Malifalensi a Kabuku ka Umoyo
© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JANUARY 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 32-33
Tonthozani Aja Amene Ali na Nkhawa
it-1 710
Elihu
Elihu analibe tsankho. Iye sanali kucita zinthu pofuna kungokondweletsa munthu. Anazindikila kuti mofanana na Yobu, nayenso anapangidwa na dothi ndipo Wamphamvuzonse ndiye Mlengi wawo. Elihu sanali na colinga comuopseza Yobu, koma anakamba naye monga bwenzi lenileni, mwa kumuchula dzina, zimene Elifazi, Bilidadi, na Zophari sanacite.—Yobu 32:21, 22; 33:1, 6.
Kodi Mumaona Anthu Ofooka Mmene Yehova Amawaonela?
8 Tikhoza kuŵamvetsa bwino abale athu tikamakumbukila zimene iwo akupilila. Ena mwa iwo akudwala, ena ali pabanja na munthu wosakhulupilila, ndipo ena akuvutika kwambili na nkhawa. Mwina tsiku lina ifenso tidzakumana na mavuto omwewo. Aisiraeli ali ku Iguputo anali osauka ndiponso ofooka. Ndiyeno asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, anakumbutsidwa kuti ‘asamaumile mtima’ abale awo ovutika. Yehova anali kufuna kuti iwo asamanyoze anthu osauka koma aziŵathandiza.—Deut. 15:7, 11; Lev. 25:35-38.
9 Tiyenela kulimbikitsa anthu amene akukumana na mavuto osati kuŵaweluza kapena kuŵakayikila. (Yobu 33:6, 7; Mat. 7:1) Tiyelekezele kuti munthu wacita ngozi pamsewu n’kufika naye kucipatala. Kodi madokotala amayamba kufufuza ngati wacititsa ngozi ni iyeyo? Ayi, koma amayamba mwamsanga kumuthandiza. N’cimodzimodzinso na Mkhristu mnzathu amene wafooka cifukwa cokumana na mavuto. Tiyenela kuyamba mwamsanga kumulimbikitsa.—Ŵelengani 1 Atesalonika 5:14.
10 Kuganizila kwambili zimene abale athu akukumana nazo kungatithandize kuona zofooka zawo m’njila yoyenela. Mwacitsanzo, taganizilani za alongo amene akhala akutsutsidwa na amuna awo kwa zaka zambili. Iwo akhoza kuoneka ofooka komabe amasonyeza cikhulupililo colimba komanso kupilila. Kodi mumamva bwanji mukamaona mlongo amene akulela yekha ana akubwela ku misonkhano limodzi na anawo? Kodi mumamuyamikila cifukwa ca cikhulupililo cake ndiponso khama lake? Nanga mumamva bwanji mukaona acinyamata amene akukhala okhulupilika ngakhale kuti amakumana na mayeselo kusukulu? Kukhala odzicepetsa kungatithandize kuzindikila kuti anthu amene amaoneka ngati ofooka angakhale “olemela m’cikhulupililo” mofanana na anthu amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendela.—Yak. 2:5.
Kodi Nthawi Yoyenela Kukamba ni Iti?
17 Munthu wacinayi amene anakamba na Yobu anali Elihu, m’bululu wake wa Abulahamu. Iye anali kumvetsela pamene Yobu na amuna atatuwo anali kulankhula. Mwacionekele, pa nthawiyo Elihu anali kumvetsela mwachelu. Takamba conco cifukwa pambuyo pake, iye anakwanitsa kupatsa Yobu uphungu mwacikondi koma mosapita m’mbali. Uphunguwo unathandiza Yobu kuwongolela maganizo ake. (Yobu 33:1, 6, 17) Colinga cacikulu ca Elihu cinali kulemekeza Yehova, osati kudzilemekeza iye mwini kapena wina aliyense. (Yobu 32:21, 22; 37:23, 24) Pa citsanzo ca Elihu tiphunzilapo kuti pali nthawi yoyenela kukhala cete na nthawi yoyenela kukamba. (Yak. 1:19) Tiphunzilaponso kuti pamene tipatsa ena uphungu, colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala kulemekeza Yehova osati kudzipezela ulemu.
18 Tingaonetse kuti timayamikila mphatso ya kulankhula mwa kutsatila malangizo a m’Baibo onena za nthawi yoyenela kukamba na nthawi yoyenela kukhala cete. Mfumu ya nzelu Solomo anauzilidwa kulemba kuti: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenela ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miy. 25:11) Ngati timvetsela mwachelu pamene ena akamba, komanso kuganizilapo tisanayankhe, mawu athu adzakhala monga zipatso za maapozi agolide. Adzakhala abwino komanso opindulitsa. Mwa kutelo, zokamba zathu kaya zikhale zocepa kapena zambili, zidzakhala zolimbikitsa kwa ena, ndiponso tidzakondweletsa Yehova. (Miy. 23:15; Aef. 4:29) Ndithudi, iyi ni njila yabwino kwambili yoonetsela kuti timayamikila mphatso yocokela kwa Mulungu imeneyi ya kulankhula!
Kufufuza Cuma Cauzimu
w13 1/15 19 ¶10
Pitilizani Kuyandikila Yehova
10 M’pomveka kuganizilanso za maonekedwe athu. Koma si bwino kumangoganizila zimene tingacite kuti tifufute zizindikilo zonse za ukalamba. Zizindikilo zotelezo zikhoza kusonyeza kuti ndife anzelu, olemekezeka komanso kuti munthu wamkati ni wokongola. Pajatu Baibo imati: “Imvi ndizo cisoti cacifumu ca ulemelelo zikapezeka m’njila yacilungamo.” (Miy. 16:31) Umu ni mmene Yehova amationela ndipo ifenso tizidziona conco. (Ŵelengani 1 Petulo 3:3, 4.) Cotelo kodi ni bwino kucititsa maopaleshoni oopsa kapena kuyamba kugwilitsa nchito mankhwala oopsa n’colinga coti tizingooneka okongola? “Cimwemwe cimene Yehova amapeleka” n’cimene cimakongoletsa munthu ngakhale wokalamba kapena wodwala cifukwa cakuti cimacokela mumtima. (Neh. 8:10) M’dziko latsopano ni mmene tidzakhala na thanzi langwilo komanso kuoneka okongola ngati kamwana. (Yobu 33:25; Yes. 33:24) Poyembekezela nthawi imeneyo, tiyeni tizicita zinthu mwanzelu ndiponso kukhala na cikhulupililo camphamvu. Kucita zimenezi kungatithandize kuyandikilabe Yehova ndiponso kukhala na moyo wabwino ngakhale pali pano.—1 Tim. 4:8.
JANUARY 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 34-35
Ngati Zinthu Sizikukuyendelanipa Umoyo
Kodi Mulungu Ali Na Makhalidwe Abwanji?
Nthawi zonse Mulungu amacita zoyenela. Ndipo ‘Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuzonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.’ (Yobu 34:10) Ziweluzo zake n’zolungama, monga mmene wamasalimo anauzila Yehova kuti: “Mudzaweluza anthu molungama.” (Salimo 67:4) Popeza “Yehova amaona mmene mtima ulili,” iye sapusitsika na cinyengo, koma amadziŵa zoona zeni-zeni na kupeleka ziweluzo zoyenelela. (1 Samueli 16:7) Kuwonjezela apo, Mulungu amadziŵa kupanda cilungamo kulikonse komanso ziphuphu zimene zikucitika padziko lapansi, ndipo walonjeza kuti posacedwa “oipa adzacotsedwa padziko lapansi.”—Miyambo 2:22.
Kodi Cidzacokapo N’ciani Ufumu wa Mulungu Ukadzabwela?
5 Kodi Yehova adzacita ciyani? Palipano, iye wapeleka mwayi kwa anthu oipa kuti asinthe khalidwe lawo. (Yes. 55:7) Woipa aliyense payekha akalibe kulandila ciweluzo cake. Koma dziko loipali linaweluzidwa kale kuti lidzawonongedwa. Nanga bwanji za anthu oipa amene sadzasintha, amene adzapitiliza kucilikiza dongosolo loipali mpaka pamene cisautso cacikulu cidzayamba? Yehova anakamba kuti adzaŵawononga kothelatu. (Ŵelengani Salimo 37:10.) Anthu ena oipa angaganize kuti adzapulumuka ciwonongeko cimeneco. Ambili m’dzikoli amayesetsa kubisa zocita zawo zoipa, ndipo nthawi zambili salandila cilango pa zocita zawozo. (Yobu 21:7, 9) Koma, Baibo imati: “Maso [a Mulungu] amayang’anitsitsa njila za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse. Kulibe mdima wandiweyani woti amene akucita zopweteka ena abisaleko.” (Yobu 34:21, 22) Kukamba zoona, palibe amene angathaŵe ciweluzo ca Yehova Mulungu. Iye sanganamizidwe na munthu aliyense wacinyengo. Mulungu amaona ciliconse, ndipo palibe cimene cingamulepheletse kuona zoipa zimene munthu amacita ngakhale atabisa bwanji. Pambuyo pa Aramagedo, tidzaona pamene panali kukhala oipa, koma sadzapezekapo. Iwo sadzakhalakonso.—Sal. 37:12-15.
Kodi Mudzapunthwa Cifukwa ca Yesu?
19 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. Ambili masiku ano amakhumudwa nafe cifukwa cakuti sititengako mbali m’zandale. Iwo amafuna kuti tizivotako pa masankho. Komabe, timadziŵa kuti tikasankha mtsogoleli waumunthu kuti azitilamulila, ndiye kuti tikukana Yehova. (1 Sam. 8:4-7) Anthu amaona kuti tiyenela kumanga masukulu, zipatala, komanso kucita zinthu zina zothandiza anthu. Iwo amakana uthenga wathu cifukwa timasumika maganizo athu pa nchito yolalikila, osati pa kuthetsa mavuto amene ali padzikoli.
20 Tingacite ciyani kuti tisapunthwe? (Ŵelengani Mateyu 7:21-23.) Colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala pa kugwila nchito imene Yesu anatilamula. (Mat. 28:19, 20) Tisatengeke na zandale kapena kutangwanika pofuna kuyesa kuthetsa mavuto a m’dzikoli. Timakonda anthu, ndipo timasamala za mavuto awo. Koma tidziŵa kuti njila yabwino yothandizila anansi athu, ni kuŵaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu ndiponso kuŵathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino na Yehova.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Yehova Atamandike Cifukwa ca Kudzipeleka Kwanu!
3 Yehova sanam’dzudzule Elihu pamene anafunsa kuti: “Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa ciyani [Mulungu]? Kodi amalandila ciyani kucokela m’manja mwanu?” (Yobu 35:7) Kodi pamenepa Elihu anali kutanthauza kuti zimene timacita potumikila Mulungu n’zopanda phindu? Iyayi. Anali kutanthuza kuti Yehova payekha ni wacikwane-kwane. Pamene timulambila sitimupangitsa kukhala wolemela, kapena wamphamvu kwambili. M’malomwake, zinthu zilizonse zabwino, maluso, kapena mphamvu zimene tili nazo ni mphatso zocokela kwa Mulungu, ndipo iye amakondwela ngati tizigwilitsa nchito moyenela.
JANUARY 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 36-37
Cifukwa Cake Muyenela Kukhulupilila Lonjezo la Mulungu la Moyo Wosatha
Kodi Mulungu Ndi Wosamvetsetseka?
MULUNGU ALIBE CHIYAMBI KOMANSO MAPETO: Baibo imanena kuti Mulungu wakhala alipo “kuyambila kalekale” ndipo adzakhalapo “mpaka kalekale.” (Salimo 90:2) Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu alibe ciyambi komanso mapeto. Anthufe sitingathe kumvetsa zimenezi cifukwa “zaka zake n’zosaŵelengeka.”—Yobu 36:26.
Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Mulungu amatilonjeza kuti adzatipatsa moyo wosatha ngati titamudziŵa n’kumacita zimene amafuna. (Yohane 17:3) Kodi zikanakhala zomveka kuti Mulungu alonjeze anthu moyo wosatha zikanakhala kuti Mulunguyo sadzakhalapo mpaka kalekale? Ni “Mfumu yamuyaya” yokha yomwe ingalonjeze zimenezi.—1 Timoteyo 1:17.
Kodi Mumayamikila Mphatso Zimene Mulungu Anakupatsani?
6 Padziko lapansi pali madzi cifukwa cakuti dziko lili pa mtunda woyenelela kucokela ku dzuŵa. Dziko likanakhalako pafupi na dzuŵa, sembe madzi onse anauma, ndipo pa dziko pakanakhala potentha kwambili ndiponso popanda camoyo ciliconse. Komanso, dziko likanakhala kutali pang’ono na dzuŵa, madzi onse akanaundana, ndipo pa dziko pakanakhala ayisi yekha-yekha na sinoo. Popeza kuti Yehova anaika dziko lapansi pamalo oyenelela, zungulile-zungulile wa madzi padzikoli umathandiza kuti pakhalebe zamoyo. Dzuŵa likawomba pa nyanja ndiponso pa mtunda, madzi amacita nthunzi n’kukwela kumwamba kukapanga mitambo. Pa caka, madzi amene amakwela kumwamba monga nthunzi cifukwa ca dzuŵa, amakhala ambili kuposa a m’nyanja zonse padziko lapansi, kupatulapo cabe a m’nyanja zamcele (maosheni). Madzi akakwela kumwamba monga nthunzi, amakhala kumeneko kwa masiku pafupi-fupi 10, kenako amagwa monga mvula kapena sinoo. Zikatelo, madziwo amabwelelanso ku nyanja na ku mitsinje, ndipo zomwe takamba zija zimayambanso kucitika. Yehova anapanga dongosolo limeneli n’colinga cakuti pa dziko pazikhala madzi nthawi zonse. Izi zionetsa kuti iye ni wanzelu komanso wamphamvu.—Yobu 36:27, 28; Mlal. 1:7.
Pitilizani Kulimbitsa Ciyembekezo Canu
16 Ciyembekezo cathu codzakhala na moyo kwamuyaya, ni mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Mulungu. Tiyembekezela mwacidwi tsogolo labwino limeneli, limene ndife otsimikiza kuti lidzabweladi. Ciyembekezoci cili monga nangula. Cimatithandiza kuti tisasunthike polimbana na mayeso, pozunzidwa, ngakhale poyang’anizana na imfa. Cilinso ngati cisoti colimba cimene cimateteza maganizo athu kuti tikanize zosayenela na kumamatila ku zabwino. Ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo cimeneci, cimatiyandikilitsa kwa Mulungu, komanso cimaonetsa kukula kwa cikondi cathu pa iye. Timapindula kwambili tikamasunga ciyembekezo cathu cili colimba.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 492
Kulankhulana
M’nthawi za m’Baibo, anthu anali kutumizilana mauthenga na malingalilo m’njila zosiyanasiyana. Nthawi zambili, nkhani za m’dziko lomwelo komanso za ku maiko ena zinali kufalitsidwa mwa uthenga wa pakamwa. (2 Sam. 3:17, 19; Yobu 37:20) Anthu amene anali kuyenda maulendo aatali pogwilitsa nchito ngamila kapena abulu, ni amene anali kusimba nkhani za ku maiko akutali akaima kuti adye cakudya, kumwa madzi, komanso kucitako zinthu zina mumzinda, kapena pa malo ena ake. Kambili nkhani za m’dzikolo kapena za ku maiko ena, anthu anali kuzimvela ku malo ocitilako malonda mumzinda.
JANUARY 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 38-39
Kodi Mumapatula Nthawi Kuyang’ana Zacilengedwe?
Kodi Mudzayembekezela Yehova Moleza Mtima?
7 Pofotokoza mmene Yehova analengela dziko lapansi, Baibo imakamba kuti iye “anaika miyezo yake,” “maziko ake,” komanso “mwala wake wapakona.” (Yobu 38:5, 6) Iye anatenganso nthawi yoyang’ana zinthu zimene analenga. (Gen. 1:10, 12) Ganizilani mmene angelo anamvelela atayamba kuona zinthu zimene Yehova anali kulenga. Iwo ayenela kuti anakondwela ngako na zimenezi! Ndipo pa nthawi ina, iwo “anayamba kufuula ndi cisangalalo.” (Yobu 38:7) Kodi tiphunzilaponji pamenepa? Tiphunzilapo kuti Yehova anatenga zaka masauzande kuti atsilize kulenga zinthu zonse. Ndipo atayang’ana zonse zimene analenga mwaluso, iye anaona kuti “zinali zabwino kwambili.”—Gen. 1:31.
Ciukililo Cimaonetsa Kuti Mulungu ni Wacikondi, Wanzelu, Komanso Woleza Mtima
2 Coyamba, Yehova analenga Mwana wake, Yesu. Ndiyeno kupitila mwa Mwana wake ameneyu, “zinthu zina zonse zinalengedwa,” kuphatikizapo angelo mamiliyoni ambili. (Akol. 1:16) Yesu anali kukondwela kwambili kuseŵenzela pamodzi na Atate wake. (Miy. 8:30) Nawonso angelo anali kukondwela. Iwo anali kuona pamene Yehova na Yesu Mmisili Waluso anali kulenga kumwamba na dziko lapansi. Kodi anaonetsa bwanji cisangalalo cawo? Baibo imakamba kuti dziko litalengedwa, iwo “anayamba kufuula ndi cisangalalo.” Ndipo mosakayikila anapitiliza kusangalala na zonse zimene Yehova analenga, maka-maka anthu. (Yobu 38:7; Miy. 8:31) Zolengedwa zonsezi zimaonetsa kuti Yehova ni wacikondi komanso wanzelu.—Sal. 104:24; Aroma 1:20.
Phunzilani Zambili za Yehova Poyang’ana Cilengedwe Cake
8 Yehova ni woyenela kumukhulupilila. Yehova anathandiza Yobu kuti akulitse cidalilo cake mwa iye. (Yobu 32:2; 40:6-8) Pamene Mulungu anali kukamba na Yobu anachula zinthu zambili zacilengedwe, monga nyenyezi, mitambo, komanso mphenzi. Yehova anakambanso za nyama monga ng’ombe yamphongo ya kuchile na hachi. (Yobu 38:32-35; 39:9, 19, 20) Zinthu zonsezi zinapeleka umboni wakuti Mulungu ali na mphamvu zazikulu, cikondi, na nzelu zakuya. Cifukwa ca makambilano amenewa, Yobu anayamba kum’khulupilila kwambili Yehova kuposa kale lonse. (Yobu 42:1-6) Mofananamo, tikamaphunzila zacilengedwe timakumbutsidwa kuti Yehova ali na nzelu zakuya komanso ni wamphamvu kupambana ife. Ndipo mosapeneka konse, iye adzathetsanso mavuto onse amene timakumana nawo. Mfundo imeneyi ingatithandize kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa iye.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 222
Wopeleka malamulo
Yehova monga Wopeleka malamulo. Yehova yekha ndiyedi woyenela kupeleka malamulo m’cilengedwe. Iye ndiye anaika malamulo amene amatsogolela zolengedwa zopanda moyo, (Yobu 38:4-38; Sal. 104:5-19), komanso nyama. (Yobu 39:1-30) Munthu nayenso monga colengedwa ca Yehova, ayenela kutsatila malamulo ake a m’cilengedwe. Ndipo popeza munthu amatha kusiyanitsa cabwino na coipa, kusinkhasinkha, kumvetsa zinthu, komanso kulambila, ayenelanso kumvela malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino. (Aroma 12:1; 1 Akorr. 2:14-16) Kuwonjezela pa zimenezi, nawonso angelo, omwe ni zolengedwa zauzimu, amatsatila malamulo a Yehova.—Sal. 103:20; 2 Pet. 2:4, 11.
Palibe amene angaphwanye malamulo a Yehova a m’cilengedwe. (Yer. 33:20, 21) Malamulo ake a m’cilengedwe cimene timaona, sasintha-sintha ndipo ni odalilika. Koma munthu akasankha kucita zinthu mosiyana na malamulo a m’cilengedwe amenewa, nthawi yomweyo amakumana na mavuto. N’cimodzimodzi na malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino. Nawonso ni osasinthika, ndipo munthu sangawanyalanyaze kapena kuwaphwanya popanda kulandila cilango, ngakhale kuti nthawi zina sangalangidwe nthawi yomweyo. Baibo imati: “Mulungu sapusitsika. Ciliconse cimene munthu wafesa adzakololanso comweco.”—Agal. 6:7; 1 Tim. 5:24.
JANUARY 29–FEBRUARY 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 40-42
Zimene Tiphunzilapo pa Zinacitikila Yobu
“Ndani Akudziŵa Maganizo a Yehova?”
4 Tikamasinkhasinkha zocita za Yehova tiyenela kupewa cizolowezi comuweluza poyelekezela na mfundo zimene anthu amayendela. Cizolowezi cimeneci cachulidwa m’mawu a Yehova opezeka pa Masalimo 50:21. Lembali limati: “Unali kuganiza kuti ine ndikhala ngati iwe.” Izi n’zofanana na zimene katswili wina wa Baibo ananena zaka 175 zapitazo. Iye anati: “Anthu amakonda kuweluza Mulungu malinga na mmene iwo amaonela zinthu ndipo amaganiza kuti iye ni womangika na malamulo amene anthuwo amaona kuti ni oyenela kuwatsatila.”
5 Tiyenela kusamala kwambili kuti tisamaganize zoti Yehova ayenela kumacita zinthu mogwilizana na mfundo kapena zofuna zathu. N’cifukwa ciyani zimenezi zili zofunika? Tikamaphunzila nkhani zina za m’Baibo, tingamaganize kuti Yehova sanacite bwino pa nkhaniyo. Tingakhale na maganizo amenewa cifukwa cakuti sitidziŵ zambili ndiponso ndife opanda ungwilo. Aisiraeli anali na maganizo olakwikawa ndipo anali kuona kuti Yehova sakuyendetsa bwino zinthu pakati pawo. Taonani zimene Yehova anawauza: “Anthu inu mudzanena kuti: ‘Njila za Yehova n’zopanda cilungamo.’ Tamvelani inu a nyumba ya Isiraeli. Kodi njila zanga ndiye zopanda cilungamo? Kodi njila za anthu inu sindizo zopanda cilungamo?”—Ezek. 18:25.
6 Cinthu cofunika kwambili kuti tisakhale na maganizo oweluza Yehova malinga na mfundo zimene timayendela, ni kuzindikila kuti ife sitidziŵa zambili ndipo nthawi zina timakhala na maganizo olakwika kwambili. Izi n’zimene Yobu anafunika kudziŵa. Pa nthawi imene anali kuvutika, Yobu anathedwa nzelu n’kuyamba kumangodziganizila yekha. Iye sanali kuonanso zinthu zikuluzikulu zofunika, koma Yehova anamuthandiza kuti aziona zinthu moyenela. Iye anamufunsa mafunso oposa 70 amene sanathe kuwayankha. Pocita zimenezi, Yehova anathandiza Yobu kuzindikila kuti sanali kudziŵa zinthu zambili. Zitatelo Yobu anadzicepetsa n’kusintha mmene anali kuonela zinthu.—Ŵelengani Yobu 42:1-6.
Muziika Maganizo Anu pa Nkhani Yaikulu
12 Kodi Yehova anacita nkhanza mwa kupatsa Yobu uphungu wamphamvu pambuyo pakuti wapilila ciyeso cacikulu? Iyayi, sanacite nkhanza, ndipo Yobu nayenso sanaganize conco. Ngakhale kuti anali pa mavuto aakulu, Yobu anayamikila malangizo amene Mulungu anam’patsa. Anafika pokamba kuti: “Ndikubweza mawu anga, ndipo ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” Umu ni mmene uphungu wamphamvu komanso wolimbikitsa wa Yehova unam’khudzila Yobu. (Yobu 42:1-6) Asanapatsidwe uphungu na Mulungu, Yobu anali atalandilapo kale uphungu wina wopelekedwa na Elihu. (Yobu 32:5-10) Yobu atalandila uphungu wa Mulungu na kusintha maganizo ake, Yehova anauza anzake a Yobu mawu omuyamikila cifukwa ca kukhulupilika kwake pa ciyeso.—Yobu 42:7, 8.
“Yembekezela Yehova”
17 Yobu ni citsanzo cimodzi cabe ca atumiki a Yehova amene anakhalabe olimba pokumana na mayeso. M’kalata yake kwa Aheberi, mtumwi Paulo anakambanso za ena ambili, powachula kuti “mtambo wa mboni waukulu.” (Aheb. 12:1) Onsewo anakumanapo na mayeso aakulu, koma anakhalabe okhulupilika kwa Yehova. (Aheb. 11:36-40) Kodi kupilila kwawo komanso kugwila nchito kwawo molimbika kunangopita pacabe? Kutalitali! Ngakhale kuti iwo sanaone kukwanilitsidwa kwa malonjezo onse a Mulungu m’nthawi yawo , anayembekezelabe Yehova. Ndipo cifukwa anali kudziŵa bwino lomwe kuti Yehova anali kuwayanja, iwo anali na cidalilo cakuti adzaona kukwanilitsidwa kwa malonjezo ake. (Aheb. 11:4, 5) Citsanzo cawo cimatilimbikitsa kuti tisaleke kuyembekezela Yehova.
18 Masiku ano, tikukhala m’dziko limene zinthu zikungoipilaipila. (2 Tim. 3:13) Satana akali kuŵayesa anthu a Mulungu. Mosasamala kanthu na zopinga zimene tingakumane nazo kutsogolo, tiyeni tigwilebe nchito ya Yehova molimbika, tili na cidalilo cakuti “ciyembekezo cathu cili mwa Mulungu wamoyo.” (1 Tim. 4:10) Tisaiŵale kuti madalitso amene Mulungu anapatsa Yobu pamapeto pake, anaonetsa kuti “Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.” (Yak. 5:11) Tiyeni tikhalebe okhulupilika kwa Yehova, tili na cidalilo cakuti iye “amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.”—Ŵelengani Aheberi 11:6.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 808
Citonzo
Pamene anali kutonzedwa kwambili na “anzake” atatu, Yobu anali kuona kuti akutonza iye osati Mulungu. Pambuyo pake, Mulungu anafotokozela Yobu kuti otonzawo m’ceniceni anali kunena zabodza zokhudza Mulungu. (Yobu 42:7) Mofananamo, pamene Aisiraeli anali kufuna mfumu, Yehova anauza mneneli Samueli kuti: “Pakuti sanakane iweyo koma akana ine kuti ndisakhale mfumu yawo.” (1 Sam. 8:7) Nayenso Yesu anauza ophunzila ake kuti, “Mitundu yonse idzadana nanu [osati cifukwa ca zolakwa zanu, koma] cifukwa ca dzina langa.” (Mat. 24:9) Kuganizila zimenezi kudzathandiza Mkhristu kukhala na maganizo oyenela pamene apilila citonzo, ndipo kudzamuyeneleza kulandila mphoto cifukwa ca kupilila kwake.—Luka 6:22, 23.
FEBRUARY 5-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 1-4
Khalani ku Mbali ya Ufumu wa Mulungu
“Ndigwedeza Mitundu Yonse ya Anthu”
8 Kodi anthu aulandila motani uthenga umenewu? Ambili amaukana. (Ŵelengani Salimo 2:1-3.) Mitundu ya anthu ni yokwiya kwambili. Iwo amam’kana Wolamulila woikidwa na Yehova. Uthenga wa Ufumu umene timalalikila sauona kukhala “uthenga wabwino.” Ndipo maboma ena afika ngakhale poletsa nchito yathu yolalikila. Ngakhale kuti olamulila a dzikoli amati amatumikila Mulungu, iwo safuna kutula pansi udindo wawo. Conco, monga anacitila olamulila m’nthawi ya Yesu, olamulila masiku ano amatsutsa Wodzozedwa wa Yehova mwa kuzunza otsatila ake okhulupilika.—Mac. 4:25-28.
Pewani Kutenga Mbali m’Ndale za Dziko Loipali
11 Kukonda cuma. Ngati timaona kuti ndalama ndiponso katundu wathu n’zofunika kwambili, ndiye kuti zingakhale zovuta kupewa ndale. Pofika ca m’ma 1970, Mboni zambili ku Malawi zinathaŵa na kusiya katundu wawo yense cifukwa cokana kuloŵa m’cipani candale. Koma comvetsa cisoni n’cakuti ena analephela kukhala na umoyo wosalila zambili. Mlongo wina dzina lake Ruth anati: “Ena anathaŵa nafe limodzi kupita ku dziko lina, koma pambuyo pake analoŵa m’cipani na kubwelela kwao cifukwa cakuti sanafune kukhala mumsasa wa othaŵa kwao.” Koma anthu ambili a Mulungu alibe maganizo otelo. Amapewa kutenga mbali m’ndale ngakhale kuti kucita zimenezo kungacititse kuti akhale na ndalama zocepa kapena asakhale na ciliconse.—Aheb. 10:34.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 425
Mankhusu
Mankhusu ni makoko amene amateteza mbewu monga balele na tiligu. Pambuyo pokolola, mankhusu anali kukhala opanda nchito. Conco amaimilako zinthu zosafunika komanso zosakhumbilika, zomwe ziyenela kucotsedwa ku mbewu na kuzitaya. Izi zionetsa bwino mmene Yehova Mulungu amacotsela ampatuko pakati pa anthu ake, komanso mmene amacotsela anthu oipa na mitundu yotsutsana naye. (Yobu 21:18; Sal. 1:4; 35:5; Yes. 17:13; 29:5; 41:15; Hos. 13:3) Ufumu wa Mulungu udzapwanyilatu adani ake moti adzakhala tuzidutswa tung’ono-tung’ono tumene tungauluzike mosavuta ngati mankhusu. (Dan. 2:35) Yohane M’batizi anakambilatu za kuwonongedwa kwa anthu a cipembedzo conyenga. Wopuntha, Yesu Khristu, adzasonkhanitsa tiligu, “koma mankhusu adzawatentha ndi moto umene sungazimitsidwe.”—Mat. 3:7-12; Luka 3:17.
FEBRUARY 12-18
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 5-7
Khalanibe Okhulupilika Ngakhale Anthu Ena Azicita Zoipa
Mmene Tingapezele Mphamvu m’Malemba
7 Kodi mnzanu kapena wa m’banja lanu anakucitilani zinthu zokukhumudwitsani? Ngati n’conco, mudzapindula kuona zimene zinathandiza Mfumu Davide, pamene mwana wake Abisalomu anamuukila na kuyesa kum’landa ufumu.—2 Sam. 15:5-14, 31; 18:6-14.
8 (1) Pemphelani. Muli na nkhaniyi m’maganizo, muuzeni Yehova mmene mumvelela pa zoipa zimene ena anakucitilani. (Sal. 6:6-9) Muuzeni zonse mwacindunji. Ndiyeno pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuona mfundo zimene zingakutsogoleleni pamene muyesa kupilila vuto lalikulu limene mwakumana nalo.
Kodi Mumakhulupililadi Kuti Muli na Coonadi?
3 Cikhulupililo cathu sicifunika kuzikidwa cabe pa cikondi cimene anthu a Mulungu ali naco. Cifukwa ciyani? Cifukwa ngati cikhulupililo cathu n’cozikidwa cabe pa cikondi cimeneco, cingakhale cosavuta kutaya cikhulupililoco. Mwacitsanzo, tingaleke kutumikila Yehova ngati m’bale kapena mlongo, mwina ngakhale mkulu kapena mpainiya wacita chimo lalikulu. Tingalekenso kutumikila Yehova ngati m’bale kapena mlongo watikhumudwitsa, kapena ngati wakhala wampatuko n’kumakamba kuti zimene timakhulupilila n’zabodza. Conco, kuti tikhale na cikhulupililo colimba, tifunika kukhala pa ubale wolimba na Yehova. Ngati cikhulupililo canu mwa Mulungu n’cozikidwa cabe pa zimene anthu ena amacita osati pa ubale wanu na iye, ndiye kuti n’cosalimba. Mmene mumaonela Yehova komanso anthu ake, zingakuthandizeni kukulitsa cikhulupililo canu pa mlingo winawake. Koma cina cofunika kwambili ni kuphunzila Baibo mozama, kumvetsetsa zimene mukuphunzilazo, ndiponso kufufuza n’colinga cakuti mukhutile kuti zimene mumaphunzila ni coonadi conena za Yehova. Mufunika kudzipezela maumboni inu eni oonetsa kuti Baibo imaphunzitsa coonadi ponena za Yehova.—Aroma 12:2.
4 Yesu anakamba kuti ena amalandila coonadi “mwacimwemwe,” koma akakumana na mavuto cikhulupililo cawo cimafooka. (Ŵelengani Mateyu 13:3-6, 20, 21.) Mwina iwo amafooka cifukwa cakuti poyamba sanazindikile kuti ngati munthu wasankha kutsatila Yesu, akhoza kukumana na mavuto. (Mat. 16:24) Mwinanso anali kuganiza kuti munthu akakhala Mkhristu ndiye kuti basi sazikumana na mavuto alionse, azingolandila madalitso okha-okha. Koma popeza tikukhala m’dziko loipali, tidzakumanabe na mavuto. Nthawi iliyonse zinthu zingasinthe mu umoyo, ndipo cimwemwe cathu cingacepe.—Sal. 6:6; Mlal. 9:11.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 995
Manda
Pa Aroma 3:13 mtumwi Paulo anagwila mawu Salimo 5:9, poyelekezela m’melo wa anthu oipa komanso acinyengo na “manda otseguka.” Monga mmene manda otseguka ayenela kudzala na anthu akufa komanso zinthu zoipa, mmelo wawo umatulutsa mawu akupha komanso oipa.—Yelekezelani na Mat. 15:18-20.
FEBRUARY 19-25
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 8-10
“Ndidzakutamandani Inu Yehova”!
Muziyamikila Malo Anu M’banja la Yehova
6 Yehova anatikonzela malo abwino okhalamo. Kale kwambili, Yehova asanalenge munthu woyamba, anapanga dziko lapansi kuti anthu azikhalamo. (Yobu 38:4-6; Yer. 10:12) Popeza Yehova ni woganizila ena komanso woolowa manja, anakonza zinthu zabwino zambili kuti tizikondwela nazo. (Sal. 104:14, 15, 24) Atayang’ana zinthu zimene anali kulenga, “anaona kuti zili bwino.” (Gen. 1:10, 12, 31) Iye analemekeza anthu poŵapatsa “mphamvu kuti alamulile” zinthu zonse zimene analenga padziko lapansi. (Sal. 8:6) Colinga ca Mulungu cinali cakuti anthu angwilo asamalile cilengedwe cake cokongola kwamuyaya. Kodi mumamuyamikila Yehova nthawi zonse pa colinga cake cabwino cimeneci?
Kodi Mumayamikila Mphatso Zimene Mulungu Anakupatsani?
10 Njila imodzi imene tingaonetsele kuti timayamikila mphatso ya kulankhula, ni mwa kuuzako anthu okhulupilila cisanduliko cifukwa cake ife timakhulupilila kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse. (Sal. 9:1; 1 Pet. 3:15) Anthu amene amakhulupilila ciphunzitso cimeneci amafuna kuti nafenso tizikhulupilila kuti dziko na zamoyo zonse zili mmenemo zinangokhalako zokha. Ngati tiseŵenzetsa Baibo komanso mfundo zina zimene takambilana m’nkhani ino, tidzakwanitsa kuikila kumbuyo Atate wathu wakumwamba. Ndiponso tidzakwanitsa kufotokozela anthu a maganizo oyenela, cifukwa cake timakhulupilila kuti Yehova ndiye analenga kumwamba na dziko lapansi.—Sal. 102:25; Yes. 40:25, 26..
Kodi Ndinu “Citsanzo . . . M’kalankhulidwe”?
13 Muziimba mocokela pansi pamtima. Tikamaimba nyimbo za Ufumu, colinga cathu cacikulu ni kutamanda Yehova. Mlongo wina dzina lake Sara amaona kuti sadziŵa kuimba bwino. Koma amafuna kutamanda Yehova m’nyimbo. Conco, iye wapeza kuti n’kothandiza kukonzekela nyimbozo ali ku nyumba, monga mmene amakonzekelela mbali zina za msonkhano. Amaziyeseza nyimbozo na kuona mmene mawu ake akugwilizanila na mfundo zimene adzaphunzila ku msonkhano. Iye anati: “Izi zimanithandiza kusumika maganizo anga pa mawu, osati mmene nikuimbila.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 832
Cala
Mophiphilitsa, Baibo imati Mulungu amagwila nchito na “cala (zala) cake, “ monga kulemba Malamulo Khumi pa miyala yosema (Eks. 31:18; Deut. 9:10), kucita zozizwitsa (Eks. 8:18, 19), na kulenga kumwamba (Sal. 8:3). Umboni woonetsa kuti “zala” za Mulungu zimene anagwilitsa nchito polenga zinthu ni mzimu woyela, kapena mphamvu yake yogwila nchito, umapezeka m’nkhani ya m’buku la Genesis yokamba za cilengendwe. Buku la Genesis limati mphamvu ya Mulungu (ruʹach, “mzimu”) inali kuyenda-yenda pamwamba pa madzi. (Gen 1:2) Koma Malemba a Cigiriki Acikhristu amatithandiza kumvetsa bwino tanthauzo la cala ca Mulungu. M’buku la Mateyu timaŵelenga kuti Yesu anatulutsa ziŵanda na ‘mzimu woyela wa Mulungu’, pomwe buku la Luka limatiuza kuti anaseŵenzetsa “cala ca Mulungu.”—Mat. 12:28; Luka 11:20.
FEBRUARY 26–MARCH 3
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 11-15
Yelekezani Kuti Muli m’Dziko Latsopano la Mulungu Komanso la Mtendele
w06 5/15 18 ¶3
Mfundo Zazikulu za Cigawo Coyamba ca Masalmo
11:3—Kodi ni maziko otani amene akupasuka? Amenewa ni maziko amene amanga anthu pamodzi—malamulo, bata, komanso cilungamo. Zimenezi zikasokonekela, pamakhala cisokonezo pakati pa anthu ndipo sipakhala cilungamo. Zikatelo, munthu aliyense “wolungama” ayenela kudalila Mulungu na mtima wonse.—Salimo 11:4-7.
Kodi Zidzatheka Kukhala M’dziko Lopanda Nkhanza?
Baibo imalonjeza kuti posacedwa Mulungu adzayeletsa dziko lino lankhanza. Nkhanza zimene zilipo masiku ano pa dziko lapansi zidzathelatu pa “tsiku laciweluzo ndi ciwonongeko ca anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:5-7) Anthu ankhanza sadzavutitsanso ena. Tingatsimikize bwanji kuti Mulungu afuna kuthetselatu nkhanza?
Baibo imakamba kuti, “Mulungu amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa.” (Salimo 11:5) Mlengi amakonda mtendele na cilungamo. (Salimo 33:5; 37:28) N’cifukwa cake sangalole anthu ankhanza kukhalapo mpaka kalekale.
Kodi Mudzayembekezela Moleza Mtima?
15 N’cifukwa ciyani Davide anali wokonzeka kuyembekezela moleza mtima? Yankho ili mu salimo limodzi-modzi mmene iye anafunsa kanayi konse kuti: “Kufikila liti?” M’salimo limeneli, iye anati: “Koma ine ndakhulupilila kukoma mtima kwanu kosatha. Mtima wanga ukondwele cifukwa ca cipulumutso canu. Ndidzaimbila Yehova cifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.” (Sal. 13:5, 6) Davide anakhulupilila kukoma mtima kosatha kwa Yehova. Iye anali kuganizila za mmene Yehova anamuthandizila m’mbuyomo, ndiponso anali kuyembekezela mwacidwi nthawi imene Mulungu adzamupulumutsa. Zoonadi, Davide anadziŵa kuti anafunika kuyembekezela kuti alandile madalitso a Mulungu.
Ufumu Ukwanilitsa Cifunilo ca Mulungu Padziko Lapansi
16 Citetezo. Mtsogolomu, mawu a pa Yesaya 11:6-9 adzakwanilitsidwa mwakuthupi. Amuna, akazi, na ana adzakhala otetezeka kulikonse kumene adzapita padziko lapansi. Sitidzaopa ciliconse kaya ni munthu kapena nyama. Ganizilani mmene zinthu zidzakhalila pamene kulikonse m’dzikoli kudzakhala monga kunyumba kwanu. Simudzacita mantha kusambila m’mitsinje kapena m’nyanja, simudzaopa kuyenda m’mapili kapena m’chile. Ndipo simudzaopa ciliconse usiku. Mawu a pa Ezekieli 34:25 adzakwanilitsidwa moti anthu a Mulungu ‘adzakhala m’cipululu popanda cowaopsa ndipo adzagona m’nkhalango.’
Kufufuza Cuma Cauzimu
w13 9/15 19 ¶12
Kodi Mwasandulika?
12 N’zacisoni kuti ifenso tikukhala ni anthu amene khalidwe lawo ni lofanana na la anthu amene Paulo anafotokoza. Iwo amaona kuti miyezo na mfundo za m’Malemba ni zinthu zacikale. Aphunzitsi na makolo ambili amalimbikitsa ana kucita zinthu zimene anawo afuna. Iwo amakamba kuti aliyense ali na ufulu wosankha zilizonse zimene afuna. Ngakhale anthu ambili amene amanena kuti ni opembedza amaona kuti ali na ufulu wocita zimene aona kuti n’zabwino, ndipo samvela Mulungu kapena kutsatila malamulo ake. (Sal. 14:1) Akhristu oona angatengele mosavuta maganizo amenewa. Akhristu amene ali na malingalilo amenewa angamaone dongosolo la gulu m’njila yolakwika. Iwo angakane kutsatila malangizo a mumpingo na kuyamba kudandaula na zilizonse zimene sanakonde. Kapena angamakaikile malangizo a m’Baibo okhudza zosangulutsa, kugwilitsila nchito Intaneti, komanso kufuna-funa maphunzilo apamwamba.