LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 November tsa. 6
  • Umboni wa Dalitso la Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Umboni wa Dalitso la Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • “Ndani Kweni-kweni Amene Ali Kapolo Wokhulupilika Ndi wanzelu?”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Kodi Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu Ndani?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • “Kumbukilani Amene Akutsogolela Pakati Panu”
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 November tsa. 6

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 8–9

Umboni wa Dalitso la Yehova

8:6-9, 12; 9:1-5, 23, 24

Yehova anagwetsa moto umene unanyeketsa nsembe zopseleza zimene ansembe a m’banja la Aroni anapeleka atangolongedwa unsembe. Izi zinaonetsa kuti Yehova anawavomeleza ansembewo komanso kuti anali kuwacilikiza. Mwa kucita zimenezi, Yehova analimbikitsa Aisiraeli amene anasonkhana na kuona zocitikazo kuti aziwacilikiza na mtima wonse ansembewo. Masiku ano, Yehova akuseŵenzetsa Yesu Khristu waulemelelo monga Mkulu wa Ansembe wapamwamba. (Aheb. 9:11, 12) Mu 1919, Yesu anaika kagulu kocepa ka abale odzozedwa kukhala “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Kodi pali umboni wotani woonetsa kuti Yehova anamuvomeleza kapoloyu ndipo akumudalitsa na kum’cilikiza?

  • Olo kuti anthu a Mulungu akhala akuzunzidwa mosalekeza, kapolo wokhulupilika wapitiliza kupeleka cakudya cauzimu

  • Monga mmene ulosi unakambila, uthenga wabwino ukulalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mat. 24:14

Kodi tingamucilikize bwanji kapolo wokhulupilika ndi wanzelu na mtima wonse?

Zithunzi: 1. Yesu Khristu waulemelelo akulamulila dziko lapansi. 2. Abale otumikila monga kapolo wokhulupilika ndi wanzelu akumana pamodzi kuti apeleke cakudya cauzimu. 3. M’bale akulalikila uthenga wabwino kwa munthu wina.
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani