Malifalensi a Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
NOVEMBER 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 105
“Amakumbukila Pangano Lake Mpaka Kalekale”
Tingalimbitse Motani Cikhulupililo Cathu pa Lonjezo la Yehova la Dziko Latsopano?
11 Onani zina mwa zinthu zooneka ngati zosatheka zimene Yehova analonjeza anthu ake kalelo. Iye anauza Abulahamu na Sara kuti adzakhala na mwana mu ukalamba wawo. (Gen. 17:15-17) Anamuuzanso kuti mbadwa zake zidzapatsidwa dziko la Kanani. Kwa zaka zambili zimene Aisiraeli, amene anali mbadwa za Abulahamu, anali mu ukapolo ku Iguputo, lonjezo limeneli linaoneka ngati losatheka. Koma linakwanilitsidwa. Patapita nthawi, Yehova ananena kuti Elizabeti wacikalambile adzakhala na mwana. Iye anauzanso namwali Mariya kuti adzabeleka Mwana wa Mulungu. Izi zinali kudzakwanilitsa lonjezo limene Yehova anapanga m’munda wa Edeni zaka masauzande kumbuyoko.—Gen. 3:15.
12 Tikaona mmene Yehova anakwanilitsila malonjezo ake kumbuyoku, timalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti iye adzakwanilitsanso lonjezo lake la dziko latsopano. (Ŵelengani Yoswa 23:14; Yesaya 55:10, 11.) Izi zimatilimbikitsa kuthandiza ena kuti azindikile kuti dziko latsopano ni lenileni, osati maloto cabe. Ponena za kumwamba kwatsopano na dziko lapansi latsopano, Yehova iye mwini anati: “Mawu amenewa ndi odalilika komanso oona.”—Chiv. 21:1, 5.
it-2-E 1201 ¶2
Mawu
Zolengedwa za moyo komanso zopanda moyo, zimadalila mawu a Mulungu, ndipo angaziseŵenzetse pokwanilitsa colinga cake. (Sal. 103:20; 148:8) Mawu ake ni odalilika cifukwa iye akalonjeza cina cake amakwanilitsa. (Deut. 9:5; Sal. 105:42-45) Ndipo monga mmene iye mwini anakambila, mawu ake “adzakhalapo mpaka kalekale”; sadzabwelela popanda kukwanilitsa colinga cake.—Yes. 40:8; 55:10, 11; 1Pe 1:25.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w86-CN 11/1 18 ¶15
Achichepere—Mbali Yanu m’Banja Lacimwemwe, ndi Logwilizana
15 “Anapweteka miyendo yake [ya Yosefe] ndi matangadza; anam’goneka mu unyolo; kufikila nthawi imene, mawu a Yehova anamuyesa.” (Salmo 105:17-19) Kwa zaka 13, Yosefe anavutika monga kapolo ndi wandende kufikila lonjezo la Yehova linakwanilitsidwa. Mwa cokumana naco cimeneci iye anayesedwa. Ngakhale kuti Yehova sanacititse mavutowo, iye anawalola kaamba ka cifuno. Kodi Yosefe akasungabe ciyembekezo cakeco mu “mawu a Yehova” mosasamala kanthu za kukhala m’nsautso yadzawoneni? Kodi iye akakhwimitsa mikhalidwe yake yabwino kwambiliyo, ndi kukulitsa kuleza mtima, kudzicepetsa, nyonga yauzimu, ndi citsimikizo zofunikazo kusamalila gawo lovuta? Eya, Yosefe anatuluka ali wofanana ndi golidi m’moto wa woyenga—woyengeka kwambili ndipo wamtengo wapatali koposelapo kwa Mulungu, amene anam’gwilitsila nchito kwambili pambuyo panthawiyo.—Genesis 41:14, 38-41, 46; 42:6, 9.
NOVEMBER 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 106
“Iwo Anaiwala Mulungu, Mpulumutsi Wawo”
“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”
13 Aisiraeli anacita mantha na mtambo wakuda, mphenzi, na zizindikilo zina zocititsa mantha zocokela kwa Mulungu. Kaamba ka ici, iwo anapempha kuti Mulungu asakambe nawo mwacindunji, koma kuti Mose aziwauza zilizonse zimene Mulunguyo adzakamba naye pa Phili la Sinai. Ndipo Mose anacitadi zimenezo. (Eks. 20:18-21) Mose anakwela m’phililo, ndipo anakhalamo kwa nthawi yaitali. Aisiraeli anayamba kuona ngati kuti ali okha-okha m’cipululumo popanda mtsogoleli aliyense. Zioneka kuti cikhulupililo ca anthuwo cinali kudalila kwambili pa Mose, mtsogoleli wawo waumunthu. Conco iwo anada nkhawa, ndipo anauza Aroni kuti: “Tipangile mulungu woti atitsogolele, cifukwa sitikudziŵa zimene zacitikila Mose, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.”—Eks. 32:1, 2.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 7/15 13 ¶9
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachitatu ndi Chachinayi cha Masalimo
106:36, 37. Mavesiwa akusonyeza kuti kulambila mafano kumagwilizana ndi nsembe zopelekedwa ku ziwanda. Zimenezi zikutanthauza kuti, munthu amene amapembedza mafano angayambe kugwilitsidwa nchito ndi ziwanda. Baibulo limatilangiza kuti: “Dzisungileni nokha kupewa mafano.”—1 Yoh. 5:21.
NOVEMBER 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 107-108
“Yamikani Yehova Chifukwa Iye Ndi Wabwino”
w07-CN 4/15 20 ¶2
Mpingo Uyenela Kutamanda Yehova
2 Mpingo si gulu wamba, komanso si bungwe kapena gulu la anthu okonda maseŵela ndiponso zosangalatsa zinazake. Koma mpingo wapangidwa n’colinga cotamanda Yehova Mulungu. Zimenezi zakhala conco kuyambila kalekale, malinga ndi kufotokoza kwa buku la Masalimo. Ndipotu lemba la Salmo 35:18 limati: “Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu, m’cikhamu ca anthu ndidzakulemekezani.” Mofananamo, Salmo 107:31, 32 limatilimbikitsa kuti: “Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cake, ndi zodabwiza zake za kwa ana a anthu! Am’kwezenso mu msonkhano wa anthu.
Yamikani Yehova Ndipo Mudzadalitsidwa
4 Khama ndi lofunika kuti tikhalabe oyamikila kwa Yehova. Coyamba, tiyenela kuzindikila zinthu zabwino zimene Yehova waticitila. Ndiyeno, tiyenela kuona mmene zinthu zimenezi zimasonyezela cikondi cacikulu cimene Mulungu ali naco pa ife. Wamasalimo anadabwa kwambili atazindikila kuculuka kwa zinthu zabwino zimene Yehova anam’citila.—Ŵelengani Salimo 40:5; 107:43.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2-E 420 ¶4
Mowabu
Patapita nthawi, Davide akulamulila monga Mfumu, panacitika nkhondo pakati pa Aisiraeli na Amowabu. Amowabu anagonjetsedwa kothelatu ndipo analamulidwa kuti azipeleka msonkho kwa Davide. Mwacionekele, kumapeto kwa nkhondoyo, magulu aŵili mwa magulu atatu a asilikali Acimowabu anaphedwa. Zioneka kuti Davide anawagoneka pansi mu mzele na kupima mzelewo kuti adziŵe magulu aŵili oti awaphe komanso gulu limodzi lotsala. (2 Sam. 8:2, 11, 12; 1 Mbiri 18:2, 11) N’kutheka kuti ni pa nkhondo imodzimodziyo pamene Benaya mwana wa Yehoyada “anapha ana aŵili a Ariyeli wa ku Mowabu.” (2 Sam. 23:20; 1 Mbiri 11:22) Kupambana kwa Davide kumeneku kunakwanilitsa ulosi wa Balamu umene unanenedwa zaka zoposa 400 izi zisanacitike. Ulosiwo unali wakuti: “Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo, Ndodo yacifumu idzatuluka mu Isiraeli. Ndipo iye adzaphwanyadi cipumi ca Mowabu. Ndi mitu ya asilikali onse ankhanza.” (Num. 24:17) N’kuthekanso kuti wamasalimo anali kunena za kupambana kumeneku pamene anakamba kuti Mulungu anali kuona Mowabu monga ‘beseni lake losambilamo.’—Sal. 60:8; 108:9.
NOVEMBER 25–DECEMBER 1
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 109-112
Thandizilani Yesu Amene ni Mfumu!
w06-CN 9/1 13 ¶6
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachisanu cha Masalmo
110:1, 2—Kodi “Ambuye [wa Davide],” Yesu Kristu, anacita ciyani atakhala kudzanja lamanja la Mulungu? Yesu atauka kwa akufa, anakwela kumwamba ndipo anadikila kudzanja lamanja la Mulungu mpaka mu 1914 pamene anayamba kulamulila monga Mfumu. Nthawi imene Yesu anali kudikilayo, analamulila otsatila ake odzozedwa, powatsogolela pa nchito yawo yolalikila ndi kupanga ophunzila ndiponso powakonzekeletsa kuti akalamulile limodzi naye mu Ufumu wake.—Mateyu 24:14; 28:18-20; Luka 22:28-30.
w00-CN 4/1 17 ¶3
Omenyana Ndi Mulungu Sadzapambana!
3 Anthu a Yehova akhala akuukilidwa kuyambila kuciyambi ca zaka za zana la 20. M’mayiko ambili, anthu oipa mtima akhala akuyesa kusokoneza, inde, kuthetsa kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Asonkhezeledwa ndi Mdani wathu wamkulu, Mdyelekezi, amene “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwile.” (1 Pet. 5:8) “Nthaŵi zawo za anthu akunja” zitatha mu 1914, Mulungu analonga Mwana wake kukhala Mfumu yatsopano ya dziko lapansi, ndi kum’lamula kuti: “Citani ufumu pakati pa adani anu.” (Luka 21:24; Salimo 110:2) Posonyeza mphamvu zake, Khristu anacotsa Satana kumwamba ndi kum’tsekela kudziko lapansi. Podziŵa kuti nthaŵi yam’thela, Mdyelekezi akulusila Akhristu odzozedwa ndi mabwenzi awo. (Chivumbulutso 12:9, 17) Kodi kuukila kobwelezabweleza kwa olimbana ndi Mulungu ameneŵa kwakhala ndi zotsatila zotani?
be-CN 76 ¶2
Khalani Womapitabe Patsogolo
Langizo lakuti gwilitsani nchito mphatso yanu limatanthauza kugwilitsa nchito nzelu. Kodi mumanyamuka nokha kuti mukagwile nchito yakumunda pamodzi ndi ena? Kodi mumafunafuna mipata yoti muthandize atsopano mumpingo wanu, ang’onoang’ono, kapena olemala? Kodi mumadzipeleka panchito yokayeletsa ku Nyumba ya Ufumu kapena kuthandiza m’njila zosiyanasiyana pamisonkhano ikuluikulu? Kodi mukhoza kumalembetsa nthaŵi ndi nthaŵi upainiya wothandiza? Kodi mungatumikile ngati mpainiya wokhazikika kapena kukathandiza kumpingo wosoŵa? Ngati muli m’bale, kodi mukukalamila kuti mukafikile ziyeneletso za m’Malemba za atumiki otumikila ndi akulu? Kudzipeleka kwanu kuti muthandize ndi kulandila udindo kuli umboni wa kupita patsogolo.—Sal. 110:3.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 524 ¶2
Pangano
Pangano lokhala wansembe monga Melekizedeki.
Panganoli limachulidwa pa Salimo 110:4, ndipo wolemba buku la m’Baibo la Aheberi, pa Aheberi 7:1-3, 15-17 anafotokoza kuti limakamba za Khristu. Ni pangano la pakati pa Yehova na Yesu Khristu cabe. Mwacionekele, Yesu anali kukamba za pangano limeneli pamene anali kucita pangano la ufumu na otsatila ake. (Luka 22:29) Mwa lumbilo la Yehova, Yesu Khristu amene ni Mwana wa Mulungu wa kumwamba, anali kudzakhala wansembe monga Melekizedeki. Melekizedeki anali mfumu komanso wansembe wa Mulungu padziko. Yesu Khristu anali kudzakhala Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe kumwamba, osati padziko lapansi. Anapatsidwa maudindo amenewa mwacikhalile atapita kumwamba. (Aheb. 6:20; 7:26, 28; 8:1) Panganoli lidzagwila nchito kwamuyaya, popeza Yesu adzakhala pansi pa citsogozo ca Yehova monga Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe kwamuyaya.—Aheb. 7:3.
DECEMBER 2-8
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 113-118
Kodi Tidzamubwezela Chiyani Yehova?
w01-CN 1/1 11 ¶13
Kulani M’chikondi
13 Kucokela m’mawu a Yesuwo, n’zoonekelatu kuti coyambilila tiyenela kukonda Yehova. Komabe, sitibadwa okhoza kumukonda kwambili Yehova. N’cinthu comwe tiyenela kucikulitsa. Titamva za iye kwa nthaŵi yoyamba, tinakopeka naye cifukwa ca zomwe tinamvazo. Pang’ono ndi pang’ono, tinaphunzila momwe analengela dziko kuti anthu akhalemo. (Genesis 2:5-23) Tinaphunzila momwe wakhala akucitila ndi anthu, sanatinyalanyaze pamene chimo linaloŵa m’banja la anthu, koma anacitapo kanthu kuti atiwombole. (Genesis 3:1-5, 15) Omwe anali okhulupilika anawacitila cifundo, ndipo pambuyo pake anapeleka Mwana wake wobadwa yekha kuti macimo athu athe kukhululukidwa. (Yohane 3:16, 36) Cidziŵitso cowonjezeka cimeneci cinakulitsa ciyamiko cathu kwa Yehova. (Yesaya 25:1) Mfumu Davide inati inakonda Yehova cifukwa ca cisamalilo cake cacikondi. (Salimo 116:1-9) Lelolino, Yehova amatisamalila, kutitsogolela, kutilimbitsa, ndi kutilimbikitsa. Tikamaphunzila zambili za iye, m’pamene cikondi cathu cimazama.—Salimo 31:23; Zefaniya 3:17; Aroma 8:28.
w09-CN 7/15 29 ¶4-5
Landilani Moyamikira Ndipo Perekani ndi Mtima Wonse
Wamasalimo anafunsa kuti: “Ndidzabwezela Yehova ciyani cifukwa ca zokoma zake zonse anandicitila?” (Sal. 116:12) Kodi ndi zinthu zokoma ziti zimene iye analandila? Yehova anamuthandiza kwambili pa nthawi imene anali mu “nsautso ndi cisoni.” Yehova ‘analanditsanso moyo wake ku imfa.’ Ndipo nayenso anafuna kucita zinazake kuti ‘abwezele’ Yehova. Ndiyeno kodi n’ciyani cimene wamasalmoyo akanacita? Iye anati: “Ndidzacita zowinda zanga za kwa Yehova.” (Sal. 116:3, 4, 8, 10-14) Iye anatsimikiza kukwanilitsa zonse zimene anawinda kuti adzacitila Yehova ndipo anatsimikiza kupeleka mangawa ake onse amene anali nawo kwa Yehova.
Nanunsotu mungathe kucita zimenezi. Kodi mungacite bwanji zimenezi? Mungatelo mwa kutsatila malamulo ndi mfundo za Mulungu pa moyo wanu wonse. Conco, onetsetsani kuti pa moyo wanu mukuika kulambila Yehova patsogolo ndipo mukulola mzimu wa Mulungu kukutsogolelani pa zilizonse zimene mumacita. (Mla. 12:13; Agal. 5:16-18) Kunena zoona, simungakwanitse kubwezela Yehova zinthu zonse zimene wakucitilani. Koma ngakhale zili conco, mukamayesetsa kudzipeleka ndi mtima wonse pomutumikila, ‘mumakondweletsa mtima wa Yehova.’ (Miy. 27:11) Ndi mwayitu waukulu kukondweletsa mtima wa Yehova mwa njila imeneyi!
Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko
9 Mfundo yaciŵili: Timatumikila Yehova cifukwa comuyamikila. Kuti timvetsetse mfundoyi, tiyeni tikambilane za nsembe zaciyanjano. Kupeleka nsembe zimenezi, inali mbali inanso yofunika kwambili pa kulambila koona mu Isiraeli wakale. Buku la Levitiko limakamba kuti Aisiraeli anali kupeleka nsembe zaciyanjano “posonyeza kuyamikila.” (Lev. 7:11-13, 16-18) Aisiraeli anali kupeleka nsembe zimenezi, osati mocita kulamulidwa, koma mwa kufuna kwawo. Anali kucita izi cifukwa cokonda Mulungu wawo Yehova. Munthu wopeleka nsembeyo, banja lake, na wansembe, anali kudya nyama ya nsembeyo. Koma ziwalo zina za nyamayo zinali kupelekedwa kokha kwa Yehova. Kodi ziwalo zimenezo ni ziti?
10 Mfundo yacitatu: Timapatsa Yehova zabwino koposa cifukwa timam’konda. Yehova anali kuona mafuta kukhala mbali yabwino koposa ya nyama. Iye anafotokozanso kuti ziwalo zina za nyama, kuphatikizapo impso zinali zofunika kwambili. (Ŵelengani Levitiko 3:6, 12, 14-16.) Conco, Yehova anali kukondwela ngako Mwisiraeli akapeleka modzifunila ziwalo zofunika kwambili za nyama komanso mafuta. Mwisiraeli akapeleka nsembe imeneyo, anali kuonetsa kuti akufunitsitsa kupatsa Mulungu zabwino koposa. Yesu anacita zofanana na zimenezi. Modzifunila, anapatsa Yehova zabwino koposa mwa kum’tumikila na mtima wonse cifukwa com’konda. (Yoh. 14:31) Yesu anali kukondwela kucita cifunilo ca Mulungu, ndipo anali kukonda kwambili cilamulo cake. (Sal. 40:8) Ndithudi, Yehova anakondwela kwambili kuona kuti Yesu akum’tumikila na mtima wonse!
11 Utumiki wathu kwa Yehova uli ngati nsembe zaciyanjano. Pamene tim’tumikila, timaonetsa kuti timam’konda. Timapatsa Yehova zabwino koposa, ndipo timacita zimenezi cifukwa timam’konda na mtima wonse. Kukamba zoona, Yehova amakondwela kwambili akaona olambila ake ofika m’mamiliyoni, akumutumikila na mtima wonse cifukwa comukonda kwambili, komanso cifukwa cokonda miyezo yake! Tidziŵa kuti Yehova saona cabe zimene timacita pom’tumikila, koma amaonanso cimene cimatisonkhezela kucita zimenezo. Izi zimatitonthoza kwambili. Mwacitsanzo, ngati ndimwe okalamba ndipo simukwanitsa kucita zambili monga mmene mumafunila, dziŵani kuti Yehova amakumvetsetsani. Mwina mumaona kuti simucita zambili. Koma Yehova amaona cikondi canu cacikulu cimene cimakusonkhezelani kucita zimene mungathe pom’tumikila, ndipo amakondwela ngati mucita zimenezo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w12-CN 5/15 22 ¶1-2
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Wamasalimo anaimba mouzilidwa kuti: “M’maso mwa Yehova imfa ya anthu ake okhulupilika ndi nkhani yaikulu.” (Sal. 116:15) Yehova amaona kuti moyo wa munthu aliyense amene amamulambila ndi wamtengo wapatali kwambili. Koma mawu a pa Salimo 116 sakungonena za imfa ya munthu mmodzi.
Pokamba nkhani ya malilo a Mkhristu, si bwino kugwilitsa ntchito lemba la Salimo 116:15 pofotokoza za munthu womwalilayo ngakhale kuti iye wamwalila ali wokhulupilika kwa Yehova. N’cifukwa ciyani tikutelo? Cifukwa cakuti mawu a wamasalimoyu sakunena za munthu mmodzi womwalila. Mawuwa akutanthauza kuti Mulungu amaona kuti imfa ya gulu lonse la anthu ake okhulupilika ndi nkhani yaikulu kwambili moti sangalole kuti zicitike.—Onani Salimo 72:14; 116:8.
DECEMBER 9-15
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 119:1-56
“Kodi Wacinyamata Angakhale Bwanji Woyela pa Moyo Wake?”
w87-CN 11/1 18 ¶10
Kodi Mukukhalabe Osadetsedwa m’Njira Iriyonse?
10 Pa Aefeso 5:5 Paulo anacenjeza kuti: “Pakuti ici muchidziŵe kuti wadama yense, kapena wacidetso, kapena wosilila, amene apembedza mafano, alibe colowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.” Komabe, zikwi caka ciliconse zimadzudzulidwa kapena kucotsedwa cifukwa ca mkhalidwe woipa wa cisembwele—‘kucimwila thupi.’ (1 Akorinto 6:18) Kaŵilikaŵili, ico cili kokha cotulukapo ca “kusasamalila monga mwa mawu a [Mulungu].” (Masalimo 119:9) Abale ambili, mwacitsanzo, amacotsa kudzicinjiliza kwawo kwa makhalidwe mkati mwa nthaŵi ya chuthi. Kunyalanyaza mayanjano a teokratiki, iwo amayambitsa ubwenzi ndi anthu a pachuthi a kudziko. Akumalingalila kuti awo ‘alidi anthu abwino,’ Akhristu ena agwilizana nawo m’macitacita okaikitsa. Mofananamo, ena akhala aubwenzi kwambili ndi ogwila nawo ntchito. Mkulu mmodzi Wacikristu anakhala wodzilowetsamo kwambili ndi mkazi wogwila naye nchito kotelo kuti iye anasiya banja lake ndi kuyamba kukhala ndi iye! Kucotsedwa kunatulukapo. Ali mowona cotani nanga mawu a Baibulo, “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma”!—1 Akorinto 15:33.
w06-CN 6/15 25 ¶1
“Zikumbutso Zanu Ndizo Zondikondweretsa!”
YEHOVA amapatsa anthu ake zikumbutso kuti awathandize kulimbana ndi zovuta za masiku athu ano. Zina mwa zikumbutso zimenezi zimabwela munthu akamaŵelenga yekha Baibulo, ndipo zina zimacokela mu nkhani kapena ndemanga zopelekedwa pa misonkhano yacikhristu. Zambili zimene timaŵelenga kapena kumva pa nthawi zimenezi si zacilendo kwa ife. Mosakayikila, tinamvapo zinthu ngati zimenezi m’mbuyomu. Koma popeza siticedwa kuiwala, tifunika kupitilizabe kudzikumbutsa za zolinga, malamulo, ndi malangizo a Yehova. Tiyenela kuyamikila zikumbutso za Mulungu. Zimatilimbikitsa potikumbutsa zifukwa zomwe zinaticititsa kuyamba kukhala moyo wogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu. Conco wamasalmo anaimba kwa Yehova kuti: “Mboni [“zikumbutso,” NW] zanu zomwe ndizo zondikondwetsa.”—Salmo 119:24.
w10-CN 4/15 20 ¶2
Musamaone Zinthu Zachabe!
2 Komabe, zimene timaona zikhozanso kutiwononga. Pali kugwilizana kwambili pakati pa zimene timaona ndi zimene timaganiza, moti zimene timaona zingatipangitse kuti tizilakalaka zinazake. Ndipo popeza tikukhala m’dziko loipa ndiponso la anthu odzikonda, lomwe wolamulila wake ndi Satana Mdyelekezi, timaona ndi kumva zinthu zimene zingatisoceletse mosavuta ngakhale titangoziyang’ana kanthawi kocepa. (1 Yoh. 5:19) Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti wamasalmo anapempha Mulungu kuti: “Mucititse mlubza maso anga ndisapenye zacabe, mundipatse moyo mu njila yanu.”—Sal. 119:37.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05-CN 4/15 10 ¶2
Khulupirirani Mawu a Yehova
2 Nkhani yaikulu mu Salmo 119 yagona pa phindu la mawu, kapena kuti uthenga wa Mulungu. Mwinamwake pofuna kuti azikumbukila mosavuta, mlembi ameneyu analemba nyimboyi motsatila ndondomeko ya zilembo za alifabeti. Mavesi ake onse okwana 176 anawalemba motsatila ndondomeko ya zilembo za alifabeti yaciheberi. M’ciheberi coyambilila, salmo limeneli lili ndi zigawo 22 ndipo ciliconse mwa zigawo zimenezi cili ndi mizela 8 yomwe ikuyamba ndi cilembo cofanana. Salmo limeneli likutchula mawu, cilamulo, zikumbutso, njila, malangizo, malemba, malamulo ndi maweluzo a Mulungu. M’nkhani ino komanso mu nkhani yotsatira tikambilana Salmo 119 malinga ndi mmene analimasulila m’Baibulo kucokela ku Ciheberi. Kusinkhasinkha zocitika pa moyo wa atumiki a Yehova akale ndi amakono omwe, kutithandiza kumvetsa bwino nyimbo youzilidwa ndi Mulungu imeneyi, ndiponso kukulitsa mtima wathu woyamikila Baibulo, Mawu olembedwa a Mulungu.
DECEMBER 16-22
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 119:57-120
Zimene Zingatithandize Kupilila Mavuto
w06-CN 6/15 20 ¶2
“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”
2 Mwina mungafunse kuti, “Kodi cilamulo ca Mulungu cinalimbikitsa ndi kutonthoza bwanji wamasalmoyo?” Comwe cinamulimbikitsa ndi cikhulupililo cake coti Yehova ankamufunila zabwino. Kudziŵa bwino ubwino wotsatila cilamulo cimeneco kunacititsa wamasalimoyo kukhala wosangalala, ngakhale anali ndi mavuto amene adani ake anam’bweletsela. Iye anadziŵa kuti Yehova wamucitila zabwino. Ndiponso, kugwilitsa nchito malangizo a m’cilamulo ca Mulungu kunacititsa wamasalimoyo kukhala wanzelu kuposa adani ake ndipo kunateteza moyo wake. Kumvela cilamulo kunam’patsa mtendele wa mumtima ndi cikumbumtima cabwino.—Salimo 119:1, 9, 65, 93, 98, 165.
w00-CN 12/1 14 ¶3
Kodi Zikumbutso za Yehova Mumazikonda Kwambiri?
3 Zikumbutso za Yehova zinali zamtengo wapatali kwa wamasalmo yemwe anaimba kuti: “Ndinafulumila, osacedwa, kusamalila malamulo anu. Anandikulunga nazo zingwe za oipa; koma sindinaiwala cilamulo canu.” (Salimo 119:60, 61) Zikumbutso za Yehova zimatithandiza kupilila cizunzo cifukwa cakuti tili n’cidalilo conse kuti Atate wathu wakumwamba angadule zingwe za zitsendelezo zomwe adani angatikulunge nazo. M’nthaŵi yake, amatilanditsa ku zipsinjo zotelozo kotelo kuti tithe kugwila nchito yolalikila Ufumu.—Marko 13:10.
w06-CN 9/1 14 ¶4
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachisanu cha Masalmo
119:71—Kodi kuzunzidwa kungakhale kokoma m’njira yanji? Mavuto angatiphunzitse kudalila Yehova kwambili, kupemphela kwa iye ndi mtima wonse, ndi kucita khama pophunzila Baibulo ndi kutsatila zimene limanena. Ndiponso, zimene timacita tikamazunzidwa zingavumbule zolakwika zina pa umunthu wathu zimene tiyenela tikonze. Tikalola mavuto kutiyenga, pamapeto pake sitingakhumudwe nawo.
“Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”
3 Yehova, Atate wathu wacifundo wakumwamba, ndiye gwelo lalikulu la citonthozo. (Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Iye, amene ni wacifundo kwambili kuposa aliyense, anauza anthu ake kuti: “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.”—Yes. 51:12; Sal. 119:50, 52, 76.
5 Ngati tafedwa, tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzatithandiza. Conco, tizikhala womasuka kupemphela kwa Mulungu ndi kum’fotokozela zonse zokhudza cisoni cimene tili naco. N’zolimbikitsa ngako kudziŵa kuti Yehova amamvetsetsa mmene timvelela, ndipo amatipatsa citonthozo cofunikila. Koma kodi amacita bwanji zimenezi?
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 9/1 14 ¶5
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachisanu cha Masalmo
119:96—Kodi mawu akuti “malekezero ake a ungwiro wonse” akutanthauza chiyani? Apa wamasalimo akulankhula za ungwilo malinga ndi maganizo aumunthu. Ayenela kuti anali kuganiza za ungwilo, kuti munthu sangathe kuumvetsa cifukwa nzelu zake zili ndi malile. Kusiyana ndi zimenezo, lamulo la Mulungu lilibe malile. Mfundo zake n’zothandiza pa zocitika zonse za m’moyo wathu.”
DECEMBER 23-29
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 119:121-176
Mmene Tingapewele Kudzibweletsela Zopweteka
Lolani Malamulo a Mulungu na Mfundo Zake Kuphunzitsa Cikumbumtima Canu
5 Kuti tipindule na malamulo a Mulungu, tifunika kucita zambili osati cabe kuyaŵelenga kapena kuyadziŵa. Tifunika kumayakonda na kuyalemekeza. Mau a Mulungu amati: “Danani ndi coipa ndipo muzikonda cabwino.” (Amosi 5:15) Koma kodi tingacite bwanji zimenezi? Cofunika kwambili ni kuphunzila kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti imwe muli na vuto losoŵa tulo. Mutapita kucipatala, dokota wakupatsani malangizo okhudza kadyedwe, kucita maseŵela olimbitsa thupi, na kusintha zinthu zina mu umoyo wanu. Pambuyo potsatila malangizowo, mukuona kuti mwayamba kugona bwino tsopano. Mwacionekele, mungamuyamikile dokotayo cifukwa cokuthandizani kuthetsa vuto lanu.
6 Mofanana ndi zimenezi, Mlengi wathu watipatsa malamulo amene angatiteteze ku zotulukapo zoipa za ucimo na kutithandiza kukhala na umoyo wabwino. Ganizilani cabe mmene timapindulila cifukwa comvela malamulo a m’Baibo oletsa kunama, kucita cinyengo, kuba, ciwelewele, ciwawa, na zamizimu. (Ŵelengani Miyambo 6:16-19; Chiv. 21:8) Tikaona mapindu amene timapeza cifukwa comvela malamulo a Yehova, timayamba kukonda na kuyamikila kwambili Yehova na malamulo ake.
w93-CN 4/15 17 ¶12
Achichepere—Kodi Mukulondola Chiyani?
12 Koposa zonse, muyenela kuphunzila kuda, kunyansidwa, ndi kuipidwa ndi coipa. (Salmo 97:10) Kodi mungade motani cimene poyamba cingakhale cotsitsimula kapena cokondweletsa? Mwakuganiza za zotulukapo zake! “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta. Pakuti wakufesela kwa thupi la iye yekha, cocokela m’thupi adzatuta civundi.” (Agalatiya 6:7, 8) Pamene muli paciyeso cakuti mugonjele ku cilakolako, talingalilani za cotulukapo cowopsaco—mmene kudzampwetekera mtima Yehova Mulungu. (Yelekezelani ndi Salmo 78:41.) Ganizaninso, za kuthekela kwa mimba yosafunika kapena kutenga nthenda, monga AIDS. Talingalilani za kusweka mtima ndi kutaikilidwa ulemu wanu kumene mudzavutika nako. Pangakhalenso zotulukapo zanthaŵi yaitali. Mkazi wina Wacikristu akuvomeleza kuti: “Mwamuna wanga ndi ine tinali kucita cisembwele ndi anthu ena tisanakwatilane. Ngakhale kuti tsopano tonsefe ndife Akhristu, moyo wathu wacisembwele wakalewo ukucititsa kuvutana ndi nsanje muukwati wathu.” Ndiponso, zosayenela kunyalanyazidwa ndizo kutaikilidwa mathayo ateokratiki kapena kuthekela kwakucotsedwa mumpingo Wacikristu! (1 Akorinto 5:9-13) Kodi cisangalalo cakanthaŵi ciliconse ncoyenelela kutaikilidwa konseko?
Kufufuza Cuma Cauzimu
Khalani Otsimikiza Kuti ‘Mawu a Mulungu Ndi Coonadi’
2 Pokhala atumiki a Yehova, ndife otsimikiza kuti iye ni “Mulungu wa coonadi,” ndipo nthawi zonse amatifunila zabwino. (Sal. 31:5; Yes. 48:17) Timakhulupilila zimene timaŵelenga m’Baibo, cifukwa tidziŵa kuti: “Mawu onse [a Mulungu] ndi coonadi cokha-cokha.” (Ŵelengani Salimo 119:160.) Tingagwilizane naye katswili wina wa Baibo pa zimene analemba. Iye anati: “Pa ciliconse cimene Mulungu angakambe kuti adzacita, sipakhala bodza lililonse kapena kulephela kulikonse ayi. Anthu a Mulungu amakhulupilila zimene iye wanena, cifukwa amakhulupilila Mulungu amene wanena zimenezo.”
DECEMBER 30–JANUARY 5
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 120-126
Anabyala Akulila, Koma Anakolola Akusangalala
w04-CN 6/1 16 ¶10
Odala Ndi Amene Amapatsa Mulungu Ulemerero
10 Tikasenza goli lokhala ophunzila a Yesu, ndiye kuti tikulimbana ndi Satana. Yakobo 4:7 amalonjeza kuti: “Kanizani Mdyelekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” Apa sitikunena kuti n’zapafupi kuchita zimenezi. Kutumikila Mulungu kumafuna khama. (Luka 13:24) Komano Baibulo, pa Salmo 126:5, limatilonjeza kuti: “Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwela.” Eya, Mulungu amene ife timam’lambila amayamikila. Iye ali “wobwezela mphoto iwo akum’funa Iye,” ndipo amadalitsa anthu amene amam’patsa ulemelelo.—Aheberi 11:6.
Kodi Cikhulupililo Canu Cidzakhala Colimba Motani?
17 Kodi muli na cisoni cifukwa cofeledwa munthu amene mumam’konda? Muzipatula nthawi kuti mulimbitse cikhulupililo canu cakuti akufa adzauka, mwa kuŵelenga nkhani za m’Baibo zokamba za anthu amene anaukitsidwa. Kodi muli na cisoni cifukwa wa m’banja mwanu anacotsedwa mu mpingo? Ŵelengani na kufufuza kuti mutsimikize zakuti cilango ca Yehova n’copindulitsa nthawi zonse. Kaya mukumane na vuto lotani, seŵenzetsani mpata umenewo kuti mulimbitse cikhulupililo canu. Khuthulani za mu mtima mwanu kwa Yehova. Musamadzipatule, koma gwilizanani kwambili na abale na alongo anu. (Miy. 18:1) Muzicita zinthu zimene zingakuthandizeni kupilila, olo kuti mungamalile pamene mukucita zimenezo. (Sal. 126:5, 6) Musaleke kupezeka ku misonkhano, kulalikila, na kuŵelenga Baibo. Cina, sumikani maganizo anu pa madalitso amene Yehova wakusungilani. Mukamaona mmene Yehova akukuthandizilani, cikhulupililo canu mwa iye cidzalimbila-limbilako.
w01-CN 7/15 18-19 ¶13-14
Limbikirani Ntchito yotuta!
13 Mawu opezeka pa Salmo 126:5, 6 ali olimbikitsa kwambili kwa otuta makamaka amene amazunzidwa. Mawuwo amati: “Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwela. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbewu yakufesa; adzabwelanso ndithu ndi kufuula mokondwela, alikunyamula mitolo yake.” Mawu a wamasalmo onena za kufesa ndi kututa akusonyeza cisamalilo ndi madalitso a Yehova kwa otsala amene anabwelako ku ukapolo ku Babulo wakale. Anakondwa kwambili atamasulidwa, koma ayenera kuti analila pofesa mbewu m’dziko labwinja lomwe sanalimemo kwa zaka 70 zomwe anali ku ukapolo. Komabe, amene anapitiliza nchito yawo yofesa ndi kumanga anapeza zokolola zambili komanso kukhutila ndi nchito yawo.
14 Tingakhetse misozi poyesedwa kapena pamene ifeyo ndi okhulupilila anzathu tikuzunzidwa cifukwa ca cilungamo. (1 Petro 3:14) Pa nchito yathu yotutayi, mwina zinthu zingativute poyamba cifukwa cakuti tikuona ngati palibe umboni wosonyeza phindu la khama lathu mu utumiki. Koma ngati tilimbikira kufesa ndi kuthilila, Mulungu adzakulitsa, mwinanso kuposa mmene tingaganizire. (1 Akorinto 3:6) Zimenezi zikusonyezedwa bwino lomwe ndi mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Malemba omwe tagaŵila.
Kufufuza Cuma Cauzimu
cl-CN 73 ¶15
Mphamvu Zoteteza—“Mulungu Ndiye Pothaŵirapo Pathu”
15 Coyamba, talingalilani citetezo cakuthupi. Pokhala olambila Yehova, tingayembekeze kutitetezera motelo monga gulu. Apo ayi, Satana akanatilikwila mosavuta. Taganizilani izi: Satana, “mkulu wa dziko ili lapansi,” palibe cina cimene amafuna koma kuthetsa kulambila koona. (Yohane 12:31; Chivumbulutso 12:17) Maboma ena amphamvu kwambili padziko lapansi aletsa nchito yathu yolalikila ndipo ayesetsa kuti angotifafanizilatu. Komatu, anthu a Yehova akhalabe olimba ndipo apitiriza kulalikira mosaleka! N’cifukwa ciyani mayiko amphamvu alephela kuletsa nchito ya gulu la Akhristu ocepaŵa ndi ooneka ngati opanda citetezo? N’cifukwa cakuti Yehova watitcingila ndi mapiko ake amphamvu!—Salmo 17:7, 8.