Kodi Munadzifunsapo Mafunso Awa?
Popeza tonse mtendele timaufuna, n’cifukwa ciyani padziko lapansi pakucitika nkhondo zambili conci?
Kodi n’zothekadi kukhala ndi mtendele weniweni m’dziko lodzala ndi ciwawali?
Kodi nkhondo zidzathadi padzikoli?
Mungadabwe ndi mayankho amene Baibo imapeleka pa mafunso amenewa, ndipo mayankho amenewa adzakulimbikitsani.
Mungacite bwino kudziwelengela nokha zimene Baibo imakamba pa nkhani yofunika imeneyi? Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda ingakuthandizeni kucita zimenezi.