Tamandani Kristu, Mfumu Yaulemelelo!
“Upambane mu ulemelelo wako.”—SAL. 45:4.
1, 2. N’cifukwa ciani lemba la Salimo 45 ndi locititsa cidwi kwa ife?
MFUMU yaulemelelo yakwela pa hachi cifukwa ca coonadi ndi cilungamo ndipo ikupita kukagonjetsa adani ake. Pambuyo popambana nkhondo imeneyo, mfumuyo idzakwatila mkazi wokongola kwambili. Anthu adzapitiliza kukumbukila ndi kutamanda mfumuyo ku mibadwo yonse yobwela mtsogolo. Imeneyi ndiyo mfundo yaikulu ya lemba la Salimo 45.
2 Nkhani yopezeka pa lemba la Salimo 45 ndi yocititsa cidwi ndipo mapeto ake ndi osangalatsa. Koma zocitika za m’nkhani imeneyi zimatiphuzitsanso zinthu zina. Zocitikazi zimakhudza moyo wathu masiku ano ndiponso tsogolo lathu. Motelo, tiyeni tipende salimo limeneli mosamala kwambili.
“MTIMA WANGA WAGALAMUKA CIFUKWA CA NKHANI YOSANGALATSA”
3, 4. (a) Kodi ndi “nkhani yosangalatsa” iti imene imatikhudza? Nanga imakhudza bwanji mtima wathu? (b) N’cifukwa ciani tinganene kuti ‘Nyimbo yathu imanena za mfumu?’ Nanga lilime lathu limakhala bwanji ngati colembela?
3 Ŵelengani Salimo 45:1. “Nkhani yosangalatsa” imene inakhudza ndi ‘kugalamutsa’ mtima wa wamasalimo ndi yokhudza mfumu. Liu la Ciheberi limene analitembenuza kuti ‘kugalamuka’ limatanthauza “kubwatama” kapena “kuŵila.” Nkhani yokhudza mfumu inapangitsa mtima wa wamasalimo kuŵila cifukwa ca cisangalalo ndipo lilime lake linakhala ngati “colembela ca wokopela malemba waluso.”
4 Nanga bwanji ponena za ife? Uthenga wabwino wa Ufumu wa Mesiya ndi nkhani imene imatisangalatsa. Uthenga wa Ufumu unakhaladi nkhani yosangalatsa kwambili mu 1914. Kuyambila m’caka cimeneco, uthengawu sukamba za Ufumu wamtsogolo, koma umakamba za boma leni-leni limene tsopano likulamulila kumwamba. Umenewu ndiwo ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ umene timalalikila “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Kodi uthenga wa Ufumu ‘umagalamutsa’ mtima wathu? Kodi timalalikila uthenga wabwino wa Ufumu mwacangu? Mofanana ndi wamasalimo, ‘nyimbo yathu imanena za mfumu’ imene ndi Yesu Kristu. Timalengeza kuti iye anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya kumwamba. Ndiponso timauza mafumu ndi anthu ao onse kuti ayenela kugonjela ku ulamulilo wake. (Sal. 2:1, 2, 4-12) Lilime lathu limakhala monga “colembela ca wokopela malemba waluso” cifukwa cakuti timagwilitsila nchito kwambili Mau olembedwa pa nchito yathu yolalikila.
Mosangalala, timalengeza uthenga wabwino wonena za Mfumu yathu, Yesu Kristu
‘MAU OSANGALATSA ATULUKA M’KAMWA MWA MFUMU’
5. (a) Kodi Yesu anali wokongola pa zifukwa ziti? (b) Kodi n’ciani cinapangitsa ‘mau otuluka m’kamwa mwa Mfumu kukhala osangalatsa’? Ndipo ife tingatengele bwanji citsanzo cake?
5 Ŵelengani Salimo 45:2. Malemba samakamba zambili ponena za maonekedwe a Yesu. Popeza kuti anali wangwilo, mosakaikila iye anali “wokongola.” Komabe, Yesu anali wokongola mwapadela cifukwa cakuti anali wokhulupilika kwa Yehova ndiponso anali ndi mtima wosagawanika. Kuonjezela pamenepo, Yesu anali kulalikila uthenga wa Ufumu ‘mogwila mtima.’ (Luka 4:22; Yoh. 7:46) Kodi inuyo mumayesetsa kutengela citsanzo cake pa nchito yolalikila mwa kugwilitsila nchito mau ogwila mtima polalikila?—Akol. 4:6.
6. Kodi Mulungu anam’dalitsa bwanji Yesu “kosatha”?
6 Cifukwa cakuti Yesu anali wodzipeleka ndi mtima wonse, Yehova anamudalitsa pa utumiki wake padziko lapansi. Yesu atapeleka moyo wake monga nsembe ndi kuukitsidwa, Mulungu anam’patsa mphoto. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Atakhala munthu, anadzicepetsa ndi kukhala womvela mpaka imfa. Anakhala womvela mpaka imfa ya pamtengo wozunzikilapo. Pa cifukwa cimenecinso, Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomela mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse. Anacita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo ao. Kutinso aliyense avomeleze poyela ndi lilime lake kuti Yesu Kristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” (Afil. 2:8-11) Yehova anadalitsa Yesu “mpaka kalekale” mwa kumuukitsa kuti akhale ndi moyo wosakhoza kufa.—Aroma 6:9.
MFUMU IKWEZEDWA KUPOSA “MAFUMU ENA”
7. Kodi Mulungu anadzoza Yesu kuposa “mafumu ena” m’njila zotani?
7 Ŵelengani Salimo 45:6, 7. Cifukwa cakuti Yesu amakonda kwambili cilungamo ndipo amadana ndi ciliconse cimene cinganyozetse dzina la Atate wake, Yehova anam’dzoza kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. Mulungu anadzoza Yesu ndi “mafuta acikondwelelo cacikulu” kuposa “ca mafumu ena,” kutanthauza mafumu aciyuda omwe anali mu mzela wa Davide. Kodi Mulungu anadzoza Yesu kuposa mafumu ena m’njila zotani? Coyamba, Yesu anadzozedwa mwacindunji ndi Yehova. Caciŵili, Yehova anam’dzoza monga Mfumu ndiponso monga Mkulu wa Ansembe. (Sal. 2:2; Aheb. 5:5, 6) Cacitatu, Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyela osati ndi mafuta, ndipo ufumu wake si wa padziko lapansi koma ndi wakumwamba.
8. N’cifukwa ciani tinganene kuti ‘Mulungu ndiye mpando wacifumu’ wa Yesu? Kodi tikudziŵa bwanji kuti ufumu wake ndi wolungama?
8 Yehova anaika Mwana wake monga Mfumu Mesiya kumwamba mu 1914. ‘Ndodo yake yacifumu ndiyo ndodo yacilungamo.’ Conco, ulamulilo wake udzakhala wosakondela ndiponso wacilungamo. Iye ndi woyenela kukhala mfumu cifukwa cakuti Mulungu ‘ndiye mpando wake wacifumu.’ Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova ndi amene anamuika kukhala Mfumu. Kuonjezela pamenepo, ulamulilo wa Yesu udzakhalapo “mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.” Timanyadila kutumikila Yehova motsogoleledwa ndi Mfumu yamphamvu imene Mulungu anaika.
MFUMU ‘IMANGILILA LUPANGA LAKE M’CIUNO’
9, 10. (a) Kodi ndi liti pamene Kristu anamangilila lupanga m’ciuno mwake? Ndipo analigwilitsila nchito bwanji atangolimangilila? (b) Kodi Kristu adzagwilitsila nchito motani lupanga lake mtsogolo?
