LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 April tsa. 7
  • “Cotsani Milungu Yacilendo”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Cotsani Milungu Yacilendo”
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Kukaniza Mizimu Yoipa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Khalani Wodzipeleka kwa Yehova Yekha
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Yakobo na Esau Akhalanso Pamtendele
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Sankhani Zosangalatsa Zovomelezeka kwa Yehova
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 April tsa. 7
Ataya mkanda wovala mkhosi wokhudzana na zamizimu.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

“Cotsani Milungu Yacilendo”

Yakobo anadziŵa kuti Yehova amafuna kuti tidzipeleke kwa iye yekha, ngakhale kuti Mulungu anali asanapeleke lamulo loletsa mafano. (Eks. 20:3-5) Conco, pamene Yehova anauza Yakobo kuti abwelele ku Beteli, iye anapempha onse amene anali naye kuti acotse mafano awo. Pambuyo pake, iye anataya mafanowo, kuphatikizapo masikiyo amene mwina anali kuvala monga zithumwa. (Gen. 35:1-4) Mosakayikila, Yehova anakondwela na zimene Yakobo anacita.

Masiku ano, kodi tingadzipeleke bwanji kwa Yehova yekha? Tingatelo mwa kupewa ciliconse cokhudzana na mafano kapena zamizimu. Izi zingaphatikizepo kutaya ciliconse cokhudza zamatsenga, komanso kupenda zosangalatsa zathu mosamala. Mwacitsanzo, mungadzifunse kuti: ‘Kodi nimakonda kuŵelenga mabuku kapena kutamba mafilimu oonetsa zinthu monga vipuku, ziŵanda, kapena zamatsenga? Pa zosangalatsa zanga, kodi pali zina zoonetsa kuti kucita zamizimu, kulodza anthu ena kapena kuwatembelela kulibe vuto?’ Tiyenela kukhala kutali na ciliconse cimene Yehova amadana naco.—Sal. 97:10.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “TSUTSANI MDYELEKEZI,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Mwana wagona pabedi, atavala mphinjili kudzanja lake. Cakumbuyo, kuli mayi wa mwanayo, amene ni wophunzila Baibo, iye akambilana na banja limene limaphunzila naye Baibo.

    Kodi wophunzila Baibo dzina lake Palesa anakumana na vuto lanji mu umoyo wake?

  • Banjalo na wophunzila Baibo wawo akambilana na akulu aŵili kuti awathandize.

    N’cifukwa ciani n’canzelu kupempha thandizo kwa akulu pa nkhani zokhudza zamizimu?

  • Wophunzila Baibo akutentha mphinjili ya mwana wake mu stovu.

    Tsutsani Mdyelekezi, ndipo yandikilani Mulungu. —Yak. 4:7, 8

    Kodi anthu ofuna citetezo ca Yehova afunika kutaya zinthu ziti?

  • Kodi Palesa sanazengeleze kucita ciani?

  • Kudela lanu, ni njila zina ziti zimene mungatsatile kuti mupewe kuvutitsidwa na ziŵanda?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani