Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
MARCH 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 7-8
“Zimene Tingaphunzile pa Dongosolo la Msasa wa Aisiraeli”
it-1 497 ¶3
Mpingo
1Mu Isiraeli, amuna a paudindo nthawi zambili anali kucita zinthu moimilako anthu onse. (Ezara 10:14) N’cifukwa cake “atsogoleli a mafuko” ndiwo anapeleka zopeleka cihema citatha kumangidwa. (Num. 7:1-11) Komanso m’nthawi ya Nehemiya, ansembe, alevi, na “atsogoleli a anthu” ndiwo anatsimikizila “pangano lodalilika” ndi cidindo moimilako anthu onse. (Neh. 9:38–10:27) Pa ulendo wa Aisiraeli m’cipululu, panali “atsogoleli a anthu, owaimila ku misonkhano, amuna ochuka.” Amuna 250 mwa atsogoleli amenewo anagwilizana na Kora, Datani, Abiramu, na Oni, ndipo anasonkhana potsutsana na Mose na Aroni. (Num. 16:1-3) Potsatila malangizo a Mulungu, Mose anasankha amuna 70 mwa akulu a Isiraeli, amene anali oyang’anila kuti amuthandize “kusenza udindo woyang’anila anthu” umene unamukulila. (Num. 11:16, 17, 24, 25) Levitiko 4:15 imakamba za “akulu a khamu la Isiraeli,” ndipo cioneka kuti amuna amene anali kuimila anthu anali kukhala akulu a mtunduwo, atsogoleli awo, oweluza, komanso oyang’anila awo.—Num. 1:4, 16; Yos. 23:2; 24:1.
it-2 796 ¶1
Rubeni
Mu msasa wa Aisiraeli, Arubeni anali kumanga misasa yawo Kum’mwela kwa cihema copatulika, ndipo mbadwa za Simiyoni zinali kumanga misasa yawo kumbali imodzi, mbadwa za Gadi zinali kumanga kumbali inayo. Pa nthawi yosamuka, cigawo ca mafuko atatu ca Yuda, Isakara, na Zebuloni cikasamuka, panali kutsatila cigawo ca mafuko atatu cotsogoleledwa na fuko la Rubeni. (Num. 2:10-16; 10:14-20) Dongosolo limeneli ndilo linatsatilidwa pamene mafuko a Isiraeli anabweletsa zopeleka pa tsiku lotsegulila cihema copatulika.—Num. 7:1, 2, 10-47.
w04 8/1 25 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Numeri
8:25, 26. Anthu acikulile anali kulamulidwa kupuma pa nchito yomwe mwalamulo anali kufunika kugwila. Anali kucita izi pofuna kuonetsetsa kuti pali amuna oyenelela ogwila nchito za Alevi, ndiponso poganizila msinkhu wa anthu acikulilewo. Komabe anali kudzipeleka kuti athandize Alevi ena. Ngakhale kuti masiku ano palibe nthaŵi yopuma pa nchito yolengeza Ufumu, mfundo ya lamuloli itipatsa phunzilo lofunika kwambili. Ngati Mkhristu sangakwanitse kugwila nchito zina cifukwa ca ukalamba, iye angathe kugwila nchito zina zimene angazikwanitse.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 835
Woyamba Kubadwa
Ana aamuna oyamba kubadwa mu Isiraeli anali kuimila mtundu wonse cifukwa anali kudzakhala atsogoleli a mabanja. Ndipo Yehova anati mtundu wonse wa Isiraeli unali ‘mwana wake woyamba kubadwa.’ Anauchula conco cifukwa ca pangano lake na Abulahamu. (Eks. 4:22) Cifukwa cakuti Yehova anapulumutsa ana aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli, iye analamula kuti amupatulile “mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa, wa munthu ndi wa ciweto” pakati pa ana a Isiraeli. (Eks. 13:2) Conco, ana aamuna oyamba kubadwa anapelekedwa kwa Mulungu.
