LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr19 January masa. 1-7
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
  • Tumitu
  • JANUARY 7-13
  • nwtsty mfundo younikila pa Mac. 22:16
  • JANUARY 14-20
  • JANUARY 21-27
  • JANUARY 28–FEBRUARY 3
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
mwbr19 January masa. 1-7

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

JANUARY 7-13

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 21-22

“Cifunilo ca Yehova Cicitike”

bt mape. 177-178 mapa. 15-16

“Cifunilo ca Yehova Cicitike”

15 Pamene Paulo anali kunyumba ya Filipo, kunafika mlendo wina wolemekezeka dzina lake Agabo. Anthu amene anasonkhana kunyumba ya Filipo anali kudziŵa kuti Agabo ni mneneli, ndipo analosela njala yaikulu imene inacitika m’nthawi ya ulamulilo wa Kalaudiyo. (Mac. 11:27, 28) Mwina iwo anadzifunsa kuti: ‘N’cifukwa ciyani Agabo wabwela kuno? Kodi wabwela na uthenga wotani?’ Pamene iwo anamuyang’anitsitsa, iye anatenga lamba wa Paulo amene anali kumanga m’chiuno ndipo anali kutha kusungamo ndalama na zinthu zina. Atatelo, Agabo anadzimanga miyendo na manja ndi lambayo. Kenako ananena uthenga woopsa wakuti: “Mzimu woyela wati, ‘Mwiniwake wa lambayu, Ayuda adzamumanga conci ku Yerusalemu ndi kumupeleka m’manja mwa anthu a mitundu ina.’”—Mac. 21:11.

16 Ulosiwu unatsimikizila kuti Paulo apita ku Yerusalemu. Unasonyezanso kuti nchito yake yolalikila kwa Ayuda ikacititsa kuti apelekedwe “m’manja mwa anthu a mitundu ina.” Ulosiwu unawakhudza kwambili anthu amene anali pamalowo ndipo Luka analemba kuti: “Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi anthu akumeneko, tinayamba kucondelela Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. Koma Paulo anayankha kuti: ‘N’cifukwa ciani mukulila ndi kunditayitsa mtima? Dziŵani kuti ine ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha, komanso kukafa ku Yerusalemu cifukwa ca dzina la Ambuye Yesu.’”—Mac. 21:12, 13.

bt peji 178 pala. 17

“Cifunilo ca Yehova Cicitike”

17 Taganizani zimene zinacitika. Luka pamodzi na abalewo anacondelela Paulo kuti asapite ku Yerusalemu ndipo ena anali kulila. Popeza kuti abalewo anasonyeza kuti anali kumudela nkhawa, Paulo mokoma mtima anawauza kuti ‘akumutayitsa mtima.’ Malinga ndi mmene Mabaibulo ena anagwilitsila nchito mawu acigiriki amene anawamasulila kuti ‘kutayitsa mtima,’ anthuwo “ankaswa mtima” wake. Komabe, iye anali wotsimikiza ndi mtima wonse, ndipo mofanana ndi mmene zinalili pamene anakumana na abale ku Turo, sakanalola kuti asinthe maganizo ake cifukwa coti abale akumucondelela kapena akumulilila. M’malomwake, anawafotokozela cifukwa cake ayenela kupita. Apatu Paulo anasonyeza kuti anatsimikiza komanso anali wolimba mtima. Mofanana ndi Yesu, Paulo anatsimikiza na mtima wonse kupita ku Yerusalemu. (Aheb. 12:2) Iye sanacite zimenezi n’colinga coti afele cikhulupililo cake, koma ngati zimenezo zikanacitika, iye akanaona kuti ndi mwayi kufa monga wotsatila wa Yesu Khristu.

bt peji 178 pala. 18

“Cifunilo ca Yehova Cicitike”

18 Kodi abalewo anayankha bwanji Paulo atawauza zimenezi? Anayankha mwaulemu, cifukwa Luka analemba kuti: “Titalephela kumusintha maganizo, tinangovomeleza ndi kunena kuti: ‘Cifunilo ca Yehova cicitike.’” (Mac. 21:14) Abale amene anali kucondelela Paulo kuti asapite ku Yerusalemu sanaumilile maganizo awo. Iwo anamvetsela zimene Paulo ananena ndipo anangovomeleza. Abalewo anadziŵa cifunilo ca Yehova ndipo analola kuti cicitike ngakhale kuti zimenezo zinali zovuta kwa iwo. Paulo anapitiliza ulendo wopita ku Yerusalemu ndipo zimene zinacitika kumeneko, patapita nthawi zinacititsa kuti pamapeto pake aphedwe. Paulo anaona kuti zikanakhala bwino ngati anthu amene anali kumukondawo akanapanda kumunyengelela kuti asapite ku Yerusalemu.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

bt mape. 184-185 mapa. 10-12

“Mvetselani Mawu Anga Odziteteza”

10 Komabe, Paulo anasonyeza kuti anali kuwamvetsa anthu amene anali kutsatila miyambo ina yaciyuda monga kupewa kugwila nchito pa tsiku la Sabata kapena kupewa kudya zakudya zina. (Aroma 14:1-6) Ndipo iye sanaike malamulo okhudza mdulidwe. Mwacitsanzo, Paulo anadula Timoteyo pofuna kupewa kukhumudwitsa Ayuda amene anali kudziŵa kuti bambo ake anali Mgiriki. (Mac. 16:3) Munthu aliyense anali na ufulu wosankha kudulidwa kapena ayi. N’cifukwa cake Paulo anauza Agalatiya kuti: “Kudulidwa kapena kusadulidwa zilibe phindu, koma cikhulupililo cimene cimagwila nchito kudzela m’cikondi.” (Agal. 5:6) Komabe, kunali kulakwa kuti munthu adulidwe potsatila Cilamulo kapena poganiza kuti zimenezo n’zofunika kuti azikondedwa na Yehova cifukwa wocita zimenezi akanasonyeza kuti alibe cikhulupililo.

11 Akhristu aciyuda anakhumudwa kwambili ngakhale kuti mphekesela zimene anamva zinali zabodza. Motelo akulu analangiza Paulo kuti: “Tili ndi amuna anayi amene anacita lumbilo. Utenge amuna amenewa ndipo ukacite mwambo wa kudziyeletsa pamodzi ndi iwo. Uwalipilile zonse zofunika, kuti amete tsitsi lawo. Ukatelo, aliyense adzadziŵa kuti mphekesela zimene anamva za iwe ndi nkhambakamwa cabe. Adzaona kuti ukucita zinthu motsatila dongosolo, komanso kuti umasunga Cilamulo.”—Mac. 21:23, 24.

12 Paulo akanatha kuuza akuluwo kuti mphekesela zimene anamvazo zinalibe vuto leni-leni, koma Akhristu aciyudawo, amene anali kuumilila kwambili Cilamulo ca Mose, ni amene anali na vuto. Koma iye anali wofunitsitsa kusintha kuti agwilizane ndi zinthu zonse zimene akulu anamuuza kucita, ngati zinthuzo sizikanamucititsa kuphwanya mfundo za Mulungu. M’mbuyomu, iye analemba kuti: “Kwa anthu otsatila cilamulo ndinakhala ngati wotsatila cilamulo kuti ndipindule anthu otsatila cilamulo, ngakhale kuti sindili pansi pa cilamulo.” (1 Akor. 9:20) Pa nkhaniyi, Paulo anacita zinthu momvela akulu a ku Yerusalemu ndipo anakhala “ngati wotsatila cilamulo.” Pocita zimenezi, iye anatipatsa citsanzo cabwino masiku ano kuti tizimvela akulu ndiponso tisamaumilile kucita zinthu mmene ifeyo tikufunila.—Aheb. 13:17.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 22:16

kusamba kuti ucotse macimo ako mwa kuitana pa dzina lake: Kapena kuti “kusamba kuti ucotse macimo na kuitana pa dzina lake.” Macimo a munthu angasambitsidwe osati cabe mwa ubatizo wa madzi, komanso mwa kuitana pa dzina la Yesu. Tingacite izi mwa kukhulupilila Yesu na kuonetsa cikhulupililoco mwa kucita nchito zacikhristu.—Mac. 10:43; Yak. 2:14, 18.

JANUARY 14-20

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 23-24

‘Apatsidwa Mlandu Wakuti ni Wovutitsa Komanso Woukila Boma’

bt peji 191 mapa. 5-6

“Limba Mtima!”

5 Mawu olimbikitsa amene Paulo anauzidwa anali a pa nthawi yake. Tsiku lotsatila, Ayuda oposa 40 “anakonza ciwembu ndi kulumbila mwa kudzitembelela kuti sadya kapena kumwa kanthu kufikila atapha Paulo.” Zikuoneka kuti Ayudawo anatsimikiza ndi mtima wonse kuti aphe mtumwiyu cifukwa anakonza “ciwembu cocita kulumbililaci.” Iwo anali kukhulupilila kuti ciwembu cawoco cikalepheleka, ndiye kuti iwo akhala otembeleledwa kapena cinacake coipa ciwacitikila. (Mac. 23:12-15) Ciwembu cawoco, cimene cinavomelezedwa ndi ansembe aakulu komanso akulu, cinali coti apemphe mkulu wa asilikali kuti Paulo apitenso ku Khoti Lalikulu la Ayuda kuti akapitilize kumufunsa ngati kuti akufuna kumvetsetsa bwino nkhani yokhudza mtumwiyu. Koma aciwembuwo anakonza zoti adikilile Paulo panjila n’kumupha.

6 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo anamva za ciwembuci ndipo anakauza Paulo. Kenako Paulo anauza mnyamatayo kuti akauze Kalaudiyo Lusiya, mkulu wa asilikali. (Mac. 23:16-22) N’zoonekelatu kuti Yehova amakonda acinyamata ngati mwana wa mlongo wa Paulo ameneyu, yemwe sanaculidwe dzina. Acinyamata amenewa amathandiza atumiki ake molimba mtima ndiponso amacita mokhulupilika zilizonse zimene angathe kuti apititse patsogolo nchito ya Ufumu.

bt peji 192 pala. 10

“Limba Mtima!”

10 Ku Kaisareya, Paulo ‘anamusunga m’nyumba ya mfumu Herode ndi kumuyang’anila’ poyembekezela kuti anthu amene anali kumuimba mlandu afike kucokela ku Yerusalemu. (Mac. 23:35) Patapita masiku asanu, kunafika Mkulu wa Ansembe Hananiya, munthu wina wodziŵa kulankhula dzina lake Teritulo komanso akulu ena. Coyamba Teritulo anayamikila Felike cifukwa ca zimene anali kucitila Ayuda, mwina pofuna kumukopa kuti awakondele pa mlanduwo. Kenako polankhulapo za mlanduwo, Teritulo ananena kuti Paulo ndi “wovutitsa kwabasi, ndipo akuyambitsa zoukila boma pakati pa Ayuda onse padziko lapansi kumene kuli anthu. Ndiponso ndi mtsogoleli wa gulu lampatuko wa Anazareti. Iyeyu anayesanso kudetsa kacisi, ndipo tinamugwila.” Ayuda ena “analowelela kumuukila. Iwo anali kunena motsindika kuti zimenezo n’zoonadi.” (Mac. 24:5, 6, 9) Milandu yoyambitsa kuukila boma, kutsogolela gulu loopsa lampatuko ndiponso kudetsa kacisi inali yoopsa kwambili ndipo anthu amene apalamula milandu imeneyi nthawi zina anali kuphedwa.

bt mape. 193-194 mapa. 13-14

“Limba Mtima!”

13 Paulo anatipatsa citsanzo cabwino ca zimene tiyenela kucita ngati anthu atatitengela kwa akulu-akulu a boma kapena oweluza cifukwa ca cikhulupililo cathu n’kumatinamizila milandu yoyambitsa cisokonezo, kuukila boma kapena kutinena kuti tili “m’gulu loopsa lampatuko.” Paulo sanayese kukopa bwanamkubwayo kuti amukonde ponena mawu omusangalatsa ngati mmene Teritulo anacitila. Iye analankhula modekha, mwaulemu ndipo anasankha mawu mwanzelu. Anafotokozanso mfundo zoona komanso zomveka bwino. Paulo ananenanso kuti pa mlanduwu panalibe “Ayuda ena ocokela m’cigawo ca Asia” amene ankamunamizila kuti anadetsa kacisi ndipo mogwilizana ndi malamulo, iye anayenela kuonana nawo kuti amve yekha zimene anali kumunenezazo.—Mac 24:18, 19.

14 Ndipotu Paulo sanasiye kunena za cikhulupililo cake. Molimba mtima, mtumwiyu anabwelezanso kunena za cikhulupililo cake cakuti akufa adzauka, ngakhale kuti nkhani imeneyi ndi imene inayambitsa cisokonezo m’Khoti Lalikulu la Ayuda. (Mac. 23:6-10) Podziteteza, Paulo anatsindika za ciyembekezo cimene anali naco cakuti akufa adzauka. N’cifukwa ciani anacita zimenezi? Cifukwa cakuti iye anali kucitila umboni za Yesu ndiponso zakuti anauka kwa akufa. Koma anthu otsutsawo sanavomeleze zimenezi. (Mac. 26:6-8, 22, 23) Inde, nkhani yaikulu inagona pa kukhulupilila zakuti akufa adzauka, maka-maka kukhulupilila Yesu ndiponso kuti iye anauka kwa akufa.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 23:6

ine ndine Mfarisi: Ena mwa omvetselawo anali kum’dziŵa Paulo. (Mac. 22:5) Ndipo Afarisi a Khoti Yapamwamba ya Ayuda anaona kuti pamene Paulo anakamba kuti ndine mwana wa Afarisi, anali kuvomeleza kuti ngakhale kuti anakhala Mkhristu, panali zinthu zina zofanana pakati pa iwo na iye. Anadziŵanso kuti iye sanali kubisa mbili yake. Koma palembali, pamene Paulo anakamba kuti ni Mfarisi, ayenela kuti anali kungotanthauza kuti zimene iye anali kukhulupilila pankhani ya kuuka kwa akufa, zinali zofanana ndi zimene Afarisi anali kukhulupilila. Mwa kukamba zimenezo, Paulo anathandiza Afarisi kuona kuti zinthu zina zimene iye anali kukhulupilila zinali zofanana na zimene iwo anali kukhulupilila. Mwacionekele iye anakhulupilila kuti kukamba mfundo imeneyo kudzacititsa kuti mamemba ena a Khoti Yapamwamba ya Ayuda amucitile cifundo, ndipo pulani imeneyi inaseŵenza. (Mac. 23:7-9) Mawu a Paulo pano pa Mac. 23:6 agwilizana na mawu amene anakamba nthawi ina pamene anadziteteza pamaso pa Mfumu Agiripa. (Mac. 26:5) Ndipo pamene anali kulembela Akhristu anzake a ku Filipi, Paulo anachulanso za colowa cake monga Mfarisi. (Afil. 3:5) N’zokondweletsanso kudziŵa mmene Akhristu ena amene kale anali Afarisi awafotokozela pa Mac. 15:5.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 24:24

Durusila: Anali mwana wacitatu komanso wamg’ono pa ana aakazi a Herode Agiripa Woyamba, ochulidwa pa Mac. 12:1. Iye anabadwa ca mu 38 C.E. ndipo anali mlongosi wake wa Agiripa Waciŵili na Berenike. Bwanamkubwa Felike anali mwamuna wake waciŵili. Mwamuna wake woyamba anali Mfumu ya Asuri ya ku Emesa, dzina lake Azizu, koma anamusudzula na kukwatiwa na Felike ca mu 54 C.E., pamene anali na zaka pafupi-fupi 16. N’kutheka kuti iye analipo pamene Paulo anali kukamba na Felike za “kulankhula za cilungamo, za kudziletsa, ndi za ciweluzo cimene cikudzaco.” (Mac. 24:25) Pamene Felike analoŵedwa mmalo na Fesito, anasiya Paulo m’ndende cifukwa “ankafuna kuti Ayuda azimukonda.” Anthu ena amaganiza kuti anacita izi kuti akondweletse mkazi wake wacicepele, amene anali mayi waciyuda.—Mac. 24:27.

JANUARY 21-27

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 25-26

“Paulo Apempha Kukaonekela kwa Kaisara Kenako Alalikila Mfumu Herode Agiripa”

bt peji 198 pala. 6

“Ndikupempha Kuti Ndikaonekele kwa Kaisara!”

6 Colinga ca Fesito cofuna kuti Ayuda azimukonda cikanacititsa kuti Paulo aphedwe. Conco pofuna kudziteteza, Paulo anagwilitsa nchito ufulu wake monga nzika ya Roma. Iye anauza Fesito kuti: “Ine ndaimilila kutsogolo kwa mpando woweluzila milandu wa Kaisara, kumene ndiyenela kuweluzidwa. Ayuda sindinawalakwile ciliconse, monga mmene inunso mukuonela . . . Ndikupempha kuti ndikaonekele kwa Kaisara!” Munthu akapempha kukaonekela kwa Kaisara, kawili-kawili zinali zosatheka kusintha pempho limeneli. Fesito anatsindika zimenezi ponena kuti: “Popeza kuti wapempha kukaonekela kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” (Mac. 25:10-12) Popempha kuti akaonekele kwa woweluza waudindo waukulu, Paulo anapeleka citsanzo cabwino kwa Akhristu oona masiku ano. Izi zili conco cifukwa cakuti anthu otsutsa akamayesa kuyambitsa “mavuto mwa kupanga malamulo,” Mboni za Yehova zimagwilitsa nchito malamulo a m’dziko lawo poteteza uthenga wabwino.—Sal. 94:20.

bt mape. 198-201 mapa. 10-16

“Ndikupempha Kuti Ndikaonekele kwa Kaisara!”

10 Mwaulemu, Paulo anathokoza Mfumu Agiripa pomupatsa mwayi wodziteteza pamaso pake, ndipo anavomeleza kuti mfumuyi inali katswili pa miyambo yonse ya Ayuda komanso pa zonse zimene Ayudawo anali kukangana. Kenako Paulo anafotokoza mmene moyo wake unalili poyamba. Iye anati: “Ndinalidi Mfarisi, wa m’gulu lampatuko lotsatila kulambila kwathu mokhwimitsa zinthu kwambili.” (Mac. 26:5) Monga Mfarisi, Paulo anali kuyembekezela kubwela kwa Mesiya. Koma tsopano atakhala Mkhristu, anayamba kulalikila molimba mtima kuti Yesu Khristu ndi Mesiya amene Ayudawo anali kumuyembekezela kwa nthawi yaitali. Paulo anazengedwa mlandu pa tsikuli cifukwa ca cikhulupililo cimene iyeyo komanso anthu amene anamuneneza mlanduwo anali naco. Cikhulupililo cimeneci cinali cokhudza ciyembekezo cimene iwo anali naco coti Mulungu adzakwanilitsa zimene analonjeza makolo awo. Agiripa anacita cidwi ndi zimene Paulo anafotokoza ndipo anafuna kumva zambili.

11 Pofotokoza mmene kale anali kuzunzila Akhristu, Paulo anati: “Inetu ndinali kuganiza mumtima mwanga kuti ndiyenela kucita zambili zotsutsana ndi dzina la Yesu Mnazareti . . . Popeza ndinali nditakwiya nawo kwambili [otsatila a Khristu], ndinafika pa kuwazunza ngakhale m’mizinda yakunja.” (Mac. 26:9-11) Apa Paulo sanali kukokomeza ayi. Anthu ambili anali kudziŵa kuti iye anali kuzunzadi Akhristu mwankhaza kwambili. (Agal. 1:13, 23) Conco mwina Agiripa anadzifunsa kuti, ‘N’ciani cinacititsa kuti munthu ameneyu asinthe?’

12 Mawu a Paulo otsatilawa akupeleka yankho. Iye anati: “Ndinanyamuka ulendo wopita ku Damasiko mwa mphamvu ndi cilolezo ca ansembe aakulu. Koma ndili mumsewu [nthawi ya masana], Inu mfumu, ndinaona kuwala koposa kunyezimila kwa dzuŵa kocokela kumwamba kutandizungulila pamodzi ndi amene ndinali nawo pa ulendowo. Ndiyeno tonse titagwa pansi, ndinamva mawu akundiuza m’Ciheberi kuti, ‘Saulo, Saulo, n’cifukwa ciani ukundizunza ine? Ukungovutika popitiliza kucita ngati nyama imene ikuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosela.’ Koma ine ndinati, ‘Mbuyanga, ndinu ndani kodi?’ Ndipo Ambuye anati, ‘Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza.’”—Mac. 26:12-15.

13 Paulo asanaone masomphenya odabwitsawa, mophiphilitsa iye ‘anali kuponya miyendo yake ndi kumenya zisonga zotosela.’ Paulo anadzivulaza mwauzimu pocita zinthu zotsutsana ndi cifunilo ca Mulungu. Zimene iye anali kucita zinali zofanana ndi zimene nyama yonyamula katundu imacita. Nyamayi imadzivulaza yokha poponya miyendo yake n’kumamenya zisonga zakuthwa zotosela. Paulo asanakhale Mkhristu, anali munthu woona mtima ndithu, koma n’zoonekelatu kuti anali atasoceletsedwa. Conco poonekela kwa iye pamsewu wopita ku Damasiko, Yesu amene anali ataukitsidwa, anam’thandiza kwambili kusintha maganizo.—Yoh. 16:1, 2.

14 Paulo anasinthadi kwambili pa moyo wake. Polankhula ndi Agiripa, iye anati: “Ine sindinacite zinthu zosonyeza kusamvela masomphenya a kumwambawo. Koma kuyambila kwa okhala ku Damasiko ndi ku Yerusalemu, komanso m’dziko lonse la Yudeya ndi kwa anthu a mitundu ina, ndinafikitsa uthenga wakuti alape ndi kutembenukila kwa Mulungu mwa kucita nchito zosonyeza kulapa.” (Mac. 26:19, 20) Kwa zaka zambili, Paulo anakhala akukwanilitsa nchito imene anapatsidwa ndi Yesu Khristu m’masomphenya aja. Kodi zotsatila zake zinali zotani? Ena mwa anthu amene anamvetsela uthenga wabwino umene Paulo anali kulalikila, analapa n’kusiya khalidwe lawo laciwelewele ndiponso locita zinthu mwacinyengo ndipo anayamba kutumikila Mulungu. Anthu amenewo anakhala nzika zabwino ndipo anali kulemekeza malamulo na kuthandizila kuti m’dziko mukhale bata ndi mtendele.

15 Koma Ayuda amene anali kutsutsa Paulo analibe nazo nchito zimenezi. Paulo ananena kuti: “Cifukwa ca zimenezi, Ayuda anandigwila m’kacisi ndipo anafuna kundipha. Komabe, popeza ndinalandila thandizo kucokela kwa Mulungu, ndikupitiliza kucitila umboni kwa anthu ochuka ndi kwa anthu wamba mpaka lelo.”—Mac. 26:21, 22.

16 Ifenso, monga Akhristu oona, tiyenela kukhala “okonzeka nthawi zonse” kuteteza cikhulupililo cathu. (1 Pet. 3:15) Tikamafotokoza zimene timakhulupilila kwa oweluza komanso olamulila, tingacite bwino kutsatila njila imene Paulo anagwilitsa nchito polankhula kwa Agiripa ndi Fesito. N’kutheka kuti anthu audindo angafewetse mitima yawo ngati titawauza mwaulemu mmene coonadi ca m’Baibulo catisinthila ifeyo komanso anthu ena amene anamvetsela uthenga wathu.

bt peji. 202 pala. 18

“Ndikupempha Kuti Ndikaonekele kwa Kaisara!”

18 Koma Paulo anayankha bwanamkubwayo kuti: “Wolemekezeka a Fesito, inetu sindinacite misala ayi, koma ndikulankhula mawu a coonadi ndiponso anzelu. Kunena zoona, inu mfumu amene ndikulankhula nanu mwaufulu cotele, mukudziŵa bwino zimenezi . . . Kodi inuyo, Mfumu Agiripa, mumakhulupilila Zolemba za aneneli? Ndikudziŵa kuti mumazikhulupilila.” Koma Agiripa anayankha kuti: “M’kanthawi kocepa ungathe kundikopa kuti ndikhale Mkhristu.” (Mac. 26:25-28) Kaya Agiripa ananena mawu amenewa moona mtima kapena ayi, n’zoonekelatu kuti mfumuyi inakhudzidwa mtima ndi zimene Paulo ananena.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 26:14

kuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosela: Cisonga cotosela ni ndodo yosongoka yochaila nyama pozitsogolela. (Ower. 3:31) Mawu akuti “kuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosela,” ni mwambi umene umapezeka m’mabuku a Cigiriki. Mwambiwu unacokela pa mmene ng’ombe yaimuna yoching’a imacitila ikaona cisonga cotosela. Posafuna cisongaco, imacimenya zibakela, ndipo zimenezi zimapangitsa kuti idzivulaze. Umu ni mmenenso Saulo analili asanakhale Mkhristu. Mwa kuvutitsa otsatila a Yesu, amene anali kuthandizidwa na Yehova Mulungu, Paulo akanadzivulaza. (Yelekezani na Mac. 5:38, 39; 1 Tim. 1:13, 14.) Pa Mlal. 12:11, “zisonga zobayila ng’ombe” zikuchulidwa m’lingalilo lophiphilitsa. Ndipo ziimila mawu a munthu wanzelu amene amalimbikitsa womvetsela kutsatila uphungu.

nwt matanthauzo a mawu ena

Cisonga Cotosela. Ndodo ya kacitsulo kosongoka imene alimi anali kuseŵenzetsa potsogolela nyama. Cisonga cotosela aciyelekezela na mawu a munthu wanzelu amene angalimbikitse womvetsela kutsatila uphungu wanzelu. Mawu akuti “kuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosela,” anatengedwa ku zimene ng’ombe yaimuna yoching’a imacita ikaona cisonga cotosela. Posafuna cisongaco, imacimenya zibakela ndipo zimenezi zimapangitsa kuti idzivulaze.—Mac. 26:14; Ower. 3:31.

w03 11/15 mape. 16-17 pala. 14

Thandizani Ena Kulabadila Uthenga wa Ufumu

14 Paulo anadziŵa kuti Agiripa anali Myuda dzina lokha. Poona kuti Agiripa anali kudziŵa zaciyuda, Paulo ananena kuti nchito yake yolalikila inali kweni-kweni yokhudza ‘osati kanthu kena koma zimene aneneli ndi Mose ananena kuti zidzafika’ zokhudza imfa ndi kuuka kwa Mesiya. (Machitidwe 26:22, 23) Polankhula mwacidunji kwa Agiripa, Paulo anafunsa kuti: “Mfumu Agiripa, mukhulupilila aneneli kodi?” Agiripa anasoŵa coyankha. Akanayankha kuti sakhulupilila aneneli, akanawononga mbili yake monga Myuda wokhulupilila. Ndipo akanagwilizana ndi maganizo a Paulo, kukanakhala kusonyeza poyela kuti akugwilizana na mtumwiyo ndiponso akanachedwa Mkhristu. Paulo anayankha mwanzelu funso lake lomwe, kuti: ‘Ndidziŵa kuti muwakhulupilila.’ Kodi mtima wa Agiripa unamulimbikitsa kuyankha zotani? Iye anayankha kuti: “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesela Mkhristu.” (Machitidwe 26:27, 28) Ngakhale kuti Agiripa sanakhale Mkhristu, mwacionekele Paulo anamufika pamtima ndi uthenga wake.—Aheberi 4:12.

JANUARY 28–FEBRUARY 3

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 27-28

“Paulo Apita ku Roma”

bt peji 208 pala. 15

“Palibe Aliyense wa Inu Amene Ataye Moyo Wake”

15 N’zacidziŵikile kuti Paulo anali kulalikila kwa anthu ambili m’ngalawamo za “ciyembekezo pa lonjezo limene Mulungu anapeleka.” (Mac. 26:6; Akol. 1:5) Tsopano poona kuti nthawi iliyonse ngalawayo ikhoza kusweka, Paulo anapatsa anthuwo ciyembekezo powatsimikizila kuti apulumuka. Iye anati: “Usiku mngelo . . . , anaima pafupi nane, ndi kunena kuti, ‘Usaope Paulo. Uyenela kukaima pamaso pa Kaisara, ndipo taona! Cifukwa ca iwe, Mulungu mokoma mtima adzapulumutsa onse amene uli nawo pa ulendowu.’” Kenako Paulo anawalimbikitsa kuti: “Conco khalani osangalala amuna inu, pakuti ndikukhulupilila Mulungu kuti zonse zicitika ndendende mmene wandiuzila. Komabe, ngalawa yathuyi iwonongeka pafupi ndi cilumba cinacake.”—Mac. 27:23-26.

bt peji 209 pala. 18

“Palibe Aliyense wa Inu Amene Ataye Moyo Wake”

18 Anthu opulumukawo anapezeka ali pacilumba ca Melita, kum’mwela kwa Sisile. (Onani bokosi yakuti, “Kodi ku Melita Kunali Kuti?”) Anthu apacilumbaco, amene anali kulankhula cinenelo cacilendo, ‘anawasonyeza kukoma mtima kwapadela.’ (Mac. 28:2) Iwo anasonkhela moto alendowo, amene anafika ali onyowa komanso akunjenjemela cifukwa cozizidwa. Motowo unawathandiza kuti afundidweko cifukwa kunali kukuzizila komanso kukugwa mvula ndipo unathandizilanso kuti pacitike cozizwitsa.

