LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 2/1 masa. 5-7
  • Kodi Ndani Maka-maka Amacititsa Nkhondo ndi Mavuto?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Ndani Maka-maka Amacititsa Nkhondo ndi Mavuto?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIZINDIKILO CA MASIKU OTSILIZA
  • KUONONGA NCHITO ZA MDYELEKEZI
  • Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Ndalama Matililiyoni Zawonongedwa pa Nkhondo—Koma Kodi ni Ndalama Zokha Zawonongeka?
    Nkhani Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 2/1 masa. 5-7

NKHANI YA PACIKUTO | NKHONDO IMENE INASINTHA ZINTHU PADZIKO

Kodi Ndani Maka-maka Amacititsa Nkhondo ndi Mavuto?

Pa November 11, m’caka ca 1918, Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse inatha. Pa tsikulo anthu anatseka mabizinesi ao ndipo anali kuvina m’miseu. Koma cisangalaloco sicinakhalitse. Nkhondo yoyamba itangotha, tsoka lina limene linali loopsa kuposa nkhondoyo linayamba.

Mu June caka ca 1918, asilikali amene anali ku France anagwidwa ndi mlili woopsa wochedwa Fuluwenza ya ku Spain. M’kanthawi kocepa, mliliwo unapha anthu ambili. Mwacitsanzo, pa miyezi yocepa cabe, mliliwo unapha asilikali ambili a ku America amene anali ku France kuposa amene anaphedwa ndi adani pankhondo. Nkhondoyo itatha, asilikali anabwelela kwao. Koma popeza kuti anali asanacile matendawo, io anafalitsa mliliwo mwamsanga padziko lonse.

Nkhondo itatha, kunabukanso mavuto a njala ndi umphawi wadzaoneni. Anthu ambili a ku Ulaya anavutika ndi njala pamene nkhondo inatha mu 1918. Pofika m’caka ca 1923, ndalama ya ku Germany inathelatu mphamvu. Podzafika mu 1929, cuma ca dziko lonse cinagwelatu. Ndipo mu 1939, nkhondo yaciŵili ya padziko lonse inayamba. Zinali monga kuti nkhondo imeneyi inali kupitiliza nkhondo yoyamba. Kodi n’ciani cinacititsa masoka otsatizana-tsatizana amenewa?

CIZINDIKILO CA MASIKU OTSILIZA

Ulosi wa m’Baibulo umatithandiza kudziŵa cimene cimacititsa mavuto ena amene akhala akucitika m’dziko monga Nkhondo Yoyamba ya Padziko lonse. Yesu analosela za nthawi pamene “mtundu udzaukilana ndi mtundu wina” ndipo njala ndi milili zidzakhala paliponse m’dziko. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11) Iye anauza ophunzila ake kuti mavuto amenewa adzapanga cizindikilo ca masiku otsiliza. Buku la Chivumbulutso limafotokoza zambili pankhaniyi, ndipo limaonetsa kuti masoka amene akucitika padzikoli ali kaamba ka nkhondo imene inacitika kumwamba.—Onani bokosi lakuti “Nkhondo Kumwamba ndi Padziko Lapansi.”

Buku la m’Baibulo limeneli limafotokozanso za anthu anai okwela pa mahachi. Atatu mwa anthu okwela pa mahachi amenewa amaimila masoka amene Yesu analosela. Masoka amenewo ndi nkhondo, njala ndi milili. (Onani kamutu kakuti “Kodi Anthu Anai Okwela pa Mahachi Alidi pa Liwilo?”) N’zoonekelatu kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayambitsa mavuto amene akhala ovuta kuwathetsa. Ndipo Baibulo limasonyeza kuti Satana ndiye anayambitsa mavuto amenewa. (1 Yohane 5:19) Kodi Satana adzapitiliza kucititsa mavuto amenewa mpaka liti?

Buku la Chivumbulutso limatitsimikizila kuti Satana wangotsala ndi “kanthawi kocepa.” (Chivumbulutso 12:12) Ndiye cifukwa cake iye ndi wokwiya kwambili ndipo akuyambitsa masoka osaneneka pano padziko lapansi. Koma mavuto amene timaona ndi umboni winanso wakuti Satana watsala ndi kanthawi kocepa.

KUONONGA NCHITO ZA MDYELEKEZI

Kunena zoona, Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse inasintha zinthu kwambili padzikoli. Nkhondoyi inali ciyambi ca nkhondo zoopsa zimene zakhala zikucitika, ndipo zimenezi zapangitsa anthu kugalukila maboma ndi kukaikila atsogoleli ao. Nkhondo imeneyi ndi umboni wosatsutsika wakuti Satana anathamangitsidwa kumwamba. (Chivumbulutso 12:9) Wolamulila wosaoneka ameneyu anakwiya kwambili monga mmene wolamulila wankhanza amene akudziŵa kuti watsala pang’ono kulandidwa ulamulilo amakwiila. Satana akadzacotsedwa, mavuto amene anayambila pa Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse adzatha.

Ulosi wa m’Baibulo umatithandiza kukhulupilila kuti Yesu Kristu, Mfumu yathu ya kumwamba, posacedwapa ‘adzaononga nchito za Mdyelekezi.’ (1 Yohane 3:8) Anthu mamiliyoni ambili masiku ano amapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele. Kodi inunso mumatelo? Kudzela mu Ufumu umenewo, anthu okhulupilika adzaona mmene cifunilo ca Mulungu cidzakwanilitsidwila padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Mu Ufumu wa Mulungu simudzakhalanso nkhondo ya padziko lonse kapena nkhondo ina iliyonse. (Salimo 46:9) Tikukupemphani kuti muphunzile za Ufumu umenewo kuti mudzakhale ndi moyo pa nthawi imene mtendele udzadzaza dziko lonse lapansi.—Yesaya 9:6, 7.

“Nkhondo Kumwamba ndi Padziko Lapansi”

Zaka 1,900 Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse isanayambe, Satana analonjeza Yesu kuti adzamupatsa “maufumu onse a padziko.” (Mateyu 4:8, 9) Yesu anakana, ndipo pambuyo pake ananena kuti Mdyelekezi ndiye “wolamulila wa dziko.” (Yohane 14:30) Mtumwi Yohane nayenso analemba kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

Popeza kuti Satana Mdyelekezi ali ndi ulamulilo waukulu padziko lapansi, m’pomveka kunena kuti iye ndi amene anacititsa nkhondo yoyamba ya padziko lonse ndi mavuto amene anatsatilapo. Ndiye cifukwa cake buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti Satana ndiye wakhala akucititsa mavuto padziko lapansi kuyambila mu 1914 .Onani zocitika izi zimene lemba la Chivumbulutso caputala 12 limanena:

  • Vesi 7 Nkhondo inabuka kumwamba pakati pa Mikayeli (Yesu Kristu) ndi cinjoka (Satana).

  • Vesi 9 Mdyelekezi, “amene akusoceletsa dziko lonse lapansi,” anaponyedwa padziko lapansi.

  • Vesi 12 “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, cifukwa Mdyelekezi watsikila kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.”

Kuŵelengela nthawi kwa m’Baibulo ndi zocitika za padzikoli zimasonyeza kuti nkhondo ya kumwamba imeneyi inacitika pambuyo pakuti Ufumu wa Mulungu wakhazikitsidwa kumwamba mu 1914.a Conco, nkhondo ya kumwamba ndi ya padziko lapansi zinacitika m’caka capadela cimeneci.

a Onani caputala 8 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Anthu Anai Okwela pa Mahachi Alidi pa Liwilo?

Hachi yoyela, imene wokwelapo wake ndi mfumu ya kumwamba. Mfumu Yesu Kristu ndi amene wakwela pahachi cifukwa ca cilungamo. (Salimo 45:4) Nchito yake yoyamba inali kucotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba.—Chivumbulutso 6:2; 12:9.

Hachi yofiila ngati moto, imene wokwelapo wake ali ndi mphamvu ‘yocotsa mtendele padziko lapansi.’ (Chivumbulutso 6:4) Kuyambila mu 1914, anthu akhala akuvutika kwambili ndi nkhondo. Patapita zaka 21 zokha kucokela pamene Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse inatha, nkhondo yaciŵili ya padziko lonse inayamba, ndipo inapha anthu ambili kuposa amene anafa pa nkhondo yoyamba. Malinga ndi zimene ofufuza ena anapeza, anthu pafupi-fupi 60 miliyoni anafa pa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Nkhondo zimene zakhala zikucitika kucokela m’caka ca 1945 ndi za paciweni-weni, koma nazonso ndi zoononga kwambili. Akatswili ena a mbili yakale amanena kuti anthu oposa 100 miliyoni anafa pa nkhondo m’zaka za m’ma 1900.

Hachi yakuda, imene wokwelapo wake ali ndi sikelo m’dzanja lake imene ikuimila njala. (Chivumbulutso 6:5, 6) Pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, anthu pafupi-fupi 750,000 anafa ndi njala ku Germany cifukwa ca mpanda umene adani anamanga pofuna kuti anthu a m’dzikolo asamatuluke. Anthu oposa 2,000,000 anafa ndi njala ku Russia mu 1921. Patapita nthawi yocepa, ku madela ena kunagwanso njala. Anthu pafupi-fupi 70 miliyoni anafa ndi njala kuyambila m’caka ca 1901 mpaka mu 2000. Ndipo caka ciliconse, ana oposa 3,000,000 amene sanakwanitse zaka 5 amafa ndi njala cifukwa cosoŵa cakudya.

Hachi yotuwa, imene wokwelapo wake akubweletsa imfa mwa kucitsa milili yoopsa. (Chivumbulutso 6:8) Mlili waukulu woyamba m’zaka za m’ma 1900 unali fuluwenza ya ku Spain. Anthu amasiyana-siyana maganizo ponena za ciŵelengelo ca anthu amene anafa ndi mliliwu, koma ena amanena kuti mliliwu unapha anthu pafupi-fupi 50 miliyoni. Buku lina limati: “Umenewu unali umodzi mwa milili yoopsa kwambili imene inacitikapo. Ngakhale mlili wocokela ku makoswe sunaphe anthu oculuka cotelo pa nthawi yocepa.” (Man and Microbes) Nthomba, malungo ndi TB ndi ena mwa matenda opatsilana amene apha anthu mamiliyoni ambili-mbili m’zaka za m’ma 1900.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani