CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 36-37
Yosefe Anacitilidwa Nsanje
37:3-9, 11, 23, 24, 28
Zimene Yosefe anakumana nazo zionetsa kuopsa kokhala na nsanje yosayenela. Gwilizanitsani malemba na zifukwa zake zimene tiyenela kuthetsela nsanje iliyonse yosayenela.
LEMBA
1 Sam. 18:8, 9
Miy. 14:30
2 Akor. 12:20
Agal. 5:19-21
CIFUKWA
Anthu a nsanje sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu
Nsanje imasokoneza mtendele na mgwilizano mu mpingo
Nsanje imavulaza kuthupi
Nsanje imalepheletsa kuona zabwino mwa ena
N’zocitika ziti zimene zingatipangitse kuyamba kucitila nsanje anthu ena?