LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w22 February tsa. 31
  • Kodi Mudziŵa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mudziŵa?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mudziŵa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
w22 February tsa. 31

Kodi Mudziŵa?

N’cifukwa ciani njiŵa komanso ana a nkhunda zinali kulandilidwa monga nsembe?

PANSI pa Cilamulo, njiŵa komanso ana a nkhunda zinali kulandilidwa monga nsembe kwa Yehova. Mitundu iŵili ya mbalame imeneyi imachulidwa pamodzi m’malamulo okamba za kupeleka nsembe. Ngati munthu analibe njiŵa, anali kupeleka ana a nkhunda. (Lev. 1:14; 12:8; 14:30) Kodi izi zinali zopindulitsa motani? Cifukwa cimodzi n’cakuti, nthawi zina cinali covuta kupeza ana a nkhunda. Cifukwa ciani?

Njiŵa

Njiŵa ni mbalame zosamuka-samuka zimene zinali kukhala ku Isiraeli m’miyezi yotentha. Mwezi wa October ukafika, mbalame zimenezi zinali kusamukila ku maiko othuma, ndipo zinali kubwelela ku Isiraeli kukayamba kutentha. (Nyimbo 2:​11, 12; Yer. 8:7) Izi zinapangitsa kuti cikhale covuta kwa Aisiraeli kumapeleka njiŵa monga nsembe m’nyengo yozizila.

Nkhunda

Koma nkhunda ni mbalame zimene sizisamuka-samuka. Conco, zinali kupezeka ku Isiraeli caka conse. Kuwonjezela apo, mbalamezi zinali zoti munthu akhoza kuweta. (Yelekezelani na Yohane 2:​14, 16.) Buku lina lakuti Bible Plants and Animals limati: “Anthu onse m’midzi komanso m’matauni a ku Palestine anali kuweta nkhunda. Mwininyumba aliyense anali kukhala na khola la nkhunda, kapena mphako zimene anali kugoba pacipupa.”—Yelekezelani na Yesaya 60:8.

Nkhunda m’mphako yake

Yehova anaonetsa kuti ni wacikondi, komanso wololela mwa kulola Aisiraeli kupeleka nsembe mbalame zimene zinali kupezeka caka conse.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani