UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Yehova Anatiphunzitsa Kulela Bwino Ana Athu
Kodi makolo angaphunzile ciani kwa Atate wawo wakumwamba Yehova, cimene cingawathandize kulela bwino ana awo? Tambitsani vidiyo yakuti Yehova Anatiphunzitsa Kulela Bwino Ana Athu, kenako yankhani mafunso otsatilawa okhudza m’bale Abilio na mlongo Ulla Amorim:
Kodi zimene iwo anapitamo ali ana, zinawathandiza bwanji kukhala makolo abwino?
Ni zosangalatsa zabwanji za pa ubwana zimene ana awo amakumbukila?
Kodi m’bale Abilio na mlongo Ulla analiseŵenzetsa bwanji lemba la Deuteronomo 6:6, 7?
N’cifukwa ciani sanali kungowauza zocita ana awo?
Kodi anawathandiza bwanji ana awo kupanga tsogolo labwino?
Iwo nthawi zonse anali kulimbikitsa ana awo kucita utumiki wanthawi zonse. Kodi izi zinatanthauza kudzimana ciani monga makolo? (bt peji 178 pala. 19)