bt peji 210 pala. 21

“Palibe Aliyense wa Inu Amene Ataye Moyo Wake”

21 M’delalo munali kukhala munthu wina wolemela amene anali ndi malo aakulu, dzina lake Papuliyo. Mwina iyeyu anali msilikali wamkulu wa Aroma pacilumba ca Melita. Luka anafotokoza kuti Papuliyo anali “munthu . . . wolemekezeka pacilumbaco.” Iye anagwilitsila nchito mawu olondola osonyeza udindo wa Papuliyo. Mawu amenewa anapezekanso m’zolembedwa zinazake ziŵili za ku Melita. Iye analandila bwino kwambili Paulo ndi anzake aja ndipo anawaceleza kwa masiku atatu. Koma bambo ake a Papuliyo anali kudwala. Panonso Luka anafotokoza molondola kwambili za matenda ake pogwilitsa nchito mawu azacipatala. Iye analemba kuti bambowo “anali cigonele akuvutika ndi malungo komanso kamwazi.” Paulo anapemphela n’kusanjika manja ake pa bambowo ndipo anacila. Anthu apacilumbaco anagoma kwambili ataona zimenezi ndipo anayamba kubweletsa odwala ena kuti adzacilitsidwe. Iwo anabweletsanso mphatso zoti zithandize Paulo ndi anzake aja pa ulendo wawo.—Mac. 28:7-10.

bt peji 213 pala. 10

‘Kucitila Umboni Mokwanila’

10 Gulu la anthu apaulendowo litafika ku Roma, “Paulo analoledwa kumakhala yekha ndi msilikali womulondela.” (Mac. 28:16) Akaidi osaopsa kwambili nthawi zambili anali kuwamangilila ndi unyolo kwa msilikali wowalondela kuti asathawe. Ngakhale kuti Paulo anamangidwa mwanjila imeneyi, iye anali mlaliki wa Ufumu ndipo unyolowo sunamulepheletse kulalikila. Conco, iye atangopuma masiku atatu okha, anaitanitsa akulu-akulu a Ayuda ku Roma kuti amudziŵe komanso kuti awalalikile.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 27:9

kusala kudya kwa tsiku la mwambo wophimba macimo: Kapena kuti “kusala kudya kwa m’malanga.” Mawu ake eni-eni ni “kusala kudya.” Liwu la Cigiriki lakuti “kusala kudya” limatanthauza kusala kudya kochulidwa mu Cilamulo ca Mose, kumene ni kusala kudya kwa caka ciliconse kumene kugwilizana kwambili na tsiku la mwambo wophimba macimo, umene umachedwanso Yom Kippur (mu Ciheberi, yohm hak·kip·pu·rimʹ, “tsiku lophimba [macimo]”). (Lev. 16:29-31; 23:26-32; Num. 29:7) Liwu lakuti “kudzisautsa,” limene anali kuliseŵenzetsa pokamba za Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, nthawi zambili limaphatikizapo kucita zinthu zosonyeza kudzimana kothelatu, monga kusala kudya. (Lev. 16:29) Mawu akuti “kusala kudya” a pa Mac. 27:9 aonetsa kuti kudzisautsa kumene kunali kucitika pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, kunali kuphatikizapo kusala kudya. Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo linali kucitika ca kumapeto kwa September kapena kumayambililo kwa October.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 28:11

Ana Amapasa a Zeu: Kulingana na zimene Agiriki na Aroma amakhulupilila, “ana amapasa a Zeu” (mu Cigiriki, Di·oʹskou·roi) anali Kasitolo ndi Polakisi, ndipo anawa anali mapasa a mulungu Zeu (Jupiter) na Mfumukazi ya ku Sparta yochedwa Leda. Anthu anali kukhulupilila kuti anawa amateteza oyendetsa ngalawa, na kuwapulumutsa pakacitika zoopsa panyanja. Kuchulidwa kwa cizindikilo ca kutsogolo kwa ngalawa, kuonetsa kuti wolembayo anaona zinthuzo na maso ake.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani