LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 March tsa. 7
  • Seŵenzetsani Mavidiyo Pophunzitsa Anthu Baibo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Seŵenzetsani Mavidiyo Pophunzitsa Anthu Baibo
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mavidiyo Pophunzitsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Kubweleza Cigawo 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Zamkati
    Galamuka!—2019
  • Seŵenzetsani Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mu Ulaliki
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 March tsa. 7
Mlongo akutambitsa vidiyo munthu amene amaphunzila naye Baibo

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Seŵenzetsani Mavidiyo Pophunzitsa Anthu Baibo

Zinthu zooneka zimathandiza munthu kukumbukila na kumvetsetsa zimene anaphunzila. Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova, anaseŵenzetsa zinthu zooneka pophunzitsa mfundo zofunika. (Gen. 15:5; Yer. 18:1-6) N’zimenenso Yesu, Mphunzitsi Waluso anacita. (Mat. 18:2-6; 22:19-21) Ndiye cifukwa cake mavidiyo akhala njila yophunzitsila yogwila mtima kwambili m’zaka zaposacedwa. Kodi mavidiyo mumawaseŵenzetsa mokwanila pophunzitsa anthu amene mumaphunzila nawo Baibo?

Pakonzedwa mavidiyo 10, otithandiza pophunzitsa nkhani za m’bulosha yakuti, Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. Mitu ya mavidiyo amenewo imagwilizana na mafunso amene ali m’zilembo zakuda kwambili m’bulosha imeneyi. Bulosha ya pa webusaiti ili na malinki otikumbutsa pamene tingatambitse mavidiyowo. Kuwonjezela apo, mavidiyo ena amafotokoza mfundo zowonjezela pa mfundo zopezeka m’zofalitsa zophunzitsila za mu Thuboksi yathu.

Kodi pali nkhani ina ya m’Baibo imene ingakhale yovuta kumvetsetsa pokambilana na wophunzila Baibo? Kodi wophunzila Baibo wanu akukumana na mayeselo enaake? Sakilani mavidiyo pa jw.org® kapena pa JW Broadcasting® amene angamuthandize. Mungacite bwino kutamba imodzi mwa mavidiyo amenewo pamodzi na wophunzilayo, kenako muikambilane.

Mwezi uliwonse kumatuluka mavidiyo atsopano. Pamene muyatamba, ganizilani mmene mungayaseŵenzetsele pophunzitsa ena.

MAVIDIYO OTHANDIZILA PA NKHANI ZA M’BULOSHA YA UTHENGA WABWINO

  • Vidiyo yakuti Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?

    Phunzilo 2

    Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?

  • Vidiyo yakuti Ndani Analemba Baibulo?

    Phunzilo 3

    Ndani Analemba Baibulo?

  • Vidiyo yakuti Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona?

    Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona?

  • Vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Yesu Anafa?

    Phunzilo 4

    N’cifukwa Ciani Yesu Anafa?

  • Vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?

    Phunzilo 5

    N’cifukwa Ciani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?

  • Vidiyo yakuti Kodi Akufa Ali mu Mkhalidwe Wabwanji?

    Phunzilo 6

    Kodi Akufa Ali mu Mkhalidwe Wabwanji?

  • Vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

    Phunzilo 7

    Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

  • Vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?

    Phunzilo 8

    N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?

  • Vidiyo yakuti Kodi Mulungu Amavomeleza Kulambila Kulikonse?

    Phunzilo 10

    Kodi Mulungu Amavomeleza Kulambila Kulikonse?

  • Vidiyo yakuti Kodi Mulungu amamva mapemphelo onse?

    Phunzilo 12

    Kodi Mulungu amamva mapemphelo onse?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani