Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
MARCH 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 12-14
“Kodi Kuonetsa Cikondi Cacikhristu Kumatanthauza Ciani?”
it-1 55
Cikondi
Cikondi ca pa abale (Mu Cigiriki, phi·la·del·phiʹa, mawu ake eni-eni, ni “kukonda m’bale”) cifunika kukhalapo pakati pa onse mu mpingo wacikhristu. (Aroma 12:10; Aheb. 13:1; onaninso 1 Pet. 3:8) Conco, ubale mu mpingo ufunika kukhala wathithithi kapena kuti wolimba, komanso waubwenzi monga wa m’banja. Olo kuti onse mu mpingo amaonetsana cikondi ca pa abale, akulimbikitsidwa kuti azicionetsa mowonjezeleka.—1 Ates. 4:9, 10.
Liwu la Cigiriki lakuti phi·loʹstor·gos, lotanthauza kukhala na “cikondi ceni-ceni,” amaliseŵenzetsa pokamba za munthu amene ali pa ubwenzi wabwino na wina. Liwu lofananako lakuti sterʹgo, kambili amaliseŵenzetsa pokamba za cikondi cacibadwa ca pakati pa anthu a pacibululu. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kukulitsa khalidwe limeneli. (Aroma 12:10) Paulo anaonetsanso kuti m’masiku otsiliza anthu adzakhala “osakonda acibale awo,” (Mu Cigiriki, aʹstor·goi) ndipo anakamba kuti anthu aconco ni oyenelela imfa.—2 Tim. 3:3; Aroma 1:31, 32.
w09 10/15 8 ¶3
‘Khalani Mwamtendele ndi Anthu Onse’
3 Ŵelengani Aroma 12:17. Paulo anafotokoza kuti anthu akamaticitila zinthu zoipa, tisamawabwezele pocitanso zoipa. Kumvela malangizo amenewa n’kothandiza kwambili maka-maka m’mabanja amene mwamuna ndi mkazi ndi osiyana zipembedzo. Mwamuna kapena mkazi amene ali Mkhristu m’banja loteleli, sayenela kubwezela mawu oipa kapena kucitanso zinthu zoipa pofuna kubwezela. Sitipindula m’njila iliyonse ‘pobwezela coipa ndi coipa.’ Kucita zimenezi kungangocititsa kuti zinthu ziipile-ipile.
w07 7/1 24-25 ¶12-13
“Musabwezele Coipa pa Coipa”
12 Malangizo a Paulo otsatila, onena za mmene tiyenela kucitila zinthu ndi anthu okhulupilila ndiponso osakhulupilila amati: “Musabwezele coipa pa coipa.” Mawu a Paulo amenewa akugwilizana ndi zimene iye ananena poyamba kuti: “Nyansidwani ndi coipa.” Kodi munthu anganene bwanji kuti amanyansidwadi ndi coipa pamene iyeyo akubwezela ena coipa? Kucita zimenezi n’kosemphana kwambili ndi kusonyeza ‘cikondi cosakhala caciphamaso.’ Ndiyeno Paulo anati: “Citani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino.” (Aroma 12:9, 17) Kodi mawuwa tingawagwilitse nchito motani?
13 M’kalata yake kwa Akorinto, Paulo analembamo za cizunzo cimene atumwi anakumana naco. Iye anati: “Takhala ngati coonetsedwa m’bwalo la masewelo ku dziko, kwa angelo, ndi kwa anthu. . . . Pamene akutinenela zacipongwe, timadalitsa; pozunzidwa, timapilila; ponyozedwa, timayankha mofatsa.” (1 Akorinto 4:9-13) Masiku anonso, Akhristu oona akuonetsedwa kwa anthu m’dzikoli. Pamene anthu amaona zinthu zabwino zimene tikucita ngakhale ena akuticitila zinthu mopanda cilungamo, angayambe kumvetsela uthenga wathu wacikhristu.—1 Petulo 2:12.
w12 11/15 29 ¶13
Muzikhululukilana ndi Mtima Wonse
13 Nthawi zina munthu amene si Mkhristu akhoza kukulakwilani. Zikatelo, mwina mukhoza kumuthandiza kudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “‘Ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse cakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse cakumwa. Pakuti mwa kutelo udzamuunjikila makala a moto pamutu pake.’ Musalole kuti coipa cikugonjetseni, koma pitilizani kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino.” (Aroma 12:20, 21) Mukamakhalabe aulemu pamene wina wakuyambani, mukhoza kumuthandiza kuti nayenso ayambe kukhala munthu wabwino. Mukamasonyeza kuti mukumumvetsa ndiponso mukamamucitila cifundo, iye angayambe kufuna kuphunzila Baibulo. Kaya aphunziladi kapena ayi, ulemu wanu ungamuthandize kuti acite cidwi ndi khalidwe lanu.—1 Pet. 2:12; 3:16.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Mmene Tingasankhile Zosangalatsa
5 Ciliconse cimene timacita mu umoyo cimakhudza kulambila kwathu Yehova. Paulo anaunika mfundoyi pamene anati: “Mupeleke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyela ndi yovomelezeka kwa Mulungu.” (Aroma 12:1) Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Nthawi zonse, timafuna kupatsa Yehova zabwino koposa. Aisiraeli akale popeleka nsembe kwa Yehova, anafunikila kupeleka nyama za thanzi labwino. Mulungu sanali kulandila nyama yokhala na cilema. (Levitiko 22:18-20) Cimodzi-modzinso masiku ano. Yehova angakane kulambila kwathu. Motani?
6 Yehova amatiuza kuti: “Mukhale oyela, cifukwa ine ndine woyela.” (1 Petulo 1:14-16; 2 Petulo 3:11) Yehova amangolandila kulambila kumene ni koyela, kosadetsedwa. (Deuteronomo 15:21) Koma sikungakhale koyela ngati ticita zinthu zimene Yehova amanyansidwa nazo, monga zaciwelewele, ciwawa, olo zamizimu. (Aroma 6:12-14; 8:13) Komanso, Yehova amakhumudwa ngati tisangalala na zinthu zimenezi. Pa cifukwa cimeneci, kulambila kwathu kungakhale kodetsedwa komanso kosalandilika kwa Yehova. Ndipo zingawononge ubale wathu na iye.
w08 6/15 31 ¶4
Mfundo Zazikulu za M’kalata ya Aroma
13:1—Kodi “olamulila amene alipowa ali m’malo awo osiyana-siyana mololedwa ndi Mulungu” m’njila yotani? Olamulila a maboma “ali m’malo awo osiyana-siyana mololedwa ndi Mulungu,” m’njila yakuti Mulungu wawalola kuti alamulile, ndipo nthawi zina Mulungu anali atadziŵilatu za ulamulilo wawo. Mwacitsanzo, Baibulo linalosela za anthu ena amene anadzakhala olamulila.
MARCH 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 15-16
“Yang’anani kwa Yehova Kuti Akuthandizeni Kupilila na Kukutonthozani”
“Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”
11 Lemba limene limakamba za cisoni cacikulu cimene Yesu anamvela pamene Lazaro anamwalila, ni lotonthoza kwambili, ndipo n’limodzi cabe mwa malemba ambili-mbili olimbikitsa opezeka m’Mawu a Mulungu. N’cifukwa cake Baibo imati, “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa ciyembekezo cifukwa malembawa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.” (Aroma 15:4) Ngati munafedwa, mungapeze citonthozo pa malemba monga awa:
▪ “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Sal. 34:18, 19.
▪ “Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mawu anu [Yehova] otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”—Sal. 94:19.
▪ “Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ndipo amatilimbikitsa m’njila yosalephela ndiponso anatipatsa ciyembekezo cabwino, mwa kukoma mtima kwakukulu, alimbikitse mitima yanu.”—2 Ates. 2:16, 17.
“Mulole Kuti Kupilila Kumalize Kugwila Nchito Yake”
5 MuzipemphaYehova kuti akuthandizeni. Yehova ndi “Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupilila ndiponso amene amatitonthoza.” (Aroma 15:5) Ndi yekhayo amene amadziŵa bwino kwambili mavuto athu, mmene timamvelela, ndi mmene tinakulila. Cotelo, amadziŵanso bwino zimene timafunikila kuti tipilile. Baibulo limati: “Anthu amene amamuopa adzawacitila zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” (Sal. 145:19) Koma kodi Mulungu amayankha bwanji tikamupempha kuti atipatse mphamvu zotithandiza kupilila?
w14 6/15 9 ¶11
“Uzikonda Yehova Mulungu Wako”
11 Yehova watipatsa ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha. (Aroma 15:13) Ciyembekezo cimene Mulungu watipatsa cimatithandiza kupilila mayeso. Akhristu odzozedwa amene adzaonetsa ‘kukhulupilika kwawo mpaka imfa adzapatsidwa mphoto ya moyo kumwamba’. (Chiv. 2:10) Ndipo Akhristu ena okhulupilika akuyembekezela kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso padziko lapansi. (Luka 23:43) Kodi timamva bwanji kukhala ndi ciyembekezo cimeneci? Timakhala acimwemwe, ndi amtendele, ndiponso timakonda Mulungu amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.”—Yak. 1:17.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w89 12/1 24 ¶3
“Ciyeso ca Kuona kwa Cikondi Canu”
Motsimikizilika, abale awo Akunja angakhale anafulumizidwa kuthandiza ku tsoka lawolo. Ndiiko nkomwe, iwo anali ndi “mangawa” apadela kwa Akhristu okhala m’Yerusalemu. Kodi ku Yerusalemu sikumene kunacokela mbili yabwino kufalikila kupita kwa Akunja? Paulo akupeleka lingalilo lakuti: “Ngati Akhristu Aciyuda anagawana cuma cawo cauzimu ndi Akunja, Akunja ali ndi thayo lowonekela la kuthandizila ku zosoŵa zawo zakuthupi.”—Aroma 15:27, The New English Bible.
it-1 858 ¶5
Kudziŵilatu za Kutsogolo, Kukonzelatu
Mesiya, kapena kuti Khristu, ndiye anali Mbewu yolonjezedwayo, imene kupitila mwa iyo, anthu olungama a mabanja onse padziko lapansi anali kudzadalitsidwa. (Agal. 3:8, 14) “Mbewu” imeneyi, inachulidwa koyamba cipanduko ca mu Edeni citacitika kale, koma Abele asanabadwe. (Gen. 3:15) Izi zinacitika kukali zaka 4,000, “cinsinsi copatulika” cisanavumbulidwe bwino lomwe kuti ‘mbewuyo’ inali Mesiya. Ndithudi, cinakhala “cobisika kuyambila nthawi zakale.”—Aroma 16:25-27; Aef. 1:8-10; 3:4-11.
MARCH 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 1-3
“Kodi Ndimwe Munthu Wakuthupi Kapena Wauzimu?”
Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauzanji?
4 Coyamba, onani maganizo amene munthu wakuthupi amakhala nawo. Anthu ambili m’dzikoli amaika maganizo awo onse pa kukhutilitsa zilakolako za thupi. Paulo anakamba kuti mzimu umenewu, kapena kuti ‘kaganizidwe kameneka tsopano kakugwila nchito mwa ana a kusamvela.’ (Aef. 2:2) Mzimu umenewu umasonkhezela anthu kumangotsatila zimene anthu ambili amaona kuti ndiye zabwino. Conco, ambili amakonda kucita zinthu zimene amaona kuti n’zoyenela kwa iwo, ndipo safuna kutsatila miyezo ya Mulungu. Nthawi zambili, munthu wakuthupi amafunitsitsa kukhala wochuka, amakonda kufuna-funa zinthu zakuthupi, ndiponso amaumilila kuteteza ufulu wake.
5 N’ciani cina cimene cimaonetsa kuti munthu ni wakuthupi? Aliyense amene amacita “nchito za thupi” ni munthu wakuthupi. (Agal. 5:19-21) M’kalata yoyamba imene Paulo analembela mpingo wa ku Korinto, iye anafotokoza makhalidwe ena amene anthu akuthupi amakhala nawo. Makhalidwewo amaphatikizapo kulimbikitsa magaŵano, kukhalila mbali, kutengelana ku makhoti, kusagonjela umutu, ndi kukondetsa kudya na kumwa. Munthu wakuthupi akakumana na ciyeso, amagonja mosavuta. (Miy. 7:21, 22) Yuda anafotokoza za anthu amene adzafooka mpaka kufika pokhala opanda “mzimu wa Mulungu.”—Yuda 18, 19.
Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauzanji?
6 Nanga kodi kukhala “munthu wauzimu” kumatanthauza ciani? Mosiyana ndi munthu wakuthupi, munthu wauzimu amakonda kucita zimene Mulungu amafuna. Anthu okonda zauzimu amayesetsa ‘kutsanzila Mulungu.’ (Aef. 5:1) Izi zitanthauza kuti iwo amayesetsa kuphunzila mmene Yehova amaonela zinthu, ndipo amayamba kuziona mmene iye amazionela. Mulungu ni weni-weni kwa iwo. Mosiyana ndi anthu akuthupi, anthu auzimu amayesetsa kutsatila miyezo ya Yehova pa zocita zawo zonse. (Sal. 119:33; 143:10) Munthu wokonda zinthu zauzimu sacita nchito za thupi, koma amayesetsa kukhala na “makhalidwe amene mzimu woyela” umabala. (Agal. 5:22, 23) Kuti timveketse bwino tanthauzo la mau akuti “munthu wokonda zinthu zauzimu,” ganizilani citsanzo ici: Ngati munthu amadziŵa kwambili zamalonda, tingakambe kuti ni wokonda bizinesi. Nayenso munthu amene amaona zinthu zauzimu kukhala zofunika, amadziŵika monga munthu wokonda zinthu zauzimu.
Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauzanji?
15 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Khristu aliyense payekha? Pa 1 Akorinto 2:16, Baibo imaonetsa kuti tiyenela kukhala na “maganizo a Khristu.” Nalonso lemba la Aroma 15:5 limanena kuti tifunika kukhala na “maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.” Conco, kuti tikhale monga Khristu, tifunika kudziŵa bwino maganizo na makhalidwe ake onse. Kenako, tiyenela kutsatila mapazi ake. Nthawi zonse, Yesu anali kuganizila zinthu zimene zikanalimbitsa ubwenzi wake na Mulungu. Motelo, kutsatila citsanzo ca Yesu kumatithandiza kumuyandikila kwambili Yehova. Izi zionetsa kuti kuphunzila mmene Yesu anali kuganizila n’kofunika kwambili.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 1193 ¶1
Nzelu
Anthu okhala na nzelu za dziko anakana makonzedwe a Mulungu kupitila mwa Khristu, ndipo anawaona kukhala opusa. Olamulila a dziko ngakhale kuti anali kukwanitsa kuweluza moyenelela, iwo anapacika “Ambuye waulemeleloyo.” (1 Akor. 1:18; 2:7, 8) Koma Mulungu anayamba kucititsa nzelu za dziko kukhala zopusa. Anacita izi mwa kucititsa manyazi anthu anzelu, poseŵenzetsa cinthu cimene iwo anaciona kukhala “cinthu copusa ca Mulungu,” komanso poseŵenzetsa anthu amene anali kuonedwa ‘opusa, ofooka, na ocititsa manyazi,’ kuti akwanilitse cifunilo cake cosalepheleka. (1 Akor. 1:19-28) Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Korinto kuti “nzelu ya nthawi ino kapena ya olamulila a nthawi ino” idzawonongedwa. Conco, nzelu imeneyi siinali mbali ya uthenga wauzimu wa mtumwi ameneyu. (1 Akor. 2:6, 13) Paulo anacenjeza Akhristu a ku Kolose kuti asagwidwe na “nzelu za anthu [phi·lo·so·phiʹas, mawu ake eni-eni, ni kukonda nzelu] ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.”—Akol. 2:8; yelekezelani na mavesi 20-23.
w08 7/15 27 ¶6
Mfundo Zazikulu za M’makalata a ku Korinto
2:3-5. Mwina n’zotheka kuti Paulo anali kukayikila ngati angawafike pa mtima omvela ake panthawi imene anali kulalikila ku Korinto, mzinda umene unali likulu la maphunzilo ndi nzelu za Cigiriki. Komabe, sanalole cofooka ciliconse kapena mantha amene anali nawo kumulepheletsa kucita utumiki umene Mulungu anamupatsa. Ifenso tikakumana ndi zinthu zosazoloŵeleka, tisamalole zimenezi kutilepheletsa kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Tiyenela kudalila Yehova ndi mtima wathu wonse ngati Paulo.
MARCH 25-31
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 4-6
“Cofufumitsa Cacing’ono Cimafufumitsa Mtanda Wonse”
it-2 230
Cofufumitsa
Mtumwi Paulo anaseŵenzetsa mawu ophiphilitsa amenewa pamene anali kulamula mpingo wa ku Korinto kuti ufunika kucotsa munthu waciwelewele mu mpingo. Iye anati “Kodi simukudziŵa kuti cofufumitsa cacing’ono cimafufumitsa mtanda wonse? Cotsani cofufumitsa cakaleco, kuti mukhale mtanda watsopano, popeza ndinu opanda cofufumitsa. Pakuti Khristu wapelekedwa monga nsembe yathu ya pasika.” Ndiyeno anafotokoza momveka bwino zimene anatanthauza pokamba mawu akuti “cofufumitsa.” Iye anati; “Cotelo tiyeni ticite cikondweleloci, osati ndi cofufumitsa cakale, kapena cofufumitsa coimila zoipa ndi ucimo, koma ndi mikate yopanda cofufumitsa yoimila kuona mtima ndi coonadi.” (1 Akor. 5:6-8) Apa Paulo anali kukamba tanthauzo lophiphilitsa la Cikondwelelo ca Ayuda ca Mikate Yopanda Cofufumitsa, cimene cinali kucitika pambuyo pa cikondwelelo ca Pasika. Monga mmene ufa waung’ono wokanda wokhala ndi cofufumitsa umafufumitsila mtanda wonse wa mkate, nawonso mpingo monga thupi ungakhale wodetsedwa m’maso mwa Yehova, ngati munthu waciwelewele sacotsedwa mumpingo. Mpingo ufunika kucitapo kanthu kuti ucotse “cofufumitsa” pakati pawo, monga mmene Aisiraeli anali kucotsela cofufumitsa ciliconse m’nyumba zawo pa nthawi ya cikondwelelo cimeneco.
it-2 869-870
Satana
Kodi mawu akuti “mupeleke munthu ameneyu kwa Satana kuti thupilo liwonongedwe” atanthauza ciani?
Polangiza mpingo wa ku Korinto zimene unafunika kucita na munthu wosalapa, amene anali kucita ciŵelewele na mkazi wa atate ake, mtumwi Paulo anati: “Mupeleke munthu ameneyu kwa Satana kuti thupilo liwonongedwe.” (1 Akor. 5:5) Apa Paulo analamula kuti munthuyo acotsedwe mu mpingo na kuleka kuyanjana naye. (1 Akor. 5:13) Kupeleka munthuyo kwa Satana kutanthauza kumucotsa mu mpingo, na kumupeleka ku dziko kumene Satana ndiye mulungu na wolamulila wake. Monga “cofufumitsa cacing’ono” mu “mtanda wonse,” munthuyo anali “thupi” kapena kuti thupi lokhala na cofufumitsa mkati mwa mpingo. Conco, mwa kucotsa munthu waciweleweleyo, mpingo wokonda zinthu zauzimu umenewo, unawononga “thupi” limene linali pakati pake. (1 Akor. 5:6, 7) Mofananamo, Paulo anapeleka Hemenayo na Alekizanda kwa Satana, cifukwa cikhulupililo cawo cinacepa, ndipo cikumbumtima cawo cinaleka kugwila nchito. Pothela pake, cikhulupililo cawo cinathelatu.—1 Tim. 1:20.
lvs 241, mfundo za kumapeto
Kucotsa Munthu mu Mpingo
Munthu akacita chimo lalikulu koma salapa, saloledwa kukhalabe mu mpingo. Iye amacotsedwa mu mpingo. Akacotsedwa, sitimacita naye ciliconse, ndipo timalekelatu kukamba naye. (1 Akorinto 5:11; 2 Yohane 9-11) Makonzedwe a kucotsa munthu mu mpingo, amathandiza kuti dzina la Yehova komanso mpingo, zikhalebe zoyela. (1 Akorinto 5:6) Kucotsedwa mu mpingo, ni cilangonso cimene cingathandize wocimwayo kulapa kuti abwelele kwa Yehova.—Luka 15:17.
▸ Mutu 3, ndime 19
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w09 5/15 24 ¶16
Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikila Anthu”
16 Akhristu akamayesedwa, amakhala “pacionetselo” pamaso pa angelo. (1 Akor. 4:9) Angelo amakondwela kwambili akamaona kukhulupilika kwathu ndipo amasangalala wocimwa akalapa. (Luka 15:10) Angelo amaonanso makhalidwe auzimu a akazi acikhristu. Baibulo limasonyeza kuti “mkazi ayenela kukhala ndi cizindikilo ca ulamulilo pamutu wake cifukwa ca angelo.” (1 Akor. 11:3, 10) Inde, angelo amasangalala kuona akazi acikhristu komanso atumiki onse a Mulungu akucita zinthu mogwilizana ndi dongosolo la Mulungu ndiponso kumvela mutu wawo. Zimenezi zimakumbutsa ana a Mulungu akumwambawa kuti nawonso azikhala omvela.
it-2 211
Lamulo
Lamulo kwa Angelo. Ngakhale kuti angelo ni apamwamba kwambili kuposa anthu, nawonso amamvela malamulo a Mulungu. (Aheb. 1:7, 14; Sal. 104:4) N’cifukwa cake Yehova analamula Satana mdani wake na kumuletsa kucita zinazake. (Yobu 1:12; 2:6) Pokangana na Mdyelekezi, Mikayeli mkulu wa angelo analemekeza Yehova monga woweluza wamkulu, mwa kuuza Mdyelekeziyo kuti: “Yehova akudzudzule.” (Yuda 9; yelekezelani na Zek. 3:2) Yehova Mulungu anaika Yesu Khristu waulemelelo kuti azilamulila angelo. (Aheb. 1:6; 1 Pet. 3:22; Mat. 13:41; 25:31; Afil. 2:9-11) N’cifukwa cake Yesu analamula mngelo kupita kwa Yohane monga mthenga. (Chiv. 1:1) Komabe, pa 1 Akorinto 6:3, mtumwi Paulo anakamba kuti abale auzimu a Khristu, adzaweluza angelo, mwina cifukwa cakuti adzatengako mbali poweluza angelo oipa.