LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 August tsa. 3
  • Muziyanjana na Anthu Okonda Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muziyanjana na Anthu Okonda Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kumuopa Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Yehova Amadalitsa Anthu Ocita Zinthu Molimba Mtima
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Yehoyada Anali Wolimba Mtima
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Acinyamata—Kodi Mudzakhala na Tsogolo Lotani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 August tsa. 3

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Muziyanjana na Anthu Okonda Yehova

N’cifukwa ciani tifunika kuceza na anthu okonda Yehova? Cifukwa anthu amene timayanjana nawo angatilimbikitse kucita zinthu zabwino kapena zoipa. (Miy. 13:20) Mwacitsanzo, Mfumu Yehoasi anali “kucita zoyenela pamaso pa Yehova” pamene anali kuyanjana na Mkulu wa Ansembe, Yehoyada. (2 Mbiri 24:2) Koma pamene Yehoyada anamwalila, Yehoasi anapandukila Yehova cifukwa cogwilizana na anthu oipa. —2 Mbiri 24:17-19.

M’nthawi ya Akhristu oyambilila, mtumwi Paulo anayelekezela mpingo wacikhristu na “nyumba yaikulu,” ndipo anthu a mu mpingowo anawayelekezela na “ziwiya” za m’nyumbamo. Timakhalabe “ciwiya ca nchito yolemekezeka” ngati tipewa kuyanjana na aliyense amene amacita zinthu zokhumudwitsa Yehova, kaya akhale wacibale kapena wa mu mpingo. (2 Tim. 2:20, 21) Conco, tiyeni tipitilize kupanga ubwenzi na anthu amene amakonda Yehova, ndiponso amene angatilimbikitse kum’tumikila.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI PHUNZILANI KUPEWA MAKHALIDWE OIPA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi mosadziŵa tingayambe bwanji kuyanjana na anthu oipa?

  • Mu vidiyo imene tatamba, n’ciani cinathandiza Akhristu atatu kuleka kuyanjana na anthu oipa?

  • Ni mfundo za m’Baibo ziti zimene zingakuthandizeni kusankha bwino anthu oyanjana nawo?

John athila moŵa wa makasitomala m’makapu mu lesitilanti; Kristin akuyang’ana pa malo ocezela pa intaneti; Jayden akuchaya gemu pa intaneti; John na banja lake, Kristin, na Jayden ali pa misonkhano

Kodi ndine “ciwiya ca nchito yolemekezeka”?—2 Tim. 2:21

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani