May 4-10
GENESIS 36-37
Nyimbo 114 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yosefe Anacitilidwa Nsanje” (10 min.)
Gen. 37:3, 4—Yosefe abale ake anali kumuzonda kwambili cifukwa atate ake anali kum’konda (w14 8/1 12-13)
Gen. 37:5-9, 11—Maloto a Yosefe anawonjezela nsanje ya abale ake (w14 8/1 13 ¶2-4)
Gen. 37:23, 24, 28—Nsanje inapangitsa abale ake a Yosefe kum’citila zinthu mwankhanza
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Gen. 36:1—N’cifukwa ciani Esau anapatsidwa dzina lina lakuti Edomu? (it-1 678)
Gen. 37:29-32—N’cifukwa ciani abale ake a Yosefe anaonetsa Yakobo mkanjo wa Yosefe umene unali wong’ambika komanso wamagazi? (it-1 561-562)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 36:1-19 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Muzikamba Zosavuta Kumvetsa, ndiyeno kambilanani phunzilo 17 m’bulosha ya Kuphunzitsa.
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) w02 10/15 30-31—Mutu: N’cifukwa Ciani Akhristu Afunika Kukhala na Nsanje Yaumulungu? (th phunzilo 6)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kodi Ndimwe Wokonzeka?”: (15 min.) Nkhani yokambidwa na mkulu. Tambitsani vidiyo yakuti Kodi Mwakonzekela Tsoka la Zacilengedwe?. Phatikizamponi zikumbutso zocokela ku ofesi yanthambi ndiponso kwa akulu, ngati zilipo.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 113
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 84 na Pemphelo