Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
OCTOBER 7-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YAKOBO 3-5
“Muzionetsa Nzelu Yaumulungu”
cl 221-222 ¶9-10
Kodi “Nzelu Yocokela Kumwamba” Ikugwila Nchito M’moyo Wanu?
“Iyamba kukhala yoyela.” Kukhala woyela kumatanthauza kukhala waudongo ndi wosaipitsidwa, osati kunja kokha komanso mkati. Baibo imati nzelu imaloŵa mu mtima, komatu nzelu yakumwamba singaloŵe mu mtima umene waipitsidwa ndi maganizo oipa, zikhumbo zoipa, ndi zolinga zoipa. (Miyambo 2:10; Mateyu 15:19, 20) Komabe, ngati mtima wathu uli woyela, ndiko kuti monga mmene kungakhalile kotheka kwa anthu opanda ungwilo, ‘tidzasiyana naco coipa n’kucita cokoma.’ (Salimo 37:27; Miyambo 3:7) Kodi si koyenela kuti ciyelo ndilo khalidwe loyamba kuchulidwa la nzelu? Indedi, ngati sitili oyela mwamakhalidwe ndi mwauzimu, kodi makhalidwe enawo a nzelu yocokela kumwamba tingawasonyeze motani?
“Nikhalanso yamtendele.” Nzelu yakumwamba imaticititsa kukhala a mtendele, womwe ndi cipatso ca mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Timayesetsa kupewa kusokoneza ‘comangila ca mtendele’ cimene cimagwilizanitsa anthu a Yehova. (Aefeso 4:3) Timacitanso khama kubwezeletsa mtendele pamene wasokonezeka. N’cifukwa ciani zimenezi n’zofunika? Baibo limati: “Khalani mumtendele; ndipo Mulungu wacikondi ndi mtendele akhale pamodzi ndi inu.” (2 Akorinto 13:11) Motelo malinga ngati tipitiliza kukhala mwamtendele, Mulungu wa mtendele adzakhala pamodzi nafe. Mmene timacitila zinthu ndi olambila anzathu zimakhudza mwacindunji ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi tingaonetse motani kuti timakhazikitsa mtendele? Lingalilani citsanzo ici.
cl 223-224 ¶12
Kodi “Nzelu Yocokela Kumwamba” Ikugwila Nchito M’moyo Wanu?
“Yololela.” Kodi kukhala wololela kumatanthauzanji? Malinga n’kunena kwa akatswili a Baibo, mawu acigiriki oyambilila omwe anatembenuzidwa kuti “yaulele [“yololela,” NW]” pa Yakobo 3:17 ndi ovuta kutembenuza. Otembenuza ena agwilitsa nchito mawu monga “yodekha,” “yodziletsa,” ndi “yoganizila ena.” Mawu acigirikiwo kweni-kweni amatanthauza kuti “kuvomeleza.” Kodi tingaonetse motani kuti mbali imeneyi ya nzelu yocokela kumwamba ikugwila nchito mwa ife?
cl 224-225 ¶14-15
Kodi “Nzelu Yocokela Kumwamba” Ikugwila Nchito M’moyo Wanu?
“Yomvela bwino.” Mawu acigiriki otembenuzidwa kuti “yomvela bwino” amapezeka malo okhawa m’Malemba Acigiriki Acikhristu. Malinga n’kunena kwa katswili wina, mawu amenewa “kaŵili-kaŵili amagwilitsidwa nchito ndi anthu ankhondo.” Amapeleka lingalilo la “kukopeka mosavuta” ndiponso “kugonjela.” Munthu amene nzelu yocokela kumwamba ikumutsogolela amagonjela mosavuta ku zimene Malemba akunena. Sadziŵika monga munthu womva zake zokha yemwe safuna kumva mfundo zotsutsana ndi zake. Koma amasintha mofulumila akapatsidwa umboni womveka bwino wa m’Malemba wakuti akucita zinthu zolakwika kapena kuti wasankha zinthu zolakwika. Kodi ndimo mmene ena amakudziŵilani inuyo?
“Yodzala Cifundo ndi Zipatso Zabwino”
“Yodzala cifundo ndi zipatso zabwino.” Cifundo ndi mbali yofunika kwambili ya nzelu yocokela kumwamba, cifukwa nzelu yoteloyo ikunenedwa kuti ndi “yodzala cifundo.” Taonani kuti “cifundo” ndi “zipatso zabwino” zachulidwila pamodzi. Zimenezi n’zoyenela, cifukwa m’Baibo mawu akuti cifundo kaŵili-kaŵili amanena za kuthandiza ena powadela nkhaŵa, kapena kuti kuwamvela cisoni kumene kumabweletsa zipatso zoculuka za zocita zokoma mtima. Buku lina limati cifundo ndi “kumvela cisoni munthu wina amene zinthu zoipa zamucitikila ndi kuyesa kucitapo kanthu pa vutolo.” Motelo munthu amene ali ndi nzelu ya Mulungu sakhala wopanda nsangala, wosasamala za ena, kapenanso sangokhala wophunzila kwambili cabe. Koma iye amakhala waubwenzi, amakhudzika mtima, ndipo amazindikila mofulumila zimene zikucitikila ena. Kodi tingasonyeze motani kuti ndife odzala cifundo?
cl 226-227 ¶18-19
Kodi “Nzelu Yocokela Kumwamba” Ikugwila Nchito M’moyo Wanu?
“Yopanda tsankho.” Nzelu za Mulungu zimapatsa mphamvu yopewa kusankhana mitundu ndi kunyadila mtundu wako. Ngati nzelu zotelozo zikutitsogolela, timayesetsa kuthetsa m’mitima mwathu cizoloŵezi ciliconse cokondela anthu ena. (Yakobo 2:9) Siticitila anthu ena zabwino cifukwa ca kuphunzila kwawo, kupeza bwino kwawo, kapena maudindo awo mumpingo. Ndiponso sitinyoza wolambila mnzathu aliyense, kaya aoneke kuti ndi wosauka motani. Ngati anthu amenewo Yehova wawapatsa cikondi cake, ndithudi iwo amayenela cikondi cathu.
“Yosadzikometsela pamaso.” Mawu acigiriki omwe anenedwa kuti “kudzikometsela pamaso” anganene za “munthu amene anacita nawo seŵelo.” M’nthaŵi zakale, Agiriki ndi Aroma pocita maseŵelo anali kuvala zinyawu. Motelo mawu acigiriki a “kudzikometsela pamaso,” kapena kuti cinyengo, anayamba kugwilitsidwa nchito kwa munthu amene anali kucita zinthu monyengezela, kapena amene anali kumata ena phula m’maso. Mbali imeneyi ya nzelu za Mulungu iyenela kukhudza osati kokha mmene timacitila zinthu ndi olambila anzathu, koma zimenenso timawaganizila.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w08 11/15 20 ¶6
Mfundo Zazikulu za M’makalata a Yakobo ndi Petulo
4:5—Kodi mawu a Yakobo pa vesiyi akucokela pa lemba linalake? Mawu a Yakobo pa vesili sakucokela pa lemba lililonse. Komabe mfundo ya m’mawu ouzilidwa amenewa iyenela kuti ikucokela pa mfundo za m’malemba monga Genesis 6:5; 8:21; Miyambo 21:10 ndi Agalatiya 5:17.
w97 11/15 20-21 ¶8
Cikhulupililo Cimatipanga Kukhala Oleza Mtima ndi Olimbikila Kupemphela
Kuneneza wokhulupilila mnzako ndi chimo. (Yakobo 4:11, 12, NW) Komabe ena amakonda kudzudzula Akhristu anzawo, mwinamwake cifukwa ca mzimu wawo wodzilungamitsa kapena cifukwa cakuti amafuna kudzikweza mwa kunyoza ena. (Salimo 50:20; Miyambo 3:29) Liwu lacigiriki lotembenuzidwa kuti ‘neneza’ limapeleka lingalilo la cidani ndipo limatanthauza kukokomeza mlandu kapena kunamizila. Kumeneku kumakhala kuweluza m’bale moŵaŵa. Kodi ndi motani mmene kumeneku kulili ‘kuneneza kapena kuweluza lamulo la Mulungu’? Eya, alembi ndi Afarisi ‘anakaniza mocenjela lamulo la Mulungu’ naweluza mwa malamulo awo-awo. (Maliko 7:1-13, NW) Mofananamo, ngati taweluza mbale amene Yehova sanamuweluze, kodi sindiye kuti ‘taweluza lamulo la Mulungu’ ndipo mocimwa tatanthauza kuti n’lopeleŵela? Ndipo mwa kudzudzula mbale wathu popanda cifukwa, tingakhale tikulephela kukwanilitsa lamulo la cikondi.—Aroma 13:8-10.
OCTOBER 14-20
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 PETULO 1-2
“Mukhale Oyela”
Dipo—‘Mphatso Yangwilo’ Yocokela kwa Atate
Nanga ise tingaonetse bwanji kuti timaikonda dzina la Yehova? Tingaonetse mwa zocita zathu. Yehova afuna kuti tizikhala oyela. (Ŵelengani 1 Petulo 1:15, 16.) Izi zitanthauza kuti tiyenela kulambila Yehova yekha cabe, ndi kumumvela na mtima wathu wonse. Ngakhale pamene tizunzidwa, timayesetsa mmene tingakwanitsile kukhala moyo mogwilizana ndi mfundo ndi malamulo ake olungama. Mwa zocita zathu zabwino, timaonetsa kuwala kwathu ndi kucititsa kuti dzina la Yehova lilemekezeke. (Mat. 5:14-16) Pokhala anthu oyela, timaonetsa mwa zocita zathu kuti malamulo a Yehova ni abwino, ndi kuti zokamba za Satana n’zabodza. Tikalakwa, timalapa moona mtima ndi kuleka kucita zinthu zosalemekeza Yehova.—Sal. 79:9.
Mmene Tingasankhile Zosangalatsa
Yehova amatiuza kuti: “Mukhale oyela, cifukwa ine ndine woyela.” (1 Petulo 1:14-16; 2 Petulo 3:11) Yehova amangolandila kulambila kumene ni koyela, kosadetsedwa. (Deuteronomo 15:21) Koma sikungakhale koyela ngati ticita zinthu zimene Yehova amanyansidwa nazo, monga zaciwelewele, ciwawa, olo zamizimu. (Aroma 6:12-14; 8:13) Komanso, Yehova amakhumudwa ngati tisangalala na zinthu zimenezi. Pa cifukwa cimeneci, kulambila kwathu kungakhale kodetsedwa komanso kosalandilika kwa Yehova. Ndipo zingawononge ubale wathu na iye.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w08 11/15 21 ¶10
Mfundo Zazikulu za M’makalata a Yakobo ndi Petulo
1:10-12. Angelo analakalaka kusunzumila m’zinthu zozama za coonadi ca Mulungu zimene aneneli a Mulungu akale analemba zokhudza mpingo wa Akhristu odzozedwa. Zinthu zimenezi zinayamba kudziŵika bwino pamene Yehova anayamba kutsogolela mpingowo. (Aef. 3:10) Mofanana ndi angelowo, ifenso tiyenela kucita khama pofufuza “zinthu zozama za Mulungu.” —1 Akor. 2:10.
it-2 565 ¶3
Woyang’anila
Woyang’anila Wamkulu Koposa. Mawu a pa 1 Petulo 2:25, ayenela kuti anagwidwa pa Yesaya 53:6, pokamba za anthu amene anali “ngati nkhosa zosocela.” Ndiyeno Petulo anati: “Koma tsopano mwabwelela kwa m’busa wanu ndi woyang’anila miyoyo yanu.” Woyang’anila amene akuchulidwa apa, ayenela kuti ni Yehova Mulungu, cifukwa anthu amene Petulo analembela mawu amenewa, sanasocele mwa kucoka kwa Khristu Yesu ayi. Koma kupitila mwa Yesuyo, anthuwo anatsogoleledwa kubwelelanso kwa Yehova Mulungu, amene ni M’busa wamkulu wa anthu ake. (Sal. 23:1; 80:1; Yer. 23:3; Ezek. 34:12) Yehova alinso woyang’anila, amene amatifufuza. (Sal. 17:3) Kufufuza kapena kuti kuyendela (m’Cigiriki, e·pi·sko·peʹ) kungatanthauze kupeleka ciweluzo monga mmene zinacitikila kwa anthu okhala ku Yerusalemu m’nthawi ya atumwi, mzinda umene anthu ake sanazindikile kuti nthawi ‘yoyendela inali itakwana’ [m’Cigiriki, e·pi·sko·pesʹ].” (Luka 19:44) Kapena kungatanthauzenso madalitso, monga kwa anthu otamanda Mulungu pa tsiku “lake loyendela” [m’Cigiriki, e·pi·sko·pesʹ].”—1 Pet. 2:12.
OCTOBER 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 PETULO 3-5
“Mapeto a Zinthu Zonse Ayandikila”
“Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphela”
MUNTHU wina amene anali kugwila nchito ya ulonda anati: “Kukhala maso kumavuta kwambili pa nthawi imene kunja kuli pafupi kuca.” Ndithudi, anthu ena amene anagwilako nchito imeneyi angavomeleze mfundo imeneyi. Tingayelekezele zimenezi ndi nthawi imene tikukhalamo. Dziko la Satana lili pafupi kutha, ndipo anthu ambili ali m’tulo tofa nato mwa kuuzimu. N’cifukwa cake Akhristu afunikila kucita khama kuti akhalebe maso. (Aroma 13:12) Kugona mwakuuzimu nthawi ino yamapeto ndi koopsa kwambili. Motelo, tifunika ‘kukhala oganiza bwino’ ndi kumvela malangizo a m’Malemba akuti: “Khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphela.”—1 Pet. 4:7.
w99 4/15 22 ¶3
Mmene Mungadziŵile ndi Kuthetsela Cofooka Ciliconse Cauzimu
Pomalizila pake, nthawi zonse muzikumbukila uphungu wacikondi wa mtumwi Petulo wakuti: “Citsilizilo ca zinthu zonse cili pafupi; cifukwa cake khalani anzelu, ndipo dikilani m’mapemphelo; koposa zonse mukhale naco cikondano ceni-ceni mwa inu nokha; pakuti cikondano cikwililitsa unyinji wa macimo.” (1 Petulo 4:7, 8) N’kosavuta kulola zophophonya zaumunthu—za anthu ena ndi zathu zomwe—kuloŵa m’mitima yathu ndi m’maganizo mwathu ndi kukhala zopinga ndi miyala yokhumudwitsa. Satana amadziŵa bwino kuti anthu ali ndi cofooka cimeneci. Macenjela ake ena ndiwo kupatutsa anthu ndi kuwagonjetsa. Conco, tiyenela kufulumila kukwilila macimo otelowo ndi cikondi cacikulu pa wina ndi mnzake ndi ‘kusam’patsa malo Mdyelekezi.’—Aefeso 4:25-27.
Kucelezana ni Khalidwe Lofunika Kwambili
Cimodzi mwa zinthu zimene zikanawathandiza ni kukhala oceleza. Petulo anawauza kuti “muzicelezana popanda kudandaula.” (1 Pet. 4:9) Liu la Cigiriki lomasulidwa kuti “kuceleza” limatanthauza “kukonda alendo kapena kuwakomela mtima.” Komabe, onani kuti Petulo anauza Akhristu anzake kuti “muzicelezana.” Apa, iye anali kuwalimbikitsa kuti aziceleza Akhristu anzawo. Kodi kukhala oceleza kukanawathandiza bwanji?
Kukanawathandiza kuti akhale ogwilizana ngako. Kodi munakhalapo na mwayi woitanidwa ku nyumba kwa munthu wina kuti mukaceze? Kodi imeneyo siinali nthawi yosangalatsa kwa inu? Nanga bwanji pamene munaceleza abale na alongo ena a mu mpingo mwanu, kodi ubwenzi wanu na iwo sunalimbe? Tikamaceleza abale na alongo athu, timawadziŵa bwino kuposa mmene tingawadziŵile m’zocitika zina. Akhristu a m’nthawi ya Petulo anafunika kukhala ogwilizana pamene zinthu zinali kuipila-ipila. N’cimodzimodzinso kwa ise Akhristu “masiku otsiliza” ano.—2 Tim. 3:1.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w13 6/15 23
Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga
Kodi mawu a pa 1 Petulo 3:19 akuti Yesu “anapita kukalalikila kwa mizimu imene inali m’ndende” amatanthauza ciani?
▪ Mtumwi Petulo ananena kuti mizimu imeneyi ndi imene “inali yosamvela pa nthawi imene Mulungu anali kuleza mtima m’masiku a Nowa.” (1 Pet. 3:20) Apa zikuonekelatu kuti Petulo anali kunena za angelo amene anasankha kugwilizana ndi Satana yemwe ndi mdani wa Mulungu. Nayenso Yuda ananena za “angelo amene sanasunge malo awo oyambilila koma anasiya malo awo okhala.” Ananenanso kuti “Mulungu anawasunga kosatha m’maunyolo, mu mdima wandiweyani kuti adzaweluzidwe pa tsiku lalikulu.”—Yuda 6.
M’masiku a Nowa, kodi angelo ena anacita zinthu ziti zosonyeza kusamvela Mulungu? Cigumula cisanacitike, angelo oipawa anavala matupi a anthu ndipo izi zinali zosemphana ndi colinga ca Mulungu. (Gen. 6:2, 4) Komanso iwo anali kugonana ndi akazi. Izinso zinali zosemphana ndi mmene Mulungu anawalengela. (Gen. 5:2) Pa nthawi yake yoyenelela, Mulungu adzawononga angelo oipawa. Mogwilizana ndi zimene Yuda ananena, panopa iwo ali “mu mdima wandiweyani,” ndipo zili ngati ali m’ndende.
Kodi ndi liti pamene Yesu analalikila “mizimu imene inali m’ndende,” ndipo anacita bwanji zimenezi? Petulo analemba kuti Yesu anacita izi ‘ataukitsidwa monga mzimu.’ (1 Pet. 3:18, 19) Onaninso kuti Petulo ananena kuti Yesu “anapita kukalalikila.” Mawu amenewa akusonyeza kuti iye analalikila mizimuyo Petulo asanalembe kalata yake yoyambayi. Conco zikuoneka kuti nthawi inayake ataukitsidwa, Yesu analengeza kwa mizimu yoipayi za cilango cimene ikuyenela kulandila. Iye sanalalikile uthenga wopatsa ciyembekezo koma waciweluzo. (Yona 1:1, 2) Yesu anali woyenelela kulengeza uthenga umenewu cifukwa anali atakhala wokhulupilika mpaka imfa, kenako n’kuukitsidwa. Izi zinasonyeza kuti Mdyelekezi analibe mphamvu iliyonse pa iye.—Yoh. 14:30; 16:8-11.
Angelo amenewa akali mu mdima wandiweyani. Koma posacedwa, Yesu adzamanga Satana ndi angelo akewa n’kuwaponya kuphompho. (Luka 8:30, 31; Chiv. 20:1-3) Pamapeto pake, iwo adzawonongedwa.—Chiv. 20:7-10.
w08 11/15 21 ¶8
Mfundo Zazikulu za M’makalata a Yakobo ndi Petulo
4:6—Kodi “uthenga wabwino unalengezedwa” kwa “akufa” ati? Awa ndi anthu amene anafa mwauzimu ‘cifukwa ca zolakwa zawo ndi macimo awo.’ Iwo anali akufa asanamve uthenga wabwino. (Aef. 2:1) Koma atakhulupilila uthenga wabwino anakhalanso “amoyo” mwauzimu.
OCTOBER 28–NOVEMBER 3
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 PETULO 1-3
“Muzikumbukila Nthawi Zonse Kukhalapo Kwa Tsiku la Yehova”
w06 12/15 27 ¶11
Yehova ‘Adzaonetsetsa Kuti Cilungamo Cacitika’
Komabe, kodi ndi motani mmene tingamvetsele lonjezo la Yesu lakuti Yehova adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika “mwamsanga”? Mawu a Mulungu amasonyeza kuti ‘ngakhale kuti [Yehova] amaleza mtima,’ adzaonetsetsa kuti pa nthawi yake cilungamo cicitike mwamsanga. (Luka 18:7, 8; 2 Petulo 3:9, 10) M’nthawi ya Nowa, pamene Cigumula cinafika, oipa anawonongedwa mwamsanga-msanga. Cimodzimodzinso m’tsiku la Loti, pamene moto unagwa kucokela kumwamba, anthu oipa anawonongedwa. Yesu anati: “Zidzakhalanso momwemo pa tsikulo pamene Mwana wa munthu adzaonekela.” (Luka 17: 27-30) Anthu oipa ‘adzawonongedwanso modzidzimutsa.’ (1 Atesalonika 5:2, 3) Ndithudi, tingakhulupilile ndi mtima wonse kuti nthawi yowononga dziko la Satana ikadzakwana, Yehova sadzalola kuti lipitilize kukhalapo ngakhale kwa tsiku lina limodzi, cifukwa kutelo sikungakhale cilungamo.
w06 12/15 19 ¶18
“Tsiku la Yehova Lili Pafupi”
N’cifukwa cake mtumwi Petulo akutilimbikitsa kuti nthawi zonse tizikumbukila za “kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” Kodi tingacite motani zimenezi? Njila imodzi ndiyo kukhala otanganidwa ndi nchito zoyela ndiponso za kudzipeleka kwa Mulungu. (2 Petulo 3:11, 12) Kucita nawo nthawi zonse zinthu zimenezi kudzatithandiza kudikila ndi cidwi kufika kwa “tsiku la Yehova.” Mawu a Cigiriki omasulilidwa kuti “kukumbukila nthawi zonse” makamaka amatanthauza “kufulumiza.” N’zoona kuti sitingathe kucititsa nthawi imene yatsalayi kuti ifulumile mpaka kufika pa tsiku la Yehova. Komabe, pamene tikudikilila tsikulo, nthawi ingaoneke ngati ikudutsa mofulumila kwambili ngati tili otanganitsidwa muutumiki wa Mulungu.—1 Akorinto 15:58.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w08 11/15 22 ¶2
Mfundo Zazikulu za M’makalata a Yakobo ndi Petulo
1:19—Kodi “nthanda” ikuimila ndani ndipo iyeyo anatuluka liti? Nanga tidziŵa bwanji kuti zimenezi zinacitika kale? “Nthanda” ikuimila Yesu Khristu atakhala mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Chiv. 22:16) Mu 1914, Yesu anaimilila pamwamba pa zolengedwa zonse monga Mfumu Mesiya, ndipo nthawi imeneyi inali ngati mbandakuca wa tsiku latsopano. Kusandulika kwake kunasonyeza ulemelelo wake komanso wa Ufumu wake ndipo zimenezi zinatsimikizila kuti mawu a ulosi a Mulungu ndi oona. (Maliko 9:1-3) Kuganizila mosamala mawu amenewa kumatithandiza kumvetsa zinthu. N’cifukwa cake tikutha kudziŵa kuti Nthanda anatuluka kale.
w08 11/15 22 ¶3
Mfundo Zazikulu za M’makalata a Yakobo ndi Petulo
2:4—Kodi “Tatalasi” n’ciani ndipo kodi angelo opanduka anaponyedwamo liti? Tatalasi ndi ndende yophiphilitsila imene munaponyedwa zolengedwa zauzimu zokha osati anthu. Zolengedwa zimenezi sizidziŵa zolinga za Mulungu komanso zilibe ciyembekezo, moti tingati zili mumdima wandiweyani. Mulungu anaponya angelo osamvela ku Tatalasi m’masiku a Nowa kuti akhale kumeneko mpaka pamene adzawonongedwe.