LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr22 May masa. 1-6
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2022
  • Tumitu
  • MAY 2-8
  • MAY 9-15
  • MAY 16-22
  • MAY 23-29
  • MAY 30–JUNE 5
  • JUNE 6-12
  • JUNE 13-19
  • JUNE 20-26
  • JUNE 27–JULY 3
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2022
mwbr22 May masa. 1-6

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

MAY 2-8

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 27–29

“Mapulani a Davide a Kamenyedwe ka Nkhondo”

it-1 41

Akisi

Kaŵili konse, pamene Davide anali kuthaŵa Sauli, anapeza citetezo m’dela lolamulidwa na Mfumu Akisi. Pa ulendo woyamba, Akisi anaganizila Davide kukhala mdani. Pofuna kudzipulumutsa, Davide anadzipanga ngati wamisala, ndipo Akisi anamulola kuti apite monga citsilu cosadetsa nkhawa. (1 Sam. 21:10-15; Sal. 34: Tumawu twapamwamba; 56:Tumawu twapamwamba) Pa ulendo waciŵili, Davide anali na asilikali 600 pamodzi na mabanja awo, ndipo Akisi anawauza kuti azikhala mumzinda wa Zikilaga. Pa nthawi yokwana caka cimodzi na miyezi inayi imene anakhala kumeneko, Akisi anali kukhulupilila kuti Davide na asilikali ake anali kukacita nkhondo na mizinda yaciyuda, pamene iwo m’ceni-ceni anali kukathila nkhondo mizinda ya Agesuri, Agirezi, na Aamaleki. (1 Sam. 27:1-12) Davide anacita zinthu mocenjela kwambili cakuti Akisi anamukhulupilila, ndipo anamuika kukhala msilikali wake womulondela pamene Afilisiti anali kukonzekela zokacita nkhondo na Mfumu Sauli. Koma atatsala pang’ono kupita kunkhondoko, olamulila ena ogwilizana acifilisiti anaumilila kuti Davide na asilikali ake abwelele ku Zikilaga, ndipo anabweleladi. (1 Sam. 28:2; 29:1-11) Davide atakhala mfumu, anakathila nkhondo mzinda wa Gati. Koma zioneka kuti Akisi sanamuphe. Iye anakhalabe na moyo mpaka mu ulamulilo wa Solomo.—1 Maf. 2:39-41.

w21.03 4 ¶8

Abale Acinyamata—Kodi Mungacite Ciyani Kuti Ena Azikudalilani?

8 Onani copinga cina cimene Davide anakumana naco. Pambuyo pakuti wadzozedwa monga mfumu, Davide anafunika kuyembekezela kwa zaka zambili kuti ayambe kulamulila monga mfumu ya Yuda. (1 Sam. 16:13; 2 Sam. 2:3, 4) Kodi n’ciyani cinamuthandiza kuyembekezela moleza mtima panthawi yonseyo? M’malo molefuka, Davide anasumika maganizo pa zimene akanakwanitsa kucita. Mwacitsanzo, pamene Davide anali kukhala umoyo wothaŵa-thaŵa m’dziko la Afilisiti, anaseŵenzetsa nthawiyo kumenyana na adani a Isiraeli. Mwa kucita zimenezo, Davide anateteza malile a ufumu wa Yuda.—1 Sam. 27:1-12.

it-2 245 ¶6

Bodza

Baibo imaletsa kunama bodza. Koma izi sizitanthauza kuti munthu ayenela kukakamizika kuulula zinthu kwa anthu amene sayenela kuzidziŵa. Yesu Khristu anapeleka malangizo akuti: “Musamapatse agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyela nkhumba ngale zanu, kuopela kuti zingapondeponde ngalezo kenako n’kutembenuka ndi kukukhadzulani.” (Mat. 7:6) Ici ndiye cifukwa cake Yesu nthawi zina sanali kufotokoza mfundo zonse, kapena kupeleka mayankho acindunji pa mafunso ena, ngati kucita zimenezo kukanabweletsa mavuto ena. (Mat. 15:1-6; 21:23-27; Yoh. 7:3-10) Mwacionekele, zimene Abulahamu, Isaki, Rahabi, na Elisa anacita posoceletsa kapena kubisa mfundo zina kwa anthu osalambila Yehova, ziyenela kuonedwa mwanjila imeneyi.—Gen. 12:10-19; capu. 20; 26:1-10; Yos. 2:1-6; Yak. 2:25; 2 Maf. 6:11-23.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w10 1/1 20 ¶5-6

Kodi Akufa Angathandize Amoyo?

Taganizilani izi: Baibo imanena kuti munthu akamwalila “amabwelela kunthaka” ndiponso “zimene anali kuganiza zimathelatu.” (Salimo 146:4) Sauli ndiponso Samueli anali kudziŵa kuti Mulungu amadana na okhulupilila mizimu. N’cifukwa cake Sauli asanayambe kukhulupilila mizimu, anagwila nchito yaikulu yothana na kulambila mizimu.—Levitiko 19:31.

Taganizilani bwino-bwino nkhaniyi. Zikanakhala kuti Samueli anali moyo kwinakwake ngati mzimu, kodi akanalolela kuphwanya lamulo la Mulungu pogwilizana na sing’anga n’colinga coti alankhule na Sauli? Yehova anali atakana kulankhula na Sauli. Ndiyeno kodi sing’anga angakakamize Mulungu, amene ni Wamphamvuzonse kuti alankhule na Sauli kudzela mwa Samueli? Ayi. Apa n’zacidziŵikile kuti mzukwawo sunali Samueli, amene anali mtumiki wokhulupilika wa Mulungu. Koma cinali ciŵanda cimene cinanamizila kuti cinali Samueli amene anamwalila kale.

MAY 9-15

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 30–31

“Dzilimbitseni mwa Yehova Mulungu Wanu”

w06 8/1 28 ¶12

Opani Yehova Kuti Mukhale Acimwemwe

12 Kuopa Yehova kunathandiza Davide kupewa kucita zoipa ndipo kunam’thandiza m’njila zinanso. Kunam’limbikitsa kucita zinthu motsimikiza ndiponso mwanzelu pamene anakumana na zovuta. Kwa caka cimodzi na miyezi inayi, Davide na asilikali ake anathaŵa Sauli n’kukabisala ku Zikilaga m’dziko la Afilisti. (1 Samueli 27:5-7) Nthawi ina iwowa atacokapo, gulu la Aamaleki linaloŵelela mumzinda wawo, kuuyatsa moto n’kutenga akazi awo onse, ana awo onse, na nkhosa zawo zonse. Atabwelela n’kuona zimene zacitika, Davide na asilikali ake analila. Posakhalitsa cisoni cija cinasanduka ukali, ndipo asilikaliwo anayamba kunena zoti am’ponya miyala Davideyo kuti afe. Ngakhale kuti Davide anali atavutika maganizo, sanataye mtima. (Miyambo 24:10) Cifukwa coopa Mulungu, iye anadalila Yehova ndipo “anadzilimbitsa mwa Yehova.” Mothandizidwa na Mulungu, Davide na asilikali ake anagonjetsa Aamaleki na kuwalandanso zinthu zawo zonse zija.—1 Samueli 30:1-20.

w12 4/15 30 ¶14

Yehova Amatiteteza Kuti Tidzapulumuke

14 Davide anakumana na mavuto ambili pa moyo wake. (1 Sam. 30:3-6) Mawu ake ouzilidwa amasonyeza kuti Yehova anali kudziŵa mmene Davide anali kumvela. (Ŵelengani Salimo 34:18; 56:8.) Mulungu amadziŵanso mmene ife timamvela. Iye amatiyandikila tikakhala na “mtima wosweka” kapena ‘tikamadzimvela cisoni mumtima.’ Zimenezi zingatilimbikitse ngati mmene zinalimbikitsila Davide. Iye anaimba kuti: “Ndidzakondwela ndi kusangalala cifukwa ca kukoma mtima kwanu kosatha, pakuti mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwela.” (Sal. 31:7) Koma sikuti Yehova amangoona pamene tikuvutika n’kusiyila pomwepo. Iye amatitonthoza ndiponso kutilimbikitsa kuti tipilile. Njila imodzi imene amacitila zimenezi ni kudzela m’misonkhano yacikhristu.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w05 3/15 24 ¶8

Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba

30:23, 24. Cosankha ici, cogwilizana na lemba la Numeri 31:27, cikusonyeza kuti Yehova amaona anthu amene akugwila nchito zing’ono-zing’ono mumpingo kukhala ofunika kwambili. Cotelo pa ciliconse cimene tikucita tiyenela ‘kucicita ndi moyo wathu wonse ngati kuti tikucitila Yehova, osati anthu.’—Akolose 3:23.

MAY 16-22

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 1-3

“Tiphunzilapo Ciyani pa Nyimbo Yochedwa ‘Uta’?”

w00 6/15 13 ¶9

Lemekezani Anthu Opatsidwa Ulamulilo pa Inu

9 Kodi Davide anavutika maganizo pamene anali kuzunzidwa motelo? “Pali anthu . . . ankhanza amene akufuna moyo wanga,” analila motelo Davide kwa Yehova. (Salimo 54:3) Iye anatsanulila mtima wake kwa Yehova nati: “Inu Mulungu wanga, ndilanditseni kwa adani anga . . . Anthu amphamvu akundiukila, ngakhale kuti ine sindinapanduke kapena kucita chimo lililonse. Iwo akuthamanga ndi kukonzekela kundiukila, ngakhale kuti sindinalakwe ciliconse. Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundicitikila.” (Salimo 59:1-4) Kodi inunso munamvapo cimodzimodzi—kuti palibe cimene munalakwa kwa munthu waulamulilo, koma anapitilizabe kukusautsani? Davide sanalephele kusonyeza ulemu kwa Sauli. Sauli atamwalila, m’malo mosangalala, Davide analemba nyimbo yacisoni yakuti: “Sauli ndi Yonatani, anthu okondeka ndi osangalatsa pamene anali ndi moyo . . . Iwo anali aliwilo kuposa ciwombankhanga, amphamvu kuposa mikango. Ana aakazi a Isiraeli inu, mulilileni Sauli.” (2 Samueli 1:23, 24) Citsanzo cogwila mtima zedi ca ulemu weni-weni kwa wodzozedwa wa Yehova, ngakhale kuti Sauli analakwila Davide!

w12 4/15 10 ¶8

Kusakhulupilika Ndi Cizindikilo ca Masiku Otsiliza

8 Koma Baibo imafotokozanso za anthu ambili amene anakhala okhulupilika. Tiyeni tikambilane zitsanzo ziŵili n’kuona zimene tikuphunzilapo. Tiyamba na munthu amene anakhala wokhulupilika kwa Davide. Yonatani anali mwana wamwamuna woyamba kubadwa wa Mfumu Sauli. Conco iye ni amene anali kuyembekezela kuloŵa ufumu wa Isiraeli. Koma Yehova anasankha Davide kuti adzakhale mfumu yotsatila. Yonatani analemekeza zimene Mulungu anasankha ndipo sankacitila nsanje Davide. M’malomwake Yonatani anayamba ‘kugwilizana kwambili ndi Davide’ ndipo anamulonjeza kuti adzakhalabe wokhulupilika kwa iye. Iye anali kulemekeza Davide monga wodzozedwa wa Mulungu mpaka anamupatsa zovala zake, lupanga lake, uta ndiponso lamba wake. (1 Sam. 18:1-4) Yonatani anacita zonse zimene akanatha kuti ‘alimbikitse Davide.’ Iye anaika moyo wake pa ngozi pofuna kuteteza Davide kuti Sauli asamuphe. Mokhulupilika, Yonatani anauza Davide kuti: “Iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala waciŵili kwa iwe.” (1 Sam. 20:30-34; 23:16, 17) M’pake kuti Yonatani atamwalila, Davide anaimba nyimbo yosonyeza kuti anali kukonda Yonatani ndipo akumva cisoni cacikulu.—2 Sam. 1:17, 26.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 369 ¶2

M’bale

Liwu lakuti “m’bale” limagwilitsidwanso nchito pokamba za anthu amene amagwilizana m’zocita, komanso amene ali na zolinga zofanana. Mwacitsanzo, Mfumu Hiramu ya ku Turo inacha Mfumu Solomo kuti “m’bale wanga,” osati cabe cifukwa cakuti anali na udindo wofanana, komanso mwina cifukwa cakuti anathandizana kupeza matabwa na zinthu zina zomangila kacisi. (1 Maf. 9:13; 5:1-12) Davide analemba kuti “Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili abale akakhala pamodzi mogwilizana!” Izi zionetsa kuti si cibale cakuthupi cokha cimene cimapangitsa anthu a m’banja limodzi kukhala mwamtendele komanso mogwilizana. (Sal. 133:1) Davide anacha Yonatani kuti “m’bale wanga,” osati cifukwa cakuti anali m’bululu wake, koma cifukwa cakuti anali kukondana komanso kugwilizana. (2 Sam. 1:26) Mabwenzi amene ali na zibadwa komanso makhalidwe ofanana amachedwa abale, ngakhale makhalidwe awo atakhala oipa.—Miy. 18:9.

MAY 23-29

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 4-6

“Khalanibe na Mantha Oyenela Oopa Kukhumudwitsa Yehova”

w05 5/15 17 ¶8

Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Wachiŵili

6:1-7. Ngakhale kuti Davide anali na zolinga zabwino, zimene anacita ponyamula Likasa pa galeta zinali zotsutsana na malamulo a Mulungu ndipo zotsatila zake zinali zoopsa. (Eksodo 25:13, 14; Numeri 4:15, 19; 7:7-9) Zimene zinacitika Uza atagwila Likasa zikusonyezanso kuti zolinga zabwino sizisintha zofuna za Mulungu.

w05 2/1 27 ¶20

Yehova Amacita Cilungamo Nthawi Zonse

20 Kumbukilani kuti Uza ayenela kuti anali kudziŵa bwino Cilamulo. Likasa linali kuimila kukhalapo kwa Yehova. Cilamulo cinanenelatu kuti munthu wamba asakhudze Likasa, ndipo cinacenjezelatu kuti ophwanya lamulo limeneli adzalangidwa mwa kuphedwa. (Numeri 4:18-20; 7:89) Motelo, nchito yosamutsa Likasa siinali nchito wamba. Zikuonetsa kuti Uza anali Mlevi (koma osati wansembe), moti ayenela kuti anali kudziŵa zimene Cilamulo cimanena. Ndiponso, zaka zambili m’mbuyomo, Likasa linasamutsidwila ku nyumba ya bambo ake kuti likasungidwe bwino. (1 Samueli 6:20–7:1) Linakhala kumeneko zaka 70, mpaka Davide ataganiza zolisamutsa. Conco kuyambila ali mwana wamng’ono, Uza ayenela kuti anali kudziŵa malamulo okhudza Likasa.

w05 2/1 27 ¶21

Yehova Amacita Cilungamo Nthawi Zonse

21 Monga tachula kale, Yehova amatha kudziŵa za mu mtima wa munthu. Popeza Mawu ake amati zimene Uza anacitazo zinali “kusalingilila,” kapena kupanda ulemu, Yehova ayenela kuti anaona kudzikonda kwa mtundu winawake mwa iye kumene nkhaniyo sinachule mwacindunji. Kodi kapena Uza anali wodzikuza, wokonda kupitilila malile pa zinthu zina? (Miyambo 11:2) Kapena kutsogolela poyela Likasa limene banja lake linali litasunga m’nyumba mwawo kunam’cititsa kunyada? (Miyambo 8:13) Kodi Uza mwina anali na cikhulupililo cocepa zedi, moti anaganiza kuti dzanja la Yehova n’lalifupi, ndipo sangathe kucilikiza Likasa loimila kukhalapo Kwake kuti lisagwe? Kaya cikhale cifukwa cotani, ndife otsimikiza kuti Yehova anacita cilungamo. Ayenela kuti anaona cinacake mu mtima wa Uza cimene cinam’pangitsa kupeleka ciweluzo nthawi yomweyo.—Miyambo 21:2.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w96 4/1 29 ¶1

Senzani Yehova Nkhaŵa Yanu Nthaŵi Zonse

Davide monga mfumu analinso na mlandu wa kucititsa zimenezi. Mcitidwe wake umasonyeza kuti ngakhale awo amene ali na unansi wabwino na Yehova nthaŵi zina angacite zinthu moipa pa mikhalidwe yoyesa. Coyamba Davide anakwiya. Ndiyeno anacita mantha. (2 Samueli 6:8, 9) Unansi wake wodalila Yehova unayesedwa kwambili. Pacocitikaci iye mwacionekele analephela kusenza Yehova nkhaŵa yake, sanatsatile malamulo ake. Kodi mkhalidwewo ungakhale wotelo kwa ife nthaŵi zina? Kodi timaimba mlandu Yehova wakucititsa mavuto amene amakhalapo cifukwa cakuti tanyalanyaza malangizo ake?—Miyambo 19:3.

MAY 30–JUNE 5

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 7-8

“Yehova Anacita Pangano na Davide”

w10 4/1 20 ¶3

“Mpando Wacifumu Wako Udzakhazikika”

Komabe, Yehova anasangalala kwambili na mtima umene Davide anasonyeza ndipo anamulonjeza kuti adzasankha wina m’banja lake kuti adzalamulile mpaka kale-kale. Mulungu anapangana na Davide zimenezi cifukwa coti Davide anali wodzipeleka pom’tumikila ndiponso Mulungu anali kufuna kukwanilitsa ulosi winawake wa m’Baibo. Mneneli Natani ndi amene anapeleka uthenga umenewu kwa Davide. Iye anati: “Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikika pamaso pako mpaka kalekale. Mpando wako wacifumu udzakhazikika mpaka kalekale.” (Vesi 16) Kodi Mfumu yamuyaya imene ikuchulidwa m’pangano limeneli ni ndani?—Salimo 89:20, 29, 34-36.

w10 4/1 20 ¶4

“Mpando Wacifumu Wako Udzakhazikika”

Yesu wa ku Nazarete anali mwana wa Davide. Polengeza za kubadwa kwa Yesu, mngelo wina anati: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wacifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulila monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha konse.” (Luka 1:32, 33) Conco zimene Yehova anapangana na Davide zinakwanilitsidwa mwa Yesu Khristu. Palipano iye akulamulila, osati cifukwa cosankhidwa na anthu, koma cifukwa ca zimene Mulungu analonjeza kuti iye adzalamulila mpaka kale-kale. Zimenezi zikutikumbutsa mfundo yakuti zimene Mulungu amalonjeza, nthawi zonse zimacitikadi.—Yesaya 55:10, 11.

w14 10/15 10 ¶14

Khalani ndi Cikhulupililo Cosagwedela mu Ufumu

14 Ganizilani zimene Yehova analonjeza Davide, Mfumu ya Isiraeli wakale kupyolela mu pangano la Davide. (Ŵelengani 2 Samueli 7:12, 16.) Iye anacita pangano na Davide pamene anali Mfumu ku Yerusalemu. Ndipo anam’lonjeza kuti Mesiya adzacokela m’banja lake. (Luka 1:30-33) Yehova anapeleka malangizo acindunji onena za mzele wobadwila Mesiya. Iye anakamba kuti mbewu imeneyi ya Davide idzakhala ‘yoyenelela mwalamulo’ kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. (Ezek. 21:25-27) Kupyolela mwa Yesu Mesiya, ucifumu wa Davide ‘udzakhazikika mpaka kalekale.’ Ndithudi, mbewu ya Davide “idzakhala mpaka kalekale, ndipo mpando wake wacifumu udzakhala ngati dzuŵa.” (Sal. 89:34-37) Zoonadi, ulamulilo wa Mesiya sudzaipitsidwa, ndipo zimene udzacita zidzakhala kwamuyaya!

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2 206 ¶2

Masiku Otsiliza

Ulosi wa Balamu. Aisiraeli asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, mneneli Balamu anauza Balaki Mfumu ya Mowabu kuti: “Tamvelani, ndikuuzeni zimene anthuwa adzacite kwa anthu anu kumapeto kwa masiku otsiliza. . . Ndithu nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo, ndodo yacifumu idzatulukadi mu Isiraeli. Ndipo iye adzaphwanya cipumi ca Mowabu ndi cigaza ca ana onse ankhondo.” (Num. 24:14-17) Pa kukwanilitsidwa koyamba kwa ulosiwu, “nyenyezi” inaimila Mfumu Davide amene anagonjetsa Amowabu. (2 Sam. 8:2) Conco n’zoonekelatu kuti pa kukwanilitsidwa koyamba kumeneko, “masiku otsiliza” anayamba pamene Davide anakhala mfumu. Popeza kuti Davide anali kucitila cithunzi Yesu, Mfumu yaumesiya, ulosiwu udzakwanilitsidwanso pa Yesu pa nthawi imene adzagonjetsa adani ake.—Yes. 9:7; Sal. 2:8, 9.

JUNE 6-12

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 9-10

“Davide Anaonetsa Cikondi Cosasintha”

w06 6/15 14 ¶6

Mungapezedi Cimwemwe

“Davide analemba kuti: “Wodala [wacimwemwe] ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka.” Anapitiliza kuti: “Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa. Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo. Adzachedwa wodala padziko lapansi.” (Salimo 41:1, 2) Cisamalilo cimene Davide anapatsa Mefiboseti, mwana wolemala wa Yonatani, mnzake wapamtima wa Davide, ni citsanzo ca kukoma mtima kumene tiyenela kuonetsa kwa anthu osautsika.—2 Samueli 9:1-13.

w05 5/15 17 ¶12

Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Wachiŵili

9:1, 6, 7. Davide anakwanilitsa lonjezo lake. Ifenso tiziyesetsa kukwanilitsa zimene talonjeza.

w02 2/15 14 ¶10

Anthu Okhulupilika Analimbana na Minga M’matupi Awo

10 Patapita zaka, Mfumu Davide anam’komela mtima Mefiboseti cifukwa ca cikondi cacikulu cimene anali naco kwa Yonatani. Davide anapatsa Mefiboseti minda yonse ya Sauli ndipo anauza mnyamata wa Sauli, Ziba, kuti azisamalila mindayo. Davide anauzanso Mefiboseti kuti: “Uzidya mkate patebulo langa nthawi zonse.” (2 Samueli 9:6-10) N’zosakayikitsa kuti kukoma mtima kwa Davide kunatonthoza Mefiboseti ndipo kunathandiza kucepetsa kuŵaŵa kumene anali kumva cifukwa ca kupunduka kwake. Citsanzo cabwinotu cimeneci! Ifenso tiziwakomela mtima anthu amene akulimbana na munga m’thupi mwawo.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 266

Ndevu

Anthu ambili akale a Kum’maŵa kwa Asia, kuphatikizapo Aisiraeli, anali kuona ndevu kukhala cizindikilo ca ulemu wa mwamuna. Mulungu analamula Aisiraeli kuti asamacotse “ndevu zotsikila m’masaya,” tsitsi la pakati pa makutu na maso, komanso nsonga za ndevu zawo. (Lev. 19:27; 21:5) Mosakayikila anapeleka lamuloli cifukwa m’mitundu ina, kucita zimenezi unali mwambo wacipembedzo.

JUNE 13-19

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 11-12

“Musalole Zilakolako Zoipa Kukulamulilani”

w21.06 17 ¶10

Mungathe Kuwonjoka m’Misampha ya Satana!

10 Dyela linapangitsa Mfumu Davide kuiŵala zimene Yehova anam’patsa, kuphatikizapo cuma, kuchuka, na kugonjetsa adani ake ambili pankhondo. Davide moyamikila anavomeleza kuti mphatso za Mulungu ‘zinali zoculuka kwambili moti sakanatha kuzifotokoza.’ (Sal. 40:5) Koma pa nthawi ina Davide anaiŵala zimene Yehova anam’patsa. Sanapitilize kukhala wokhutila, anali kufunanso zina. Olo kuti Davide anali na akazi ambili, analola cilako-lako cosayenela cokhumbila mkazi wa mwini kukula mu mtima mwake. Mkaziyo dzina lake anali Batiseba, ndipo mwamuna wake anali Uriya Mhiti. Modzikonda Davide anagona na Batiseba, ndipo anakhala na pathupi. Zimene anacita Davide zinali zoipa kwambili, koma anacita zoposa pamenepo. Anakonza zakuti Uriya aphedwe! (2 Sam. 11:2-15) Kodi Davide anali kuganiza ciani? Kodi anali kuganiza kuti Yehova sangaone? Mtumiki wa Yehova ameneyo yemwe poyamba anali wokhulupilika, anagwela mu msampha wa dyela ndipo anakumana na mavuto aakulu. Koma cokondweletsa n’cakuti pambuyo pake, Davide anavomeleza colakwa cake ndipo analapa. Iye anayamikila kwambili kuti wayanjidwanso na Yehova!—2 Sam. 12:7-13.

w19.09 17 ¶15

Gonjelani Yehova na Mtima Wonse

15 Davide anali mutu wa banja, ndipo Yehova anamuikanso kukhala mfumu ya mtundu wonse wa Isiraeli. Pokhala mfumu, Davide anali na mphamvu zambili za ulamulilo. Pa nthawi ina, iye anaseŵenzetsa molakwika mphamvu zake, moti anacita zolakwa zazikulu. (2 Sam. 11:14, 15) Komabe, Davide anagonjela Yehova. Motani? Analandila uphungu umene anapatsidwa. Komanso anakhuthulila Yehova nkhawa zake m’pemphelo. Ndipo anayesetsa kumvela uphungu wa Yehova. (Sal. 51:1-4) Kuwonjezela apo, anaonetsa kudzicepetsa mwa kulandila uphungu wanzelu wocokela kwa amuna, ngakhalenso kwa akazi. (1 Sam. 19:11, 12; 25:32, 33) Davide anaphunzilapo kanthu pa zolakwa zake, ndipo anasumika maganizo ake pa kutumikila Yehova.

w18.06 17 ¶7

Lolani Malamulo a Mulungu na Mfundo Zake Kuphunzitsa Cikumbumtima Canu

7 Sitifunika kucita kuphwanya malamulo a Mulungu kuti tidziŵe kuopsa kocita zimenezo. Tingaphunzilepo kanthu pa zolakwa za ena, amene nkhani zawo zinalembedwa m’Mawu a Mulungu. Lemba la Miyambo 1:5, limati: “Munthu wanzelu amamvetsela ndi kuphunzila malangizo owonjezeleka.” Kukamba zoona, timalandila malangizo abwino kwambili kucokela kwa Mulungu. Imodzi mwa njila zimene timalandilila malangizowo ni mwa kuŵelenga na kusinkha-sinkha nkhani za anthu ochulidwa m’Baibo. Mwacitsanzo, ganizilani mavuto amene Mfumu Davide anakumana nawo cifukwa cophwanya lamulo la Yehova mwa kucita cigololo na Bati-seba. (2 Sam. 12:7-14) Pamene tiŵelenga nkhaniyi, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Davide akanapewa bwanji mavuto amene anakumana nawo cifukwa cocita cigololo na Bati-seba? Ngati nitakumana na ciyeso cofanana na cimeneci, ningacite ciani? Kodi ningathaŵe monga mmene Yosefe anacitila, kapena ningagonje ngati Davide?’ (Gen. 39:11-15) Ngati tiganizila zotulukapo zoipa za chimo, tidzayamba kudana kwambili na coipa.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 590 ¶1

Davide

Komabe, Yehova anali kuona, ndipo anaulula zoipa zonse zimene Davide anacita. Yehova akanalola kuti chimo la Davide na Betiseba lisamalidwe na oweluza mogwilizana na Cilamulo ca Mose, onse aŵili akanaphedwa, ndipo mwana wam’cigololo wosabadwayo akanaphedwa pamodzi na amayi ake. (Deut. 5:18; 22:22) Komabe, Yehova anasamalila yekha nkhaniyo, ndipo anam’citila cifundo Davide cifukwa ca pangano la Ufumu (2 Sam. 7:11-16), mosakayikila cifukwanso cakuti Davide naye anacitila ena cifundo (1 Sam. 24:4-7; yelekezelani na Yak. 2:13) komanso cifukwa Mulungu anaona kuti ocimwawo alapa. (Sal. 51:1-4) Koma iwo sanapulumuke mbali zonse za cilangoco. Kupitila mwa mneneli Natani, Yehova anakamba kuti: “Taona, ndikukugwetsela tsoka m’nyumba yako yomwe.”—2 Sam. 12:1-12.

JUNE 20-26

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 13-14

“Dyela Linamubweletsela Mavuto Aakulu Aminoni”

it-1 32

Abisalomu

Kuphedwa kwa Aminoni. Kukongola kwa Tamara, mlongosi wake wa Abisalomu kunapangitsa Aminoni, mkulu wake wa Abisalomu wa mimba ina, kukopeka naye. Aminoni ananamizila kudwala ndipo anapempha kuti Tamara abwele kunyumba kwake kudzamuphikila cakudya, kenako anamugwilila. Aminoni atagwilila Tamara, anadana naye kwambili kuposa mmene anali kumukondela poyamba. Ndipo analamula kuti Tamara atulutsidwe azipita. Zitatelo, Tamara anang’amba covala cake camizele-mizele, cimene cinali kum’dziŵikitsa monga namwali, mwana wamkazi wa mfumu, ndipo anaika phulusa pamutu pake. Kenako anakumana na Abisalomu. Iye mwamsanga anadziŵa zimene zinacitikila mlongo wake, ndipo mwamsanga anaganizila Aminoni kuti ndiye anamucita cipongweco, kuonetsa kuti anali kudziŵa kale kuti Aminoni anali kukhumbila mlongo wake. Abisalomu anauza mlongo wake kuti angoileka nkhaniyo. Kenako anamutenga n’kupita kukakhala naye kunyumba kwake.—2 Sam. 13:1-20.

w17.09 5 ¶11

Phunzilani Kukhala Wodziletsa

11 M’Baibo mulinso zitsanzo zoticenjeza za anthu amene anacita ciwelewele cifukwa ca kusadziletsa. Imafotokozanso mavuto amene amatulukapo cifukwa ca kusadziletsa. Ngati mukukumana na ciyeso monga cimene Kim anakumana naco, mungacite bwino kuganizila mozama nkhani ya mnyamata wopanda nzelu wochulidwa pa Miyambo caputa 7. Mufunikanso kuganizila zimene Aminoni anacita, na mavuto amene anakumana nawo cifukwa ca khalidwe lake loipa. (2 Sam. 13:1, 2, 10-15, 28-32) Makolo angathandize ana awo kucita zinthu mwanzelu na kukhala odziletsa pa nkhani ya cikondi ca pakati pa mwamuna na mkazi. Angacite zimenezi mwa kukambilana nawo pa kulambila kwa pabanja nkhani za m’Baibo zimene tachulazi.

it-1 33 ¶1

Abisalomu

Zaka ziŵili zinapita. Tsopano inali nthawi yacikondwelelo, yometa ubweya wa nkhosa. Ndipo Abisalomu anakonza phwando ku Baala-hazori, mzinda umene unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 22, kumpoto cakum’maŵa kwa Yerusalemu. Iye anaitanila mfumu Davide kuphwandolo na ana ake. Atate ake atapempha kuti asapezekepo, Abisalomu anawaumiliza kuti atumize Aminoni mwana wawo woyamba m’malo mwa iwo. (Miy. 10:18) Kuphwandoko, pamene Aminoni ‘anasangalala mumtima mwake ndi vinyo,’ Abisalomu analamula atumiki ake kuti amuphe Aminoni. Ana ena a mfumu anabwelela ku Yerusalemu, ndipo Abisalomu na ambuye ake acisiriya anathaŵila ku dela la ufumu wa Gesuri, kum’maŵa kwa Nyanja ya Galileya. (2 Sam. 13:23-38) Apa tsopano “lupanga” limene mneneli Natani analosela linaloŵa “m’nyumba” ya Davide, ndipo silinacokemo pa nthawi yonse imene Davide anali na moyo.—2 Sam. 12:10.

Kufufuza Cuma Cauzimu

g04 12/22 8-9

Kukongola Kofunika Kwambili

Mosiyana ndi zimenezi, taganizilani za Abisalomu, mmodzi mwa ana a Davide. Anadzakhala munthu woipa kwambili ngakhale kuti anali wooneka bwino. Ponena za iye, Baibo imati: “Tsopano mu Isiraeli yense munalibe mwamuna wina wotamandika kwambili koposa Abisalomu cifukwa ca kukongola kwake. Iye analibe cilema ciliconse kuyambila kuphazi mpaka paliwombo.” (2 Samueli 14:25) Komabe, mtima wa Abisalomu wofuna kukhala na udindo unamucititsa kuukila bambo ake na kulanda ufumu wawo. Anafika mpaka pogona na akazi aang’ono a bambo ake. Cifukwa ca zimenezi, Abisalomu anakwiyitsa Mulungu ndipo anafa imfa yopweteka.—2 Samueli 15:10-14; 16:13-22; 17:14; 18:9, 15.

Kodi mumakopeka na Abisalomu? Ayi ndithu. Iye anali munthu wakhalidwe lonyansa. Kukongola kwake kogometsa sikunalungamitse kukula mtima na kusakhulupilika kwake, ndiponso sikunamuteteze kuti asawonongedwe. Koma m’Baibo muli zitsanzo zambili za anthu anzelu ndiponso okopa amene sanachulidwe maonekedwe awo. Mwacidziŵikile, cimene cinali cofunika kwambili cinali kukongola kwawo kwa mumtima.

JUNE 27–JULY 3

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 15-17

“Dyela Linamubweletsela Mavuto Aakulu Aminoni”

it-1 860

Kalambulabwalo

Malinga na cikhalidwe ca anthu a kum’mawa kwa Asia, panali kukhala anthu othamanga amene anali kutsogola galeta la mfumu lisanafike n’colinga cokonzekela komanso kulengeza za kubwela kwa mfumu, na kukam’thandiza pa mbali zosiyanasiyana. (1 Sam. 8:11) Podzifunila ulemu wacifumu ngati umenewo, Abisalomu na Adoniya anadziikila amuna 50 othamanga patsogolo pa magaleta awo, pa nthawi imene aliyense wa iwo anapandukila mfumu. Iwo anacitanso izi pofuna kuchuka komanso kupangitsa anthu kuona kuti iwo ni ovomelezeka kukhala mfumu.—2 Sam. 15:1; 1 Maf. 1:5.

w12 7/15 13 ¶5

Tumikilani Mulungu Amene Amapeleka Ufulu

5 M’Baibulo muli zitsanzo zambili za anthu amene anapotoza maganizo a anzawo. Citsanzo cina ni mwana wa Mfumu Davide, dzina lake Abisalomu. Iye anali mwamuna wooneka bwino kwambili. Koma mofanana na Satana, anayamba kulakalaka udindo ndiponso mphamvu. Anayamba kusilila mpando wacifumu wa abambo ake ngakhale kuti sanali woyenela kukhala pa mpandowu. Pofuna kulanda ufumu mocenjela, Abisalomu ankanamizila kuti amakonda kwambili Aisiraeli anzake. Anali kuwacititsa kuganiza kuti mfumu na anthu ake sawaganizila. Mofanana na Mdyelekezi m’munda wa Edeni, Abisalomu anali kudzionetsa ngati akufuna kuthandiza anthu koma pa nthawi imodzimodziyo akuipitsa mbili ya atate wake.—2 Sam. 15:1-5.

it-1 1083-1084

Heburoni

Patapita zaka, Abisalomu mwana wa Davide anabwelela ku Heburoni, ndipo kumeneko anakonza ciwebu colanda ufumu atate ake, koma analephela. (2 Sam. 15:7-10) Abisalomu anasankha mzinda wa Heburoni kukhala koyambila kampeni yake yofuna kulanda ufumu. Cioneka kuti anayambila kumeneko cifukwa pa nthawi ina mzindawo unali likulu la Yuda, ndipo n’kumenenso anabadwila. Patapita nthawi, Mfumu Rehobowamu mdzukulu wa Davide, anamanganso mzinda wa Heburoni. (2 Mbiri 11:5-10) Pambuyo pakuti Ufumu wa Yuda waonongedwa na Ababulo ndipo Ayuda amene anatengedwela ku ukapolo abwelela, ena mwa Ayudawo anakakhala ku Heburoni (kapena kuti Kiriyati-ariba).—Neh. 11:25.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w18.08 6 ¶11

Kodi Mudziŵa Bwino Zoona Zake?

11 Aliyense wa ise nthawi ina angacitilidwe zinthu zopanda cilungamo cifukwa cakuti anthu ena anafalitsa nkhani yabodza yokhudza ise. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika pakati pa Mfumu Davide na Mefiboseti. Davide anaonetsa kuwoloŵa manja na kukoma mtima kwa Mefiboseti mwa kum’bwezela munda wonse wa Sauli, ambuye ake. (2 Sam. 9:6, 7) Koma pambuyo pake, Davide anauzidwa zinthu zina zabodza zokhudza Mefiboseti. Popanda kufufuza zoona pa nkhaniyo, Davide analanda Mefiboseti zinthu zake zonse. (2 Sam. 16:1-4) Koma pambuyo pokamba naye Mefiboseti, Davide anazindikila kuti analakwitsa, ndipo anam’bwezela Mefiboseti zinthu zake. (2 Sam. 19:24-29) Davide akanayamba wafufuza zoona zeni-zeni za nkhaniyo, m’malo mofulumila kucitapo kanthu, akanapewa kucita colakwa cimeneci.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani