Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JANUARY 6-12
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 127-134
Makolo, Pitilizani Kusamalila Colowa Canu ca Mtengo Wapatali
Muziyamikila Malo Anu M’banja la Yehova
9 Yehova anapatsa anthu mphamvu zobeleka ana, komanso udindo wowaphunzitsa kukonda Yehova na kum’tumikila. Ngati ndimwe kholo, kodi mumayamikila mphatso yapadela imeneyi? Ngakhale kuti Yehova anapatsa angelo mphatso zambili zabwino, iwo sanapatsidwe mphatso yobeleka. Conco ngati ndinu kholo, muziyamikila udindo wapadela umenewu wolela ana. Munapatsidwa udindo wofunika kwambili, wolela ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4; Deut. 6:5-7; Sal. 127:3) Pofuna kuthandiza makolo, gulu la Mulungu lapeleka zida zophunzilila Baibo, monga mabuku, mavidiyo, nyimbo, komanso nkhani za pa webusaiti yathu. N’zoonekelatu kuti, Atate wathu wakumwamba na Mwana wake amakonda acicepele athu. (Luka 18:15-17) Ngati makolo amadalila Yehova, na kucita zonse zimene angathe posamalila ana awo amtengo wapatali, Yehova amakondwela. Makolo otelo amapatsa ana awo ciyembekezo codzakhala m’banja la Yehova kwamuyaya.
Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova
20 Khalani ozindikila. Salimo 127 imakamba kuti ana ali ngati mivi. (Ŵelengani Salimo 127:4.) Mivi imakhala ya zitsulo zosiyana-siyana, komanso imasiyana-siyana kukula kwake. Ni mmenenso ana alili. Mwana aliyense ni wosiyana na mnzake. Telo, makolo afunika kudziŵa mmene angaphunzitsile mwana aliyense payekha. Mwamuna wina na mkazi wake m’dziko la Israel, amene anakwanitsa kuthandiza ana awo kuyamba kutumikila Yehova, anafotokoza cimene cinawathandiza. Iwo anati: “Tinali kuphunzila Baibo na mwana aliyense payekha.” Conco, mutu wa banja aliyense angaone ngati n’zofunika kapena n’zotheka kuphunzila ndi ana awo mwanjila imeneyi.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 543
Zomela zochulidwa m’Baibo
Mphukila za mitengo ikulu-ikulu ya maolivi nthawi zambili amazigwilitsa nchito pobyala mitengo yatsopano. Ndiponso mitengoyi ikakhwima imatulutsa mphukila ku mizu yake. Izi zimacititsa kuti ipitilize kukhala ndi moyo. Mofanana ndi mphukilazi, ana anali kudzazungulila bambo wawo na kuthandiza kuti m’banja mukhale cimwemwe.
JANUARY 13-19
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 135-137
“Ambuye Wathu Ndi Wamkulu Kuposa Milungu Ina Yonse”
it-2-E 661 ¶4-5
Mphamvu, Nchito Zamphamvu
Mulungu amalamulila mphamvu za m’cilengedwe m’njila yapadela. M’pomveka kuyembekezela kuti Yehova angalamulile mphamvu za m’cilengedwe pofuna kuonetsa kuti iye ndiye Mulungu woona. Iye amacita zimenezi mogwilizana na tanthauzo la dzina lake. (Sal. 135:5, 6) Popeza dzuŵa, mwezi, mapulaneti, nyenyezi, nyengo, mbalame, dzombe na zinthu zina zimangotsatila malamulo a m’cilengedwe, zinthu zimenezi n’zosakwanila kuyeletsa dzina la Mulungu kwa otsutsa ndi alambili onyenga.
Ngakhale n’telo, Yehova Mulungu angapangitse cilengedwe na zinthu zina kupeleka umboni wakuti ndiyedi Mulungu woona mwa kuzigwilitsa nchito pokwanilitsa colinga cake. Angazipangitse kucita mosiyana ndi mmene zimacitila nthawi zonse. N’zoona kuti zinthu monga cilala, mvula zamkuntho, na zinthu zina zotelo, sizinali zapadela pa izo zokha. Koma zikacitika pokwanilitsa ulosi wa Yehova, zinali kukhala zapadela. (Yelekezelani na 1 Maf. 17:1; 18:1, 2, 41-45.) Komabe, zocitikazi nthawi zambili zinali zapadela cifukwa ca ukulu wake (Eks. 9:24) kapena cifukwa cocitika m’njila imene anthu anali asanaonepo kapena pa nthawi yosayembekezeleka.—Eks. 34:10; 1 Sam. 12:16-18.
Kodi Cikondi Cosasintha ca Yehova N’ciani?
16 Yehova akakhala Pothaŵilapo pathu, timamva kukhala otetezeka. Ngakhale n’telo, nthawi zina tingalefuke cakuti tingayambe kuona kuti sitilinso otetezeka. Pa nthawi zotelo, kodi Yehova adzacitanji kwa ife? (Ŵelengani Salimo 136:23.) Iye mwacikondi adzatinyamula na manja ake, na kutithandiza kuti tisakhalenso olefuka. (Sal. 28:9; 94:18) Mmene timapindulila: Kudziŵa kuti Mulungu adzaticilikiza, kumatithandiza kukumbukila kuti ndife odalitsika m’njila ziŵili izi: Yoyamba, tili na malo othaŵilapo acitetezo, mosasamala kanthu za kumene tikhala. Yaciŵili, Atate wathu wacikondi wakumwamba amasamala kwambili za ife.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 1248
Ya
Liwu lakuti Ya limapezeka m’mawu otamanda, m’nyimbo, m’mapemphelo na m’mawu ocondelela. Nthawi zambili limapezeka pamene nkhani ikamba za kusangalala cifukwa copambana na kupulumutsidwa, kapena povomeleza kuti Mulungu ni wamphamvu. Pali zitsanzo zambili zoonetsa liwuli likugwilitsidwa nchito mu njila imeneyi. Mawu akuti, “Tamandani Ya, anthu inu!” (kapena kuti Haleluya) ni mawu otamanda Mulungu, ndipo m’Masalimo amapezeka koyamba pa Salimo 104:35. M’masalimo ena mawuwa angakhale kuciyambi cabe (Sal. 111; 112), nthawi zina mkati mwa salimo (135:3), nthawi zinanso kumapeto kokha (Sal. 104, 105, 115-117), koma kambili amakhala kuciyambi na kumapeto (Sal. 106, 113, 135, 146-150). M’buku la Chivumbulutso, zolengedwa za kumwamba zimaseŵenzetsa mawu amenewa mobwelezabweleza potamanda Mulungu.—Chiv. 19:1-6.
M’Malemba ena otsala, mawu akuti “Ya” amaseŵenzetsedwa m’nyimbo zoonetsa kukwezeka kwa Yehova komanso pomucondelela. Mwacitsanzo, pali nyimbo ya Mose yokamba za kupulumutsidwa. (Eks. 15:2) Pofuna kugogomeza, m’nyimbo zolembedwa na Yesaya maina onse aŵili anachulidwa nthawi imodzi kuti, “Ya Yehova.” (Yes. 12:2; 26:4) M’ndakatulo yacisangalalo imene Hezekiya analemba pambuyo pocilitsidwa mozizwitsa atatsala pang’ono kufa, anaonetsa kukhudzika mtima kwambili mwa kubweleza mawu akuti Ya. (Yes. 38:9, 11) M’Masalimo ena muli mawu oonetsa ciyamikilo cifukwa ca cipulumutso, kutetezedwa, komanso kuwongoleledwa.—Sal. 94:12; 118:5, 14.
JANUARY 20-26
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 138-139
Musalole Mantha Kukulepheletsani Kutengako Mbali pa Misonkhano
Tamandani Yehova Pakati pa Mpingo
10 Kodi mumakhuta befu cifukwa ca mantha nthawi iliyonse mukafuna kupeleka ndemanga pa misonkhano? Ngati n’conco, dziŵani kuti sindimwe mwekha. Ambili a ife timakhalako na mantha popeleka ndemanga pa misonkhano. Koma kuti mucepetse mantha amenewa, coyamba muyenela kuzindikila zimene zimakupangitsani kukhala na mantha. Kodi mumayopa cifukwa coganiza kuti mudzaiŵala zokamba popeleka ndemanga? Kapena mumayopa kuti mungapeleke ndemanga yolakwika? Kapenanso mumayopa cifukwa coganiza kuti ndemanga yanu siingakhale yabwino poyelekezela na ndemanga za ena? Mantha amenewa angakhale cizindikilo cakuti muli na khalidwe labwino. Angaonetse kuti ndimwe wodzicepetsa, komanso kuti mumaona ena kukhala okuposani. Ndipo Yehova amakonda anthu odzicepetsa. (Sal. 138:6; Afil. 2:3) Koma Yehova amafunanso kuti muzimutamanda, na kulimbikitsa abale na alongo pa misonkhano. (1 Ates. 5:11) Iye amakukondani, ndipo adzakuthandizani kukhala wolimba mtima kuti mukwanitse kupeleka ndemanga.
Tizilimbikitsana pa Misonkhano ya Mpingo
7 Mungapindule kwambili kuŵelenganso mfundo zothandiza m’magazini a Nsanja ya Mlonda aposacedwa. Mwacitsanzo, muzikonzekela bwino. (Miy. 21:5) Mukaimvetsa bwino nkhani imene mudzaphunzila, cidzakhala cosavuta kukapelekapo ndemanga pamsonkhano. Cina, mayankho anu azikhala aafupi. (Miy. 15:23; 17:27) Yankho lanu likakhala lalifupi simudzadodoma kwambili. Yankho lalifupi, mwina lokhala na ciganizo cimodzi kapena ziŵili, limakhala losavuta kwa abale na alongo kulimvetsa, kupambana yankho lamtatakuya lokhala na mfundo zambili. Mukapeleka ndemanga yaifupi m’mawu anu-anu, zidzaonetsa kuti munakonzekela bwino, komanso kuti munaimvetsa bwino nkhaniyo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 862 ¶4
Kukhululuka
Mkhristu ayenela kukhululukila ena akamulakwila mosasamala kanthu kuti amulakwila kangati. (Luka 17:3, 4; Aef. 4:32; Akol. 3:13) Mulungu sakhululukila anthu omwe sakhulukila anthu ena. (Mat. 6:14, 15) Komabe, ngakhale kuti ‘munthu woipa’ angacotsedwe mu mpingo wacikhristu cifukwa ca colakwa cacikulu, m’kupita kwa nthawi angakhululukidwe ngati waonetsa kuti ni wolapadi. Pa nthawi imeneyo onse mu mpingo angamutsimikizile kuti amamukonda. (1 Akor. 5:13; 2 Akor. 2:6-11) Koma ngakhale n’telo, si kuti Akhristu ayenela kukhululukila ocimwa osafuna kulapa amene amavutitsa anzawo ndi kucimwila dala. Amenewo amakhala adani a Mulungu.—Aheb. 10:26-31; Sal. 139:21, 22.
JANUARY 27–FEBRUARY 2
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 140-143
Muzicitapo Kanthu pa Zimene Mwapempha
“Mvela Mawu a Anthu Anzelu”
13 Tiziona uphungu kukhala cikondi ca Mulungu pa ife. Yehova amatifunila zabwino. (Miy. 4:20-22) Iye akatipatsa uphungu kupitila m’Mawu ake, m’zofalitsa zozikika pa Baibo, kapena Mkhristu wokhwima mwauzimu, ndiye kuti amatikonda. Iye “amatilanga kuti tipindule,” malinga n’kunena kwa Aheberi 12:9, 10.
14 Ikani maganizo pa uphunguwo osati mmene aupelekela. Nthawi zina, tingaone kuti uphungu umene tapatsidwa sunapelekedwe m’njila yabwino. N’zoona kuti aliyense wopeleka uphungu, ayenela kuupeleka m’njila yakuti zisakhale zovuta kuulandila. (Agal. 6:1) Koma ngati ndife tikupatsidwa uphungu, tingacite bwino kusumika maganizo pa phindu la uphunguwo, ngakhale pamene taona kuti sunapelekedwe m’njila yabwino. Tingadzifunse kuti: ‘Ngakhale kuti sin’nakonde mmene uphungu wapelekedwela, kodi pali cina cake cimene niphunzilapo pa uphunguwo? Kodi sininganyalanyaze zophophonya za wopeleka uphunguwo n’colinga cakuti nipindule nawo?’ N’cinthu canzelu kwa ife kuona mmene tingaseŵenzetsele uphunguwo kuti tipindule.—Miy. 15:31.
w10-CN 3/15 32 ¶4
Khalanibe ‘Oyera Mtima’ Masiku Ovuta Ano
Atumiki a Mulungu ena amavutika cifukwa ca kutsutsidwa, mavuto a zacuma ndiponso matenda akulu. Nthawi zina, zimenezi zimacititsa kuti azivutika mu mtima mwawo. Izi n’zimene zinacitikilanso Mfumu Davide. Iye anati: “Mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m’kati mwanga.” (Sal. 143:4) Kodi n’ciyani cinamuthandiza kupilila pa nthawi yovuta imeneyi? Davide anakumbukila zimene Mulungu anacitila atumiki Ake ndiponso mmene anamupulumutsila iyeyo. Anaganizila zimene Yehova anali atacita cifukwa cha dzina Lake lalikulu. Davide ankaganizila kwambili nchito za Mulungu. (Sal. 143:5) Ifenso, tikamaganizila za Mlengi wathu, zimene anaticitila ndiponso zimene akuticitila, tidzatha kupilila tikamayesedwa.
Kodi Kukwatiwa “Mwa Ambuye” N’kofunikabe?
Nthawi zina mungamve monga mmene wamasalimo anamvela pamene anati: “Fulumilani, ndiyankheni inu Yehova. Mphamvu zanga zatha. Musandibisile nkhope yanu.” (Sal. 143:5-7, 10) Pa nthawi ngati zimenezo, mungafunike kuyembekezela Atate wanu wakumwamba kuti akuonetseni cimene cili cifunilo cake kwa inu. Mungacite zimenezi mwa kupeza nthawi yoŵelenga Mau ake ndi kusinkhasinkha pa zimene mukuŵelenga. Mudzamvetsa malamulo ake ndi kuona mmene anacitila zinthu ndi anthu ake akale. Mwa kutelo, cikhulupililo canu cidzakhala colimba mwa Mulungu.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2-E 1151
Poizoni
Mophiphilitsa. Mawu a anthu oipa, abodza, komanso onenela anthu ena zoipa, ali ngati poizoni wakupha wa njoka, cifukwa amawononga mbili ya wonenezedwayo. (Sal. 58:3, 4) Ponena za anthu onenela anzawo zoipa, Baibo imati, “Pansi pa milomo yao pali ululu wa mphili” (kapena kuti “kumbuyo kwa milomo yawo”). N’cimodzimodzi na njoka. Kaciwalo kotulutsa poizoni kali kumbuyo kwa mlomo na mano ake a cibwano ca m’mwamba. (Sal. 140:3, BL; Aroma 3:13, BL) Lilime la munthu likagwilitsidwa nchito kunena misece, kunenela ena zoipa, kuphunzitsa mabodza kapena kukamba mawu ena ovulaza, limakhala “lodzaza ndi poizoni wakupha.”—Yak. 3:8.
FEBRUARY 3-9
CUMA COPEZEA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 144-146
“Osangalala Ndi Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova!”
Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga
2. Kamasulidwe katsopanoka n’kogwilizana bwino na mavesi ena a m’salimoyi. Cifukwa coseŵenzetsa liu lakuti “ndiyeno” pa vesi 12, tsopano madalitso ochulidwa m’mavesi 12 mpaka 14 amamveka kuti ni opita kwa olungama, amene anapempha kuti ‘amasulidwe ndi kulanditsidwa m’manja mwa anthu’ oipa (vesi 11). Kusintha kumeneku kukuonekelanso mu vesi 15. Mau a mu vesi imeneyi tsopano amamveka ogwilizana bwino. Tikutelo cifukwa lomba mau onse aŵili akuti “odala” m’vesiyi amamveka kuti akamba za anthu amodzi-modzi, “anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” Komanso, tiyenela kukumbukila kuti mavesi a Ciheberi oyambilila analibe zizindikilo za m’kalembedwe, monga mitengelo (koteshoni). Conco, omasulila amafunika kumvetsetsa tanthauzo lolondola la mauwo. Kuti atelo amafunika kuganizila kalembedwe ka Ciheberi, mavesi apambuyo ndi patsogolo, na malemba ena ogwilizana ndi nkhaniyo.
3. Kamasulidwe katsopanoka kamagwilizana ndi malemba ena a m’Baibo amene amakamba kuti Mulungu adzadalitsa anthu okhulupilika. Cifukwa ca kusintha kwa kamasulidwe ka liu lakuti asher, Salimo 144 lomba imaonetsa bwino ciyembekezo cimene Davide anali naco. Ciyembekezo cakuti Mulungu akadzapulumutsa Aisiraeli kwa adani awo, adzawadalitsa mwa kuwapatsa umoyo wacimwemwe ndi waulemelelo. (Lev. 26:9, 10; Deut. 7:13; Sal. 128:1-6) Mwacitsanzo, Deuteronomo 28:4 imati: “Cidzadalitsika cipatso ca mimba yako, cipatso ca m’dziko lanu, cipatso ca ziŵeto zako, ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.” Mogwilizana na mau amenewa, mu ulamulilo wa Solomo, mwana wa Davide, mtundu wa Aisiraeli unali pa mtendele na ulemelelo wosaneneka. Koposa pamenepo, zimene zinacitika mu ulamulilo wa Solomo zimacitila cithunzi mmene zinthu zidzakhalila mu ulamulilo wa Mesiya.—1 Maf. 4:20, 21; Sal. 72:1-20.
Pitilizani Kulimbitsa Ciyembekezo Canu
16 Ciyembekezo cathu codzakhala na moyo kwamuyaya, ni mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Mulungu. Tiyembekezela mwacidwi tsogolo labwino limeneli, limene ndife otsimikiza kuti lidzabweladi. Ciyembekezoci cili monga nangula. Cimatithandiza kuti tisasunthike polimbana na mayeso, pozunzidwa, ngakhale poyang’anizana na imfa. Cilinso ngati cisoti colimba cimene cimateteza maganizo athu kuti tikanize zosayenela na kumamatila ku zabwino. Ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo cimeneci, cimatiyandikilitsa kwa Mulungu, komanso cimaonetsa kukula kwa cikondi cathu pa iye. Timapindula kwambili tikamasunga ciyembekezo cathu cili colimba..
17 “M’kalata yake yopita kwa Aroma, mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti: “Kondwelani ndi ciyembekezoco.” (Aroma 12:12) Paulo anakondwela na ciyembekezoci cifukwa anali wotsimikiza kuti akakhalabe wokhulupilika, adzakhala na moyo kwamuyaya kumwamba. Nafenso tingakondwele na ciyembekezo cathu cifukwa sitikayikila kuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake. Wamasalimo analemba kuti: “Wodala ndi munthu . . . amene ciyembekezo cake cili mwa Yehova Mulungu wake;. . . Wosunga coonadi mpaka kalekale.”—Sal. 146:5, 6.
N’cikondi Cotani Cimene Cimabweletsa Cimwemwe Ceni-ceni?
19 Dziko la Satanali lacititsa kuti anthu avutike kwa zaka zoposa 6,000, koma posacedwapa lidzawonongedwa. Tsopano m’dzikoli muli anthu ambili odzikonda, okonda ndalama, na zosangalatsa. Anthu amenewa ni adyela, ndipo amangofuna kukhutilitsa zokhumba zawo. Anthu aconco sakhala na cimwemwe ceni-ceni. Mosiyana na zimenezi, wamasalimo anati: “Wodala [wosangalala] ndi munthu amene thandizo lake limacokela kwa Mulungu wa Yakobo, amene ciyembekezo cake cili mwa Yehova Mulungu wake.”—Sal. 146:5.
20 Cikondi pa Mulungu cikukulila-kulila pakati pa anthu ake. Ndipo caka ciliconse, anthu ambili amabwela m’gulu lathu. Umenewu ni umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila, ndipo posacedwa udzabweletsa madalitso osaneneka pa dzikoli. Munthu amapeza cimwemwe ceni-ceni komanso cokhalitsa ngati acita cifunilo ca Mulungu, na kudziŵa kuti akukondweletsa Yehova. Ndipo anthu amene amakonda Yehova adzakhala osangalala kwamuyaya.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 111 ¶9
Nyama
Baibo imatiphunzitsa mobweleza-bweleza kuti tiyenela kukhala acifundo komanso okoma mtima pocita zinthu ndi nyama. Kunena zoona, Yehova waonetsa kuti ndi Wosamalila Wacikondi wa moyo wa nyama. (Miy. 12:10; Sal. 145:15, 16) M’Cilamulo ca Mose, Aisiraeli analamulidwa kuti nyama zoweta azizisamalila bwino. Nyama ikasocela, anafunika kuibweza kwa mwiniwake. Ngati munthu wapeza nyama yolemedwa na katundu, anayenela kumasula katunduyo. (Eks. 23:4, 5) Nyama anayenela kuzigwilitsa nchito mwacifundo. (Deut. 22:10; 25:4) Monga zinalili kwa munthu, nazonso nyama zinayenela kupumula pa Sabata. (Eks. 20:10; 23:12; Deut. 5:14) Nyama zolusa anafunika kuziyang’anila kapena kuzipha. (Gen. 9:5; Eks. 21:28, 29) Kukwelanitsa nyama za mitundu yosiyana kunali koletsedwa.—Lev. 19:19.
FEBRUARY 10-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 147-150
Tili na Zifukwa Zambili Zotamandila Ya
N’cifukwa Ciani Tifunika Kutamanda Yehova?
5 Yehova sanatonthoze cabe Aisiraeli monga mtundu, koma anatonthozanso Mwiisiraeli aliyense payekha. Ni mmenenso amacitila masiku ano. Ponena za Mulungu, wamasalimo analemba kuti: “Iye amacilitsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Sal. 147:3) Ndithudi, Yehova amasamalila anthu amene akumana ndi mavuto. Amawathandiza mwakuthupi ndi kuwalimbikitsa. Tikakhala na nkhawa, Yehova ni wokonzeka kutitonthoza ndi kutitsitsimula. (Sal. 34:18; Yes. 57:15) Iye amatipatsa nzelu ndi mphamvu zotithandiza kupilila mavuto aliwonse amene tingakumane nawo.—Yak. 1:5.
6 Pambuyo pake, wamasalimo anayamba kukamba za kumwamba. Iye anakamba kuti Yehova “amawelenga nyenyezi zonse, ndipo zonsezo amazichula mayina ake.” (Sal. 147:4) N’cifukwa ciani iye anayamba kukamba za nyenyezi zakumwamba? Ganizilani izi: Panthawiyo wamasalimo anali kuziona nyenyezi, koma sanali kudziŵa kuti zilipo zingati. Masiku ano, anthu amakwanitsa kuona nyenyezi zambili-mbili kuposa kale. Anthu ena amakamba kuti mumlalang’amba wathu, wochedwa Milky Way, muli nyenyezi mabiliyoni ambili. Ndipo cioneka kuti mumlengalenga muli milalang’amba mathililiyoni ambili. Zoonadi, kwa ise anthu, nyenyezi n’zosaŵelengeka. Koma Mlengi amachula nyenyezi iliyonse ndi dzina lake. Izi zitanthauza kuti Yehova amaona nyenyezi iliyonse kukhala yapadela. (1 Akor. 15:41) Nanga kodi iye amawaona bwanji anthu padziko lapansi? Popeza kuti nthawi zonse Mulungu amatha kudziŵa pamene nyenyezi iliyonse ili, inunso amakudziŵani bwino panokha. Amadziŵa bwino-bwino pamene muli, mmene mumvelela, ndi zimene mufunikila panthawi iliyonse!
N’cifukwa Ciani Tifunika Kutamanda Yehova?
7 Yehova amakukondani inu panokha, komanso ali na cifundo ndi mphamvu moti angathe kukuthandizani pa mavuto anu. (Ŵelengani Salimo 147:5.) Nthawi zina, mungaone kuti mavuto amene mwakumana nawo ni aakulu kwambili cakuti simungakwanitse kuwapilila. Mulungu amadziŵa kufooka kwathu; “amakumbukila kuti ndife fumbi.” (Sal. 103:14) Cifukwa copanda ungwilo, tingacite colakwa mobweleza-bweleza. Cimatiŵaŵa kwambili tikakamba mau oipa cifukwa cokangiwa kulamulila lilime lathu. Cimatiŵaŵanso tikagonja ku zizoloŵezi zoipa zathupi, kapenanso tikalephela kuthetsa nsanje. Koma Yehova salakwitsa ciliconse. Ngakhale n’conco, iye amatidziŵa bwino ndipo amatimvetsetsa kwambili.—Yes. 40:28.
N’cifukwa Ciani Tifunika Kutamanda Yehova?
18 Wamasalimo anadziŵa kuti Mulungu anali kuwakonda anthu ake a m’nthawi yakale. Iwo anali mtundu wokhawo umene Mulungu anaupatsa ‘mau ake, malangizo ake ndi zigamulo zake.’ (Ŵelengani Salimo 147:19, 20.) Ifenso ndife odala masiku ano cifukwa ndise cabe amene timadziŵika na dzina la Mulungu. Tili pa ubale wabwino na Yehova cifukwa tinamudziŵa ndipo timatsatila Mau ake pa umoyo wathu. Molingana ndi wolemba Salimo 147, kodi si zoona kuti tili na zifukwa zambili zofuulila kuti “Tamandani Ya!” ndi kulimbikitsakonso ena kucita zimenezi?
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 316
Mbalame
Wamasalimo anati “mbalame zamapiko” zitamande Yehova. (Sal. 148:1, 10) Ndipo mbalame zimatamandadi Yehova cifukwa ca mmene matupi awo alili komanso cifukwa zinapangidwa mogometsa. Mwacitsanzo, mbalame imodzi ingakhale na nthenga 1,000 mpaka 20,000 kapena kuposelapo. Nthenga iliyonse imakhala na thunthu lokhala na nthambi zambilimbili zolowanalowana. Nthambi iliyonse imakhala na tunthambi twina twambili tung’ono-tung’ono, ndipo natonso tumakhala na tunthambi twake tung’ono-tung’ono kwambili komanso twina tumene tumakola tunzake. Nthenga imodzi cabe ya masentimita 15 ya phiko la njiŵa ili na tunthambi masauzande ambilimbili ndipo tunthambito tuli na tunthambi twake mamiliyoni. Mapiko a mbalame komanso matupi awo anapangidwa mogometsa komanso mwaluso kwambili kuposa ndeke za masiku ano. Popeza mafupa a mbalame amakhala na mphako, mbalamezo zimakhala zopepuka. Conco, mafupa a mbalame ya ku nyanja yochedwa frigate amalemela magilamu 110 cabe ngakhale kuti mapiko ake ni aatali kufika mamita aŵili. Mafupa a m’mapiko a mbalame zina amakhala na tunthu toyacilikiza mumphako.
FEBRUARY 17-23
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 1
Inu Acinyamata, Kodi Mudzamvela Ndani?
Acicepele—Musalole Ciliconse Kukumanitsani Mphoto
16 Nanga bwanji ngati ndinu wacicepele, ndipo muona kuti makolo anu acikhristu sakumvetsetsani kapena sakupatsani ufulu wokwanila? Mwina mungakhumudwe n’kuyamba kuona ngati kutumikila Yehova n’kosakondweletsa. Koma mukaleka kutumikila Yehova cifukwa cokhumudwa, posakhalitsa mudzadzionela mwekha kuti palibe wina aliyense amene amakukondani zeni-zeni, mofanana na makolo anu acikhristu kapena abale na alongo mu mpingo.
17 Mwacionekele, na imwe mudziŵa kuti ngati makolo anu amakupatsani malangizo, ndiye kuti amakukondani. (Aheb. 12:8) Koma mwina simukondwela na mmene amakupatsilani malangizowo. M’malo mokhumudwa na kapelekedwe ka malangizo, yesetsani kuganizila cifukwa cimene amapelekela malangizo mwanjila imeneyo. Conco, muzikhala wodekha ndi kupewa kukhumudwa akakupatsani uphungu. Mau a Mulungu amati: “Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziŵa zinthu, ndipo munthu wozindikila amakhala wofatsa.” (Miy. 17:27) Phunzilani kucita zinthu mwaucikulile. Muzilandila uphungu moleza mtima, na kuuseŵenzetsa popanda kudandaula na mmene wapelekedwela. (Miy. 1:8) Kukhala na makolo amene amakonda Yehova na mtima wonse ni dalitso. Iwo amafuna kukuthandizani kuti mukalandile mphoto ya moyo.
w05-CN 2/15 19-20 ¶11-12
Kuteteza Dzina Lathu Monga Akristu
11 Kondweretsani Mulungu, osati anthu. N’zacibadwa kufuna kudziŵika kuti tili m’gulu linalake. Aliyense amafuna kukhala ndi anzake, ndipo timamva bwino kukhala pagulu la anzathu. Ana akamafika pamsinkhu wacinyamata ndiponso akakula ndithu, angatengeke kwambili ndi zocita za anzawo. Izi zingakulitse mtima wofunitsitsa kutsanzila ena kapena kuwasangalatsa. Komatu dziŵani kuti anzathu ndiponso anthu amsinkhu wathu sikuti nthawi zonse amatifunila zabwino ayi. Nthawi zina amangofuna wina woti azicita naye limodzi zoipazo. (Miyambo 1:11-19) Mkhristu akagonjela anzake amene akum’kakamiza kucita zoipa, nthawi zambili amayesetsa kudzibisa kuti ndi Mkhristu. (Salmo 26:4) Mtumwi Paulo anacenjeza kuti: “Musatengele khalidwe la dzikoli.” (Aroma 12:2, The Jerusalem Bible) Yehova amatithandiza kukhala olimba kuti tisatengeke ndi zochita za ena.—Ahebri 13:6.
12 Ngati tikutengeka ndi zochita za anthu, zomwe zingaipitse dzina lathu monga Akhristu, ndi bwino kukumbukila kuti kukhala wokhulupilika kwa Mulungu n’kofunika kwambili kuposa maganizo a anthu kapena zocita za anthu oculuka. Mfundo yabwino kwambili pankhaniyi ikupezeka pa lemba la Eksodo 23:2 lomwe limati: “Usatsata unyinji wa anthu kucita coipa.” Aisrayeli oculuka atakayikila kuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo Ake, molimba mtima Kalebi anakana kuyendela maganizo a anzakewo. Iye anali wotsimikiza kuti malonjezo a Mulungu ndi odalilika, ndipo anapindula kwambili cifukwa ca kulimba mtima kwakeko. (Numeri 13:30; Yoswa 14:6-11) Kodi nanunso ndinu wotsimikiza mofananamo kukanitsitsa kuyendela maganizo amene anthu ambili akutsatira, pofuna kuti muteteze ubwenzi wanu ndi Mulungu?
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 846
Wopusa
M’Baibo, mawu akuti “wopusa” satanthauza munthu amene nzelu zake n’zopeleŵela. M’malo mwake, nthawi zambili amakamba za munthu amene amakana nzelu ndipo amakhala umoyo wosatsatila mfundo zolungama za Mulungu.
FEBRUARY 24–MARCH 2
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 2
N’cifukwa Ciyani Muyenela Kuyikilapo Mtima pa Phunzilo la Inu Mwini?
“Yendanibe M’coonadi”
16 Si tonse amene timakonda kuŵelenga na kuphunzila. Koma Yehova akutipempha kuti ‘tizifuna-funa’ coonadi na ‘kucifufuza’ kuti ticimvetsetse. (Ŵelengani Miyambo 2:4-6.) Tikamayesetsa mwakhama, tidzapindula. Ponena za kuŵelenga Baibo payekha, m’bale Corey anakamba kuti amafufuza vesi iliyonse payokha. Iye anati: “Nimaŵelenga mawu a m’munsi, mavesi ena ofotokoza mfundo yofanana na ya vesiyo, ndiponso kufufuza m’mabuku ena. . . . Nimadziŵa zambili cifukwa coŵelenga mwa njila imeneyi.” Kaya timagwilitsa nchito njila imeneyi kapena ina, timaonetsa kuti timayamikila coonadi pothelapo nthawi yociphunzila, komanso kuikilapo mtima.—Sal. 1:1-3.
Nzelu Yeniyeni Imafuula
3 Nzelu ni luso logwilitsa nchito zimene timadziŵa kuti tipange zisankho zabwino. Koma nzelu yeniyeni imaloŵetsamo zambili. Baibo imati: “Kuopa Yehova ndiko ciyambi ca nzelu. Kudziŵa Woyela Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.” (Miy. 9:10) Conco, tikafuna kupanga cisankho cacikulu, coyamba tiyenela kudziŵa maganizo a Yehova pa cisankhoco. Tingacite zimenezi mwa kufufuza m’Baibo, na m’zofalitsa zozikika pa Baibo. Tikatelo, tidzaonetsa kuti tili na nzelu yeniyeni.—Miy. 2:5-7.
4 Ni Yehova yekha amene angatipatse nzelu zenizeni. (Aroma 16:27) N’cifukwa ciyani Yehova ndiye Gwelo la nzelu? Coyamba, pokhala Mlengi wathu, iye amadziŵa zonse zokhudza cilengedwe cake. (Sal. 104:24) Caciŵili, zocita zonse za Yehova zimaonetsa nzelu. (Aroma 11:33) Cacitatu, uphungu wanzelu wa Yehova nthawi zonse umapindulila awo amene amaugwilitsa nchito. (Miy. 2:10-12) Conco, kuti tipeze nzelu zenizeni, tiyenela kuvomeleza mfundo za coonadi zimenezi, na kulola kuti zizititsogolela popanga zisankho, komanso pa zocita zathu.
Wacicepele, Limbitsa Cikhulupililo Cako
2 Monga mtumiki wacicepele wa Yehova, kapena wophunzila za iye, tidziŵa kuti iwe umakhulupilila mwa Mlengi. Koma kodi nthawi zina, umakhumbila zimene anzako ambili amakhulupilila, monga ciphunzitso ca cisanduliko? Ngati inde, pali masitepu amene angakuthandize kulimbilitsa cikhulupililo cako. Sitepu yoyamba ni kuseŵenzetsa luso la kulingalila limene Mulungu anakupatsa. Luso limenelo ‘lidzakuyang’anila’ na kukucinjiliza ku ziphunzitso zimene zingawononge cikhulupililo cako.—Ŵelengani Miyambo 2:10-12.
3 Cikhulupililo ceni-ceni cimacokela pa kum’dziŵa bwino Mulungu. (1 Tim. 2:4) Conco, pamene uphunzila Mau a Mulungu na zofalitsa zathu, osangoŵelenga mwacisawawa yayi. Uziseŵenzetsa luso lako la kulingalila kuti ‘uzindikile tanthauzo’ la zimene uŵelenga. (Mat. 13:23) M’nkhani ino, tidzaona mmene kucita zimenezi kungakuthandizile kulimbitsa cikhululupililo cako mwa Mulungu Mlengi, na m’Mau ake Baibulo. Ndipo pali maumboni ambili otsimikizilika okhudza nkhani zimenezi.—Aheb. 11:1.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 1211 ¶4
Kukhulupilika
N’zotheka kukhala wokhulupilika, osati mwa mphamvu za munthu, koma mwa kukhala na cikhulupililo colimba komanso kudalila Yehova na mphamvu zake zopulumutsa. (Sal. 25:21) Mulungu analonjeza kuti adzakhala “cishango” komanso “malo acitetezo” kwa anthu okhulupilika. (Miy. 2:6-8; 10:29; Sal. 41:12) Popeza anthu amenewa nthawi zonse amafuna kuti Yehova awayanje, umoyo wawo umakhala wosatekeseka, ndipo amatha kuyenda pa njila yowongoka mpaka atakwanilitsa colinga cawo. (Sal. 26:1-3; Miy. 11:5; 28:18) Yobu anazindikila kuti ngakhale kuti anthu opanda colakwa amavutika anthu oipa akayamba kulamulila ndipo angafe limodzi na oipawo, Yehova amatitsimikizila kuti Iye amaona umoyo wa munthu wopanda colakwa, komanso kuti colowa ca munthu woteloyo cidzakhalapobe, tsogolo lake lidzakhala la mtendele, ndiponso adzalandila zinthu zabwino. (Yobu 9:20-22; Sal. 37:18, 19, 37; 84:11; Miy. 28:10) Monga zinalili kwa Yobu, kukhala munthu wamtengo wapatali komanso wolemekezeka, sikudalila cuma cimene munthu ali naco, koma kumadalila pa kukhulupilika kwake. (Miy. 19:1; 28:6) Ana a kholo lotelo amakhala osangalala (Miy. 20:7), ndipo citsanzo ca bambo wawo cimakhala colowa cawo camtengo wapatali. Amasangalala na mbili ya bambo wawo komanso ulemu umene anadzipezela.