Mmene Tingagwilitsile Nchito Kabuku kakuti Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?
Kabuku Katsopano Kanapangidwa Kutithandiza Kutsogolela Ophunzila Baibo ku Gulu
1. Kodi kabuku kakuti Cifunilo ca Yehova kanapangidwa pa zifukwa zitatu ziti?
1 Kodi mwayamba kugwilitsila nchito kabuku kakuti Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano? Colinga ca kabukuka ndi (1) kuthandiza ophunzila Baibo kuti atidziŵe bwino, (2) kuwathandiza kuti adziŵe zimene timacita, ndi (3) kuwaonetsa mmene gulu lathu limacitila zinthu. Kabuku kakuti Cifunilo ca Yehova kali ndi nkhani zazifupi zimene mungakambitsilane ndi munthu kwa mphindi 5 mpaka 10 cabe pambuyo pakuti mwamaliza phunzilo lanu.
2. Fotokozani mmene kabuku kakuti Cifunilo ca Yehova kalili.
2 Mmene Kanapangidwila: Kabukuka kanagaŵidwa m’mbali zitatu, mbali iliyonse ifotokoza za gulu la Yehova monga mmene ndime 1 yanenela. Kalinso ndi mitu 28, ndipo mutu uliwonse unalembedwa monga funso, ndipo tumitu tung’ono-tung’ono totsatila tumene tunalembedwa m’zilembo zakuda tumapeleka yankho la funso limenelo. Kali ndi zithuzi-thunzi za m’maiko oposa 50 zoonetsa mmene nchito yathu imacitikila padziko lonse. Maphunzilo ambili ali ndi mabokosi akuti “Dziŵani zambili,” mmene muli mfundo zimene mungalimbikitsile wophunzila wanu kuzitsatila.
3. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji kabuku kakuti Cifunilo ca Yehova?
3 Mmene Mungakagwilitsile Nchito: Yambani mwa kuonetsa munthu funso la mutu wa phunzilo. Ndiyeno pamene muŵelenga pamodzi phunzilolo, gogomezani mfundo zimene zafotokozedwa pa tumitu tung’ono-tung’ono. Kumapeto, kambilanani funso lobwelelamo lili pansi pa tsamba. Mungaŵelengeletu ndime zonse za phunzilo nthawi imodzi kapena mungaŵelenge ndi kukambilana ndime iliyonse payokha. Muyenela kusankha bwino malemba osagwidwa mau amene mungaŵelenge. Musaiwale kukambilana zithunzi-thunzi ndi mabokosi akuti “Dziŵani zambili.” Nthawi zambili, kabukuka kayenela kuphunzilidwa motsatila manambala a maphunzilo. Ngakhale ndi conco, mungapite pa phunzilo lina lililonse limene wophunzila angafune kuti aphunzile nthawi imeneyo. Mwacitsanzo, ngati msonkhano wadela kapena wacigawo uli pafupi, mungapite pa phunzilo 11.
4. N’cifukwa ciani ndinu osangalala kukhala ndi kabuku katsopano kameneka?
4 Tikamaphunzila Baibo ndi munthu, timam’thandiza kuti adziŵe bwino Atate wathu wa kumwamba. Koma tifunikanso kumuphunzitsa kuti adziŵe gulu la Yehova. (Miy. 6:20) Ndife osangalala kwambili kukhala ndi kabuku katsopano kameneka kotithandiza kucita zimenezi!