CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 42-43
Yosefe Anacita Zinthu Modziletsa Kwambili
42:5-7, 14-17, 21, 22
Ganizilani cabe mmene Yosefe anamvelela pamene anaonana na abale ake pamaso m’pamaso mosayembekezela. Mwamsanga akanafuna kudziulula, ndipo akanawakumbatila, kapena akanasankha kubwezela pa zimene iwo anamucitila. Koma iye sanacite zinthu mopupuluma. Kodi mungacite ciani ngati a m’banja lanu kapena anthu ena akukucitilani zinthu zopanda cilungamo? Citsanzo ca Yosefe citiphunzitsa kuti kucita zinthu modziletsa n’kofunika. Citiphunzitsanso kuti tifunika kukhala wodekha m’malo motsatila mtima wathu wonyenga kapena kucita zinthu mogwilizana na mmene timvelela mu mtima.
Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yosefe pa zocitika zosiyana-siyana zimene mumakumana nazo?