UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Yesani Kudziŵa Cithunzi ca Nkhani Yonse
Poŵelenga nkhani za m’Baibo, yesani kudziŵa cithunzi ca nkhani yonse. Ŵelengani malemba ena ozungulila, phunzilani za anthu a m’nkhaniyo, komanso zifukwa zimene zinapangitsa kuti acite zinthu zimene anacitazo. M’maganizo mwanu, onani zinthuzo, mvelani mawuwo, nunkhizani tumafungo tokomato, ndiponso mvelani mmene anthu a m’nkhaniyo anali kumvelela.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MMENE TINGAPINDULILE KWAMBILI POŴELENGA BAIBO—KAMBALI KAKE, PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi n’zifukwa ziti zimene mwina zinapangitsa kuti abale ake a Yosefe asamagwilizane naye?
N’ciani cimene mwina cinapangitsa abale ake a Yosefe nthawi zina kumacita zinthu mwaukali popanda kuganizila zotulukapo zake?
Tingaphunzile ciani m’Malemba zokhudza Yakobo, tate wake wa Yosefe?
Kodi Yakobo anawaphunzitsa mfundo yabwino iti ana ake pankhani yothetsa kusemphana maganizo?
Kodi mwapindula bwanji na vidiyoyi?