LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp25 na. 1 masa. 14-15
  • Kupeza Mtendele wa Mumtima pa Nthawi ya Nkhondo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kupeza Mtendele wa Mumtima pa Nthawi ya Nkhondo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2025
  • Nkhani Zofanana
  • Pa Nkhondo Pamacitika Zinthu Zoipa Kwambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2025
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Kodi Mulungu amamvela bwanji akaona kuti muvutika?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Kodi Nkhondo Zidzatha Bwanji?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2025
wp25 na. 1 masa. 14-15
Mwamuna wacikulile amene manja ake anaduka pa nkhondo, wakhala pa njinga ya olumala pamene akusangalala ndi cakudya limodzi ndi banja lake.

Kupeza Mtendele wa Mumtima pa Nthawi ya Nkhondo

Gary, amene kale anali msilikali anati: “N’sanaphunzile Baibo, sin’nali kudziwa cifukwa cake padziko lapansi pali kucitika zinthu zankhanza, kupanda cilungamo, komanso mavuto ena ambili. Koma tsopano ndili ndi mtendele wa mumtima. Ndikudziwa kuti Yehova Mulungu adzacititsa kuti dziko lapansi likhale malo amtendele.”

Si Gary yekha amene amamva mwanjila imeneyi. Onani mmene Baibo yathandizilanso anthu ena.

BAIBO IMATI: “Inu Yehova, ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.”​—Salimo 86:5.

MMENE LEMBALI LIMATHANDIZILA: “Lembali limandithandiza kuona kuti Yehova ndi wacifundo. Ndipo ndidziwa kuti iye ndi wofunitsitsa kundikhululukila zinthu zonse zankhanza zimene n’nacita pamene n’nali kumenyako nkhondo.”​—Anatelo Wilmar, wa ku Colombia.

BAIBO IMATI: “Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Ndipo zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso kapena kuvutitsa maganizo.”​—Yesaya 65:17.

MMENE LEMBALI LIMATHANDIZILA: “Ndimakhala ndi nkhawa yaikulu komanso ndimavutika kwambili maganizo ndikakumbukila zinthu zimene zinacitika pamene n’nali msilikali. Koma lemba limeneli limandikumbutsa kuti posacedwapa, Yehova adzandithandiza kuiwalilatu zoipa zonse zimene zimandivutitsa maganizo. Ndipo sizidzabwelanso m’maganizo kapena mumtima mwanga. Zidzakhaladi zosangalatsa zedi!”​—Anatelo Zafirah, wa ku America.

BAIBO IMATI: “Mʼmasiku a ulamulilo wake, wolungama zinthu zidzamuyendela bwino. Ndipo padzakhala mtendele woculuka kwa nthawi yonse imene mwezi udzakhalepo.”​—Salimo 72:7.

MMENE LEMBALI LIMATHANDIZILA: “Nthawi zambili ndimaganizila mawu amenewa. Posacedwapa, nkhondo ndi mavuto onse amene amabwela cifukwa ca nkhondo adzatha. Ndipo sitidzakhalanso ndi nkhawa ya mmene tingatetezele okondedwa athu.”​—Anatelo Oleksandra, wa ku Ukraine.

BAIBO IMATI: “Anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo. . . . Dzukani ndipo mufuule mosangalala, inu anthu okhala m’fumbi!”​—Yesaya 26:19.

MMENE LEMBALI LIMATHANDIZILA: “Pafupifupi anthu onse m’banja lathu anaphedwa pamene anthu a mtundu wina anafuna kupha anthu onse a mtundu wathu wa Atutsi. Koma vesili limanditsimikizila kuti onse ndidzawaonanso. Ndikuyembekezela mwacidwi kudzamva mawu awo acisangalalo akadzaukitsidwa!”​—Anatelo Marie, wa ku Rwanda.

BAIBO IMATI: “Kwatsala kanthawi kocepa, ndipo oipa sadzakhalaponso . . . Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”​—Salimo 37:​10, 11.

MMENE LEMBALI LIMATHANDIZILA: “Ngakhale kuti nkhondo inatha, zinthu zopanda cilungamo zikali kucitika, ndipo anthu oipa akalipo. Mavesi amenewa akhala akundilimbikitsa kwambili. Andithandiza kuona kuti Yehova amaona zonse, ndipo amamvetsa zimene ndikupitamo. Iye analonjeza kuti posacedwapa, mavuto onse adzatha ndipo sadzakumbukilidwanso.”​—Anatelo Daler, wa ku Tajikistan.

Anthu amene achulidwa m’magazini ino, ndi ena mwa a Mboni za Yehova amene Baibo yawathandiza kuti apeze mtendele wa mumtima. Iwo anaphunzila kukonda munthu aliyense mosasamala kanthu za mtundu wake, fuko, kapena dziko limene amakhala. (Aefeso 4:​31, 32) A Mboni za Yehova salowelela m’zandale, ndipo amakana kucitako zaciwawa.​—Yohane 18:36.

A Mboni za Yehova amaonetsana cikondi ndiponso amathandizana wina ndi mnzake monga banja limodzi. (Yohane 13:35) Citsanzo ndi Oleksandra, amene tam’chulapo kale m’magazini ino. Iye ndi mkulu wake anakakamizika kuthawila ku dziko lina cifukwa ca nkhondo. Oleksandra anati: “Titalowa m’dziko lina, tinaona a Mboni za Yehova amene anali kutiyembekezela kuti atilandile. Zimene anaticitila zinatithandiza kuti tisamacite cilendo pokhala m’dzikolo monga anthu othawa kwawo.”

Tikukuitanilani kuti mukabwele kumisonkhano yathu kuti mukaphunzile mmene mungakhalile ndi mtendele wa mumtima palipano, komanso za lonjezo la m’Baibo lokamba dziko la mtendele limene likubwela. Pitani pa jw.org kuti mupeze malo a msonkhano akufupi ndi kwanuko. Kapena pemphani kuti muyambe kuphunzila Baibo kwaulele ndi wa Mboni za Yehova. Phunzilo limeneli limacitika mocita kukambilana pogwilitsa nchito buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani