Mmene Tingagwilitsile Nchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!
Kabuku Katsopano Kanalembedwa Kuti Katithandize Kupanga Maulendo Obwelelako ndi Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo
1. Kodi ndi kabuku katsopano kati kamene kanatuluka pa Msonkhano wa Cigawo wakuti “Tetezani Mtima Wanu!” kamene kanalembedwa kuti katithandize kupanga maulendo obwelelako ndi kuyambitsa maphunzilo a Baibo?
1 Pa Msonkhano wa Cigawo wakuti “Tetezani Mtima Wanu!” Tinasangalala kulandila kabuku katsopano kotithandiza kupanga maulendo obwelelako ndi kuyambitsa maphunzilo a Baibo. Kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu kaloŵa m’malo kabuku kakuti Mulungu Amafunanji? Mofanana ndi kabuku kakuti Mulungu Amafunanji?, kabuku kameneka kali ndi nkhani zifupi-zifupi. Kaamba ka zimenezi, kabukuka kadzatithandiza kuti tizitha kuyambitsa maphunzilo a Baibo acidule panyumba paulendo woyamba. Mosiyana ndi kabuku ka Mulungu Amafunanji, kamene kanali kufotokoza zimene munthu ayenela kucita kuti akhale Mkristu, zimene zimakhala zovuta kuzivomeleza kwa munthu amene wangoyamba kuphunzila Baibo, kabuku katsopanoka kakamba kwambili za uthenga wabwino wopezeka m’Baibo—Mac. 15:35.
2. N’cifukwa ciani kabuku ka Uthenga Wabwino kanalembedwa?
2 N’cifukwa ciani kabuku kameneka kanalembedwa? Abale padziko lapansi akhala akufunsa ngati pangakhale cofalitsa cofeŵa cimene cingakope anthu kuyamba kuphunzila coonadi, m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, limene timagwilitsila nchito potsogoza maphunzilo a Baibo. Anthu amene amacita mantha kuphunzila Baibo mwa kugwilitsila nchito buku, kaŵili-kaŵili amakhala ofunitsitsa kuliphunzila mwa kugwilitsila nchito kabuku. Kuonjezela pamenepa, kabuku ndi kosavuta kutembenuza m’zinenelo zambili.
3. Kodi kabukuka n’kosiyana bwanji ndi zofalitsa zina zophunzitsila Baibo?
3 Mmene Kanalembedwela: Zofalitsa zathu zambili zophunzitsila Baibo, zimalembedwa m’njila yakuti munthu angaziŵelenga payekha ndi kumvetsetsa coonadi popanda wom’thandiza. Kabukuka ndi kosiyanako. Kanalembedwa m’njila yakuti munthu amene aphunzila Baibo aziphunzitsidwa ndi wina wake. Conco, pamene tikagaŵila kwa munthu, tiyenela kuŵelenga ndi kukambilana naye ndime imodzi kapena ziŵili. Ndime zake ndi zazifupi, cakuti mungazikambilane ndi munthu mwacidule panyumba kapena kunchito. Ngakhale kuti ndi bwino kuyambila m’phunzilo 1, mungayambe kuphunzila phunzilo lililonse m’kabukuka.
4. Kodi kabukuka kamatithandiza bwanji kuphunzitsa mwacindunji kucokela m’Baibo?
4 M’zofalitsa zathu zambili, mayankho a mafunso amapezeka m’ndime. Komabe, mayankho ambili m’kabukuka amapezeka m’Baibo. Anthu ambili amafuna kuphunzila kucokela m’Baibo osati m’zofalitsa zathu. Conco, pafupi-fupi malemba onse sanagwidwe mau. Koma malembawo ayenela kuŵelengedwa m’Baibo. Zimenezi zimathandiza ophunzila Baibo kudziŵa kuti zimene akuphunzila zicokela kwa Mulungu.—Yes. 54:13.
5. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti mphunzitsi azikonzekela bwino phunzilo lililonse?
5 Kabukuka sikafotokoza malemba onse. N’cifukwa ciani? Colinga n’cofuna kulimbikitsa wophunzila Baibo kuti azifunsa mafunso ndi kuti mphunzitsi azikhala ndi mpata wogwilitsila nchito luso lake la kuphunzitsa. Conco, n’kofunika kwambili kukonzekela bwino phunzilo lililonse. Koma muyenela kupewa kukamba zambili pocititsa phunzilo. N’zoona kuti timakonda kufotokoza Malemba, koma zimakhala zothandiza kwambili ngati tipatsa mpata wophunzila Baibo kuti afotokoze maganizo ake pa Malemba. Tikamagwilitsila nchito mafunso mwaluso, tingam’thandize kuti amvetsetse tanthauzo la lemba lililonse.—Mac. 17:2.
6. Kodi tingakagwilitsile nchito bwanji kabukuka: (a) kwa anthu amene sakhulupilila Mulungu ndi Baibo? (b) mu ulaliki wa nyumba ndi nyumba? (c) poyambitsa maphunzilo a Baibo paulendo woyamba? (d) pocita maulendo obwelelako?
6 Mofanana ndi zofalitsa zina zophunzitsila Baibo, kabukuka kangagaŵilidwe nthaŵi iliyonse, ngakhale kuti mweziwo tigaŵila zofalitsa zina. Ambili adzakonda kukagwilitsila nchito cifukwa azitha kuyambitsa phunzilo lacidule paulendo woyamba. Komanso, monga mmene anakambila pa msonkhano wa cigawo, kukagwilitsila nchito paulendo wobwelelako kwa anthu amene anaonetsa cidwi “kungapangitse kuti makambitsilanowo akhaledi ogwila mtima!”—Onani mabokosi patsamba 5 mpaka 7.
7. Kodi mungatsogoze bwanji phunzilo la Baibo m’kabukuka?
7 Mmene Tingakagwilitsile Nchito Potsogoza Phunzilo la Baibo: Tingayambe kukambitsilana mwa kuŵelenga funso lili m’zilembo zakuda, limene lili ndi nambala. Ndiyeno, ŵelengani ndime ndi malemba amene ali m’zilembo zopendeka. Gwilitsilani nchito mafunso mwaluso kuti muthandize mwininyumba kumvetsa zimene malemba amatanthauza. Ndiyeno, musanapite pa funso lina, funsani mwininyumba funso limene mwamaliza kukambitsilana lili m’zilembo zakuda, kuti mutsimikize ngati wamvetsetsa. Pa maulendo angapo oyamba, kungakhale bwino kungokambitsilana funso limodzi lili m’zilembo zakuda. M’kupita kwa nthaŵi, mungayambe kukambilana phunzilo lonse.
8. Kodi tiyenela kuchula motani malemba? Ndipo n’cifukwa ciani?
8 Malemba olembedwa kuti “ŵelengani” ndi amene ali ndi mayankho acindunji pa mafunso amene ali m’zilembo zakuda. Pochula lemba, pewani kukamba kuti, “Mtumwi Paulo analemba kuti” kapena, “Onani zimene Yeremiya analosela.” Mwininyumba angaganize kuti tingoŵelenga mau a anthu. Kungakhale bwino kukamba kuti, “Mau a Mulungu amakamba kuti” kapena, Onani zimene Baibo inalosela.”
9. Kodi tiyenela kuŵelenga malemba onse osagwidwa mau potsogoza phunzilo?
9 Kodi tiyenela kuŵelenga malemba onse osagwidwa mau kapena aja okha olembedwa kuti “ŵelengani”? Cidzadalila ndi mkhalidwe panthawiyo. Malemba onse ali ndi colinga. Lemba lililonse limene lili paphunzilo lili ndi mfundo zoyenela kukambitsilana. Koma nthawi zina ngati wophunzila Baibo alibe nthawi yokwanila, cidwi, kapena ngati amavutika kuŵelenga, zingakhale bwino kungoŵelenga malemba olembedwa kuti “ŵelengani.”
10. Ndi liti pamene tingayambe phunzilo m’buku la zimene Baibo imaphunzitsa?
10 Ndi Liti Pamene Tingayambe Phunzilo M’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa?: Pambuyo pakuti takhala ndi makambitsilano angapo ndipo takhala tikuphunzila mokhazikika, tingasankhe kuyamba kutsogoza phunzilo m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa kapena kupitiliza m’kabuku ka Uthenga Wabwino mpaka kukamaliza. Ofalitsa ayenela kuona pamene angayambe kutsogoza phunzilo m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa. Tikayamba kuphunzila buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa, kodi tiyenela kuyamba kuphunzila kumayambililo? Tingaone pamene tingayambile. Ngakhale kuti anthu amasiyana kamvedwe ka zinthu, ophunzila Baibo ambili adzapindula mwa kuphunzila mwakuya m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa, nkhani zimene anaphunzila kale m’kabuku ka Uthenga Wabwino.
11. N’cifukwa ciani tiyenela kugwilitsila nchito bwino kabuku katsopanoka?
11 M’dziko lino limene kaŵili-kaŵili timalandila uthenga woipa, tili ndi mwai waukulu kwambili wolengeza uthenga wabwino koposa, wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila tsopano ndi kuti posacedwapa udzalamulila m’dziko latsopano mmene mudzakhala cilungamo! (Mat. 24:14; 2 Pet. 3:13) Ndife otsimikiza mtima kuti ambili amene akumva uthengawu adzavomeleza mau ouzilidwa akuti: “Mapazi a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapili pobweletsa uthenga wabwino, ndi okongola kwabasi! Munthu yemwe akulengeza za mtendele, yemwe akubweletsa uthenga wabwino wa zinthu zabwino kuposa kale, yemwe akulengeza za cipulumutso, yemwe akuuza Ziyoni kuti: ‘Mulungu wako wakhala mfumu!’” (Yes. 52:7) Tiyeni tigwilitsile nchito kabuku katsopanoka kuti anthu aludzu m’gawo lathu alandile uthenga wabwino wocokela kwa Mulungu!
[Bokosi papeji 5]
Kwa Anthu Amene Sakhulupilila Mulungu ndi Baibo:
● M’madela ena, ofalitsa amaona kuti polalikila akangochula za “Mulungu” ndi “Baibo” anthu samamvetsela uthenga wabwino. Ngati ndi conco, mukamakambitsilana ndi munthu paulendo woyamba, ndi bwino kukambitsilana nkhani zimene anthu amada nazo nkhawa m’dela lanu, monga kufunika kokhala ndi boma labwino, kumene angapeze malangizo othandiza onena za mabanja, ndi zimene zili mtsogolo lao. Mwina kabuku ka Uthenga Wabwino tingakagaŵile pambuyo pakuti takambitsilanapo kangapo za mmene timadziŵila kuti Mulungu aliko ndi zifukwa zimene timakhulupilila kuti Baibo ndi lodalilika.
[Bokosi papeji 6]
Pamene Mulalikila Nyumba ndi Nyumba:
● “Ndabwela pano kuti ndikuonetseni mmene tingadziŵile zimene Mulungu wasungila anthu mtsogolo. Kodi munayamba mwadzifunsapo ngati Mulungu adzakacotsapo mavuto onse? [Yembekezani ayankhe.] Kabuku aka kaonetsa kumene mungapeze yankho la funso ili m’Baibo. [M’patseni kabuku, ndipo ŵelengani ndime yoyamba pa phunzilo 1, kenako muŵelenge Yeremiya 29:11.] Mwaona kuti Mulungu afuna kuti tikhale ndi tsogolo labwino, si conco? [Yembekezani ayankhe.] Ngati mungakonde, mungatenge kabukuka. Nikadzabwelanso, tidzakambilana ndime 2 kuti tikapeze yankho pa funso ili lakuti, ‘Kodi Mulungu adzacotsapo bwanji mavuto padziko lapansi?” (Ngati mwininyumba aoneka kuti ali ndi nthawi yaikulu paulendo woyamba, mungaŵelenga ndi kukambilana ndime 2 ndi malemba atatu amene alipo. Kenako pangani makonzedwe odzabwelelako kukakambitsilana funso laciŵili m’phunzilo limenelo.)
● “Anthu ambili amakonda kupemphela, maka-maka pamene ali ndi mavuto. Kodi inuyo mumapemphela nthaŵi zina? [Yembekezani ayankhe.] Kodi muganiza kuti Mulungu amamva mapemphelo onse? Kapena kodi mapemphelo ena samam’kondweletsa? [Yembekezani ayankhe.] Ndili ndi kabuku kamene kaonetsa mmene tingapezele mayankho a m’Baibo pa mafunso awa. [M’patseni kabuku, ndipo kambilanani ndime yoyamba m’phunzilo 12 ndi kuŵelenga malemba olembedwa kuti “ŵelengani.”] Kodi si cinthu cokondweletsa kudziŵa kuti Mulungu ndi wofunitsitsa kumva mapemphelo athu? Koma kuti pemphelo litipindulitse, tiyenela kudziŵa bwino Mulungu. [Mupite m’phunzilo 2 ndi kumuonetsa tumitu.] Ngati mungakonde, ndingakusiileni kabuku aka, ndipo nthawi ina ndikadzabwela tingaŵelengenso mayankho ena a m’Baibo pa mafunso ocititsa cidwi awa.”
● “Ndabwela pano kukambitsilana ndi inu kanthu kena. Masiku ano anthu amada nkhawa za tsogolo la dzikoli. Kodi inu muganiza kuti zinthu padziko zidzakhala bwino? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambili amadabwa kudziŵa kuti Baibo ili ndi uthenga wabwino umene umatipatsa ciyembekezo. Mafunso ena amene Baibo imayankha ndi awa.” M’patseni kabuku, ndipo m’pempheni kusankha funso patsamba lothela limene angakonde kuti mukambitsilane. Ndiyeno mupite pa phunzilo limenelo, ndi kumuonetsa mmene timacitila phunzilo. Pangani makonzedwe obwelelako kuti mukakambitsilane funso lotsatila m’phunzilo limenelo.
[Bokosi papeji 7]
Yesani Kuyambitsa Phunzilo Paulendo Woyamba:
● “Ndabwela pano kuti ndikambitsilane nanu mwacidule za njila yatsopano yophunzilila Baibo. Kabuku aka kali ndi nkhani 15 zimene zionetsa kumene mungapeze mayankho a mafunso ofunika m’Baibo yanu. [Muonetseni tsamba loyamba ndi lothela.] Kodi munaphunzilapo Baibo? [Yembekezani ayankhe.] Lekani ndikuonetseni mmene nkhani zake zilili zosavuta. [Mupite m’phunzilo 3, ndiyeno mukambilane ndime yoyamba ya funso 3, ndi kuŵelenga Chivumbulutso 21:4, 5. Ngati n’kotheka, kambilanani ndime yotsatila ndi malemba olembedwa kuti “ŵelengani.”] Ngati mungakonde, ndingakusiileni kabuku aka. Bwanji osayesako kuphunzila Baibo m’njila yatsopano imeneyi? Ngati mwaikonda, mungapitilize. Ndikadzabwelanso, tidzakambitsilana phunzilo loyamba. Ndipo phunzilo limenelo ndi lalifupi.”
[Bokosi papeji 7]
Kagaŵileni Paulendo Wobwelelako:
● Pamene tipanga ulendo wobwelelako kwa munthu amene anaonetsa cidwi, tingakambe kuti: “Ndine wosangalala kuti takumananso. Ndakubweletselani kabuku aka kamene kali ndi mayankho a m’Baibo pa mafunso ambili ocititsa cidwi. [M’patseni kabuku, ndipo m’pempheni kuti ayang’ane patsamba lothela.] Kodi ndi nkhani iti imene mungakonde kuti tikambilane? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno pitani pa phunzilo limene wasankha.] Lekani ndikuonetseni mmene kabuku aka kangatithandizile kupeza yankho la m’Baibo.” Muonetseni mmene timacitila phunzilo mwa kukambitsilana ndime imodzi kapena ziŵili ndi malemba olembedwa kuti “ŵelengani.” Umu ndi mmene timaphunzilila Baibo. Musiileni kabuku mwininyumba, ndipo pangani makonzedwe obwelelako. Mukamaliza phunzilo limenelo, mungayambe kukambilana phunzilo lina limene mwininyumba wasankha kapena mungayambe kukambitsilana kuyambila m’phunzilo 1.