Anthu sangathetse nkhondo
Kodi Nkhondo Zidzatha Bwanji?
Baibo imafotokoza kuti Mulungu, osati anthu, ndiye “adzathetse nkhondo padziko lonse lapansi.”—Salimo 46:9.
MULUNGU ADZAWONONGA MABOMA ONSE A ANTHU
Mulungu adzawononga maboma onse a anthu pa nkhondo imene Baibo imacha Aramagedo.a (Chivumbulutso 16:16) Pa nthawi imeneyo, “mafumu a padziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzasonkhanitsidwa pamodzi ku “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Aramagedo ndi nkhondo ya Mulungu imene idzathetsa nkhondo zonse.
Maboma a anthu akadzawonongedwa, Ufumu wa Mulungu kapena kuti boma lake ndilo lidzayamba kulamulila dziko lapansi. Boma limeneli lizidzalamulila kucokela kumwamba ndipo silidzawonongedwa. (Danieli 2:44) Mulungu anasankha Mwana wake, Yesu Khristu, kukhala Mfumu ya Ufumu umenewu. (Yesaya 9:6, 7; Mateyo 28:18) Pamene Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kuti azipemphela kuti Ufumub wanu ubwele, anali kukamba za boma la Mulungu limeneli. (Mateyo 6:9, 10) Panthawiyo, anthu padziko lonse adzakhala ogwilizana cifukwa azidzalamulidwa ndi boma limodzi, limene wolamulila wake ndi Yesu.
Yesu sadzagwilitsa nchito mphamvu zake mwadyela ngati mmene anthu olamulila amacitila. Iye ndi wacilungamo komanso ndi wopanda tsankho. Conco, adzasamalila anthu onse mwacikondi popanda kuyang’ana mtundu wawo, cikhalidwe, kapena dziko limene akukhala. (Yesaya 11:3, 4) Ndipo anthu sadzafunika kucita kumenyela ufulu wawo. Cifukwa ciyani? Cifukwa Yesu adzaonetsetsa kuti munthu aliyense akusamalidwa bwino. Baibo imati: “Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. . . . Adzawapulumutsa kuti asapondelezedwe komanso kucitilidwa zaciwawa.”—Salimo 72:12-14.
Ufumu wa Mulungu udzacotsa ndi kuwononga zida zonse zankhondo padziko lapansi. (Mika 4:3) Udzawononganso anthu onse oipa amene safuna kuleka kumenya nkhondo kapena amene amasokoneza mtendele wa anthu ena. (Salimo 37:9, 10) Anthu onse, amuna, akazi, ndi ana adzakhala otetezeka kulikonse kumene angakhale padziko lapansi.—Ezekieli 34:28.
Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulila dziko lapansi, anthu onse adzakhala ndi umoyo wabwino kwambili. Ufumuwo udzathetsa mavuto onse amene amapangitsa kuti anthu azicita nkhondo, monga umphawi, njala, ndi kusowa pokhala. Munthu aliyense adzakhala ndi zakudya zoculuka zopatsa thanzi, komanso malo abwino okhala.—Salimo 72:16; Yesaya 65:21-23.
Ufumu wa Mulungu udzacotsa zoipa zonse zimene zimabwela cifukwa ca nkhondo. Udzapoletsa zilonda zonse ndi kuthetsa cisoni ndi kupwetekedwa mtima konse kumene anthu amamva cifukwa ca zoipa zimene zimacitika pa nkhondo. Ngakhale anthu amene anamwalila, adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi. (Yesaya 25:8; 26:19; 35:5, 6) Mabanja adzakhalilanso limodzi ndi okondedwa awo, ndipo anthu sadzakumbukilanso zinthu zankhanza zimene zinacitika cifukwa ‘zakalezo [zidzakhala] zitapita.’—Chivumbulutso 21:4.
MULUNGU ADZACOTSAPO UCIMO
Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulila dziko lapansi, anthu onse azidzalambila Yehovac, Mulungu yekhayo woona, “amene ndi wacikondi komanso wamtendele.” (2 Akorinto 13:11) Anthu adzaphunzila mmene angakhalile ndi ena mwamtendele. (Yesaya 2:3, 4; 11:9) Anthu onse amene adzamvela Mulungu, adzamasulidwa ku ucimo ndipo adzakhala angwilo.—Aroma 8:20, 21.
MULUNGU ADZAWONONGA SATANA NDI ZIWANDA ZAKE
Ufumu wa Mulungu udzawononga Satana ndi ziwanda zake, amene amasonkhezela anthu kucita nkhondo. (Chivumbulutso 20:1-3, 10) Satana ndi ziwanda zake akadzawonongedwa, padziko “padzakhala mtendele woculuka.”—Salimo 72:7.
Musakayikile kuti zimene Mulungu analonjeza zakuti adzathetsa nkhondo zidzacitikadi. Iye ali ndi mphamvu komanso ndi wofunitsitsa kuthetsa nkhondo.
Mulungu ali ndi nzelu komanso mphamvu zoculuka moti sangalephele kuthetsa nkhondo ndi ciwawa. (Yobu 9:4) Palibe cimene angalephele kucita.—Yobu 42:2.
Mulungu cimamuwawa akamaona anthu akuvutika. (Yesaya 63:9) Ndipo “amadana ndi aliyense amene amakonda ciwawa.”—Salimo 11:5.
Nthawi zonse Mulungu amacitadi zimene wanena, ndipo sanganame.—Yesaya 55:10, 11; Tito 1:2.
Mulungu adzabweletsa mtendele weniweni komanso wosatha padziko lapansi.
Mulungu adzathetsa nkhondo
a Welengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo N’ciyani?” pa jw.org.
b Tambani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciyani? pa jw.org.
c Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.