokhudza nkhosa cimene Yesu sadziŵa. Nkhosa nazonso zimam’dziŵa bwino m’busa wawo, ndipo zimakhulupilila kuti iye ni Mtsogoleli wabwino.

cf mape. 124-125 pala. 17

“Sanalankhule Nawo Ciliconse Popanda Fanizo”

17 Ataona zimene nkhosa zimacita, George A. Smith analemba m’buku lake kuti: “Nthawi zina masana tinkakonda kupuma pafupi ndi zitsime ku Yudeya, ndipo abusa atatu kapena anayi ankabwela aliyense ndi nkhosa zake. Nkhosazo zinkasakanikilana ndipo ife tinkadabwa kuti m’busa aliyense adziŵa bwanji nkhosa zake. Koma nkhosazo zikamaliza kumwa madzi ndiponso kuseŵela, m’busa aliyense ankaloŵela kwake-kwake ndi kuitana nkhosa zake. Ndipo nkhosa za m’busa aliyense zinkacoka pagulupo mwadongosolo n’kutsatila m’busa wawo.” (The Historical Geography of the Holy Land) Pamenepa Yesu anagwilitsa nchito fanizo labwino kwambili potsindika mfundo yake yakuti, tikamatsatila ndi kumvela zimene iye amaphunzitsa, “m’busa wabwino” ameneyu adzatisamalila.

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 10:16

kuzitenga: Kapena kuti “kuzitsogolela.” Liwu la Cigiriki lakuti aʹgo limene aseŵenzetsa pa vesiyi, lingatanthauze “kubweletsa (mkati)” kapena “kutsogolela,” kulingana na nkhani yake. Mu mpukutu wina wacigiriki wa zaka za m’ma 200 C.E., anaseŵenzetsa liwu la Cigiriki lofananako lakuti (sy·naʹgo) limene kambili amalimasulila kuti “kusonkhanitsa.” Monga M’busa Wabwino, Yesu amasonkhanitsa, kutsogolela, kuteteza, na kudyetsa nkhosa za khola ili (zimakambidwanso kuti “kagulu ka nkhosa” pa Luka 12:32) komanso nkhosa zina. Nkhosazi zinakhala gulu limodzi motsogoleledwa na m’busa mmodzi. Fanizo limeneli limaonetsa mgwilizano umene otsatila a Yesu anali kudzakhala nawo.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 9:38

anam’gwadila iye: Kapena kuti “anamuŵelamila; anamulemekeza mocita kugona pansi; anamupatsa ulemu.” Liwu la Cigiriki lakuti pro·sky·neʹo akaliseŵenzetsa pokamba za kulambila mulungu, amalimasulila kuti “kulambila.” (Mat. 4:10; Luka 4:8) Koma pa nkhani iyi, munthu amene anabadwa wosaona amene anacilitsidwa, anazindikila kuti Yesu anali kuimilako Mulungu, conco anamugwadila. Iye sanaone Yesu monga Mulungu kapena mulungu, koma monga “Mwana wa munthu,” Mesiya wokhala na ulamulilo waukulu. (Yoh. 9:35) Munthuyo pogwadila Yesu, ayenela kuti anacita zimenezo mofanana na anthu ochulidwa m’Malemba a Ciheberi. Iwo anali kugwada akakumana na aneneli, mafumu, kapena anthu ena oimilako Mulungu. (1 Sam. 25:23, 24; 2 Sam. 14:4-7; 1 Maf. 1:16; 2 Maf. 4:36, 37) Nthawi zambili, kugwada kumene anthu anali kucitila Yesu kunali kuonetsa kuyamikila pa zimene Mulungu anawacitila kapena pa kukoma mtima kwake.—Onani mfundo zounikila pa Mat. 2:2; 8:2; 14:33; 15:25.

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 10:22

Cikondwelelo ca Kupeleka Kacisi: Liwu la Ciheberi la cikondwelelo cimeneci ni Hanuka (chanuk·kahʹ), kutanthauza “kupatulila; kupeleka.” Cikondweleloci cinali kucitika masiku 8, kuyambila pa tsiku la 25 m’mwezi wa Kisilevi kapena kuti cakumapeto kwa mwezi wa December, (onani cigawo 19 mu Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu) pokumbukila kupatulidwanso kwa kacisi wa ku Yerusalemu mu 165 B.C.E. Mfumu ya Asuri yochedwa Antiochus IV Epiphanes anaonetsa kusalemekeza Yehova, Mulungu wa Ayuda, mwa kumuipitsila kacisi. Mwacitsanzo, iye anamanga guwa la nsembe pamwamba pa guwa la nsembe lalikulu, limene poyamba anali kupelekelapo nsembe zopseleza za masiku onse. Pofuna kuipitsilatu kacisi wa Yehova, mu 168 B.C.E pa tsiku la 25 m’mwezi wa Kisilevi, Antiochus anapeleka nsembe ya nkhumba pa guwalo ndipo anatenga supu wa nkhumbayo n’kuuwaza m’kacisi monse. Anashoka mageti a kacisi, kugwetsa mabwalo a ansembe, na kutenga guwa lansembe lagolide, thebulo la mkate wacionetselo, komanso coikapo nyale cagolide. Pambuyo pake, anapatulilanso kacisi wa Yehova kwa mulungu wonyenga wochedwa Zeu wa phili la Olympus. Patapita zaka ziŵili, Judas Maccabaeus analandanso mzindawo na kacisi wake. Kacisiyo atayeletsedwa, anapatulidwanso mu 165 B.C.E., pa tsiku la 25, m’mwezi wa Kisilevi, patapita zaka zitatu pambuyo pakuti Antiochus wapeleka nsembe zosayenela pa guwalo, kwa Zeu. Nsembe zopseleza za tsiku na tsiku zinayambanso kupelekedwa kwa Yehova. M’malemba ouzilidwa, mulibe mawu eni-eni oonetsa kuti Yehova anathandiza Judas Maccabaeus kuti apambane pa nkhondoyi na kumutsogolela kuti abwezeletse kacisi. Komabe, Yehova anaseŵenzetsapo anthu amitundu ina, mwacitsanzo Koresi wa ku Perisiya, kuti akwanilitse colinga ca Mulungu pa kulambila kwake. (Yes. 45:1) Conco m’pomveka kuganiza kuti, mwina Yehova anaseŵenzetsa munthu wa mtundu wa anthu ake okhulupilika pofuna kukwanilitsa colinga cake. Malemba amaonetsa kuti kacisi anafunika kukhalapo ndiponso kugwila nchito kuti maulosi okhudza Mesiya, utumiki wake, na kudzipeleka kwake akwanilitsidwe. Kuwonjezela apo, Alevi anali kufunika kumapelekabe nsembe mpaka pa nthawi imene Mesiya anali kudzapeleka nsembe yaikulu, kupeleka moyo wake kuti apulumutse mtundu wa anthu. (Dan. 9:27; Yoh. 2:17; Aheb. 9:11-14) Otsatila a Khristu sanalamulidwe kuti azicita Cikondwelelo ca Kupeleka Kacisi. (Akol. 2:16, 17) Komabe, palibe umboni uliwonse woonetsa kuti Yesu kapena ophunzila ake anatsutsa za kukondwelela mwambo umenewu.

OCTOBER 8-14

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 11-12

“Tengelani Cifundo ca Yesu”

nwtsty mfundo zounikila pa Yoh. 11:24, 25

Ndikudziŵa kuti adzauka: Marita anaganiza kuti Yesu anali kukamba za ciukililo ca m’tsogolo, pa tsiku lomaliza. Cikhulupililo cake pa nkhani ya kuuka kwa akufa cinali camphamvu. Atsogoleli ena a cipembedzo a m’nthawi yake ochedwa Asaduki, anali kutsutsa zakuti akufa adzauka, olo kuti ciphunzitso cimeneci cimafotokozedwa momveka bwino m’Malemba ouzilidwa. (Dan. 12:13; Maliko 12:18) Asaduki anali kukhulupilila kuti mzimu sukufa, koma umapitiliza kukhala na moyo. Komabe, Marita anali kudziŵa kuti Yesu anali kuphunzitsa za ciyembekezo ca kuuka kwa akufa. Anali kudziŵanso kuti Yesu anaukitsapo anthu ena ngakhale kuti panalibe amene anakhala m’manda kwa nthawi yaitali monga Lazaro.

Ine ndine kuuka ndi moyo: Imfa ya Yesu na kuukitsidwa kwake, zinatsegula njila yakuti akufa adzakhalenso na moyo. Pambuyo pakuti Yesu waukitsidwa, Yehova anam’patsa mphamvu zoukitsa akufa komanso zopatsa anthu moyo wosatha. Pa Chiv. 1:18, Yesu anadzicha kuti “wamoyo” amene ali na “makiyi a imfa ndi a Manda.” Conco, Yesu ndiye ciyembekezo ca anthu amoyo komanso akufa. Iye analonjeza kuti adzatsegula manda na kupeleka moyo kwa akufa, kaya okapita kumwamba kukalamulila naye pamodzi kapena kwa odzakhala padziko lapansi, amene ufumu wake wakumwamba udzawalamulila.—Yoh. 5:28, 29; 2 Pet. 3:13.

nwtsty mfundo zounikila pa Yoh. 11:33-35

Kulila: Kapena kuti “kusisima.” Liwu la Cigiriki lakuti “kulila,” kambili limatanthauza kulila motulutsa mawu. Liwu limodzi-modzili linaseŵenzetsedwa pa nthawi ina pamene Yesu analosela za ciwonongeko cokhudza Yerusalemu.—Luka 19:41.

anadzuma . . . ndi kumva cisoni: Kuphatikizidwa kwa mawu aŵiliwa m’citundu cakale coyambilila, kuonetsa kuti Yesu anamva cisoni cacikulu pa nthawiyi. Liwu la Cigiriki lomasulidwa kuti “anadzuma” (em·bri·maʹo·mai) lionetsa kuti anakhudzika kwambili. Koma pa vesiyi liwuli lionetsa kuti Yesu anakhudzika kwambili mumtima cakuti anadzuma. Tanthauzo la mawu a Cigiriki akuti “anavutika mu mtima (ta·rasʹso)” ni kumvela kuipa. Kulingana na zimene katswili wina analemba, pa vesiyi liwuli litanthauza “kucititsa munthu kusautsika mumtima; kukhudzika na kupwetekedwa kapena cisoni cacikulu.” Liwu limodzi-modzili analiseŵenzetsa pa Yoh. 13:21, pofotokoza mmene Yesu anamvelela ataganiza zakuti Yudasi adzamupeleka.—Onani mfundo younikila pa Yoh. 11:35.

mu mtima: Mawu ake-ake ni, “mu mzimu.” Cioneka kuti liwu la Cigiriki lakuti pneuʹma limene anaseŵenzetsa pa vesiyi, lifotokoza mphamvu yosonkhezela imene imatuluka mu mtima wophiphilitsila wa munthu, komanso imene imacititsa munthu kukamba na kucita zinthu mwa njila ina yake.

kugwetsa misozi: Liwu limene anaseŵenzetsa pa vesiyi (da·kryʹo) ni liwu locoka ku dzina la Cigiriki lakuti “misozi” limene analiseŵenzetsa m’Malemba monga: Luka 7:38; Mac. 20:19, 31; Aheb. 5:7; Chiv. 7:17; 21:4. Cioneka kuti malingalilo onse ali pa kugwetsa misozi osati pa kulila motulutsa mawu. M’malemba Acigiriki Acikhristu, liwu la Cigiriki limeneli anangoliseŵenzetsa pa vesiyi cabe, ndipo ni losiyana na limene anaseŵenzetsa pa Yoh. 11:33 (onani mfundo younikila) pofotokoza za kulila kwa Mariya na Ayuda. Yesu anadziŵa kuti adzaukitsa Lazaro, koma cinamukhudza kwambili ataona cisoni cacikulu cimene mabwenzi ake okondedwa anali naco. Cifukwa ca cikondi na cifundo pa mabwenzi akewo, iye anagwetsa misozi pa gulu. Cocitika ici cionetsa bwino kuti Yesu amawamvela cisoni anthu amene amataya okondedwa awo mu imfa yocokela kwa Adamu.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 11:49

mkulu wa ansembe: Pamene Aisiraeli anali kudzilamulila okha, mkulu wa ansembe anali kukhala pa udindo wake kwa moyo wonse. (Num. 35:25) Koma pamene dziko la Isiraeli linali kulamulidwa na Aroma, olamulila osankhidwa na Aromawo ndiwo anali na mphamvu zosankha kapena kucotsa mkulu wa ansembe pa udindo wake. Kayafa, amene anasankhidwa na Aroma, anali kazembe waluso kwambili amene anakhala pa udindo wake kwa zaka zambili kuposa ena onse amene anakhalako pa udindowu. Iye anasankhidwa ca m’ma 18 C.E. ndipo anakhalabe pa udindo wake mpaka ca m’ma 36 C.E. Mwa kukamba kuti Kayafa anali mkulu wa ansembe caka cimeneco, cimene ni caka ca 33 C.E., Yohane ayenela anatanthauza kuti nthawi imene Kayafa anali mkulu wa ansembe, inaphatikizapo caka cosaiŵalika cimene Yesu anapacikidwa.—Onani Cigawo 16 mu Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu kuti mudziŵe kumene kunali nyumba ya Kayafa.

nwtsty mfundo zounikila pa Yoh. 12:42

olamulila: Pa vesiyi, liwu la Cigiriki lakuti “olamulila” liyenela kuti litanthauza mamembala a khoti lalikulu la Ayuda, lochedwa Sanihedrini. Liwuli analiseŵenzetsanso pa Yoh. 3:1 pokamba za Nikodemo, membala wa khotilo.

angawacotse musunagoge: Kapena kuti “kuwapatula; kuwaletsa m’sunagoge.” M’fotokozi wa Cigiriki wakuti a·po·sy·naʹgo·gos anamuseŵenzetsa cabe pa Yoh. 9:22; 12:42, komanso pa 16:2. Munthu akacotsedwa m’sunagoge anali kupewedwa, ndipo anali kuonedwa ngati munthu wacabe-cabe wosafunika. Munthu akasalidwa conco na Ayuda anzake, anali kuvutika kwambili kuti apeze zosoŵa za banja lake. Masunagoge amene anali kuphunzitsilamo anthu, anali kuwaseŵenzetsanso monga makhoti. Makhotiwo anali kukhala na mphamvu zopeleka cilango ca kukwapula kapena kucotsa munthu m’sunagoge.

OCTOBER 15-21

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 13-14

“Ndakupatsani Citsanzo”

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 13:5

kusambitsa mapazi a ophunzila: Ku Isiraeli wakale, anthu anali kuvala nsapato za masanda. Zinali kukhala na capansi na tumalamba toloŵetsamo mapazi, na kena kogwila ku kadenene. Munthu akamayenda anali kumbuwa na fumbi kapena kucita matika poyenda mu msewu kapena m’munda. Conco, unali mwambo wake kuvula nsapato pofuna kuloŵa m’nyumba. Ndipo munthu woceleza akalandila mlendo anali kuonetsetsa kuti mapazi a mlendoyo asambikiwa. M’Baibo muli nkhani zambili zonena za cikhalidwe cimeneci. (Gen. 18:4, 5; 24:32; 1 Sam. 25:41; Luka 7:37, 38, 44) Yesu pofuna kuphunzitsa ophunzila ake mfundo yofunika pa nkhani ya kudzicepetsa na kutumikilana, anasambika mapazi a ophunzilawo mogwilizana na cikhalidwe cimeneci.

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 13:12-14

muyenela: Kapena kuti “muli na udindo wa.” Liwu la Cigiriki limene anaseŵenzetsa pa vesiyi, amaliseŵenzetsanso pa zandalama. Ndipo akaliseŵenzetsa m’lingalilo limeneli, limatanthauza “kukhala na nkhongole ya munthu wina; kubweleka cinthu cinacake kwa munthu.” (Mat. 18:28, 30, 34; Luka 16:5, 7) Pa vesiyi na mavesi ena, analiseŵenzetsa m’lingalilo linanso la kukhala na udindo wocita cinacake.—1 Yoh. 3:16; 4:11; 3 Yoh. 8.

w99 3/1 peji 31 pala. 1

Munthu Wamkulu Koposa Onse Acita Utumiki Wodzicepetsa

Mwa kusambitsa ophunzila ake mapazi, Yesu anapeleka phunzilo lofunika kwambili la kudzicepetsa. Inde, Akhristu sayenela kudziona kukhala ofunika kwambili akumafuna ena kuwatumikila nthaŵi zonse, komanso sayenela kukhumba malo aulemu na kuchuka. M’malo mwake, ayenela kutsatila citsanzo ca Yesu, amene “sanadza kutumikilidwa koma kutumikila, ndi kupeleka moyo wake dipo la anthu ambili.” (Mateyu 20:28) Ndithudi, otsatila a Yesu ayenela kukhala ofunitsitsa kucitilana mautumiki odzicepetsa kwambili wina ndi mnzake.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 14:6

Ine ndine njila, coonadi ndi moyo: Yesu ni njila cifukwa timakwanitsa kukamba na Mulungu m’pemphelo kupitila mwa iye cabe. Komanso, iye ni “njila” yothandiza anthu kukhalanso pa mgwilizano na Mulungu. (Yoh. 16:23; Aroma 5:8) Yesu ni Coonadi cifukwa anali kukamba coonadi na kukhala umoyo wogwilizana na coonadico. Iye anakwanilitsa maulosi ambili amene anaonetsa kuti ali na mbali yofunika kwambili pokwanilitsa colinga ca Mulungu. (Yoh. 1:14; Chiv. 19:10) Maulosi amenewa anakhala “inde [kapena kuti anakwanilitsidwa] kudzela mwa iye.” (2 Akor. 1:20) Yesu ni moyo cifukwa kupitila mwa dipo la nsembe yake, anapangitsa kuti mtundu wa anthu udzapezenso “moyo weniweniwo,” kutanthauza “moyo wosatha.” (1 Tim. 6:12, 19; Aef. 1:7; 1 Yoh. 1:7) Iye adzaonetsanso kuti ni “moyo” podzaukitsa anthu mamiliyoni amene ali na ciyembekezo codzakhala m’Paradaiso kwamuyaya.—Yoh. 5:28, 29.

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 14:12

nchito zazikulu kuposa zimenezi: Apa Yesu sanatanthauze kuti ophunzila ake adzacita zozizwitsa zazikulu kuposa zimene iye anacita. M’malomwake, anazindikila kuti ophunzilawo adzagwila nchito yolalikila na kuphunzitsa kuposa mmene iye anacitila. Otsatila ake anali kudzalalikila m’madela ambili, kudzafikila anthu ambili, ndiponso anali kudzalalikila kwa nthawi yaitali kuposa iye. Mawu a Yesu aonetselatu kuti anali na cidalilo cakuti otsatila ake adzapitiliza nchito yake.

OCTOBER 22-28

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 15-17

“Simuli Mbali ya Dzikoli”

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 15:19

dziko: M’nkhaniyi, liwu la Cigiriki lakuti koʹsmos litanthauza anthu amene satumikila Mulungu, anthu osalungama otalikilana na Mulungu. Ni Yohane yekha amene analemba mawu a Yesu akuti otsatila ake sali mbali ya dzikoli, kapena kuti si a dzikoli. Mfundo imodzi-modziyi inakambidwa kaŵili konse m’pemphelo la Yesu lothela ali na atumwi ake okhulupilika.—Yoh. 17:14, 16.

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 15:21

cifukwa ca dzina langa: M’Baibo, liwu lakuti “dzina” nthawi zina limaimila mwiniwake dzina, mbili yake, na umoyo wake wonse. Ponena za dzina la Yesu, limaimila ulamulilo komanso malo amene Atate wake anamupatsa. (Mat. 28:18; Afil. 2:9, 10; Aheb. 1: 3, 4) Apa Yesu anafotokoza cifukwa cake anthu a ku dziko amacita zinthu motsutsana na otsatila ake: cifukwa amene anam’tuma iye sakumudziŵa. Kudziŵa Mulungu kukanawathandiza kumvetsetsa na kuzindikila cimene dzina la Yesu limaimila. (Mac. 4:12) Izi zinali kuphatikizapo malo a Yesu monga Wolamulila wosankhidwa na Mulungu, Mfumu ya mafumu, amene anthu onse afunika kugwadila na kumugonjela kuti akapeze moyo wosatha.—Yoh. 17:3; Chiv. 19:11-16; Yelekezelani Sal. 2:7-12.

it-1 peji 516

Kulimba mtima

Akhristu amafunika kukhala olimba mtima kuti asaipitsidwe na makhalidwe kapena zocita za anthu amene amadana na Yehova Mulungu, komanso kuti akhalebe okhulupilika kwa Iye ngakhale kuti dziko limadana nawo. Yesu anauza ophunzila ake kuti: “M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.” (Yoh. 16:33) Mwana wa Mulungu sanayese ngakhale pang’ono kutengela nzelu za dziko. Iye analigonjetsa mwa kusakhala ngati wa ku dziko mwa njila ina iliyonse. Citsanzo cabwino ca Yesu Khristu amene anagonjetsa dziko komanso amene sanalakwitsepo ciliconse, cingathandize munthu kukhala wolimba mtima potengela citsanzo cake pa nkhani ya kusakhala mbali ya dziko kapena kuipitsidwa nalo.—Yoh. 17:16

nwtsty mfundo zounikila pa Yoh. 17:21-23

amodzi: Kapena kuti “ogwilizana.” Yesu anapemphelela otsatila ake oona kuti akhale “amodzi,” ogwilizana pogwila nchito ali na colinga cimodzi, monga mmene iye na Atate wake alili “amodzi,” kuonetsa mgwilizano na maganizo amodzi. (Yoh. 17:22) Pa 1 Akor. 3:6-9, Paulo anafotokoza mgwilizano umenewu kuti ndiwo umene Akhristu adzakhala nawo pogwila nchito na atumiki anzawo komanso na Mulungu.—Onani 1 Akor. 3:8.

nwtsty mfundo zounikila pa Yoh. 17:21-23

akhale mu umodzi weni-weni: Kapena kuti “kukhala ogwilizana kothelatu.” Pa vesiyi, Yesu anagwilizanitsa mgwilizano weni-weni umenewu na kukondedwa na Atate. Izi zigwilizana na Akol. 3:14, imene imati: “Cikondi, . . . cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” Mgwilizano weni-weni umenewu ni wofunika. Koma sutanthauza kuti timalingana pa zinthu zonse monga maluso, zizoloŵezi, na cikumbumtima. M’malomwake, umatanthauza kuti otsatila a Yesu amagwilizana pocita zinthu, pa cikhulupililo, ndiponso pa ciphunzitso.—Aroma 15:5, 6; 1 Akor. 1:10; Aef. 4:3; Afil. 1:27.

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 17:24

maziko a dziko: Liwu la Cigiriki lakuti “maziko” analimasulila kuti “kukhala ndi pakati,” pa Aheb. 11:11, pokamba za “mbewu.” Pa vesiyi, anaseŵenzetsa mawu akuti “maziko a dziko” ndipo cioneka kuti mawuwa atanthauza kubadwa kwa ana kucokela kwa Adamu na Hava. Yesu anagwilizanitsa “maziko a dziko” na Abele, munthu woyamba kuomboledwa komanso woyamba kulembedwa dzina “mu mpukutu wa moyo kuyambila pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” (Luka 11:50, 51; Chiv. 17:8) Mawu a pemphelo la Yesu amenewa opita kwa Atate wake, amatitsimikizila kuti kale-kale Adamu na Hava asanakhale na mbewu—Mulungu anali kumukonda Mwana wake wobadwa yekha.

OCTOBER 29–NOVEMBER 4

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 18-19

“Yesu Anacitila Umboni Coonadi”

nwtsty mfundo zounikila pa Yoh. 18:37

kudzacitila umboni coonadi: Kulingana na mmene mawuwa awaseŵenzetsela m’Malemba Acigiriki Acikhristu, liwu la Cigiriki limene analimasulila kuti “kucitila umboni coonadi” (mar·ty·reʹo) komanso liwu lakuti “umboni” (mar·ty·riʹa; marʹtys) ali na matanthauzo ambili. Mawu onse aŵili aseŵenzetsedwa m’lingalilo la kucitila umboni cinthu cimene unadzionela wekha kapena cimene udziŵa. Koma angaphatikizeponso “kulengeza; kutsimikizila; kukamba zabwino za.” Yesu sanacitile umboni cabe kapena kulengeza coonadi cimene iye anacikhulupilila, koma anakhala na umoyo wogwilizana na coonadi ca m’mawu a ulosi a Atate wake, komanso malonjezo ake. (2 Akor. 1:20) Colinga ca Mulungu mogwilizana na Ufumu wa Mesiya cinafotokozedwa mwatsatane-tsatane. Umoyo wonse wa Yesu pamene anali pa dziko lapansi, kuphatikizapo imfa yake yopeleka nsembe, zinakwanilitsa maulosi onse okhudza iye, kuphatikizapo zocitilidwa cithunzi, kapenanso zocitilidwa citsanzo za m’pangano la Cilamulo. (Akol. 2:16, 17; Aheb. 10:1) Conco mwa mawu na zocita, tingakambe kuti Yesu ‘anacitila umboni coonadi.’

coonadi: Yesu sanali kutanthauza coonadi wamba, koma coonadi conena za colinga ca Mulungu. Mbali yofunika ya colinga ca Mulungu ni yakuti Yesu, “mwana wa Davide,” azitumikila monga Mkulu wa Ansembe komanso monga Wolamulila wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 1:1) Yesu anafotokoza kuti cacikulu cimene anabwelela padziko lapansi, kukhala na moyo padziko lapansi, komanso utumiki wake cinali kudzalengeza coonadi cokamba za Ufumuwo. Angelo analengeza uthenga wofananawo Yesu asanabadwe padziko, komanso pa nthawi ya kubadwa kwake ku Betelehemu wa Yudeya, kumene kunabadwila Davide.—Luka 1:32, 33; 2:10-14.

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 18:38a

Coonadi n’ciani?: Cioneka Pilato anali kufunsa za kukamba zoona cabe, osati “coonadi” cimene Yesu anachula. (Yoh. 18:37) Cikanakhala kuti anali kufunsa za coonadi cimeneci, mosakayikila Yesu akanayankha funsolo. N’kutheka kuti Pilato pofunsa funsolo sanali kufuna yankho, ndipo sanali kukhulupilila coonadi. Zinali monga akukamba kuti, “Coonadi? N’ciani cimeneco? Kulibe coonadi!” Ndipo iye sanayembekezele ngakhale yankho, m’malomwake anangotuluka n’kupita kumene kunali Ayuda.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 19:30

kupeleka mzimu wake: Kapena kuti “anatsilizika; analeka kupuma.” Liwu lakuti “mzimu” (m’Cigiriki, pneuʹma) pa vesiyi ingatanthauze “kupuma” kapena “mphamvu ya moyo.” Tidziŵa zimenezi cifukwa coona mmene anaseŵenzetsela liwu la Cigiriki lakuti ek·pneʹo (mawu ake eni-eni ni “kufuza”) pa lemba la Maliko 15:37 komanso pa Luka 23:46 (pamene anamasulila kuti “anatsilizika,” kapena kuti, “anafuza kothela” kulingana na mawu a mu mfundo zounikila pa mavesi amenewa). Ena amakamba kuti mawu a Cigiriki amene anawamasulila kuti “kupeleka,” atanthauza kuti Yesu mwa kufuna kwake analeka kulimbikila kuti akhale na moyo, popeza zinthu zonse zinali zitakwanilitsidwa. Iye modzipeleka “anakhuthula moyo wake mu imfa.”—Yes. 53:12; Yoh. 10:11.

nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 19:31

Sabata la tsiku limeneli linali lalikulu: Tsiku la Nisani 15, pambuyo pa tsiku la Pasika, linali kukhala tsiku la Sabata, mosasamala kanthu kuti ni tsiku lanji mu wiki. (Lev. 23:5-7) Ngati Sabata yapadela yakumana na Sabata ya nthawi zonse (tsiku la 7 kwa Ayuda mu wiki, limene linali kuyamba pa Cisanu dzuŵa litaloŵa mpaka pa Ciŵelu dzuŵa litaloŵa), inali kuchedwa Sabata “lalikulu.” Sabata yaikulu imeneyi inali kukonkhana na tsiku la imfa ya Yesu, imene inacitika pa Cisanu. Kucoka mu 29 mpaka mu 35 C.E., caka cokhaco cimene Nisani 14 inakwana pa Cisanu cinali caka ca 33 C.E. Conco, umboni umenewu ucilikiza mfundo yakuti Yesu ayenela kuti anafa pa Nisani 14, mu 33 C.E.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani