Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JULY 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 57-59
Yehova Amasokoneza Olimbana na Anthu Ake
bt-CN 220-221 ¶14-15
“Mpaka Kumalekezero a Dziko Lapansi”
14 Sitefano analalikila molimba mtima asanaphedwe na adani ake. (Mac. 6:5; 7:54-60) “Cizunzo cacikulu” citabuka pa nthawiyo, ophunzila onse kupatulapo atumwi, anabalalikila m’zigawo zonse za Yudeya na Samariya. Koma zimenezi sizinaimitse nchito yolalikila. Mwacitsanzo, Filipo anapita ku Samariya na “kuyamba kulalikila za Khristu” ndipo zotsatila zake zinali zabwino kwambili. (Mac. 8:1-8, 14, 15, 25) Komanso Baibo imatiuza kuti: “Anthu amene anabalalika cifukwa ca cisautso cimene cinagwela Sitefano anayenda mpaka ku Foinike, ku Kupuro ndi ku Antiokeya. Ndipo sanali kulalikira mawu kwa wina aliyense koma kwa Ayuda okha. Koma pakati pawo panali amuna ena a ku Kupuro na ku Kurene. Amenewa atafika ku Antiokeya anayamba kulankhula na anthu olankhula Cigiriki, ndipo anali kulengeza kwa iwo uthenga wabwino wa Ambuye Yesu.” (Mac. 11:19, 20) Pa nthawiyo, kuzunzidwa kwa Akhristu kunacititsa kuti uthenga wa Ufumu ufalikile.
15 M’nthawi yathu ino, zinthu ngati zimenezi zinacitikanso m’mayiko amene kale ankapanga dziko la Soviet Union. Anthu ambili-mbili a Mboni za Yehova anawathamangitsila ku Siberia, maka-maka m’zaka za m’ma 1950. Cifukwa ca kuthamangitsidwako, Mboni za Yehova zambili zinakakhala kumadela akutali kwambili na kwawo ndipo zinamwazika m’midzi yosiyanasiyana m’dziko lonselo. Zimenezi zinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikile m’dziko la Siberia, lomwe ni lalikulu kwambili. Conco Mboni za Yehova zambili zinakwanitsa kulalikila uthenga wabwino kumadela akutali kwambili, mpaka mtunda wokwana makilomita 10,000 kucokela kwawo. Mbonizi sizikanakwanitsa kupeza ndalama zokafikila kumadela amenewa. Koma izi zinatheka cifukwa boma linawatumiza lokha kumeneko. M’bale wina anati: “Zimene akulu-akulu a boma anacitazi zinathandiza kuti anthu ambili-mbili oona mtima a ku Siberia adziŵe coonadi.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
“Khalani Olimba, Osasunthika”
16 Khalani na mtima wosasunthika. Mfumu Davide anaonetsa kuti sadzaleka kukonda Mulungu pamene anaimba kuti: “Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu.” (Sal. 57:7) Nafenso tingakhale na mtima wosasunthika, na kudalila Yehova na mtima wonse. (Ŵelengani Salimo 112:7.) Izi n’zimene zinathandiza m’bale Bob amene tam’chula uja. Atamuuza kuti adzasunga magazi ena pambali kuti mwina angafunikile, nthawi yomweyo iye anauza dokotalayo kuti ngati akonza zokamuika magazi, sadzacitila mwina koma kutuluka m’cipatala nthawi yomweyo. Patapita nthawi iye anati: “N’natsimikiza mtima kucitadi zimenezo, ndipo sin’nade nkhawa na zimene zinganicitikile.”
17 M’bale Bob sanasunthike cifukwa anali atapangilatu cisankho asanagonekedwe m’cipatala. Coyamba, anali kufuna kukondweletsa Yehova. Caciŵili, anafufuza m’Baibo komanso m’zofalitsa zozikika pa Baibo pa nkhani ya kupatulika kwa moyo na magazi. Ndipo cacitatu, anali wotsimikiza kuti kutsatila citsogozo ca Yehova kumapindulila nthawi zonse. Nafenso tingakhale na mtima wosasunthika mosasamala kanthu na zimene zingaticikile.
JULY 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 60-62
Yehova Amatiteteza, Amaticinjiliza, Ndiponso Amatilimbitsa
it-2-E 1118 ¶7
Nsanja
Yophiphilitsa. Anthu amene amakhulupilila Yehova na kumumvela amakhala otetezeka kwambili. Davide anaimba kuti: “Inu [Yehova] ndinu malo anga othaŵilako, nsanja yolimba imene imanditeteza kwa mdani.” (Sal. 61:3) Anthu amene amadziŵa tanthauzo la dzina limeneli na kulikhulupilila, komanso kuliimilako mokhulupilika, saopa ciliconse, cifukwa “dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathaŵila mmenemo ndipo amatetezedwa.”—Miy. 18:10; yelekezelani na 1 Sam. 17:45-47.
it-2-E 1084 ¶8
Tenti
“Tenti” ya munthu inali malo ampumulo ndiponso inali kumuteteza ku zinthu zosiyana-siyana. (Ge 18:1) Popeza anthu akale anali na mzimu woceleza, alendo anali kukhulupilila kuti akalandilidwa m’tenti ya munthu, adzasamalidwa bwino na kulemekezedwa. Conco, pamene Chivumbulutso 7:15 imakamba kuti a khamu lalikulu Mulungu “adzawaphimba ndi tenti yake,” imatanthauza kuti adzawasamalila na kuwateteza. (Sal. 61:3, 4) Yesaya anakamba zimene mkazi wa Mulungu, Ziyoni, anafunika kucita pokonzekela kubadwa kwa ana ake. Anauzidwa kuti ‘akulitse tenti yake.’ (Isa 54:2) Motelo anakulitsa malo otetezelapo ana ake.
w02-CN 4/15 16 ¶14
Malamulo a Mulungu Amatipindulitsa
14 Cilamulo ca Mulungu n’cosasinthika. M’nthawi zovuta zimene tikukhala zino, Yehova ndiye mwala wosasunthika, amene alipo kuyambila nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. (Salimo 90:2) Anadzinena yekha kuti: “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.” (Malaki 3:6) Miyezo ya Mulungu imene ili m’Baibo ni yodalilika kwambili osati monga malangizo a anthu amene amasinthasintha. (Yakobo 1:17) Mwacitsanzo, kwa zaka zambili akatswili a zamaganizo anali kulimbikitsa kuti anthu azilela ana mowalekelela, koma kenako akatswili ena anasintha maganizo awo n’kuvomeleza kuti malangizowo anali olakwika. Miyezo na malangizo a anthu m’dzikoli pankhani imeneyi amapita uku na uku ngati kuti akuwombedwa ni mphepo. Koma, Mawu a Yehova sasintha. Kwa zaka zambili-mbili, Baibo lapeleka malangizo a mmene makolo angalelele ana mwacikondi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Inu abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma pitirizani kuwalera powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwilizana ndi zimene Yehova amanena.” (Aefeso 6:4) N’zosangalatsa kudziŵa kuti tingadalile miyezo ya Yehova; siidzasintha!
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 6/1 11 ¶8
Mfundo Zazikulu za Cigawo Caciŵili ca Masalmo
62:11. Mulungu sadalila mphamvu zocokela kwina kwake. Iye mwini ni gwelo la mphamvu. ‘Mphamvu ndi yake ya iye.’
JULY 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 63-65
“Cikondi Canu Cokhulupilika Nʼcabwino Kuposa Moyo”
w01-CN 10/15 15-16 ¶17-18
Ndani Adzatisiyanitsa ndi Chikondi cha Mulungu?
17 Kodi cikondi ca Mulungu n’cofunika motani kwa inu? Kodi mumaganiza mmene anacitila Davide amene analemba kuti: “Pakuti cifundo [“kukoma mtima,” NW] canu ciposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani. Potelo ndidzakuyamikani m’moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m’dzina lanu.” (Salmo 63:3, 4) Ndithudi, kodi pali cina ciliconse cimene moyo m’dziko lapansi lino ungatipatse comwe n’cabwino kuposa kuti Mulungu atikonde ndi kukhala naye paubale wokhulupilika? Mwacitsanzo, kodi kufunafuna nchito yapamwamba kuli bwino kusiyana na kukhala na mtendele wamaganizo ndi cimwemwe zimene zimabwela cifukwa ca kukhala paubale weniweni na Mulungu? (Luka 12:15) Akhristu ena auzidwa kusankha kusiya kumvela Yehova kapena kuphedwa. Zimenezo zinacitikila Mboni za Yehova zambili ku misasa ya ukaidi ya Nazi m’nthaŵi ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse. Abale athu Acikhristu ambili anasankha kukhalabe m’cikondi ca Mulungu ndipo analolela kuphedwa ngati kunafunikila kutelo. Amene amakhalabe m’cikondi ca Mulungu mokhulupilika angakhale otsimikiza kuti iye adzaŵapatsa tsogolo losatha, cinthu cimene dziko lapansi silingapeleke. (Maliko 8:34-36) Komatu pali zambili kuposa moyo wosatha wokha.
18 Ngakhale kuti n’zosatheka kukhala na moyo kosatha popanda Yehova, tayesani kuyelekeza mmene moyo wautali kwambili ungakhalile popanda Mlengi. Ungakhale wosasangalatsa, wopanda colinga ceniceni. Yehova wapatsa anthu ake nchito yokhutilitsa yoti aicite m’masiku otsiliza ano. Motelo tikukhulupilila kuti Yehova, Wamkulu amene amakwanilitsa zolinga zake, akadzatipatsa moyo wosatha, padzakhala zinthu zambili zocititsa cidwi zoti tidzaziphunzile na kuzicita. (Mlaliki 3:11) Kaya tidzaphunzila zoculuka motani m’zaka zikwizikwi zikubwelazo, sitidzatha kumvetsa zonse za ‘nzelu zake zozama, ndiponso kudziŵa kwake zinthu kwambili.’—Aroma 11:33.
“Muziyamika pa Ciliconse”
Kukhala woyamikila kwa Mulungu n’kofunika kwambili. Mosakayikila, mumaganizilako zinthu zambili zauzimu na zakuthupi zimene Mulungu anatipatsa komanso zimene akupitiliza kutipatsa. (Deut. 8:17, 18; Mac. 14:17) Koma bwanji osapatula nthawi yoganizila mozama madalitso amene Mulungu akukupatsani imwe na okondedwa anu? Kusinkha-sinkha za kuolowa manja kwa Mlengi wathu, kudzatithandiza kuti tizimuyamikila kwambili. Kudzatithandizanso kuzindikila kuti iye amatikonda kwambili na kutiona kukhala ofunika.—1 Yoh. 4:9.
w15-CN 10/15 22 ¶7
Pitilizani Kusinkhasinkha Zinthu za Kuuzimu
7 Khama n’lofunika kuti tizisinkhasinkha ndi kuika maganizo pa zimene tiphunzila. Ndiye cifukwa cake tifunika kumasinkhasinkha pamene sindife otopa, tili pamalo acete, ndiponso pamene palibe zinthu zambili zosokoneza. Wamasalimo Davide anali kusinkhasinkha ali pabedi usiku. (Salimo 63:6) Yesu amene anali wangwilo, anasankha malo acete kuti asinkhesinkhe ndi kupemphela.—Luka 6:12.
w09-CN 7/15 16 ¶6
Phunzitsani Mwacikondi Ngati Yesu
6 Anthufe timamva bwino tikamalankhula za zinthu zimene timazikonda. Timalankhula mwamphamvu ndiponso mosangalala moti anthu amatha kuona kuti zikutisangalatsa. Izi zimacitika makamaka tikamalankhula za munthu amene timam’konda. Nthawi zambili timalakalaka kuuza ena zinthu zokhudza munthuyo zimene ife tikudziŵa. Timalankhula zabwino za iye, kumukweza ndiponso kumuikila kumbuyo. Timatelo cifukwa cakuti timafuna kuti anthu akopeke naye ndiponso kuti akopeke na makhalidwe ake ngati mmene ifeyo timacitila.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w07-CN 11/15 15 ¶6
Kodi Mumatsitsimula Ena?
Kumanga nyumba n’kovuta kwambili, koma kuigwetsa n’kosavuta. Mfundo imeneyi imagwilanso nchito pakalankhulidwe kathu. Tonsefe ndi opanda ungwilo ndipo timalakwitsa pocita zinthu. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Palibe munthu wolungama amene amacita zabwino nthawi zonse ndipo sacimwa.” (Mlaliki 7:20) N’zosavuta kuti tione zolakwa za munthu wina n’kumulankhula mawu opweteka kwambiri. (Salmo 64:2-4) Koma sizophweka kuti mawu athu akhale olimbikitsa.
JULY 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 66-68
Yehova Amanyamula Katundu Wathu Tsiku na Tsiku
Mmene Yehova Amayankhila Mapemphelo Athu
15 Nthawi zambili, mapemphelo athu sayankhidwa mogometsa ayi. Koma mayankho amene timalandila amakhala okwanila potithandiza kukhalabe okhulupilika kwa Atate wathu wakumwamba. Conco, muzikhala chelu kuona mmene Yehova akuyankhila mapemphelo anu. Mlongo wina dzina lake Yoko, anali kuona monga Yehova sayankha mapemphelo ake. Koma pambuyo pake anayamba kulemba zimene wapempha Yehova. Patapita nthawi, iye anayang’ana m’buku lake ndipo anazindikila kuti Yehova anali atayankha mapemphelo ake ambili, kuphatikizapo aja amene mlongoyo anawaiŵala. Conco, nthawi na nthawi tiziima na kuganizila mmene Yehova akuyankhila mapemphelo athu.—Sal. 66:19, 20.
w10-CN 12/1 23 ¶6
Muziganizila Makolo Amene Sali Pabanja
Yehova anauzila anthu ena kulemba nyimbo zapadela, kapena kuti masalimo, amene Aisiraeli ankaimba polambila. Ndiyeno taganizilani mmene amayi amasiye ndi ana amasiye ku Isiraeli ankalimbikitsidwila akamaimba nyimbo zouzilidwa ndi Mulungu zimenezi. Nyimbozi zinkawakumbutsa kuti Yehova ndi “tate” ndi “woweluza “ wawo ndipo zinkawatsimikizila kuti iye ndi wokonzeka kuwathandiza. (Salimo 68:5; 146:9) Nafenso tingauze makolo amene akulela okha ana mawu olimbikitsa amene angamawakumbukilebe ngakhale patapita zaka zambili. Ngakhale kuti papita zaka 20, Ruth amene akulela yekha ana amakumbukilabe nthawi imene bambo wina anamuuza kuti: “Mukugwila nchito yotamandika kwambili yosamalila ana anu aŵiliwa. Pitilizani, mukucita bwino kwambili.” Ruth ananena kuti: “Mawu amenewa anandilimbikitsa kwambiri.” N’zoonadi kuti “mawu abwino ni mankhwala” ndipo angalimbikitse kholo limene likulela lokha ana kuposa mmene timayembekezela. (Miyambo 15:4, Contemporary English Version) Kodi mungaganizile za zinthu zina zake zabwino zimene kholo limene likulela lokha ana likucita zimene mungaliyamikile
w09-CN 4/1 31 ¶1
Atate wa Ana Amasiye
BAIBULO limati: “Mulungu, mokhala mwake moyela, ndiye Atate wa ana amasiye.” (Salimo 68:5) Mawu ouzilidwa amenewa akutiphunzitsa mfundo yofunika kwambili yokhudza Yehova Mulungu, yakuti iye ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu osoŵa. Cilamulo cimene Mulungu anapeleka kwa Aisiraeli, cikusonyeza kuti iye amamvela cisoni ana amene makolo awo anamwalila. Tiyeni tione lemba loyamba m’Baibulo limene lili ndi mawu akuti “ana amasiye,” lomwe ndi Ekisodo 22:22-24.
Yehova Akukuthandizani Kupambana Mayeso
17 Ŵelengani Salimo 40:5. Munthu akamamanga nyumba, colinga cake cimakhala kuitsiliza na kusamukilamo. Koma nchito yomanga nyumbayo ili mkati, nthawi na nthawi munthuyo angamaime na kuganizila mmene nchitoyo ikupitila patsogolo. Mofananamo, nthawi na nthawi muziima na kuganizila mmene Yehova akukuthandizilani, ngakhale pamene muli mkati mopilila vutolo. Kumapeto kwa tsiku lililonse muzidzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova wanidalitsa motani lelo? Ngakhale kuti vutoli likalipo, kodi Yehova akunithandiza bwanji kulipilila?’ Muziyesa kupeza ngakhale cinthu cimodzi cimene Yehova wakucitilani pokuthandizani kupilila.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 6/1 10 ¶5
Mfundo Zazikulu za Cigawo Caciŵili ca Masalimo
68:18—Kodi ndani amene anali “zaufulu mwa anthu”? Amenewa anali amuna amene anatengedwa kucokela pa gulu la anthu amene anali akaidi, atalanda Dziko Lolonjezedwa. Kenaka amuna amenewa anapatsidwa nchito yothandiza Alevi pa nchito yawo.—Ezara 8:20.
JULY 29–AUGUST 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 69
Salimo 69 Inakambilatu Zocitika pa Umoyo wa Yesu
w11-CN 8/15 11 ¶17
Anthu Ankayembekezela Mesiya
17 Mesiya adzadedwa popanda cifukwa. (Sal. 69:4) Yesu anati: “Ndikanapanda kucita pakati [pa anthu] nchito zimene wina aliyense sanacitepo, akanakhala opanda chimo, koma tsopano aona ndipo adana nane, ndi kudananso ndi Atate wanga. Zili conco kuti mawu olembedwa m’Cilamulo akwanilitsidwe. Mawu ake ndi akuti, ‘Anadana nane popanda cifukwa.’” (Yoh. 15:24,25) Mawu akuti “Cilamulo” nthawi zambili amatanthauza Malemba onse. (Yoh. 10:34; 12:34) Mauthenga Abwino amatsimikizila kuti Yesu ankadedwa ndi anthu ambili, makamaka ndi atsogoleli acipembedzo aciyuda. Ndipotu Yesu ananena kuti: “Dziko lilibe cifukwa coti lizidana nanu, koma limadana ndi ine, cifukwa ndimacitila umboni kuti nchito zake ndi zoipa.”—Yoh. 7:7.
w10-CN 12/15 8 ¶7-8
Khalani Odzipeleka pa Kulambila Koona
7 Zimene Yesu anacita nthawi ina zinasonyeza bwino kuti iye anali wodzipeleka kwambili. Anacita zimenezi cakumayambililo kwa utumiki wake pa nyengo ya Pasika mu 30 C.E. Yesu ndi ophunzila ake atafika m’kacisi ku Yerusalemu anapeza “ogulitsa ng’ombe, nkhosa ndi nkhunda komanso osintha ndalama ali m’kacisi atakhala m’mipando yawo.” Kodi Yesu anacita ciyani ataona zimenezi, nanga ophunzila ake anamva bwanji ndi zimene Yesu anachitazi?—Ŵelengani Yohane 2:13-17.
8 Zimene Yesu anacita ndiponso kulankhula pa nthawi imeneyi zinakumbutsa ophunzila ake mawu aulosi opezeka mu salimo la Davide akuti: “Pakuti kudzipeleka kwambili panyumba yanu kwandidya.” (Sal. 69:9) N’cifukwa ciyani zinali conco? Cifukwa cakuti zimene Yesu anacita zikanamuika pa ngozi. Ndipotu akulu-akulu a pakacisipo monga ansembe, alembi ndi anthu ena ndi amene ankalimbikitsa anthu kucita malondawa pakacisi. Conco zimene Yesu anacita pouza anthu poyela cinyengo ca atsogoleli acipembedzo komanso kusokoneza mapulani awo kukanacititsa kuti adane naye kwambili. Ophunzila ake anazindikila kuti iye anacita zimenezi cifukwa cakuti anali ‘wodzipeleka kwambili panyumba ya Mulungu’ kapena kuti pa kulambila koona. Koma kodi mawu akuti kudzipeleka kwambili amatanthauza ciyani? Kodi ndi osiyana ndi mawu akuti cangu?
g95-E 10/22 31 ¶4
Kodi Munthu Angafe Cifukwa Cosweka Mtima?
Anthu ena amati kusweka mtima n’cimodzi mwa zinthu zimene zinacititsa Yesu kufa. Ulosi unakambilatu za iye kuti: “Mtima wanga wasweka cifukwa ca kunyozedwa, ndipo bala lake ndi losacilitsika.” (Salimo 69:20) Kodi mawuwa atanthauza kuti ni mtima weniweni wa Yesu umene unasweka? Mwina. Cifukwa m’maola othela Yesu asanamwalile anazunzika kwambili, mwa kuthupi komanso m’maganizo. (Mateyu 27:46; Luka 22:44; Aheberi 5:7) Cinanso, kunena kuti anasweka mtima kungatithandize kumvetsa cifukwa cake anatuluka “magazi ndi madzi” pamene anabayidwa na mkondo pambuyo pa imfa.—Yohane 19:34.
it-2-E 650
Comela Capoizoni
Ponena za Mesiya, ulosi unakambilatu kuti adzapatsidwa “comela capoizoni” kuti adye. (Sal. 69:21) Izi zinacitika Yesu Khristu asanapacikidwe pamtengo. Anamupatsa vinyo wosakaniza na ndulu. Mwina anamupatsa cakumwa cimeneco kuti cicepetseko ululu wake. Koma Yesu atangolaŵa cakumwaco, anacikana. Polemba za kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu, Mateyu (27:34) anagwilitsa nchito mawu Acigiriki akuti kho·leʹ (ndulu), amene amapezekanso m’Baibo ya Cigiriki ya Septuagint pa Salimo 69:21. Koma uthenga wabwino wolembedwa na Maliko umakamba za mule (Maliko 15:23), ndipo izi zapangitsa anthu ena kuyamba kukhulupilila kuti ‘comela capoizonico’ kapena “ndulu” cinali “mule.” N’kuthekanso kuti cakumwaco cinali cosakaniza na ndulu komanso mule.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w99-CN 1/15 18 ¶11
Kwezani Manja Okhulupilika m’Pemphelo
11 Anthu ambili amangopemphela akamafuna cina cake, koma kukonda kwathu Yehova Mulungu kuyenela kutisonkhezela kum’yamika na kum’tamanda m’mapemphelo athu patokha na poyela. “Musadele nkhawa konse,” Paulo analemba kuti, “Komatu m’zonse ndi pemphelo, ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendele wa Mulungu wakupambana cidziŵitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Inde, kuwonjezela pa pembedzelo ndi kupempha, tiyenela kuyamikila Yehova kaamba ka madalitso auzimu ndi akuthupi. (Miyambo 10:22) Wamasalimo anaimba kuti: “Peleka kwa Mulungu nsembe yaciyamiko; Numcitile Wam’mwambamwamba cowinda cako.” (Salimo 50:14) Ndipo nyimbo ya Davide ya pemphelo inaphatikizapo mawu awa okhudza mtima: “Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliyimbila, Ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.” (Salimo 69:30) Kodi sitiyenela kucita zomwezi m’mapemphelo athu poyela ndi patokha?
AUGUST 5-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 70-72
‘Uzani M’badwo Wotsatila’ za Mphamvu za Mulungu
w99-CN 9/1 18 ¶17
Acinyamata—Kulitsani Luso Lanu la Kuzindikila!
17 Kupewa misampha ya Satana kumafuna kuti muzikhala chelu nthaŵi zonse. Ndipo nthawi zina, kumafuna kulimba mtima kwambili. Zoona, nthaŵi zina mungapeze kuti mukukhala wosiyana osati ndi anzanu okha, komanso ndi dziko lonse. Wamasalmo Davide anapemphela kuti: “Pakuti Inu ndinu ciyembekezo canga, Ambuye Yehova; mwandikhalila wokhulupilika kuyambila ubwana wanga. Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambila ubwana wanga; ndipo kufikila lelo ndilalikila zodabwiza zanu.” (Salimo 71:5, 17) Davide akudziŵika cifukwa ca kulimba mtima kwake. Koma kodi anakhala nako liti? Pamene anali mnyamata! Ngakhale asanagonjetse Goliyati, cocitika cimene anachuka naco kwambili, Davide anali atasonyezapo kale kulimba mtima kwake poteteza nkhosa za atate wake pamene anapha mkango komanso chimbalangondo. (1 Samueli 17:34-37) Komabe, Davide anapeleka thamo lonse kwa Yehova pa kulimba mtima kulikonse kumene anakusonyeza, ndipo anamuuza kuti “mwandikhalila wokhulupilika kuyambila ubwana wanga.” Luso la Davide lodalila Yehova linam’theketsa kugonjetsa ciyeso ciliconse comwe anakumana naco. Inunso mudzaona kuti ngati mudalila Yehova, adzakupatsani kulimba mtima ndi nyonga ‘yolakila dziko lapansi.’—1 Yohane 5:4.
g04-CN 10/8 17 ¶3
Kodi Anthu Okalamba Tiyenela Kuwacitila Zinthu Motani?
Wamasalmo anapemphela kuti: “Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.” (Salmo 71:9) Mulungu ‘sataya’ atumiki ake okhulupilika, ngakhale iwowo aziona ngati atha nchito. Wamasalimo sanaone ngati Yehova anamutaya, m’malo mwake, anazindikila kuti afunika kudalila Mlengi wake, maka-maka pamene anali kukalamba. Yehova akaona munthu wokhulupilika, kapena kuti wacifundo woteloyo, amamuthandiza moyo wake wonse. (Salmo 18:25) Nthawi zambili cithandizo cimeneco cimacokela kwa Akhristu anzathu.
Tumikilani Yehova Asanafike Masiku Oipa
4 Popeza kuti ndinu wacikulile, mosakaikila mumadziŵa zinthu zambili. Komabe muyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi nidzacita ciyani na moyo wanga tsopano nikaliko na mphamvu?’ Pokhala Mkhristu wodziŵa zambili, muli na mwayi umene ena alibe. Mwacitsanzo mungaphunzitseko acinyamata zinthu zimene mwaphunzila kwa Yehova. Mungalimbikitse ena mwa kuwasimbila zocitika zimene mwasangalala nazo potumikila Mulungu. Mfumu Davide anapempha mwayi wocita zimenezi pamene analemba kuti: “Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambila pa unyamata wanga. . . . Ngakhale nditakalamba ndi kumela imvi, inu Mulungu musandisiye, kufikila nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatila, kufikila nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwela m’tsogolo.”—Sal. 71:17, 18.
5 Kodi mungathandize bwanji ena na cidziŵitso cimene mwapeza cifukwa cotumikila kwa zaka zambili? Kodi mungaitanile atumiki acinyamata kunyumba kwanu kuti mukhale na maceza olimbikitsa? Kodi mungakonze zopita nawo mu ulaliki kuti aone cimwemwe cimene muli naco cifukwa cotumikila Yehova? Munthu wakale Elihu anati: “Masiku alankhule. Zaka zambili n’zimene ziyenela kudziŵitsa anthu nzelu.” (Yobu 32:7) Mtumwi Paulo analangiza akazi acikulile Acikhristu kuti azilimbikitsa ena mwa mawu na zocita. Iye ananena kuti: “Akazi acikulile . . . akhale aphunzitsi a zinthu zabwino.”—Tito 2:3.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 768
Firate
Malile a Malo Amene Aisiraeli Anapatsidwa. Pokamba na Abulahamu, Mulungu analonjeza kuti adzapatsa mbadwa za Abulahamu malo “kuyambila kumtsinje wa Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.” (Gen. 15:18) Anabwelezanso lonjezo limeneli ku mtundu wa Aisiraeli. (Eks. 23:31; Deut. 1:7, 8; 11:24; Yos. 1:4) 1 Mbiri 5:9 imakamba kuti isanafike nthawi ya ulamulilo wa Davide, ana ena a Rubeni anakulitsa malo awo “mpaka kum’mawa poyambila cipululu pa mtsinje wa Firate.” Koma mtsinje wa Firate uli kutali, pa mtunda wa makilomita 800 kucokela ‘kum’mawa kwa Giliyadi.’ (1 Mbiri 5:10) Conco, n’kutheka kuti mawu amenewa a pa 1 Mbiri 5:9 amangotanthauza kuti a fuko la Rubeni anakulitsa dela lawo la kum’mawa kwa Giliyadi mpaka m’mbali mwa cipululu ca Siriya. Cipululu cimeneci ndico cimafika kumtsinje wa Firate. Conco, zioneka kuti nthawi yoyamba pamene lonjezo la Yehova limeneli linakwanilitsika kwathunthu ni mu ulamulilo wa Davide komanso wa Solomo. Pa nthawiyo, dela lolamulidwa na Aisiraeli linakula kwambili mpaka kukafika mu ufumu wa a Aramu ku Zoba. Conco, malile a delalo anafika m’mbali mwa mtsinje wa Firate ndipo mwacionekele anadutsila kumpoto kwa dziko la Siriya.—2 Sam. 8:3; 1 Maf. 4:21; 1 Mbiri 18:3-8; 2 Mbiri 9:26
AUGUST 12-18
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 73-74
Kodi Tingacite Ciyani Ngati Timacitila Nsanje Anthu Omwe Salambila Mulungu?
“Yehova Amapulumutsa Anthu Olefuka Mtima”
14 Amene analemba Salimo 73 anali Mlevi. Conco iye anali na mwayi wapadela wotumikila pamalo a Yehova olambilila. Ngakhale n’conco, iye analefuka panthawi ina mu umoyo wake. Cifukwa ciyani? Anayamba kucitila kaduka anthu oipa, komanso odzikuza, osati cifukwa ca zoipa zimene anali kucita, koma cifukwa cakuti anali kuoneka kuti zinthu zikuŵayendela bwino. (Sal. 73:2-9, 11-14) Iwo anali kuoneka kuti ali na zonse, cuma, umoyo wabwino, komanso wopanda nkhawa. Zimenezi zinalefula wamasalimo ameneyu cakuti anati: “Ndithudi, ndayeletsa mtima wanga pacabe, Ndipo ndasamba m’manja mwanga pacabe posonyeza kuti ndine wopanda colakwa.” N’zoonekelatu kuti iye anali pangozi yaikulu yauzimu.
“Yehova Amapulumutsa Anthu Olefuka Mtima”
15 Ŵelengani Salimo 73:16-19, 22-25. Mleviyo ‘analowa m’malo opatulika a Mulungu.’ Mmenemo, mwina ali pakati pa alambili anzake, anatha kupenda bwino-bwino mkhalidwe wake, modekha, moganiza bwino, komanso mwapemphelo. Izi zinam’thandiza kuona kuti anayamba kuganiza mopusa. Ndipo anali atayamba kuyenda panjila yowopsa imene ikanam’patutsa kwa Yehova. Iye anazindikilanso kuti anthu oipa ali “pamalo otelela” ndipo mapeto awo adzakhala owopsa. Kuti athetse kaduka na kuleka kudzimva wolefuka, Mlevi wamasalimo ameneyu, anayenela kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Mwakucita zimenezi, anakhala pamtendele ndipo anakhalanso wacimwemwe. Iye anati: “Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha [Yehova].”
16 Zimene tiphunzilapo. Tisamacitile kaduka anthu oipa amene angaoneke kuti zinthu zikuwayendela mu umoyo. Cimwemwe cawo si ceni-ceni, ndipo n’cakanthawi. Iwo sadzakhalapo kwamuyaya. (Mlal. 8:12, 13) Kuwacitila kaduka kungatilefule, ndipo kungativulaze mwauzimu. Conco, ngati mwazindikila kuti mwayamba kucitila kaduka anthu oipa amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendela, citani zimene Mlevi uja anacita. Mvelani malangizo a Mulungu acikondi na kugwilizana na anthu amene amacita cifunilo ca Mulungu. Ngati mumam’konda kwambili Yehova kuposa cina ciliconse, mudzapeza cimwemwe ceni-ceni. Ndipo mudzakhalabe panjila ya ku “moyo weniweniwo.”—1 Tim. 6:19
Tsanzilani Cikhulupililo ca Mose
5 Kodi tingakanize bwanji ‘zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo’? Tiyenela kudziŵa kuti zosangalatsa zaucimo n’zosakhalitsa. Cikhulupililo cidzatithandiza kudziŵa kuti “dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake.” (1 Yoh. 2:15-17) Ndipo tiyenela kukumbukila zimene zidzacitikila anthu ocimwa osalapa. Iwo ali ‘pamalo otelela . . . mapeto awo ndi oopsa.’ (Sal. 73:18, 19) Mukayesedwa kuti mucite chimo, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimenezi zidzakhudza bwanji tsogolo langa?’
w13-CN 2/15 25-26 ¶3-5
Musalole Ciliconse Kukulepheletsani Kupeza Ulemelelo
3 Wamasalimo ankakhulupilila kuti Yehova adzagwila dzanja lake lamanja n’kumutsogolela ku ulemelelo. (Ŵelengani Salimo 73:23, 24.) Kodi Yehova amapatsa bwanji anthu ulemelelo? Iye amatsogolela anthu ake odzicepetsa ku ulemelelo poŵadalitsa m’njila zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, amaŵathandiza kumvetsa colinga cake. (1 Akor. 2:7) Iye amalolanso kukhala pa ubwenzi wolimba na anthu amene amamumvela.—Yak. 4:8.
4 Yehova amalemekezanso atumiki ake poŵapatsa mwayi wolalikila uthenga wabwino. (2 Akor. 4:1, 7) Utumiki umenewu umatipatsa ulemelelo. Anthu amene amacita utumikiwu n’colinga coti alemekeze Yehova ndiponso kuthandiza anthu ena, akulonjezedwa kuti: “Amene akundilemekeza ndiŵalemekeza.” (1 Sam. 2:30) Anthu otelewa amakhala pa ubwenzi wabwino na Yehova ndipo nthawi zambili amalemekezedwa na atumiki anzawo.—Miy. 11:16; 22:1
5 Kodi tsogolo la anthu amene ‘amayembekezela Yehova, na kusunga njila zake’ ni lotani? Baibo limaŵalonjeza kuti: “[Yehova] adzakukweza kuti ulandile dziko lapansi. Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.” (Sal. 37:34) Iwo amayembekezela kuti Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha.—Sal. 37:29.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2-E 240
Leviyatani
Salimo 74 imakamba za mmene Mulungu amapulumutsila anthu ake, ndipo mophiphilitsa vesi 13 na 14 imakamba za mmene iye anapulumutsila Aisiraeli kucoka ku Iguputo. Pa lembali, mawu akuti “zilombo za m’nyanja,” komanso akuti “Leviyatani” aimila cinthu cimodzi. Ndipo mawu akuti “munaphwanya mitu ya Leviyatani” ayenela kuti akukamba za kugonjetsedwa kothelatu kwa Farao na magulu ake ankhondo, pa nthawi imene Yehova anatulutsa Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo. M’Baibo ya Ciaramu ya Targum, mawu akuti “mitu ya Leviyatani” anamasulidwa kuti “anthu amphamvu a Farao.” (Yelekezelani na Ezek. 29:3-5, pamene Farao akuyelekezedwa na “cilombo cacikulu ca m’nyanja” cimene cili mu mtsinje wa Nailo; komanso Ezek. 32:2) Cioneka kuti pa Yesaya 27:1, liwu lakuti Leviyatani linagwilitsidwa nchito mophiphilitsa ndipo limakamba za ufumu waukulu, bungwe la padziko lonse limene wolamulila wake amachedwa “njoka” kapena kuti “cinjoka.” (Chiv. 12:9). Ulosiwu ukamba za kubwezeletsedwa kwa Aisiraeli. Conco, mawu akuti Yehova ‘adzalanga’ Leviyatani ayenela kuti akuphatikizapo kulanga Babulo. Koma mavesi 12 na 13 akuchulanso Asuri na Iguputo. Conco, pa salimo limeneli, mwacidziŵikile Leviyatani akuimila bungwe kapena ulamulilo wa padziko lonse umene ukutsutsana na Yehova komanso alambili ake.
AUGUST 19-25
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 75-77
N’cifukwa Ciyani Simuyenela Kudzitukumula?
Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu
4 Paulo analemba kuti anthu adzakhala odzikonda ndi okonda ndalama. Kenako, analemba kuti anthu adzakhala odzimva, odzikweza, odzitukumula ndiponso onyada. Nthawi zambili, munthu amakhala na makhalidwe amenewa cifukwa codziona ngati wapamwamba kwambili kaamba ka maluso amene ali nawo, maonekedwe, cuma, kapena udindo wake. Anthu a makhalidwe amenewa amafuna kuti ena aziwatamanda. Katswili wina anafotokoza mmene munthu wonyada kwambili amadzionela. Analemba kuti: “Mu mtima mwake amakhala ngati ali na kaguwa, kamene amapitapo kukagwada n’kumadzilambila.” Ena amakamba kuti khalidwe lonyada n’loipa kwambili cakuti olo anthu onyadawo amaipidwanso na anthu anzawo onyada.
5 Yehova amadana kwambili na khalidwe la kunyada na kudzikweza. Iye amazonda anthu a “maso odzikweza.” (Miy. 6:16, 17) Kunyada na kudzikweza kumalepheletsa munthu kukhala pa ubwenzi na Mulungu. (Sal. 10:4) Amenewa ni makhalidwe a Mdyelekezi. (1 Tim. 3:6) Koma n’zomvetsa cisoni kuti ngakhale atumiki ena a Yehova anagwela mu msampha wa kudzikweza. Mwacitsanzo, mfumu ya Yuda, Uziya, anali wokhulupilika kwa zaka zambili. Koma Baibo imati: “Atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa. Conco anacita zosakhulupilika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kacisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.” Patapita zaka, nayenso Mfumu Hezekiya anakhala na mtima wodzikuza, koma anasintha mwamsanga.—2 Mbiri 26:16; 32:25, 26.
w06-CN 7/15 11 ¶3
Mfundo Zazikulu za Cigawo Cacitatu ndi Cacinayi cha Masalmo
75:4, 5, 10—Kodi mawu akuti “nyanga” amaimila ciyani? Nyanga za nyama ndi cida camphamvu. Motelo, mawu akuti “nyanga” mophiphilitsa amaimila mphamvu kapena nyonga. Yehova amanyamula nyanga za anthu ake, kuwaika pokwezeka, koma ‘amatseteka nyanga zonse za oipa.’ Tikucenjezedwa kuti ‘tisamakwezetse nyanga yathu kuti tisakhale onyada kapena odzikweza. Popeza Yehova ndiye amakweza anthu, tiyenela kuona udindo pampingo kuti umacokela kwa iye.—Salimo 75:7.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 7/15 11 ¶4
Mfundo Zazikulu za Cigawo Cacitatu ndi Cacinayi ca Masalmo
76:10—Kodi “kuzaza kwake kwa munthu” kungalemekeze bwanji Yehova? Mulungu akamalola anthu kutikwiyila cifukwa coti ndife atumiki ake, pangakhale zotsatilapo zabwino. Vuto lililonse limene tingakumane nalo lingatipatse phunzilo lina lake. Yehova amalola kuvutika n’colinga coti kuvutikako kutiphunzitse kanthu kena. (1 Petulo 5:10) ‘Cotsalila ca kuzaza kwa munthu, Mulungu adzaciletsa.’ Bwanji ngati tivutika mpaka kumwalila? Izinso zingalemekeze Yehova cifukwa anthu omwe anationa tikupilila mokhulupilika iwonso angayambe kupembedza Mulungu.
AUGUST 26–SEPTEMBER 1
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 78
Citsanzo Coticenjeza ca Aisiraeli Osakhulupilika
w96-CN 12/1 29-30
“Kumbukilani Masiku Apitawo”—Cifukwa Ninji?
Mwacisoni, Aisraeli nthawi zambili anagonjela ku chimo la kuiŵala. Ndi cotulukapo cotani? “Anabwelela m’mbuyo, nayesa Mulungu, nacepsa Woyelayo wa Israeli. Sanakumbukila dzanja lake, tsikuli anawaombola kwa msautsi.” (Salimo 78:41, 42) M’kupita kwa nthawi, kuiŵala kwawo malamulo a Yehova kunacititsa kuti awakane.—Mateyu 21:42, 43.
Citsanzo cabwino cinapelekedwa ndi wamasalimo amene analemba kuti: “Ndidzakumbukila zimene adazicita Ambuye; inde, ndidzakumbukila zodabwitsa zanu zoyambila kale. Ndipo ndidzalingalila nchito yanu yonse, ndi kulingalilabe zimene munazicita inu.” (Salimo 77:11, 12) Kukumbukila kosinkhasinkha kotelo kwa utumiki wokhulupilika wakale ndi zocita za Yehova zacikondi kudzatipatsa cisonkhezelo cofunikila, cilimbikitso, ndi ciyamikilo. Ndiponso, ‘kudzikumbutsa masiku akale’ kungathetse kutopa ndipo kungatisonkhezele kucita zonse zimene tingathe ndi kupilila mokhulupilika.
w06-CN 7/15 17 ¶16
Pewani Kudandaula
16 Munthu akamang’ung’udza amangoganizila za iye yekha ndi mavuto ake ndipo amanyalanyaza madalitso amene tili nawo monga Mboni za Yehova. Ngati tili ndi cizolowezi codandaula ndipo tikufuna kucithetsa, tifunikila kumakumbukila madalitso amenewa. Mwacitsanzo, aliyense wa ife ali ndi mwayi wosangalatsa wodziŵika ndi dzina la Yehova. (Yesaya 43:10) Tingakhale ndi ubwenzi wolimba ndi iye, ndipo timatha kulankhula ndi “Wakumva pemphelo” ameneyu panthawi iliyonse. (Salimo 65:2; Yakobo 4:8) Moyo wathu umakhala n’colinga cifukwa chakuti timamvetsa nkhani ya ulamulilo wacilengedwe conse ndipo timakumbukila kuti ndi mwayi wathu kukhala okhulupilika kwa Mulungu. (Miyambo 27:11) Tingatenge nawo mbali kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu nthawi zonse. (Mateyu 24:14) Kukhulupilila nsembe ya dipo ya Yesu Khristu kumatithandiza kukhala ndi cikumbumtima coyela. (Yohane 3:16) Amenewa ndi madalitso omwe timakhala nawo kaya tifunikila kupilila zinthu zotani.
w11-CN 7/1 10 ¶3-4
Kodi Yehova Amasangalala Kapena Kukhumudwa Ndi Zochita Zathu?
Wamasalimo ananena kuti: “Iwo analitu kumupandukila kaŵilikaŵili m’cipululu.” (Vesi 40) Vesi lotsatila limanena kuti: “Mobwelezabweleza, anali kumuyesa Mulungu.” (Vesi 41) Kodi mwaona kuti salimo limeneli likusonyeza kuti zimenezi zinkacitika mobweleza-bweleza? Aisiraeli anayamba kusalemekeza Mulungu komanso kumupandukila ali m’cipululu, pasanapite nthawi yaitali kucokela pamene Mulungu anawapulumutsa ku Iguputo. Iwo anayamba kung’ung’udza komanso kukayikila ngati Mulungu angathe kuwasamalila komanso ngati ankafunadi kuwasamalila. (Numeri 14:1-4) Buku lina lothandiza anthu omasulila Baibo limanena kuti mawu akuti ‘anali kumupandukila’ angamasulilidwenso kuti ‘anaumitsa mitima yawo kuti asamvele Mulungu’ kapena ‘anauza Mulungu kuti, “sitikufuna kuti mukhale Mulungu wathu.”’ Komabe, popeza Yehova ndi Mulungu wacifundo, iye ankakhululukila anthu akewa akalapa. Koma zikatelo iwo ankayambilanso kucita zinthu zoipa ndipo ankamupandukilanso. Akalapa, Yehova ankawakhululukilanso ndipo izi zinkacitika mobweleza-bweleza.—Salimo 78:10-19, 38.
Kodi Yehova ankamva bwanji Aisiraeli osamvelawa akamupandukila? Vesi 40 limanena kuti: “Anali kumukhumudwitsa.” Baibo lina linamasulila mawu amenewa kuti, “ankacititsa kuti Mulungu amve cisoni.” Buku lina lofotokoza nkhani za m’Baibo imati: “Mawu amenewa akutanthauza kuti zimene Ayuda ankacita zinkamupweteketsa mtima Yehova ngati mmene makolo amamvela, mwana wawo akamawacitila mwano komanso akawapandukila.” Mofanana ndi mmene mwana wosamvela amapweteketsela kwambili mtima makolo ake, Aisiraeli “anali kumvetsa cisoni Wolela wa Isiraeli.”—Vesi 41.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 7/15 11 ¶5
Mfundo Zazikulu za Cigawo Cacitatu ndi Cacinayi ca Masalmo
78:24, 25—N’cifukwa ciyani mana amachedwa “tirigu wa kumwamba” ndiponso “mkate wa omveka” kapena kuti angelo? Mawu onsewa satanthauza kuti mana cinali cakudya ca angelo. Mana anali “tirigu wa kumwamba” cifukwa cakuti ankacokela kumwamba. (Salmo 105:40) Popeza angelo, kapena kuti “omveka,” amakhala kumwamba, mawu akuti “mkate wa omveka” angatanthauze kuti mana anapelekedwa ndi Mulungu, amene amakhala kumwamba. (Salimo 11:4) Yehova angakhale kuti analinso kugwilitsa nchito angelo kupeleka mana kwa Aisraeli.