Cifukwa Cake Nkhondo Zikupitilizabe Kucitika
Baibo imafotokoza zimene zimayambitsa nkhondo, komanso cifukwa cake nkhondo zikupitilizabe kucitika.
CHIMO
Mulungu analenga makolo athu oyambilila, Adamu ndi Hava, m’cifanizilo cake. (Genesis 1:27) Izi zitanthauza kuti iwo anali kutha kuonetsa makhalidwe amene Mulungu ali nawo, monga mtendele ndi cikondi. (1 Akorinto 14:33; 1 Yohane 4:8) Koma Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu ndipo anacimwa. Zotsatilapo zake n’zakuti tonsefe tinatengela ucimo ndi imfa kwa iwo. (Aroma 5:12) Ucimo umenewo umatipangitsa kukhala ndi maganizo oipa. Ici n’cifukwa cake anthu ambili amacita zaciwawa.—Genesis 6:5; Maliko 7:21, 22.
MABOMA A ANTHU
Mulungu sanatilenge kuti tizidzilamulila tokha. Baibo imati: “Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Pa cifukwa cimeneci, maboma a anthu sangakwanitse kuthetsa nkhondo ndi zaciwawa.
SATANA NDI ZIWANDA ZAKE
Baibo imaonetsa kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) “Woipayo” ndi Satana Mdyelekezi, ndipo iye ndi wopha anthu. (Yohane 8:44) Iye ndi ziwanda zake amalimbikitsa anthu kuti azicita nkhondo ndi ciwawa.—Chivumbulutso 12:9, 12.
Anthu sangakwanitse kuthetsa zinthu zimene zimayambitsa nkhondo ndi ciwawa. Koma Mulungu yekha ndiye angathe kucita zimenezi.