Sangalalani Cifukwa ca Cikwati ca Mwanawankhosa
“Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi cimwemwe codzaza tsaya . . . cifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika.”—CHIV. 19:7.
1, 2. (a) Kodi ndi cikwati ca ndani cimene cidzabweletsa cisangalalo coculuka kumwamba? (b) Kodi pakubuka mafunso ati?
NTHAWI zonse kukonzekela mwambo wa cikwati kumatenga nthawi yaitali. M’nkhani ino, tikambilana za mwambo wapadela kwambili wa cikwati ca mfumu umene watenga zaka pafupi-fupi 2,000 kukonzekela. Nthawi ya cikwati cimeneci yayandikila kwambili. Posacedwapa, m’bwalo la Mfumu mudzakhala nyimbo za cisangalalo, ndipo makamu a kumwamba adzaimba mofuula kuti: “Tamandani Ya, anthu inu, cifukwa Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse, wayamba kulamulila monga mfumu. Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi cimwemwe codzaza tsaya. Timupatse ulemelelo, cifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.”—Chiv. 19:6, 7.
2 “Mwanawankhosa” amene cikwati cake cidzabweletsa cisangalalo kumwamba ndi Yesu Kristu. (Yoh. 1:29) Kodi iye adzavala zovala zotani pa cikwatico? Kodi mkwatibwi wake ndani? Kodi mkwatibwi ameneyo wakonzekeletsedwa bwanji kaamba ka cikwati? Nanga cikwati cimeneco cidzacitika liti? Cikwati cimeneci cidzabweletsa cisangalalo kumwamba. Koma kodi anthu amene ali ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi adzasangalala nao pa cikwati cimeneci? Tikufunitsitsa kudziŵa mayankho a mafunso amenewa. Conco, tiyeni tipitilize kupenda lemba la Salimo 45.
‘ZOVALA ZAKE NDI ZONUNKHILA’
3, 4. (a) Kodi zovala zacikwati zimene Mkwati wavala ndi zotani? Nanga n’ciani cikupangitsa kuti asangalale kwambili? (b) Kodi “ana aakazi a mafumu” ndi “mkazi wamkulu wa mfumu” amene akusangalala pamodzi ndi Mkwati ndani?
3 Ŵelengani Salimo 45:8, 9. Mkwati, Yesu Kristu, wavala zovala za cikwati zaulemelelo ndiponso zacifumu. Zovala zake zikununkhila bwino monga “mafuta onunkhila, abwino koposa.” Ndi zonunkhila monga mafuta a mule ndi kasiya amene anali kuwagwilitsila nchito pa kudzoza kopatulika ku Isiraeli.—Eks. 30:23-25.
4 Nyimbo za kumwamba zimene zikuimbidwa m’bwalo la mfumu zikupangitsa mkwatiyo kusangalala kwambili poganizila kuti mwambo wa cikwati cake wayandikila. “Mkazi wamkulu wa mfumu” akusangalala pamodzi ndi mkwatiyu. Mkazi ameneyu ndiponso “ana aakazi a mafumu,” ndi mbali ya kumwamba ya gulu la Mulungu amene ndi angelo. N’zocitsa cidwi kwambili kumva zolengedwa zakumwamba zikufuula kuti: “Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi cimwemwe codzaza tsaya . . . cifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika!”
MKWATI WAKONZEKELA CIKWATI CAKE
5. Kodi “mkazi wa Mwanawankhosa” ndani?
5 Ŵelengani Salimo 45:10, 11. Tsopano tamudziŵa mkwati, koma kodi mkwatibwi wake ndani? Mkwatibwi ameneyu si munthu weni-weni. Koma akuimila gulu lonse la Akristu odzozedwa a 144,000. Yesu ndiye mutu wa mpingo wa odzozedwa. (Ŵelengani Aefeso 5:23, 24.) Iwo adzakhala mbali ya Ufumu wa Mesiya. (Luka 12:32) Akristu 144,000 odzozedwa ndi mzimu amenewa “amatsatila Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.” (Chiv. 14:1-4) Iwo ndi “mkazi wa Mwanawankhosa” ndipo adzakhala ndi mkwati kumwamba.—Chiv. 21:9; Yoh. 14:2, 3.
6. N’cifukwa ciani odzozedwa amachedwa “mwana wamkazi wa mfumu”? Nanga n’cifukwa ciani akulangizidwa kuti ‘aiwale anthu ao’?
6 Mkwatibwi ameneyu amachedwa “mwana wamkazi” komanso “mwana wamkazi wa mfumu.” (Sal. 45:13) Kodi “mfumu” imeneyi ndani? Akristu odzozedwa akutengedwa kukhala “ana” a Yehova. (Aroma 8:15-17) Popeza kuti odzozedwa adzakhala mkwatibwi wakumwamba, io akulangizidwa kuti: “Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako [akuthupi].” Iwo afunika kuika maganizo ao “pa zinthu zakumwamba, osati pa zinthu zapadziko.”—Akol. 3:1-4.
7. (a) Kodi Yesu wakhala akukonzekeletsa bwanji mkwatibwi wake wamtsogolo? (b) Kodi mkwatibwi amamuona bwanji mwamuna wake wamtsogolo?
7 Kwa zaka zambili, Kristu wakhala akukonzekeletsa mkwatibwi wake kaamba ka mwambo wa cikwati umene udzacitika kumwamba. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Kristu ‘anakonda mpingo n’kudzipeleka yekha cifukwa ca mpingowo, ndipo anauyeletsa pousambitsa m’madzi a mau a Mulungu. Anatelo kuti iyeyo alandile mpingowo uli wokongola ndiponso waulemelelo, wopanda banga kapena makwinya kapenanso ciliconse ca zinthu zotelo, koma kuti ukhale woyela ndi wopanda cilema.’ (Aef. 5:25-27) Paulo anauzanso Akristu odzozedwa a ku Korinto kuti: “Ndikukucitilani nsanje, ngati imene Mulungu amakucitilani, popeza ndine ndinakucititsani kulonjezedwa ukwati ndi mwamuna mmodzi, Kristu, ndipo ndikufuna kukupelekani ngati namwali woyela kwa iye.” (2 Akor. 11:2) Mfumu Yesu Kristu, amene ndi Mkwati amaona kuti mkwatibwi wake ndi “wokongola” mwakuuzimu. Mkwatibwi ameneyu ‘amawelamila’ mwamuna wake wamtsogolo ameneyu ndipo amamuona monga “mbuye” wake.
MKWATI AKUMUBWELETSA KWA MFUMU
8. N’cifukwa ciani Malemba amakamba kuti mkwatibwi ali pa “ulemelelo waukulu”?
8 Ŵelengani Salimo 45:13, 14a. Mkwatibwi “wakongoletsedwela mwamuna wake” ndipo ali pa “ulemelelo waukulu” kaamba ka cikwati ca mfumu. Pa Chivumbulutso 21:2, mkwatibwi akuyelekezeledwa ndi mzinda umene ndi Yerusalemu Watsopano. Mzinda wakumwamba umenewu uli ndi “ulemelelo wa Mulungu,” ndipo ndi “wonyezimila ngati mwala wamtengo wapatali kwambili, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.” (Chiv. 21:10, 11) Buku la Chivumbulutso limafotokoza za ulemelelo wa Yerusalemu Watsopano mocititsa cidwi. (Chiv. 21:18-21) N’cifukwa cake wamasalimo anafotokoza kuti mkwatibwi ameneyu ali pa “ulemelelo waukulu.” Kuwonjezela pamenepo, cikwati cimeneci cidzacitikila kumwamba.
9. Kodi mkwatibwi akumubweletsa kwa “mfumu” iti? Nanga mkwatibwi ameneyo wavala zovala zotani?
9 Mkwatibwi akumubweletsa kwa Mfumu Mesiya amene ndi mwamuna wake. Mwamunayu wakhala akukonzekeletsa mkwatibwi wake mwa ‘kumuyeletsa pomusambitsa m’madzi a mau a Mulungu.’ Mkwatibwi ameneyu ndi ‘woyela ndiponso wopanda cilema.’ (Aef. 5:26, 27) Iye wavala bwino mogwilizana ndi cocitikaco. “Zovala zake ndi zagolide” ndipo “adzamubweletsa kwa mfumu atavala covala coluka.” Pa cikwati ca Mwanawankhosa, “iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimila ndi zoyela bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimila nchito zolungama za oyela.”—Chiv. 19:8.
‘CIKWATI CA MWANAWANKHOSA CAFIKA’
10. Kodi cikwati ca Mwanawankhosa cidzacitika liti?
10 Ŵelengani Chivumbulutso 19:7. Kodi cikwati ca Mwanawankhosa cidzacitika liti? Ngakhale kuti lemba la Chivumbulutso 19:7 likufotokoza kuti “mkazi wake wadzikongoletsa” kaamba ka cikwati, mavesi otsatila sakufotokoza za mwambo wa cikwati. M’malo mwake akufotokoza zocitika za mbali yomaliza ya cisautso cacikulu. (Chiv. 19:11-21) Kodi zimenezi zikusonyeza kuti cikwati cidzacitika Mfumu isanamalize nkhondo yolimbana ndi adani ake? Iyai. Masomphenya a m’buku la Chivumbulutso sanalembedwe mwa ndondomeko yotsatila nthawi imene adzakwanilitsidwe. Lemba la Salimo 45 limanena kuti coyamba Mfumu Yesu Kristu idzamangilila lupanga m’ciuno mwake ndi kugonjetsa adani ake. Pambuyo pa zimenezi m’pamene cikwati ca Mfumu cidzacitika.—Sal. 45:3, 4.
11. Kodi Kristu adzapambana pa nkhondo yolimbana ndi adani ake motsatila ndondomeko yotani?
11 Malinga ndi zimene timaphunzila m’Baibulo, zinthu zidzacitika mwanjila yotsatilayi: Coyamba, “hule lalikulu,” kapena kuti Babulo Wamkulu, amene ndi ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama lidzaonongedwa. (Chiv. 17:1, 5, 16, 17; 19:1, 2) Kenako pa Aramagedo, yomwe ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse, Kristu adzaononga mbali yonse yotsala ya dziko la Satanali.” (Chiv. 16:14-16; 19:19-21) Pomaliza, Mfumu Yankhondo idzapambana pa nkhondo yolimbana ndi adani ake mwa kuponya Satana ndi ziŵanda zake kuphompho kumene sadzatha kucita ciliconse.—Chiv. 20:1-3.
12, 13. (a) Kodi cikwati ca Mwanawankhosa cidzacitika liti? (b) Kodi ndani amene adzasangalala ndi cikwati ca Mwanawankhosa kumwamba?
12 M’nthawi ya kukhalapo kwa Kristu, Akristu odzozedwa akamaliza moyo wao wa padziko lapansi amaukitsidwila ku moyo wakumwamba. Pa nthawi inayake Babulo Wamkulu akadzaonongedwa, Yesu adzasonkhanitsa Akristu otsalila onse amene ali m’gulu la mkwatibwi. (1 Ates. 4:16, 17) Conco, nkhondo ya Aramagedo isanayambe, Akristu onse odzozedwa amene ndi “mkwatibwi” adzakhala ali kumwamba. Cikwati ca Mwanawankhosa cidzacitika nkhondo imeneyo ikadzatha. Cimeneco cidzakhala cikwati cosangalatsa kwambili. Lemba la Chivumbulutso 19:9 limati: “Odala ndiwo amene aitanidwa ku phwando la cakudya camadzulo la ukwati wa Mwanawankhosa.” Ndithudi, Akristu a 144,000 amene ali m’gulu la mkwatibwi adzasangalala kwambili. Ndipo Mkwati, amenenso ndi Mfumu, adzakhala ndi cimwemwe codzaza tsaya cifukwa cakuti mafumu anzake onse ‘adzadya ndi kumwa’ mophiphilitsa pamodzi naye ‘patebulo lake mu ufumu wake.’ (Luka 22:18, 28-30) Komabe, Mkwati ndi mkwatibwi si ndiwo okha amene adzasangalala cifukwa ca cikwati ca Mwanawankhosa.
13 Monga mmene taonela poyamba paja, makamu a kumwamba mogwilizana adzaimba kuti: “Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi cimwemwe codzaza tsaya. Timupatse ulemelelo, cifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.” (Chiv. 19:6, 7) Nanga bwanji za atumiki a Yehova padziko lapansi? Kodi naonso adzasangalala panthawiyo?
“ADZAWABWELETSA AKUSANGALALA”
14. Malinga ndi zimene zili pa Salimo 45, kodi “anamwali anzake” a mkwatibwi ndani?
14 Ŵelengani Salimo 45:12, 14b, 15. Mneneli Zekariya analosela kuti m’nthawi ya mapeto, anthu padziko lonse adzasangalala kutumikila Yehova pamodzi ndi otsalila a odzozedwa. Iye analemba kuti: “M’masiku amenewo, amuna 10 ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zek. 8:23) Pa Salimo 45:12, “amuna 10” ophiphilitsa amenewa akuchedwa “mwana wamkazi wa ku Turo” ndiponso “olemela pakati pa anthu.” Amuna amenewa amapita kwa otsalila a odzozedwa kuti akawacilikize pa nchito yao ndiponso kuti akapeze thandizo la kuuzimu. Kuyambila mu 1935, otsalila a odzozedwa athandiza anthu mamiliyoni ambili “kukhala olungama.” (Dan. 12:3) Anzao okhulupilika a Akristu odzozedwa amenewa ayeletsa miyoyo yao ndipo ndi anamwali mwakuuzimu. “Anamwali anzake” a mkwatibwi anadzipeleka kwa Yehova ndipo asonyeza kuti ndi okhulupilika kwa Mfumu yao.
15. Kodi “anamwali anzake” a mkwatibwi amagwila nchito bwanji limodzi ndi otsalila a Akristu odzozedwa?
15 Otsalila a odzozedwa amayamikila kwambili ‘anamwali anzao’ amenewa cifukwa cakuti amacita khama pa nchito yolalikila “uthenga wabwino uwu wa ufumu” padziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) “Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: ‘Bwela!’” komanso anthu amene amva zimenezi amanenanso kuti “Bwela.” (Chiv. 22:17) Zoonadi, a “nkhosa zina” anamva pamene Akristu odzozedwa ananena kuti “Bwela” ndipo ionso agwilizana ndi gulu la mkwatibwi mwa kunena kuti “Bwela” kwa anthu onse okhala padziko lapansi.—Yoh. 10:16.
16. Kodi Yehova wapatsa a nkhosa zina mwai wotani?
16 Otsalila a Akristu odzozedwa amakonda kwambili anzao amenewa. Iwo amasangalala kudziŵa kuti Atate a Mkwati, Yehova, apatsa mwai anzao amenewa wakuti adzasangalale nao pa cikwati ca Mwanawankhosa cimene cidzacitikila kumwamba. Baibulo limanena kuti ‘anamwali anzake’ a mkwatibwi “adzawabweletsa akusangalala ndi kukondwela.” A nkhosa zina, amene ali ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, adzasangalala nao pa cikwati ca Mwanawankhosa cimene cidzacitikila kumwamba. Ndiye cifukwa cake buku la Chivumbulutso limanena kuti a “khamu lalikulu” ‘aimilila pamaso pa mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.’ Iwo amatumikila Yehova m’bwalo la padziko lapansi la kacisi wauzimu.—Chiv. 7:9, 15..
“ANA ANU ADZATENGA MALO A MAKOLO ANU”
17, 18. Kodi cikwati ca Mwanawankhosa cidzabweletsa madalitso otani? Nanga Kristu adzakhala tate wa ndani mu Ulamulilo wake wa Zaka 1,000?
17 Ŵelengani Salimo 45:16. “Anamwali anzake” a mkwatibwi wa Kristu adzasangalala kwambili akadzaona madalitso amene cikwati ca Mwanawankhosa cidzabweletsa m’dziko latsopano. Mkwati, amenenso ndi Mfumu, adzayamba kulamulila dziko lapansi ndi kuukitsa ‘makolo ake’ amene adzakhala “ana” ake a padziko lapansi. (Yoh. 5:25-29; Aheb. 11:35) Iye adzaika ena mwa io “kukhala akalonga padziko lonse lapansi.” Mwacionekele, Kristu adzasankha ena mwa akulu okhulupilika amene tili nao masiku ano kuti akatitsogolele m’dziko latsopano.—Yes. 32:1.
18 Panthawi ya Ulamulilo wake wa Zaka Cikwi, Kristu adzakhalanso tate wa anthu ena. Anthu adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi cifukwa cokhulupilila nsembe ya dipo ya Yesu. (Yoh. 3:16) Motelo, Kristu adzakhala “Atate Wosatha” kwa io.—Yes. 9:6, 7.
TALIMBIKITSIDWA KUDZIŴIKITSA DZINA LA MFUMU
19, 20. Kodi zocitika zimene zinalembedwa pa Salimo 45 zimakhudza bwanji Akristu onse oona masiku ano?
19 Ŵelengani Salimo 45:1, 17. Kunena zoona, zocitika zimene zinalembedwa pa Salimo 45 zimakhudza Akristu onse. Akristu odzozedwa amene akali padziko lapansi amasangalala akaganizila kuti posacedwapa adzagwilizana ndi abale ao ndi Mwamuna wao kumwamba. Zimenezi zimalimbikitsa a nkhosa zina kupitilizabe kugonjela Mfumu yao yaulemelelo ndipo io amayamikila mwai umene ali nao wogwilizana ndi otsalila a odzozedwa padziko lapansi. Pambuyo pa mwambo wa cikwati cimeneci, Kristu ndi mafumu anzake adzadalitsa kwambili anthu okhala padziko lapansi.—Chiv. 7:17; 21:1-4.
20 Pamene tikuyembekezela kukwanilitsidwa kwa “nkhani yosangalatsa” imeneyi yokhudza Mfumu Mesiya, tiyeni tisaleke kudziŵikitsa dzina lake. Tiyeni tikhale m’gulu la anthu amene ‘adzatamanda Mfumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.’