CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 9-11
“Padziko Lonse Lapansi Panali Cilankhulo Cimodzi”
11:1-4, 6-9
Pa Babele, Yehova anabalalitsa anthu osamvela mwa kusokoneza citundu cawo. Masiku ano, iye akusonkhanitsa khamu lalikulu kucokela m’maiko onse na m’zinenelo, ndipo akuwapatsa “cilankhulo coyela” kuti “aziitanila pa dzina la Yehova na kumutumikila mogwilizana.” (Zef. 3:9; Chiv. 7:9) “Cilankhulo coyela” cimeneci ni coonadi conena za Yehova komanso zolinga zake zopezeka m’Malemba.
Kuphunzila citundu catsopano kumafuna zambili kuposa cabe kudziŵa mawu atsopano. Kumafuna kuphunzila kaganizidwe katsopano. Mofananamo, pamene tiphunzila cilankhulo coyela ca coonadi, maganizo athu amasintha. (Aroma 12:2) Kusintha kumeneku kumapitiliza, ndipo kumathandiza anthu a Mulungu kukhala ogwilizana. —1 Akor. 1:10.