NKHANI YA PACIKUTO | NKHONDO IMENE INASINTHA ZINTHU PADZIKO
Kodi Ndani Maka-maka Amacititsa Nkhondo ndi Mavuto?
Pa November 11, m’caka ca 1918, Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse inatha. Pa tsikulo anthu anatseka mabizinesi ao ndipo anali kuvina m’miseu. Koma cisangalaloco sicinakhalitse. Nkhondo yoyamba itangotha, tsoka lina limene linali loopsa kuposa nkhondoyo linayamba.
Mu June caka ca 1918, asilikali amene anali ku France anagwidwa ndi mlili woopsa wochedwa Fuluwenza ya ku Spain. M’kanthawi kocepa, mliliwo unapha anthu ambili. Mwacitsanzo, pa miyezi yocepa cabe, mliliwo unapha asilikali ambili a ku America amene anali ku France kuposa amene anaphedwa ndi adani pankhondo. Nkhondoyo itatha, asilikali anabwelela kwao. Koma popeza kuti anali asanacile matendawo, io anafalitsa mliliwo mwamsanga padziko lonse.
Nkhondo itatha, kunabukanso mavuto a njala ndi umphawi wadzaoneni. Anthu ambili a ku Ulaya anavutika ndi njala pamene nkhondo inatha mu 1918. Pofika m’caka ca 1923, ndalama ya ku Germany inathelatu mphamvu. Podzafika mu 1929, cuma ca dziko lonse cinagwelatu. Ndipo mu 1939, nkhondo yaciŵili ya padziko lonse inayamba. Zinali monga kuti nkhondo imeneyi inali kupitiliza nkhondo yoyamba. Kodi n’ciani cinacititsa masoka otsatizana-tsatizana amenewa?
CIZINDIKILO CA MASIKU OTSILIZA
Ulosi wa m’Baibulo umatithandiza kudziŵa cimene cimacititsa mavuto ena amene akhala akucitika m’dziko monga Nkhondo Yoyamba ya Padziko lonse. Yesu analosela za nthawi pamene “mtundu udzaukilana ndi mtundu wina” ndipo njala ndi milili zidzakhala paliponse m’dziko. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11) Iye anauza ophunzila ake kuti mavuto amenewa adzapanga cizindikilo ca masiku otsiliza. Buku la Chivumbulutso limafotokoza zambili pankhaniyi, ndipo limaonetsa kuti masoka amene akucitika padzikoli ali kaamba ka nkhondo imene inacitika kumwamba.—Onani bokosi lakuti “Nkhondo Kumwamba ndi Padziko Lapansi.”
Buku la m’Baibulo limeneli limafotokozanso za anthu anai okwela pa mahachi. Atatu mwa anthu okwela pa mahachi amenewa amaimila masoka amene Yesu analosela. Masoka amenewo ndi nkhondo, njala ndi milili. (Onani kamutu kakuti “Kodi Anthu Anai Okwela pa Mahachi Alidi pa Liwilo?”) N’zoonekelatu kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayambitsa mavuto amene akhala ovuta kuwathetsa. Ndipo Baibulo limasonyeza kuti Satana ndiye anayambitsa mavuto amenewa. (1 Yohane 5:19) Kodi Satana adzapitiliza kucititsa mavuto amenewa mpaka liti?
Buku la Chivumbulutso limatitsimikizila kuti Satana wangotsala ndi “kanthawi kocepa.” (Chivumbulutso 12:12) Ndiye cifukwa cake iye ndi wokwiya kwambili ndipo akuyambitsa masoka osaneneka pano padziko lapansi. Koma mavuto amene timaona ndi umboni winanso wakuti Satana watsala ndi kanthawi kocepa.
KUONONGA NCHITO ZA MDYELEKEZI
Kunena zoona, Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse inasintha zinthu kwambili padzikoli. Nkhondoyi inali ciyambi ca nkhondo zoopsa zimene zakhala zikucitika, ndipo zimenezi zapangitsa anthu kugalukila maboma ndi kukaikila atsogoleli ao. Nkhondo imeneyi ndi umboni wosatsutsika wakuti Satana anathamangitsidwa kumwamba. (Chivumbulutso 12:9) Wolamulila wosaoneka ameneyu anakwiya kwambili monga mmene wolamulila wankhanza amene akudziŵa kuti watsala pang’ono kulandidwa ulamulilo amakwiila. Satana akadzacotsedwa, mavuto amene anayambila pa Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse adzatha.
Ulosi wa m’Baibulo umatithandiza kukhulupilila kuti Yesu Kristu, Mfumu yathu ya kumwamba, posacedwapa ‘adzaononga nchito za Mdyelekezi.’ (1 Yohane 3:8) Anthu mamiliyoni ambili masiku ano amapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele. Kodi inunso mumatelo? Kudzela mu Ufumu umenewo, anthu okhulupilika adzaona mmene cifunilo ca Mulungu cidzakwanilitsidwila padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Mu Ufumu wa Mulungu simudzakhalanso nkhondo ya padziko lonse kapena nkhondo ina iliyonse. (Salimo 46:9) Tikukupemphani kuti muphunzile za Ufumu umenewo kuti mudzakhale ndi moyo pa nthawi imene mtendele udzadzaza dziko lonse lapansi.—Yesaya 9:6, 7.
a Onani caputala 8 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.