CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 34-35
Zotulukapo Zoopsa za Mayanjano Oipa
34:1, 2, 7, 25
Ngati maneba athu, anzathu a kunchito kapena a kusukulu ali na makhalidwe abwino, kodi zitanthauza kuti angakhale mabwenzi abwino? N’ciani cingatithandize kudziŵa ngati munthu wina ni bwenzi labwino kapena ayi?
Kodi kukhala nawo paubwenzi kudzanithandiza kulimbitsa ubale wanga na Yehova?
Kodi zokamba zawo zimaonetsa kuti cofunika kwambili kwa iwo n’ciani?—Mat. 12:34
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi mabwenzi anga amanilimbikitsa kukhala pa ubale wabwino na Yehova?’