Kodi Mudziŵa?
Kodi n’koyenela kukamba kuti amalonda amene anali kugulitsa ziweto m’kacisi ku Yerusalemu anali “acifwamba”?
BUKU la Uthenga Wabwino la Mateyu, limati: “Yesu analoŵa m’kacisi ndi kuthamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kacisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda. Iye anawauza kuti: ‘Malemba amati, “Nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphelelamo,” koma inu mukuisandutsa phanga la acifwamba.’”—Mat. 21:12, 13.
Zolemba zakale zofotokoza mbili ya Ayuda zionetsa kuti amalonda a pakacisi anali kudyela masuku pamutu makasitomala awo mwa kuwachaja mitengo yokwela kwambili. Mwacitsanzo, zolemba zina zaciyuda zimafotokoza kuti panthawi ina m’zaka 100 zoyambilila, mtengo wa nkhunda ziŵili zopelekela nsembe unakwela kufika pa dinari imodzi ya golide. Mtengo umenewu unali wolingana ndi malipilo amene munthu wamba anali kulandila akagwila nchito kwa masiku 25. Nkhunda kapena njiŵa zinali nsembe zimene anthu osauka anali kupeleka. Ngakhale n’conco, mitengo ya mbalame zimenezi anaikweza kwambili. (Lev. 1:14; 5:7; 12:6-8) Mrabi wina, dzina lake Simeon ben Gamaliel, atakhumudwa na zimenezi, anacepetsa ciŵelengelo ca nsembe zimene Ayuda anafunika kupeleka. Atangocita zimenezi, mtengo wa nkhunda ziŵili unagwelatu.
Mogwilizana ndi mfundo ili pamwambayi, Yesu sanalakwitse kuchula amalonda a pakacisi kuti “acifwamba” cifukwa anali kudyela anthu masuku pamutu ndiponso anali adyela kwambili.