Yophunzila
DECEMBER 2022
NKHANI ZOPHUNZILA: JANUARY 30–FEBRUARY 26, 2023
© 2022 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika pa dziko lonse lapansi. Nchito imeneyi timaiyendetsa na zopeleka zaufulu. Kuti mupange copeleka, pitani pa donate.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa ina. Komabe, ena mwa masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lakuti A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.
CITHUNZI CA PACIKUTO:
Mu ulamulilo wa zaka Cikwi, m’bale akunola luso lake limene anali kufunitsitsa mwacidwi kulikulitsa (Onani nkhani yophunzila 50, ndime 19)