Mulungu Amasamala za Inu
M’Baibo muli malangizo abwino kwambili cifukwa ni buku locokela kwa Mulungu. Baibo si buku la malangizo a zaumoyo. Komabe, ingatithandize kudziŵa zimene tingacite tikakumana na zinthu zosoŵetsa mtendele, tikamavutika maganizo, tikapwetekedwa mtima, kapena tikadwala matenda odetsa nkhawa.
Koposa zonse, Baibo imatitsimikizila kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu,a amamvetsa maganizo athu na mmene timamvela kuposa munthu wina aliyense. Iye ni wofunitsitsa kutithandiza pa mavuto aliwonse amene timakumana nawo. Mwacitsanzo, onani malemba aŵili awa olimbikitsa:
“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—SALIMO 34:18.
“Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ndagwila dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—YESAYA 41:13.
Koma kodi Yehova amatithandiza bwanji ngati tikudwala matenda a maganizo? Monga muonele m’nkhani zotsatilazi, Yehova amatithandiza m’njila zambili poonetsa kuti amasamaladi za ife.
a Yehova ni dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.