MBILI YANGA
Pa Zonse Zimene Nimasankha, Nimaika Yehova Patsogolo
TSIKU lina kutaca m’mawa kadzuŵa katawala bwino mu 1984, n’nali kupita ku nchito kucokela m’dela lotukuka limene n’nali kukhala, m’tauni ya Caracas ku Venezuela. Nili m’njila, n’nali kuganizila nkhani imene inali itangotuluka kumene m’magazini a Nsanja ya Mlonda. Inali kukamba za mmene anthu oyandikana nawo nyumba amationela. N’tayang’ana nyumba zapafupi, n’nadzifunsa kuti: ‘Kodi anthu oyandikana nawo nyumba amangoniona kuti ndine woseŵenza ku banki wocita bwino? Kapena amaniona kuti ndine mtumiki wa Mulungu amene amasamalila banja lake mwa kuseŵenza ku banki?’ Popeza sin’nali kufuna kuti anthu aziniona kuti ndine munthu cabe woseŵenza ku banki wandalama, n’natenga masitepu ofunikila kuti nicitepo kanthu.
N’nabadwa pa May 19, 1940, m’tauni ya Amioûn ku Lebanon. Patapita zaka zingapo, banja lathu linakukila mu mzinda wa Tripoli, kumene ine n’naleledwela mwacikondi m’banja lacimwemwe limene linali kudziŵa Yehova Mulungu na kum’konda. Ine ndiye n’nali wamng’ono kwambili pa ana asanu, atsikana atatu na anyamata aŵili. Makolo anga sanali kukonda zinthu zakuthupi. Pabanja pathu tinali kukonda kwambili kuphunzila Baibo, kupezeka ku misonkhano yacikhristu, na kuthandiza ena kudziŵa Mulungu.
Mu mpingo mwathu munali Akhristu ambili odzozedwa. Mmodzi wa iwo anali m’bale Michel Aboud, amene anali kutsogoza msonkhano umene kale tinali kuuchula kuti Phunzilo la Buku la Mpingo. M’baleyo anaphunzilila coonadi ku mzinda wa New York, ndipo ndiye anayambitsa coonadi ku Lebanon mu 1921. Nikumbukila bwino kuti m’baleyo anawathandiza kwambili alongo acitsikana aŵili, Anne na Gwen Beavor amene analoŵa Sukulu ya Giliyadi, ndipo anali kuwalemekeza kwambili. Alongowo anali mabwenzi athu abwino. Pambuyo pa zaka zambili, n’nakondwela kukumananso na mlongo Anne ku America. Patapita nthawi, n’nakumana na mlongo Gwen amene anali atakwatilana na m’bale Wilfred Gooch, ndipo anali kutumikila pa Beteli mu mzinda wa London, ku England.
KULALIKILA KU LEBANON
Pamene n’nali mnyamata Mboni zinali zocepa ku Lebanon. Koma tinali kuphunzitsa ena mokangalika zimene tinali kudziŵa za m’Baibo. Tinali kucita zimenezo ngakhale kuti atsogoleli ena acipembedzo anali kutitsutsa. Pali zocitika zina zimene nimakumbukila kwambili.
Tsiku lina, ine na mlongo wanga Sana tinali kulalikila uthenga wa m’Baibo m’nyumba ya nsanjika. Ndiyeno wansembe wina anabwela pa nsanjika pamene tinali kulalikila kwa anthu. Cioneka kuti wina anacita kumuitana. Wansembeyo anayamba kutukwana mlongo wanga. Iye anayamba kucita nkhanza, ndipo anakankhila Sana pansi pa nyumba ya nsanjika na kumuvulaza. Munthu wina anatumila foni apolisi, amene anabwela na kuonetsetsa kuti Sana wasamalidwa bwino. Apolisiwo anatenga wansembe uja n’kupita naye ku polisi. Kumeneko anapeza kuti iye anali na mfuti. Mkulu wa apolisi anamufunsa kuti: “Iwe! Kodi ndiwe ndani? Ndiwe mtsogoleli wacipembedzo kapena mtsogoleli wa anthu ocita zaciwawa?”
Cocitika cina cimene nikumbukila bwino, ni pamene mpingo wathu unacita lendi basi kuti izitipeleka ku tauni ina ya kutali kumene tinali kulalikilako uthenga wabwino. Tinali kusangalala na utumiki wathu, mpaka pamene wansembe kumeneko anamvela zimene tinali kucita. Ndipo anasonkhanitsa cigulu ca anthu kuti aticite zacipongwe. Anatiwopseza. Anafika ngakhale potitema miyala. Ndipo atate anavulazidwa. Nikumbukila kuti atate magazi anali cu! cu! cu! kumaso. Iwo na amayi anabwelela kumene kunali basi, ndipo ena tonse tinaŵatsatila apo mitima ili pha! pha! pha! na mantha. Komabe, sinidzaiŵala mawu amene amayi anakamba pamene anali kutsuka zilonda za atate. Anati: “Yehova, conde akhululukileni. Sadziŵa zimene akucita.”
Pa nthawi ina tinapita ku tauni ya kwathu kukacezela acibale. Kumeneko tinapeza bishupu, mtsogoleli wacipembedzo, ku nyumba kwa ambuya amuna. Iye anali kudziŵa kuti makolo anga ni a Mboni za Yehova. Ngakhale kuti n’nali na zaka 6 cabe, bishopuyo anayesa kunicititsa manyazi mwa kunifunsa kuti: “Iwe! N’cifukwa ciani ukalibe kubatizika?” Ine poyankha n’nakamba kuti n’nali n’kali wamng’ono, ndipo kuti nibatizike n’nafunika kudziŵa zambili za Baibo, komanso kukhala na cikhulupililo colimba. Posakondwela na yankho yanga, iye anauza ambuya kuti n’nalibe ulemu.
Koma zocitika zoipa zimenezi sizinali zambili. Kwakukulu anthu a ku Lebanon ni aubwenzi ndiponso oceleza. Conco, tinali kukhala na makambilano ambili okondweletsa, ndipo tinali kutsogoza maphunzilo a Baibo oculuka.
TINASANKHA KUSAMUKILA KU DZIKO LINA
Nikali pa sukulu, m’bale wacinyamata wa ku Venezuela anabwela kudzaceza ku Lebanon. Iye anali kusonkhana mu mpingo mwathu, ndipo anakhala pa cibwenzi na mlongosi wanga dzina lake Wafa. M’kupita kwa nthawi anakwatilana, ndipo anapita kukakhala ku Venezuela. M’makalata ake, Wafa anali kulimbikitsa atate kuti asamutsile banja lonse ku Venezuela. Anali kucita zimenezi cifukwa anali kutiyewa ngako. Pamapeto pake anakwanilitsa colinga cake cotisamutsila kumeneko!
Tinafika ku Venezuela mu 1953, ndipo tinayamba kukhala mu mzinda wa Caracas pafupi na nyumba ya a pulezidenti. Pokhala wacicepele, n’nali kukondwela kuona a pulezidenti akudutsa m’motoka yawo yodula. Koma sicinali copepuka kwa makolo anga kuzoloŵela kukhala ku dziko latsopano, kuphunzila cinenelo catsopano, kuzoloŵela cikhalidwe, zakudya, komanso nyengo. Koma atangoyamba kuzoloŵela umoyo wa kumeneko, tsoka lina lake lalikulu linatigwela.
kucoka kumanzele kupita kulamanja: Atate. Amayi. Ine na banja lathu mu 1953 pamene tinasamukila ku Venezuela
TSOKA LALIKULU LINATIGWELA
Atate anayamba kudwala. Izi zinatidabwitsa cifukwa anali olimba, komanso athanzi labwino. Sitinali kukumbukila na nthawi imene anadwalapo. Atawapima, anawapeza na khansa ya kukalambalala. Cacisoni n’cakuti anamwalila patangopita wiki imodzi.
N’zovuta kufotokoza cisoni cimene tinali naco pa nthawiyo, malinganso na mmene zinthu zinalili kwa ife. Pa nthawiyo n’nali cabe na zaka 13. Sitinayembekezele kuti atate angatisiye. Ndipo tinaona monga kuti dziko latha. Kwa nthawi yaitali, cinali covuta kwa amayi kuvomeleza kuti amuna awo anamwaliladi. Komabe, tinazindikila kuti umoyo unafunika kupitilizabe. Ndipo na thandizo la Yehova tinakwanitsa kupilila. N’natsiliza maphunzilo a ku sekondale ku Caracas nili na zaka 16, ndipo n’nali kufunitsitsa kuthandiza banja lathu.
Mlongo wanga Sana na mwamuna wake, Rubén, ananithandiza kwambili kupita patsogolo kuuzimu
Pa nthawiyo, mlongosi wanga Sana anali atakwatilana na m’bale Rubén Araujo, amene anali atatsiliza Sukulu ya Giliyadi, ndipo anali atabwelela ku Venezuela. Iwo anasankha kusamukila ku New York. Banja lathu litalinganiza zakuti nikacite maphunzilo a ku yunivesiti, n’napita ku New York kumene n’nakakhala na mlongosi wanga na amulamu anga pamene n’nali kucita maphunzilowo. Pamene n’nali kukhala nawo, ananithandiza kwambili kupita patsogolo kuuzimu. Kuwonjezela apo, mu mpingo wathu wa Spanish ku Brooklyn munali abale ambili okhwima kuuzimu. Aŵili mwa abale amene n’nakondwela kuŵadziŵa anali m’bale Milton Henschel na Frederick Franz, ndipo onsewo anali kutumikila pa Beteli ya Brooklyn.
Pa ubatizo wanga mu 1957
Nili pafupi kutsiliza caka coyamba ca maphunzilo pa yunivesiti ya ku New York, n’nayamba kuganizila mmene nidzaseŵenzetsela moyo wanga. N’nali n’taŵelenga na kuganizila mozama nkhani za m’magazini a Nsanja ya Mlonda, zolimbikitsa Akhristu kukhala na zolinga zauzimu potumikila Yehova. N’naona cimwemwe cimene apainiya na atumiki a pa Beteli a mu mpingo mwathu anali naco, ndipo n’nali kulaka-laka kukhala monga iwo. Komabe, pa nthawiyo n’nali Mkhristu wosabatizika. Posapita nthawi n’naona kufunika kopatulila moyo wanga kwa Yehova. N’natelo, ndipo n’natenga masitepu ofunikila, cakuti n’nabatizika pa March 30, 1957.
ZOSANKHA ZOFUNIKA
N’tapanga cisankho cofunika cimeneco, n’naganiza zopanganso cosankha cina. Cisankhoco cinali coyamba utumiki wanthawi zonse. N’nali kufunitsitsa kukhala mpainiya. Koma n’naona kuti kupanga cosankha cimeneci kudzakhala kovuta kwa ine. N’nali kudzifunsa kuti, ‘Nidzakwanitsa bwanji kucita upainiya na maphunzilo a ku yunivesiti?’ N’nali kulembela makalata ku Venezuela, kufotokozela amayi na azikulu anga za cisankho canga coleka maphunzilo a ku yunivesiti, na kubwelela ku Venezuela kukakhala mpainiya.
N’nabwelela ku Caracas mu June 1957. Komabe, n’nali kuona kuti zinthu sizinali bwino m’banja mwathu. Linali kufunikila munthu wina wowapezela zofunikila. Kodi n’kanacita ciani kuti nithandize? N’napatsidwa mwayi wogwila nchito ku banki, koma n’nali kufunitsitsanso kucita upainiya. Ndipo ndiye cifukwa cimene n’nabwelela ku Venezuela. N’natsimikiza mtima kucita zonse ziŵili. Kwa zaka zingapo, n’nali kugwila nchito masiku onse ku banki, ndipo n’nali kutumikilanso monga mpainiya. N’nali kukhala wotangwanika kwambili. Koma pa nthawi imodzi-modzi n’nalinso kukhala wokondwela kwambili!
Cimwemwe canga cinawonjezeka n’takwatilana na Sylvia mlongo wokongola wa ku German amene anali kukonda kwambili Yehova. Iye anali atasamukila ku Venezuela na makolo ake. M’kupita kwa nthawi tinakhala na ana aŵili, mwana wathu wamwamuna Michel (Mike), na mwana wathu wamkazi Samira. N’natenganso udindo wosamalila amayi, ndipo tinayamba kukhala nawo. Olo kuti n’nafunika kuleka upainiya kuti nizisamalila maudindo a banja, n’nakhalabe na mzimu wa upainiya. Ine na Sylvia tinali kucitako upainiya wothandiza tikakhala pa chuti.
CISANKHO CINA CACIKULU
Ana athu anali akali pa sukulu pa nthawi ya cocitika cimene nafotokoza kuciyambi kwa nkhani ino. N’nali wocita bwino mwakuthupi, ndipo anthu ena oseŵenza ku banki anali kunilemekeza. Ngakhale n’telo, kweni-kweni n’nali kufuna kuti nizidziŵika kuti ndine mtumiki wa Yehova. N’napitiliza kuganizila zimenezo. Conco, ine na mkazi wanga tinakhala pansi kukambilana za cuma cathu. N’kanaleka kugwila nchito ku banki akananipatsa ciwongola dzanja cacikulu. Popeza tinalibe nkhongole, tinaona kuti ngati tingakhale na umoyo wosalila zambili, tingakhale na ndalama zokwanila zoseŵenzetsa kwa nthawi yaitali.
Sicinali copepuka kupanga cosankha cimeneco. Koma mkazi wanga wokondeka na amayi ananicilikiza kwambili. Apanso, n’nakhala na mwayi woyambanso upainiya wanthawi zonse. N’nakondwela kwambili. N’nali wokonzeka kuyamba upainiya! Koma posapita nthawi tinalandila uthenga umene sitinauyembekezele.
MLENDO WOSAYEMBEKEZELA!
Mwana wathu wacitatu Gabriel, anali mlendo amene sitinamuyembekezele
Tsiku lina dokotala wathu anatiuza kuti mkazi wanga ali na pathupi. Tinadabwa kwambili! Kodi cosankha canga cinali kudzakhudzidwa bwanji? Mwamsanga tinasintha kaganizidwe kathu, na kuyamba kuyembekezela munthu wina m’banja. Koma n’nali kukaikila ngati nidzakwanitsa kucita upainiya.
Pambuyo pokambilana za zolinga zathu, tinagwilizana kuti ine nicite ndithu upainiya. Mwana wathu Gabriel anabadwa mu April 1985. Ngakhale n’conco, n’naleka kuseŵenza ku banki, ndipo n’nayambanso kucita upainiya mu June 1985. M’kupita kwa nthawi n’nakhala na mwayi wotumikila m’Komiti ya Nthambi. Koma ofesi ya nthambi siinali ku Caracas. Izi zinafuna kuti niziyendela masiku aŵili kapena atatu pa mlungu, pa mtunda wa makilomita 80.
TINASAMUKANSO
Ofesi ya nthambi inali ku tauni ya La Victoria. Conco, monga banja tinapanga ciganizo cosamukila ku La Victoria kufupi na Beteli. Amenewo anali masinthidwe aakulu kwa ife. Nimalinyadila banja langa, ndipo nimaliyamikila kwambili. Kuona kwawo zinthu moyenela kunathandiza kwambili. Mlongo wanga Baha anali wokonzeka kusamalila amayi athu. Mike anali atakwatila, koma Samira na Gabriel tinali nawo pakhomo. Conco, titasamukila ku La Victoria iwo anasiya mabwenzi awo ku Caracas. Cina, mkazi wanga wokondeka Sylvia anafunika kuzoloŵela kukhala m’tauni yaing’ono, m’malo mokhala mu mzinda waukulu wa zocitika zambili. Ndipo tonsefe tinafunika kuzoŵela kukhala m’nyumba yaing’ono. Inde, zambili zinasintha titapanga cosankha cosamuka ku Caracas kupita ku La Victoria.
Komabe, zinthu zinasinthanso. Gabriel anali atakwatila, ndipo Samira anali kukwanitsa kudzikhalila. Zitatelo, ine na Sylvia tinaitanidwa kukatumikila pa Beteli mu 2007. Ndipo timasangalala na utumiki umenewu mpaka lelo. Mike mwana wathu wamkulu ni mkulu mu mpingo, ndipo amakwanitsa kucita upainiya pamodzi na mkazi wake, Monica. Gabriel nayenso ni mkulu mu mpingo, ndipo akutumikila ku Italy pamodzi na mkazi wake, Ambra. Samira ni mpainiya wanthawi zonse, ndipo amatumikila monga mtumiki wa pa Beteli woseŵenzela ku nyumba.
kucoka kumanzele kupita kulamanja: Ine na mkazi wanga Sylvia, pa nthambi ya ku Venezuela.Mwana wathu wamkulu Mike na mkazi wake Monica. Mwana wathu wamkazi Samira. Mwana wathu Gabriel na mkazi wake Ambra
NINGAPANGENSO ZISANKHO ZIMODZI-MODZI
Kukamba zoona, napanga zisankho zambili zikulu-zikulu mu umoyo wanga, ndipo sinidziimba mlandu. N’kanati nipangenso zisankho, ningapangenso zisankho zimodzi-modzi. Niyamikila kwambili mwayi wa mautumiki osiyana-siyana amene nakhala nawo potumikila Yehova. Pa zaka zonsezi, naona kufunika kokhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova. Kaya tiyenela kupanga zosankha zazing’ono kapena zazikulu, iye angapeleke mtendele umene “umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afil. 4:6, 7) Ine na Sylvia timasangalala na utumiki wathu wopatulika pa Beteli. Ndipo tiona kuti zosankha zimene tinapanga, Yehova anazidalitsa cifukwa timamuika patsogolo mu umoyo wathu.