MARCH 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 9-10
“Mmene Yehova Amatsogolela Anthu Ake”
it-1 398 ¶3
Msasa
Kuyenda kwa khamu lalikulu limeneli kucoka pa malo ena kupita pa ena (Mose anachula malo otelo pafupi-fupi 40 mu Numeri 33) kunaonetsanso kuti panali dongosolo lapadela kwambili. Mtambo ukaima pamwamba pa cihema copatulika, Aisiraeli sanali kucoka pa malo amenewo. Koma mtambo ukacoka, nawonso anali kucoka. “Yehova akalamula, iwo ankamanga msasa, ndipo Yehova akalamula, iwo ankanyamuka.” (Num. 9:15-23) Panali malipenga aŵili a siliva ocita kusula amene anali kugwilitsidwa nchito popeleka malangizo a Yehova kwa Aisiraeli mumsasa. (Num. 10:2, 5, 6) Lipenga lolila mosintha-sintha likalila, cinali cizindikilo cakuti Aisiraeli afunika kunyamuka. Nthawi yoyamba pamene izi zinacitika munali mu “caka caciŵili [mu 1512 B.C.E.], m’mwezi waciŵili, pa tsiku la 20.” Pa nthawi yosamuka, likasa la pangano linali kukhala patsogolo. Pambuyo pake panali kubwela cigawo coyamba ca mafuko atatu. M’cigawoci, a fuko la Yuda anali kukhala patsogolo. Pambuyo pake panali kubwela a fuko la Isakara, kenako a fuko la Zebuloni. Pambuyo pawo panali kubwela Agerisoni na Amerari, amene anali kunyamula zipangizo za pacihema copatulika. Pambuyo pa amenewa panali kubwela cigawo ca mafuko atatu, cimene patsogolo panali kukhala a fuko la Rubeni, kenako a fuko la Simiyoni na Gadi. Pambuyo pawo panali kubwela Akohati onyamula zinthu za m’malo opatulika. Ndiyeno panali kutsatila cigawo cacitatu ca mafuko atatu, cimene patsogolo panali kukhala a fuko la Efuraimu, kenako a fuko la Manase na Benjamini. Kumbuyo kweni-kweni kunali kubwela cigawo cothela, cimene patsogolo panali a fuko la Dani, kenako a fuko la Aseri na Nafitali. Conco cigawo cimodzi ca mafuko atatu cokhala na anthu ambili komanso amphamvu cinali kukhala kutsogolo, ndipo cina cinali kukhala kumbuyo.—Num. 10:11-28.
w11 4/15 4-5
Kodi Mumaona Umboni Wakuti Mulungu Akutitsogolela?
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timafuna kutsogoleledwa na Mulungu? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Muzimvela amene akutsogolela pakati panu ndipo muziwagonjela.” (Aheb. 13:17) Koma nthawi zina kucita zimenezi kumakhala kovuta. Mwacitsanzo, tiyelekeze kuti munali m’gulu la Aisiraeli nthawi ya Mose. Ndipo pambuyo poyenda kwa kanthawi, mtambo waima. Kenako mudzifunsa kuti, ‘Kodi mtambowu uima tsiku limodzi, mlungu wathunthu kapena miyezi ingapo? Kodi nimasule katundu wanga yense?’ Mwina poyamba mukhoza kungomasula zinthu zofunika kwambili. Ndiyeno patapita masiku angapo, mukumasula katundu yense cifukwa cotopa na kufufuza-fufuza zinthu. Koma mutatsala pang’ono kumasula katundu yense, mukuona mtambowo ukunyamuka ndipo muyenela kulongedzanso katundu wanu. Zimenezi zingakhale zovuta. Komabe, Aisiraeli anayenela “kunyamuka nthawi yomweyo.”—Num. 9:17-22.
Kodi ife timacita ciani tikalandila malangizo ocokela kwa Mulungu? Kodi timayesetsa kuwatsatila “nthawi yomweyo”? Kapena kodi timangopitiliza kucita zinthu m’njila imene tinazolowela? Kodi tikudziŵa bwino malangizo atsopano okhudza zinthu monga kucititsa phunzilo la Baibo, kulalikila anthu a cinenelo cina ndiponso kulambila kwa pa banja nthawi zonse? Nanga kodi tikudziŵa bwino malangizo okhudza kucita zinthu mogwilizana na Makomiti Okambilana ndi Acipatala ndiponso okhudza mmene tiyenela kucitila zinthu pa misonkhano yathu yaikulu? Timasonyezanso kuti timafuna kutsogoleledwa na Mulungu tikamatsatila uphungu. Tikafuna kusankha zocita pa nkhani zikulu-zikulu, sitidalila nzelu zathu koma timadalila Yehova na gulu lake kuti atitsogolele. Mofanana na mwana amene amathawila kwa makolo ake kuti amuteteze kukakhala cimvula camabingu, nafenso timathawila kwa Yehova na gulu lake tikakumana na mavuto okhala ngati cimvula camabingu.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 199 ¶3
Msonkhano
Kufunika Kosonkhana. Kupezeka nthawi zonse pa misonkhano imene Yehova amatikonzela, kumatipindulitsa mwauzimu ndipo n’kofunika kwambili. Kufunika kwa misonkhanoyi kuonekela bwino tikaganizila za mwambo wapacaka wa Pasika. Mwamuna aliyense wosadetsedwa amene sanali paulendo akanyalanyaza kucita Pasika anayenela kuphedwa. (Num. 9:9-14) Mfumu Hezekiya poitana anthu a ku Yuda na ku Isiraeli kuti adzacite cikondwelelo ca Pasika ku Yerusalemu, anakambapo kuti: “Inu ana a Isiraeli, bwelelani kwa Yehova . . . musaumitse khosi lanu ngati mmene anacitila makolo anu. Gonjelani Yehova, pitani ku nyumba yake yopatulika imene waiyeletsa mpaka kalekale. Tumikilani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake umene wakuyakilani ukucokeleni. . . . Yehova Mulungu wanu ndi wacisomo ndiponso wacifundo, ndipo sadzayang’ana kumbali mukabwelela kwa iye.” (2 Mbiri 30:6-9) Kusapezeka kumsonkhanowo mwadala kukanaonetsa kuti munthuyo wasiya Mulungu. Ngakhale kuti masiku ano Akhristu siticita zikondwelelo monga Pasika, Paulo anatilimbikitsa kuti tisaleke kupezeka pamisonkhano ya anthu a Mulungu. Anati: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi monga mmene ena acizoloŵezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.”—Aheb. 10:24, 25.
MARCH 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 11-12
“N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupewa Mzimu Wodandaula?”
w01 6/15 17 ¶20
Musakhale Akumva Oiŵala
20 Akhristu oculuka sagonjela cilakolako cakuti acite ciwelewele. Komabe, m’pofunika kusamala kwambili kuti tisakhale na cizoloŵezi cocita zinthu mong’ung’udza zimene zingabweletse mkwiyo wa Mulungu pa ife. Paulo anacenjeza kuti: “Kapena tisamuyese Yehova, mmene ena mwa [Aisiraeli] anamuyesela, n’kuwonongeka polumidwa ndi njoka. Tisakhalenso ong’ung’udza, mmene ena mwa iwo anang’ung’udzila, wowonongayo n’kuwawononga onsewo.” (1 Akorinto 10:9, 10) Aisiraeli anang’ung’udza kutsutsana na Mose na Aroni—inde, ngakhalenso kutsutsana na Mulungu weniweniyo—kudandaula ndi mana opelekedwa mozizwitsa. (Numeri 16:41; 21:5) Kodi Yehova anamulakwila pang’ono na kung’ung’udzako kusiyana ndi dama lawo lija? Nkhani ya m’Baibo ionetsa kuti njoka zinapha ong’ung’udza ambili. (Numeri 21:6) Nthaŵi yoyamba ija, anthu opanduka ndi ong’ung’udza oposa 14,700 anawonongedwa. (Numeri 16:49) Cotelo tisayese kuleza mtima kwa Yehova mwa kusalemekeza zopeleka zake.
w06 7/15 15 ¶7
Pewani Kudandaula
7 Maganizo a Aisiraeli anali atasinthilatu! Poyamba, kuyamikila kwawo cifukwa ca kumasulidwa ku Iguputo na kupulumutsidwa pa Nyanja Yofiila kunawalimbikitsa kuimbila Yehova zitamando. (Ekisodo 15:1-21) Koma cifukwa ca mavuto amene anali kukumana nawo m’cipululu ndiponso kuopa Akanani, kuyamikila konse kwa anthu a Mulungu kunatha, m’malo mwake anakhala na mzimu wosakhutila. M’malo moyamikila Mulungu cifukwa ca ufulu wawo, iwo molakwika anamuimba mlandu woti anawamana zinthu. Cotelo, kudandaula kunasonyeza kuti sanayamikile zinthu zimene Yehova anawapatsa. N’cifukwa cake ananena kuti: “Kodi khamu la anthu oipa amenewa lidandaula motsutsana nane kufikila liti?”—Numeri 14:27; 21:5.
it-2 719 ¶4
Mkangano
Kung’ung’udza. Kung’ung’udza kumafooketsa komanso kumayambitsa magaŵano. Patapita nthawi yocepa kucokela pamene Aisiraeli anatuluka mu Iguputo, iwo anayamba kung’ung’udza motsutsana na Yehova. Iwo anali kudandaula kuti utsogoleli wake kupitila mwa atumiki ake, Mose na Aroni sunali wabwino. (Eks. 16:2, 7) M’kupita kwa nthawi madandaulo awo anamufooketsa kwambili Mose moti anapempha kuti afe cabe. (Num. 11:13-15) Munthu amene amakonda kudandaula angakumane na mavuto aakulu. Yehova anaona kuti kung’ung’udza kumene anthuwo anali kucita motsutsana na Mose kunali kupandukila ulamulilo wake. (Num. 14:26-30) Ambili anaphedwa cifukwa ca kudandaula kumeneko.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 309
Mana
Maonekedwe na Makomedwe Ake. Mana anali “oyela ngati njele ya mapila,” ndipo “maonekedwe” ake anali ngati utomoni woonekela mkati ngati galasi. Makomedwe ake anali “ngati makeke opyapyala othila uci” kapena “keke yotsekemela [yonzuna] yothila mafuta.” Mana akawapela pamphelo kapena kuwasinja mumtondo, anali kuwawilitsa mumphika kapena kuwapanga makeke.—Eks. 16:23, 31; Num. 11:7, 8.
MARCH 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 13-14
“Mmene Cikhulupililo Cimatithandizila Kukhala Olimba Mtima”
w06 10/1 16-17 ¶5-6
Kulimba Mtima Cifukwa ca Cikhulupililo ndi Kuopa Mulungu
5 Koma azondi aŵili, Yoswa na Kalebe, anali ofunitsitsa kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Iwo anati: Akanani “ali ngati cakudya kwa ife. Alibenso citetezo, koma ifeyo Yehova ali nafe. Musawaope ayi.” (Numeri 14:9) Kodi Yoswa na Kalebe anangotengeka maganizo? Ayi ndithu. Iwo limodzi na mtundu wonse anaona Yehova akucititsa manyazi Iguputo wamphamvu na milungu yake mwa kugwilitsila nchito Milili Khumi. Ndiyeno anaona Yehova akumiza Farao na gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiila. (Salimo 136:15) N’zoonekelatu kuti zifukwa zokhalila na mantha zimene azondi khumi limodzi ndi anthu omwe anawatsatila anali nazo zinali zosamveka. Poonetsa kupwetekedwa mtima kwambili, Yehova anati: “Kodi adzayamba liti kundikhulupilila pambuyo pa zizindikilo zonse zimene ndacita pakati pawo?”—Numeri 14:11.
6 Yehova anachula vuto leni-leni limene anthuwo anali nalo. Ndipo vutolo linali kupanda cikhulupililo kwawo kumene kunaonekela cifukwa ca mantha amene anali nawo. Inde, cikhulupililo na kulimba mtima zimayendela limodzi kwambili moti ponena za mpingo wacikhristu na nkhondo yake yauzimu, mtumwi Yohane analemba kuti: “Tagonjetsa dziko ndi cikhulupililo cathu.” (1 Yohane 5:4) Masiku ano, cikhulupililo monga ca Yoswa na Kalebe cathandiza kuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse na Mboni za Yehova zoposa 6 miliyoni. Mboni zimenezi zimaphatikizapo ana ndi akulu, amphamvu na odwala. Palibe mdani amene wakwanitsa kutseka pakamwa khamu lamphamvu ndi lolimba mtima limeneli.—Aroma 8:31.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 740
Dziko Limene Mulungu Anapatsa Aisiraeli
DZIKO limene Mulungu anapatsa Aisiraeli linalidi dziko labwino. Pamene Mose anatuma azondi kuti akazonde Dziko Lolonjezedwa na kutengako zina mwa zipatso za m’dzikolo, iwo anabweletsa nkhuyu, makangaza, na nthambi yokhala na mphesa zoculuka kwambili, moti inanyamulidwa ndi anthu aŵili pa mtengo wonyamulila. Ngakhale kuti anaopa kukalanda dzikolo cifukwa cosoŵa cikhulupililo, iwo anabweletsa uthenga wakuti, “ndithudi ndi dziko loyenda mkaka ndi uci.”—Num. 13:23, 27.
MARCH 29–APRIL 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 15-16
“Samalani na Kunyada Komanso Kudzidalila”
w11 9/15 27 ¶12
Kodi Mumadziwika Ndi Yehova?
12 Koma ali pa ulendo wopita ku Dziko Lolonjezedwa, Kora anayamba kuona kuti njila imene Yehova anali kugwilitsila nchito potsogolela Aisiraeli inali yolakwika. Ndiyeno amuna 250 anagwilizana naye poganiza kuti akhoza kusintha zinthu. Kora na anzakewo ayenela kuti anali kuganiza kuti ali pa ubwenzi wabwino na Yehova. Iwo anauza Mose kuti: “Tatopa nanu tsopano! Khamu lonseli ndi loyela, ndipo Yehova ali pakati pawo.” (Num. 16:1-3) Apa n’zoonekelatu kuti anthuwa anali odzidalila kwambili ndiponso odzikuza kwabasi. Mose anawauza kuti: “Yehova aonetsa amene ali wake.” (Welengani Numeri 16:5.) Madzulo a tsiku lotsatila, Kora na anzake amene anapanduka nawo anaphedwa.—Num. 16:31-35.
w11 9/15 27 ¶11
Kodi Mumadziwika Ndi Yehova?
11 Tikambilana zitsanzo za anthu aŵili amene anacita zinthu mosiyana kwambili pa nkhani ya kulemekeza zimene Yehova anasankha kucita. Anthu amenewa ndi Mose na Kora. Zimene anacita zionetsa mmene Yehova amationela tikamalemekeza kapena kupeputsa zimene wasankha. Kora anali wa m’banja la Kohati m’fuko la Levi ndipo anali na maudindo ambili-mbili. Iye anaona Aisiraeli akupulumutsidwa pa Nyanja Yofiila, ndipo anathandiza pamene Yehova anali kupeleka ciweluzo kwa Aisiraeli osamvela paphili la Sinai. Iye anagwilanso nchito yonyamula likasa la pangano. (Eks. 32:26-29; Num. 3:30, 31) Zioneka kuti kwa zaka zambili, Kora anali munthu wokhulupilika kwa Yehova ndiponso Aisiraeli ambili mumsasa anali kumulemekeza.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w98 9/1 20 ¶1-2
Tsimikizani Kuika Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba!
Yehova sanaione mopepuka nkhaniyi. Baibo imati: “Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: ‘Munthuyo aphedwe basi!’” (Numeri 15:35) Kodi n’cifukwa ciani Yehova anaipidwa kwambili na zimene munthuyo anacita?
Anthuwo anali na masiku asanu ndi limodzi otola nkhuni ndiponso kupeza cakudya, zovala, na pogona. Tsiku lacisanu na ciŵili anafunikila kulipatula kaamba ka zosoŵa zawo zauzimu. Ngakhale kuti kutola nkhuniko sikunali kulakwa, kugwilitsila nchito nthaŵi imene anafunikila kuipatula kuti azilambila Yehova ndiko kunali kulakwa. Ngakhale kuti Akhristu sagwilitsila nchito Cilamulo ca Mose, kodi cocitika cimeneci sicikutiphunzitsa kuti tifunikila kumaika zinthu zofunika pamalo oyamba?—Afilipi 1:10.
APRIL 5-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 17-19
“Ine Ndine . . . Colowa Cako”
w11 9/15 13 ¶9
Kodi Mukulola Yehova Kukhala Colowa Canu?
9 Taganizilani za Alevi amene sanali kulandila colowa ca malo. Popeza kuti kulambila koyela kunali cinthu cofunika kwambili kwa iwo, anali kufunika kudalila Yehova kuti apeze zofunika pa moyo wawo. Yehova anawauza kuti: ‘Ine ndine colowa canu.’ (Num. 18:20) Ngakhale kuti ifeyo sititumikila m’kacisi weni-weni ngati mmene ansembe na Alevi anali kucitila, tikhoza kuwatsanzila pokhulupilila kuti Yehova adzatisamalila. Pamene tili mkati-kati mwa masiku otsiliza m’pamenenso tifunika kudalila kwambili Mulungu kuti atipatsa zofunika pa moyo wathu.—Chiv. 13:17.
w11 9/15 7 ¶4
Yehova Ndi Colowa Canga
4 Kodi Yehova anakhala bwanji colowa ca Alevi pamene anawasankha kuti amutumikile pa udindo umenewu? Pamene Yehova ananena kuti akhale colowa cawo anali kutanthauza kuti m’malo mowapatsa malo monga colowa, awapatsa utumiki wamtengo wapatali kwambili. Colowa cawo cinali “unsembe wa Yehova.” (Yos. 18:7) Caputala 18 ca Numeri cimatithandiza kudziŵa kuti iwo anali kupezabe zofunikila pa moyo. (Welengani Numeri 18:19, 21, 24.) Alevi anayenela kupatsidwa “cakhumi ciliconse mu Isiraeli monga colowa cawo cifukwa ca utumiki wawo.” Anayenela kulandila gawo limodzi pa magawo 10 a zokolola ndiponso ziweto za Aisiraeli. Nawonso Alevi anayenela kupeleka gawo limodzi “labwino koposa” pa magawo 10 a zimene anali kulandila n’colinga coti asamalile ansembe. (Num. 18:25-29) Ansembe anali kupatsidwanso “zopeleka zonse zopatulika” zimene ana a Isiraeli anali kupeleka kwa Mulungu kumalo ake olambilila. Conco panali zifukwa zomveka zoti ansembe azikhulupilila kuti Yehova awasamalila.
Kufufuza Cuma Cauzimu
g02 6/8 14 ¶2
Mcele—Cinthu Cofunika Kwambili
Mcele unakhalanso cizindikilo cakuti cinthu n’codalilika komanso cokhalitsa. Conco, m’Baibo pangano losatha linali kuchedwa “pangano la mcele,” ndipo magulu aŵili ocita panganolo nthawi zambili anali kudyela pamodzi cakudya cothila mcele potsimikizila panganolo. (Numeri 18:19) M’Cilamulo ca Mose, nsembe zopelekedwa pa guwa lansembe anali kuzithila mcele, mwacionekele poonetsa kuti si zovunda kapena zoola.
APRIL 12-18
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 20-21
“Khalanibe Ofatsa Mukapanikizika na Mayeso”
Yesetsani Kukhala Ofatsa Kuti Mukondweletse Yehova
19 Tidzapewa kucita zolakwa. Ganizilaninso za Mose. Kwa zaka zambili anali wofatsa, ndipo anacita zinthu zokondweletsa Yehova. Koma cakumapeto kwa ulendo wa m’cipululu wa zaka 40, Mose analephela kuonetsa khalidwe la kufatsa. Mlongosi wake, Miriamu, mwacionekele amene anathandiza kupulumutsa moyo wake ku Iguputo anali atafa kumene, ndipo anaikidwa m’manda ku Kadesi. Pa nthawiyo, Aisiraeli anayambanso kudandaula kuti sanali kusamalidwa bwino. Iwo ‘anakangana ndi Mose’ pa nkhani yosoŵa madzi. Ngakhale kuti Yehova anacitila Aisiraeli zozizwitsa zambili kupitila mwa Mose, ndipo Mose anawatsogolela bwino kwa zaka zambili, iwo anapitiliza kudandaula. Sanadandaule cabe za kusoŵa kwa madzi, koma anakwiyilanso Mose, monga kuti iye ndiye anacititsa kuti asoŵe madzi.—Num. 20:1-5, 9-11.
Yesetsani Kukhala Ofatsa Kuti Mukondweletse Yehova
20 Mose anakwiya kwambili, cakuti anacita zinthu mosadekha. M’malo mokamba na thanthwe, monga mmene Yehova anam’lamulila, iye anakamba mokwiya kwa anthu. Komanso, anakamba mawu oonetsa ngati kuti iye ndiye adzatulutsa madzi. Ndiyeno, anamenya thanthwelo kaŵili, ndipo munatuluka madzi ambili. Kunyada na mkwiyo zinam’pangitsa kucita colakwa cacikulu. (Sal. 106:32, 33) Olo kuti Mose analephela kuonetsa khalidwe la kufatsa kwa kanthawi kocepa cabe, Mulungu sanamulole kukaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.—Num. 20:12.
21 Pa nkhani imeneyi, tiphunzilapo mfundo zofunika kwambili. Yoyamba, nthawi zonse tifunika kuyesetsa kukhala ofatsa. Tikalephela kukhala ofatsa, ngakhale kwa nthawi yocepa, mzimu wonyada ukhoza kutiloŵa na kutipangitsa kukamba, kapena kucita zinthu zolakwika. Yaciŵili, tifunika kuyesetsa kucita zinthu mofatsa, ngakhale pamene takwiya kapena kupanikizika maganizo.
w09 9/1 19 ¶5
Woweluza Wacilungamo
Coyamba, Mulungu sanalangize Mose kuti alankhule ndi anthu kapena kuti auze anthuwo kuti akupikisana ndi Yehova. Caciŵili, Mose na Aroni analephela kupeleka ulemelelo kwa Mulungu. N’cifukwa cake Mulungu anawauza kuti: “Simunasonyeze . . . kundilemekeza.” (Vesi 12) Ponena kuti “ticite kukutulutsilani madzi,” Mose anatanthauza kuti iye na Aroni, na amene angapatse anthuwo madzi, osati Mulungu. Cacitatu, cilango cimene Mulungu anawapatsa cinali cogwilizana ndi zilango zina zimene iye anapelekapo m’mbuyomo. Zimenezi zisanacitike, Mulungu sanalole kuti anthu amene sanamvele malamulo ake aloŵe m’dziko la Kanani, conco iye anacitanso cimodzi-modzi na Mose na Aroni. (Numeri 14:22, 23) Cacinayi, Mose na Aroni anali atsogoleli a mtundu wa Isiraeli. Conco, anthu onse amene ali na udindo, akalakwitsa cinacake, Mulungu amawaimba mlandu waukulu.—Luka 12:48.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Kodi Mumaona Anthu Ofooka Mmene Yehova Amawaonela?
12 Yehova akanalanga Aroni nthawi imeneyo cifukwa ca zolakwa zimenezi. Koma iye anazindikila kuti Aroni sanali munthu woipa. Zinaoneka kuti Aroni anasocetseledwa ndi anthu oipa. Ndiponso, pamene anauzidwa kuti wacimwa, iye anavomeleza kulakwa kwake ndipo anacilikiza ziweluzo za Yehova. (Eks. 32:26; Num. 12:11; 20:23-27) Yehova anayang’ana cikhulupililo ndi kulapa kwa Aroni. Ndiye cifukwa cake ngakhale pambuyo pa zaka zambili, Aroni ndi ana ake anaonedwabe kuti anali okhulupilika kwa Yehova.—Sal. 115:10-12; 135:19, 20.
APRIL 19-25
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 22-24
“Yehova Anasintha Tembelelo Kukhala Dalitso”
bt 53 ¶5
Kulengeza “Uthenga Wabwino Wonena za Yesu”
5 Mofanana ndi m’nthawi ya atumwi, masiku anonso anthu a Mulungu sanasiye kulalikila cifukwa cozunzidwa. Nthawi zambili, Akhristu amakakamizidwa kucoka kumalo ena n’kukakhala kumalo ena, mwina kundende kapena kudziko lina, ndipo zimenezi zacititsa kuti uthenga wabwino wa Ufumu ufalikile kwa anthu ena kudela limene apitako. Mwacitsanzo, pa nthawi ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, Mboni za Yehova zinali kulalikilabe ngakhale pamene zinali m’ndende za Nazi zozunzilako anthu. Myuda wina amene anakumana na Mboni kundendeko anafotokoza kuti: “Akaidi amene anali a Mboni za Yehova anali olimba mtima kwambili, ndipo zimenezi zinanitsimikizila kuti cikhulupililo cawo cinalidi cocokela m’Malemba, conco inenso n’nakhala Mboni.”
it-2 291
Msala
Msala Wotsutsana na Yehova. Mopanda nzelu, mneneli Balamu anafuna kutembelela Aisiraeli kuti alandile ndalama kwa Mfumu Balaki ya Amoabu. Koma Yehova analepheletsa tembelelo na zoyesa-yesa za mneneliyu. Ponena za Balamu mtumwi Petulo anakamba kuti: “Nyama yosalankhula yonyamula katundu inalankhula ngati munthu ndi kulepheletsa zocita zamisala za mneneliyo.” Ponena za msala wa Balamu, mtumwiyu anaseŵenzetsa liwu lacigiriki lakuti pa·ra·phro·niʹa lotanthauza “kuzungulila mutu.”—2 Pet. 2:15, 16; Num. 22:26-31.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w04 8/1 27 ¶2
Mfundo Zazikulu za M’buku la Numeri
22:20-22—Kodi n’cifukwa ciani Yehova anakwiyila Balamu? Yehova anali atauza mneneli Balamu kuti asatembelele Aisiraeli. (Numeri 22:12) Komabe, mneneliyu anatengana na amuna a Balaki ali na malingalilo okatembelela Isiraeli. Balamu anali kufuna kusangalatsa mfumu ya Amoabu na kulipilidwa na mfumuyi. (2 Petulo 2:15, 16; Yuda 11) Ngakhale pamene Balamu anakakamizidwa kudalitsa Aisiraeli m’malo mowatembelela, iye anafunabe kusangalatsa mfumuyo mwa kupeleka maganizo akuti akazi olambila Baala akope amuna aciisiraeli. (Numeri 31:15, 16) Motelo Mulungu anakwiya na Balamu cifukwa ca dyela lake limene linamucititsa zacinyengo.
APRIL 26–MAY 2
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 25-26
“Kodi Zocita za Munthu Mmodzi Zingapindulitse Ambili?”
“Thaŵani Dama”
MUNTHU woŵedza nsomba amapita pamalo amene adziŵa kuti angagwilepo mtundu wa nsomba zimene afuna. Amasankha nyambo yoika ku mbedza yake na kuponya pamadzi. Ndiyeno amakhala phee kuyembekezela. Ndipo nsomba ikadyela amati nthambo ija khwe! kuti mbedza ikoŵe m’kamwa mwa nsomba, kenako amaidonsa.
2 Anthu nawonso amagwilika cimodzi-modzi. Mwacitsanzo, Aisiraeli anali atayandikila kale Dziko Lolonjezedwa pamene anamanga msasa m’Cigwa ca Mowabu. Mfumu ya Mowabu inalonjeza Balamu ndalama zambili ngati angatembelele Aisiraeli. Potsilizila pake, Balamu anapeza njila yopangitsa Aisiraeli kudzibweletsela okha tembelelo. Iye anasankha nyambo yake mocenjela kwambili. Anatumiza atsikana acimowabu mu msasa wa Aisiraeli kuti akawakope.—Numeri 22:1-7; 31:15, 16; Chivumbulutso 2:14.
“Thaŵani Dama”
4 N’cifukwa ciani Aisiraeli ambili anagwela mu msampha wa Balamu? Cifukwa anali kungoganizila zofuna zawo zadyela, na kuiŵala zonse zimene Yehova anawacitila. Pa zifukwa zambili, Aisiraeli anafunika kukhala okhulupilika kwa Mulungu. Anali atawamasula mu ukapolo ku Iguputo, anawapatsa cakudya m’cipululu, mpaka kuwafikitsa motetezeka ku malile a Dziko Lolonjezedwa. (Aheberi 3:12) Koma n’zacisoni kuti iwo ananyengedwabe na zaciwelewele. M’pake kuti mtumwi Paulo anacenjeza kuti: “Tisamacite dama, mmene ena mwa iwo anacitila dama, n’kufa.”—1 Akorinto 10:8.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 359 ¶1-2
Malile
Cioneka kuti kagaŵidwe ka malo pakati pa mafuko a Isiraeli kanadalila pa zinthu ziŵili izi: zotsatilapo za maele komanso kukula kwa fuko. Maele ayenela kuti anali kungothandiza kudziŵa cigawo ca Dziko Lolonjezedwa cimene fuko lidzalandilako coloŵa cake ca malo, kaya Kumpoto kapena Kum’mwela, Kum’maŵa kapena Kum’madzulo, kumbali kwa nyanja kapena kudela la mapili. Popeza kuti zotsatilapo za maelewo zinali kucokela kwa Yehova, zinathandiza kuti mafukowo asamacitilane nsanje kapena kulimbilana malo. (Miy. 16:33) Komanso kupitila m’maele amenewo, Mulungu anayendetsa zinthu m’njila yakuti fuko lililonse lilandile coloŵa mogwilizana na ulosi wouzilidwa wolembedwa pa Genesis 49:1-33 umene Yakobo anakamba pa nthawi ya kufa kwake.
Pambuyo pakuti maele aonetsa kumene fuko lidzalandila coloŵa cake ca malo, panafunika kudziŵa ukulu wa malowo potengela kukula kwa fukolo. Mulungu anati: “Mukagaŵile dzikolo kwa mabanja anu monga coloŵa canu mwa kucita maele. Banja la anthu ambili mukaliwonjezele colowa cawo, ndipo banja la anthu ocepa mukalicepetsele colowa cawo. Malo alionse amene maele akagwele banja, akapatsidwe kwa banjalo.” (Num. 33:54) Conco akacita maele, dela kumene fuko lapatsidwa malo monga coloŵa silinali kusintha, koma nthawi zina cimene cinali kusintha ni kukula kwa malowo. Ndiye cifukwa cake ataona kuti malo a fuko la Yuda akula kwambili, anawacepetsako mwa kupeleka mbali ina ya malowo ku fuko la Simiyoni.—Yos. 19:9.