9 Ŵelengani Salimo 45:3. Yehova analamula Mfumu ‘kumangilila lupanga m’ciuno mwake.’ Mwakutelo, Mulungu anapatsa Yesu ulamulilo womenya nkhondo ndi anthu amene amatsutsa ulamulilo wa Mulungu ndi kuwaononga. (Sal. 110:2) Popeza kuti Kristu ndi Mfumu Yankhondo yosagonjetseka, iye amachedwa “wamphamvu.” Iye anamagilila lupanga lake m’ciuno m’caka ca 1914. Panthawiyo, iye anagonjetsa Satana ndi ziŵanda zake ndi kuwagwetsela padziko lapansi.—Chiv. 12:7-9.
10 Cocitika cimeneco cinali cabe ciyambi ca nkhondo ya Mfumu yokagonjetsa adani ake. Koma iye ‘adzapambana pa nkhondo yolimbana nao.’ (Chiv. 6:2) Yehova adzaononga dongosolo lonse la Satana padziko lapansi ndipo Satana ndi ziŵanda zake adzalandidwa mphamvu. Babulo Wamkulu, umene ndi ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama, adzakhala woyamba kuonongedwa. Yehova adzagwilitsila nchito olamulila andale kuononga “hule” loipa limeneli. (Chiv. 17:16, 17) Ndiyeno, Mfumu ya Nkhondo idzaononga kothelatu dongosolo landale la Satana. Kristu, amene amachedwanso “mngelo wa phompho,” adzapambana pa nkhondo yolimbana ndi adani ake pamene adzaponya Satana ndi ziŵanda zake kuphompho. (Chiv. 9:1, 11; 20:1-3) Tiyeni tipende mmene lemba la Salimo 45 linaloselela zocitika zocititsa cidwi zimenezi.
MFUMU IKWELA PAHACHI “CIFUKWA CA COONADI”
11. N’cifukwa ciani tinganene kuti Kristu anakwela pahachi “cifukwa ca coonadi”?
11 Ŵelengani Salimo 45:4. Colinga cimene Mfumu ya Nkhondo imeneyi ikumenyela nkhondo sikulanda madela kapena kufuna kupondeleza anthu. Iyo ikumenya nkhondo ya cilungamo ndi zolinga zabwino. Mfumu imeneyi yakwela pahachi “cifukwa ca coonadi, kudzicepetsa ndi cilungamo.” Yehova ndiye yekha amene ali woyenela kulamulila cilengedwe conse. Ndipo anthu onse ayenela kudziwa mfundo ya coonadi yofunika kwambili imeneyi. Satana anatsutsa kuti Yehova ndi woyenela kulamulila pamene anapandukila Mulungu. Kuyambila nthawi imene Satana anapanduka, ziŵanda ndi anthu akhala akutsutsa mfundo ya coonadi yofunika imeneyi. Ino ndiyo nthawi yakuti Mfumu imene Yehova anadzoza ikwele pahachi yake ndi kumenya nkhondo kuti anthu onse adziŵe mfundo ya coonadi yakuti ndi Yehova yekha amene ali woyenela kulamulila.
12. N’cifukwa ciani tinganene kuti Kristu anakwela pahachi ‘cifukwa ca kudzicepetsa’?
12 Mfumu yakwela pa hachi ‘cifukwanso ca kudzicepetsa.’ Monga Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, Yesu wakhala akusonyeza citsanzo ca kudzicepetsa kweni-kweni ndi kugonjela ku ulamulilo wa Atate wake. (Yes. 50:4, 5; Yoh. 5:19) Nzika zonse zokhulupilika za Mfumu ziyenela kutengela citsanzo cake ndi kugonjela modzicepetsa ku ulamulilo wa Yehova m’zinthu zonse. Anthu okhawo amene amacita zimenezi ndi amene adzaloledwa kukhala m’dziko latsopano limene Mulungu analonjeza.—Zek. 14:16, 17.
13. N’cifukwa ciani tinganene kuti Kristu anakwela pahachi ‘cifukwa ca cilungamo’?
13 Kristu wakwela pa hachi ‘cifukwanso ca cilungamo.’ Cilungamo cimene Mfumu ikumenyela nkhondo ndi ‘cilungamo ca Mulungu,’ kutanthauza miyezo ya Yehova pa zinthu zabwino ndi zoipa. (Aroma 3:21; Deut. 32:4) Ponena za Mfumu Yesu Kristu, Yesaya analosela kuti: “Mfumu idzalamulila mwacilungamo.” (Yes. 32:1) Ulamulilo wa Yesu udzabweletsa “kumwamba kwatsopano” ndi “dziko lapansi latsopano” mmene “mudzakhala cilungamo.” (2 Pet. 3:13) Nzika zonse za dziko latsopano limenelo zidzayenela kutsatila miyezo ya Yehova.—Yes. 11:1-5.
MFUMU ICITA “ZINTHU ZOCITITSA MANTHA”
14. Kodi dzanja lamanja la Kristu lidzacita bwanji “zinthu zocititsa mantha”? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
14 Pamene ikuyendetsa hachi yake, Mfumu yamangilila lupanga m’ciuno mwake. (Sal. 45:3) Koma nthawi idzafika pamene mfumu idzasolola lupanga lake ndi dzanja lamanja ndi kuligwilitsila nchito. Wamasalimo analosela kuti dzanja lake lamanja lidzacita “zinthu zocititsa mantha.” (Sal. 45:4) Yesu adzacita “zinthu zocititsa mantha” kwa adani ake pamene adzakwela pa hachi yake ndi kuononga dziko la Satana pa Armagedo. Sitikudziwa kuti mfumu idzagwilitsila nchito ciani kuti iononge dziko loipali. Koma cocitika cimeneco cidzacititsa mantha anthu a m’dzikoli amene sanamvele cenjezo lakuti afunika kugonjela ku ulamulilo wa Mfumu. (Ŵelengani Salimo 2:11, 12.) Mu ulosi wake wonena za masiku otsiliza, Yesu anakamba kuti anthu “adzakomoka cifukwa ca mantha ndi kuyembekezela zimene zicitikile dziko lapansi kumene kuli anthu, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Kenako adzaona Mwana wa munthu akubwela mumtambo ndi mphamvu ndi ulemelelo waukulu.”—Luka 21:26, 27.
15, 16. Kodi ndani amene adzakhala ‘m’magulu a nkhondo’ amene adzatsatila Kristu?
15 Buku la Civumbulutso likufotokoza za kubwela kwa Mfumu “ndi mphamvu ndi ulemelelo waukulu” kuti iononge adani a Mulungu. Lembalo limati: “Nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hachi yoyela. Wokwelapo wake dzina lake linali Wokhulupilika ndi Woona. Iyeyo anali kuweluza ndi kumenya nkhondo mwacilungamo. Komanso magulu ankhondo amene anali kumwamba, anali kumutsatila pamahachi oyela, atavala zovala zapamwamba, zoyela bwino, za mbee! M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali lakuthwa, loti aphele mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yacitsulo. Iye anali kuponda-pondanso m’copondela mphesa ca mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chiv. 19:11, 14, 15.
16 Kodi ndani amene adzakhala ‘m’magulu ankhondo’ a kumwamba amene adzatsatila Kristu pamene akumenya nkhondo imeneyi? Yesu anali ndi “angelo ake” nthawi yoyamba imene anamangilila lupanga lake m’ciuno kuti athamangitse Satana ndi ziwanda zake kumwamba. (Chiv. 12:7-9) Conco n’zomveka kunena kuti pa nkhondo ya Armagedo, magulu a nkhondo a Kristu ndi angelo oyela. Kodi magulu a nkhondo amenewa adzaphatikizapo anthu ena? Yesu analonjeza abale ake adzozedwa kuti: “Amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatila zocita zanga kufikila mapeto, ndidzamupatsa ulamulilo pa mitundu ya anthu. Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yacitsulo, ngati imenenso ine ndailandila kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwa-phwanyidwa ngati mbiya zadothi.” (Chiv. 2:26, 27) Motelo, magulu a nkhondo a kumwamba a Kristu adzaphatikizapo abale ake odzozedwa amene panthawiyo adzakhala kuti alandila mphoto yao kumwamba. Olamulila anzake amenewa adzakhala pambali pake pamene Yesu adzacita “zinthu zocititsa mantha” ndi kulamulila mitundu ya anthu ndi ndodo yacitsulo.
MFUMU IPAMBANA PA NKHONDO YAKE
17. Kodi hachi yoyela imene Kristu wakwelapo imaimila ciani? (b) Kodi lupanga ndi uta zimaimila ciani?
17 Ŵelengani Salimo 45:5. Mfumu yakwela pa hachi yoyela, zimene zikuimila nkhondo yoyela ndiponso yolungama pamaso pa Yehova. (Chiv. 6:2; 19:11) Kuonjezela pa lupanga, mfumu yanyamulanso uta. Pa lembalo timaŵelenga kuti: “Nditayang’ana, ndinaona hachi yoyela. Wokwelapo wake ananyamula uta. Iye anapatsidwa cisoti cacifumu, ndi kupita kukagonjetsa adani ake ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nao.” Lupanga ndi uta zimaimila njila imene Kristu adzagwilitsila nchito kuononga adani ake.
18. Kodi “mivi” ya Kristu idzaoneka bwanji kuti ndi yakuthwa?
18 Mwa mau andakatulo, wamasalimo analosela kuti ‘mivi ya Mfumu yakuthwa idzalasa mitima ya adani a mfumu,’ndipo ‘mitundu ya anthu idzagwa pamapazi ake.’ Anthu ambili adzaphedwa padziko lapansi. Ulosi wa Yeremiya umati: “Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kucokela kumalekezelo a dziko lapansi kufikanso kumalekezelo ena a dziko lapansi.” (Yer. 25:33) Ulosi wina wofanana ndi umenewu umati: “Ndinaonanso mngelo ataimilila padzuŵa. Iye anafuula ndi mau okweza kwa mbalame zonse zouluka capafupi m’mlengalenga, kuti: ‘Bwelani kuno, dzasonkhaneni ku phwando lalikulu la Mulungu la cakudya camadzulo, kuti mudzadye minofu ya mafumu, ya akulu-akulu a asilikali, ya amuna amphamvu, ya mahachi ndi ya okwelapo ake, ndi minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.’”—Chiv. 19:17, 18.
19. Kodi Kristu adzapambana bwanji pa nkhondo yolimbana ndi adani ake?
19 Pambuyo pakuti waononga dongosolo loipa la zinthu la Satana padziko lapansi, Kristu ‘mu ulemelelo wake adzapambana pa nkhondo yake.’ (Sal. 45:4) Iye adzapambana pa nkhondo yake mwa kuponya Satana ndi ziŵanda zake kuphompho. Iwo adzakhala kuphompho pamene Yesu ndi olamulila anzake a 144,000 adzakhala akulamulila kucokela kumwamba kwa zaka 1,000. (Chiv. 20:2, 3) Cifukwa cakuti Mdyelekezi ndi ziŵanda zake sadzakhala ndi mphamvu, anthu a padziko lapansi adzakhala ndi moyo popanda cisonkhezelo ca Satana ndipo adzakhala ndi mwai wogonjela kothelatu Mfumu yao yaulemelelo ndi yopambana. Koma asanaone dziko lapansi likusintha kukhala paladaiso, io adzasangalala ndi cocitika cina pamodzi ndi Mfumu yao ndi olamulila anzake a kumwamba. Tidzakambitsilana za cocitika cimeneco m’nkhani yotsatila.