LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 September masa. 3-16
  • Seŵenzetsani Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mu Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Seŵenzetsani Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mu Ulaliki
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Motsogozela Phunzilo la Baibo Poseŵenzetsa Buku la “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!”
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mmene Tingagwilitsile Nchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 September masa. 3-16
M’bale na mkazi wake akuseŵenzetsa bulosha yakuti “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!” polalikila munthu pa malo okwelela basi.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Seŵenzetsani Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mu Ulaliki

Ndife okondwa kukhala na bulosha komanso buku latsopano, zoseŵenzetsa potsogoza maphunzilo a Baibo! Tipempha Yehova kuti atidalitse pamene tikuyesetsa kupanga ophunzila ambili. (Mat. 28:18-20; 1 Akor. 3:6-9) Kodi tiyenela kuziseŵenzetsa bwanji zida zatsopano zimenezi?

Buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, maphunzilo a Baibo okambilana komanso zocita, lili na njila yatsopano ya kaphunzitsidwe. Conco pokonzekela ndiponso potsogoza maphunzilo a Baibo, muyenela kutsatila malangizo awa:a

  • Ŵelengani nkhaniyo na kukambilana mafunso

  • Ŵelengani malemba akuti “ŵelengani,” ndipo thandizani wophunzila Baibo kudziŵa mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’malembawo

  • Onetsani mavidiyo na kuwakambilana poseŵenzetsa mafunso amene alipo

  • Yesetsani kutsiliza phunzilo lonse pa nthawi imodzi

Mu ulaliki, gaŵilani bulosha coyamba kuti muone ngati munthu ali na cidwi. (Onani bokosi lakuti “Mmene Tingagaŵile Bulosha Yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! pa Ulendo Woyamba.”) Ngati mwatsiliza kuphunzila bulosha, ndipo wophunzilayo afuna kupitiliza kuphunzila, mugaŵileni buku na kupitiliza kuphunzila naye kuyambila pa phunzilo 04. Ngati mumaphunzila na munthu poseŵenzetsa cimodzi mwa zofalitsa zathu zotsogozela maphunzilo, samukilani m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! na kuona pamene pangakhale poyenela kuyambila.

Banja limodzimodzilo likuseŵenzetsa buku lakuti “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!” pophunzitsa munthuyo Baibo panyumba pake.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI TAKULANDILANI KU PHUNIZILO LANU LA BAIBO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi ophunzila adzaphunzila ciani m’buku latsopanoli?

  • N’cifukwa ciani muyenela kuwaonetsa vidiyo imeneyi ophunzila atsopano?

  • Ni zolinga zotani zimene pang’ono-m’pang’ono muyenela kulimbikitsa wophunzila Baibo kudziikila na kuzikwanilitsa?—Onani chati yakuti “Nkhani Yake na Zocita m’Cigawo Ciliconse”

a DZIŴANI IZI: Mbali yakuti “Fufuzani” mungasankhe kuikambilana pophunzila kapena ayi. Ngakhale n’telo, pezani nthawi yoiŵelenga kapena kuonelela vidiyo iliyonse pamene mukonzekela. Mukatelo, mudzadziŵa zimene zingam’cititse cidwi wophunzila wanu na kum’thandiza. Buku la pacipangizo lili na malinki a mavidiyo komanso nkhani zina.

NKHANI YAKE NA ZOCITA M’CIGAWO CILICONSE

 

MAPHUNZILO

NKHANI YAKE

ZOLINGA PA WOPHUNZILA

1

01-12

Onani mmene Baibo ingakuthandizileni, na mmene mungadziŵile Mwiniwake wa mawu a m’Baibo

Limbikitsani wophunzila kuti aziŵelenga Baibo, azikonzekela phunzilo, ndiponso kuti ayambe kupezeka pa misonkhano

2

13-33

Dziŵani zimene Mulungu waticitila, komanso kulambila kumene amavomeleza

Sonkhezelani wophunzila kuti aziuzako ena coonadi, komanso kuti akhale wofalitsa

3

34-47

Dziŵani zimene Mulungu amayembekezela kwa olambila ake

Limbikitsani wophunzila kuti akapatulile moyo wake kwa Yehova na kubatizika

4

48-60

Phunzilani mmene mungakhalilebe mu cikondi ca Mulungu

Phunzitsani wophunzila kusiyanitsa cabwino na coipa, na mmene angapitile patsogolo kuuzimu.

ZIMENE TINGACITE POGAŴLA BULOSHA YAKUTI KONDWELANI NA MOYO KWAMUYAYA! PA ULENDO WOYAMBA

Mofanana na mathilakiti athu, kucikuto cothela ca bulosha imeneyi, kuli funso locititsa cidwi. Yesani kucita zotsatilazi:

  • Funsani funso lokhala na mayankho ocita kusankhapo

  • Ŵelengani yankho ya m’Baibo pa Salimo 37:29

  • Kambilanani mfundo zimene zili pansi pa kamutu kakuti “Ubwino Wokhulupilila Zimenezi.” Ngati nthawi ilola, ŵelengani malemba amene alipo na kufotokozela zithunzi

  • Kambilanani funso lakuti ‘Kodi Tingakhulupililedi Zimene Baibo Imalonjeza?,’ kenako yambitsani phunzilo la Baibo pa phunzilo 01

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani