May 25-31
GENESIS 42-43
Nyimbo 120 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yosefe Anacita Zinthu Modziletsa Kwambili”: (10 min.)
Gen. 42:5-7—Yosefe anacita zinthu modziletsa pamene anaona abale ake (w15 5/1 13 ¶5; 14 ¶1)
Gen. 42:14-17—Yosefe anayesa abale ake (w15 5/1 14 ¶2)
Gen. 42:21, 22—Abale ake a Yosefe anaonetsa kulapa (it-2 108 ¶4)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 42:22, 37—Kodi Rubeni anaonetsa makhalidwe abwino ati? (it-2 795)
Gen. 43:32—N’cifukwa ciani kwa Aiguputo, kudya pamodzi na Aheberi kunali konyansa? (w04 1/15 29 ¶1)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 42:1-20 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela: Kodi m’bale uja wachula bwanji mawu oyenela pofuna kuŵelenga lemba? N’cifukwa ciani m’baleyu wagaŵila mwininyumba buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse? Nanga wacita bwanji zimenezi?
Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 15)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) lvs 38-39 ¶18 (th phunzilo 8)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Yesani Kudziŵa Cithunzi ca Nkhani Yonse”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Mmene Tingapindulile Kwambili Poŵelenga Baibo—Kambali kake. Limbikitsani omvetsela kuti akatambe vidiyo yonse.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 116
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 79 na Pemphelo