LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 August masa. 26-30
  • Mmene Ndinagonjetsera Manyazi n’Kukhala Mmishonale

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Ndinagonjetsera Manyazi n’Kukhala Mmishonale
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE
  • KUDZIIKIRA COLINGA COKHALA MMISHONALE
  • KUTUMIKIRA M’DZIKO LANKHONDO
  • KUKATUMIKIRA KU DZIKO LINA
  • KULIMBANA NDI MABVUTO A PA UMOYO
  • NDIYAMIKIRA YEHOVA CIFUKWA CA THANDIZO LAKE
  • Yehova ‘Wawongola Njila Zanga’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 August masa. 26-30
Marianne Wertholz.

MBIRI YANGA

Mmene Ndinagonjetsera Manyazi n’Kukhala Mmishonale

YOSIMBIDWA NDI MARIANNE WERTHOLZ

NDILI mwana, ndinali wamanyazi ndipo ndinali kuopa anthu. Koma m’kupita kwa nthawi, Yehova anandithandiza kuti ndikhale mmishonale wokonda anthu. Kodi anagwiritsa nchito ndani pocita zimenezo? Coyamba, anagwiritsa nchito atate amene anandiphunzitsa zinthu zabwino zokhudza Iye. Anagwiritsanso nchito mlongo wina wa zaka 16. Ndipo pothera, anagwiritsa nchito mwamuna wanga kudzera m’mau ake okoma mtima komanso anzeru. Lekani ndikusimbireni za umoyo wanga.

N’nabadwira m’banja la cikatolika mu 1951, mu mzinda wa Vienna ku Austria. Ndinali wamanyazi koma ndinali kukhulupirira Mulungu, ndipo ndinali kupemphera kwambiri. Ndili ndi zaka 9, atate anayamba kuphunzira Baibo ndi Mboni za Yehova. Ndipo posakhalitsa, amai naonso anayamba kuphunzira.

Ndili ndi m’bale wanga, Elisabeth (ali kumanzere)

Posakhalitsa, tinayamba kusonkhana ndi mpingo wa Döbling mu mzinda womwewo wa Vienna. Monga banja, tinali kucitira limodzi zinthu zambiri. Tinali kuwerenga ndi kuphunzira Baibo, kupita ku misonkhano ya mpingo, komanso kudzipereka kugwirako nchito pa misonkhano yadera. Ndili mwana, atate anandithandiza kuti ndizim’konda kwambiri Yehova. Pemphero la atate linali lakuti ine ndi m’bale wanga tikakhale apainiya. Koma pa nthawiyo, cimeneci sicinali colinga canga.

KUYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE

N’nabatizika mu 1965 ndili ndi zaka 14. Zinali zobvuta kwa ine kulalikira kwa anthu amene sin’nali kuwadziwa. Ndinalinso kudziona wosafunika poyerekezera ndi anthu a msinkhu wanga. Ndipo ndinali kulaka-laka kuti azindikonda. Conco posakhalitsa n’tangobatizika, ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi anthu amene sanali kutumikira Yehova. Ngakhale kuti ndinali kusangalala kuceza nao, cikumbumtima canga cinali kundibvutitsa cifukwa ndinali kuthera nthawi yaitali ndi anthu amene sanali Mboni. Koma zinali kundibvuta kuti ndisiye kuceza nao. Ndiye n’ciani cinandithandiza?

Marianne ndi Dorothée.

Ndinaphunzira zambiri kwa Dorothée (ali kumanzere)

Ca pa nthawiyo, mtsikana wina wa zaka 16 dzina lake Dorothée anasamukira mu mpingo mwathu. N’nacita cidwi ndi mmene anali kukondera ulaliki wa khomo ndi khomo. N’nali wosinkhukirako pang’ono pa iye, koma sin’nali wokangalika kwambiri mu ulaliki. Mu mtima n’nadziuza kuti, ‘Makolo anga ndi Mboni. Koma Dorothée ndiye yekha Mboni m’banja lao. Ngakhale kuti ndiye akudwazika amai ake, nthawi zonse iye amakhala mu ulaliki!’ Citsanzo cake cinandilimbikitsa kum’citira zambiri Yehova. Posapita nthawi, ine ndi Dorothée tinayamba kucitira pamodzi upainiya. Tinayambira upainiya wothandiza umene pa nthawiyo unali kuchedwa upainiya wa pa chuti. Kenako tinakhala apainiya a nthawi zonse. Kukangalika kwa Dorothée mu ulaliki kunandiyambukira. Anandithandiza kuyambitsa phunziro langa loyamba la Baibo. M’kupita kwa nthawi, ndinayamba kumasuka kukambirana ndi anthu pa nyumba zao, m’miseu, komanso kumalo ena.

M’caka canga coyamba monga mpainiya wa nthawi zonse, mu mpingo mwathu munasamukira m’bale Heinz wa ku Austria. Iye anaphunzira coonadi ku Canada pamene anali kucezera m’bale wake amene anali Mboni. Heinz anatumizidwa mu mpingo wathu monga mpainiya wapadera. N’tangomuona, n’nam’konda nthawi yomweyo. Koma bvuto linali lakuti anali kufuna kukhala mmishonale, colinga cimene sin’naciganizirepo. Conco poyamba, sin’nafune kuonetsa kuti n’nali kum’konda. Patapita nthawi, ine ndi Heinz tinayamba cibwenzi ndipo tinakwatirana. Kenako tinayamba kucita upainiya ku Austria.

KUDZIIKIRA COLINGA COKHALA MMISHONALE

Nthawi zambiri Heinz anali kukamba nane za colinga cake cokhala mmishonale. Sanali kundikakamiza, koma anali kundifunsa mafunso ondithandiza kuganizirapo monga lakuti, “Popeza tilibe ana, kodi sitingaonjezere zimene timacita potumikira Yehova?” Pokhala munthu wamanyazi, ndinali kucita mantha kukhala mmishonale. N’zoona kuti ndinali kutumikira monga mpainiya, koma kuganiza zocita utumiki waumishonale kunali kundicititsa mantha kwambiri. Ngakhale n’telo, Heinz anapitiriza kukambapo za colinga cokhala mmishonale. Iye anandilimbikitsanso kuti ndiziganizira kwambiri mmene ndingalimbikitsire anthu m’malo moganizira kwambiri za mantha anga. Ulangizi wake unandithandiza kwambiri.

Heinz akutsogoza Nsanja ya Mlonda mu mpingo waung’ono wa ci Serbo-Croatian ku Salzburg, Austria, mu 1974

Pang’ono m’pang’ono ndinakhala ndi cifuno coyamba umishonale. Conco, tinafunsira kulowa Sukulu ya Giliyadi. Komabe mtumiki wa nthambi anakamba kuti zingakhale bwino kuti coyamba ndiphunzire kulankhula bwino Cingerezi. Patatha zaka zitatu ndikuyeseza kulankhula bwino Cingerezi, tinadabwa titapemphedwa kukatumikira mu mpingo wa ci Serbo-Croatian mu mzinda wa Salzburg ku Austria. Tinatumikira kumeneko zaka 7 ndipo kwa caka cimodzi m’zaka 7 zimenezo, tinatumikirapo m’nchito ya m’dera. Cinenero ca ci Serbo-Croatian cinali cobvuta. Koma tinali ndi maphunziro a Baibo ambiri.

Mu 1979, abale amene anali kutsogolera anatipempha kuti kwa kanthawi kocepa tipite ku dziko la Bulgaria. Cifukwa cakuti nchito yathu inali yoletsedwa kumeneko, iwo anatipempha kuti tipiteko monga tikupita ku chuti. Anatiuza kuti tisakalalikire koma kuti tinyamule mwakabisira zofalitsa zathu zokhala mum’pangidwe waung’ono kwambiri kuti tikapatse alongo athu 5 amene anali kukhala mu mzinda waukulu wa dzikolo wa Sofia. Ndinali ndi mantha aakulu koma Yehova anandithandiza kucita utumikiwu. Kuona kulimba mtima kwa alongowo komanso cimwemwe cimene anali naco ngakhale kuti panali kuthekera kwakuti angaikidwe m’ndende, kunandipatsa cidaliro cocita utumiki ulionse umene gulu la Mulungu lingandipatse.

Patapita nthawi, tinafunsiranso kulowa Sukulu ya Giliyadi ndipo pa nthawiyi anatiyankha. Tinaganiza kuti tidzalowa kalasi ya Cingerezi ku America. Koma mu November 1981, Sukulu ya Giliyadi Yoonjezera inayamba ku nthambi ya ku Wiesbaden ku Germany. Conco tinalowa nao kalasi ya ci German comwe cinali cosabvuta kwa ine kumvetsa. Kodi anatitumiza kuti?

KUTUMIKIRA M’DZIKO LANKHONDO

Anatitumiza kukatumikira ku Kenya. Komabe, ofesi ya nthambi ya kumeneko inatifunsa ngati tingakonde kukatumikira ku dziko lapafupi nalo la Uganda. Zaka zoposa 10 kumbuyoko izi zisanacitike, gulu la asilikali linalanda ulamuliro boma la Uganda motsogoleredwa ndi mkulu wa asilikali, Idi Amini. M’zaka zimene zinatsatirapo, ulamuliro wake unabweretsa imfa kwa anthu masauzande komanso cisokonezo kwa anthu mamiliyoni. Kenako mu 1979, Idi Amini anakakamizidwa ndi anthu omutsutsa kutula pansi ulamuliro. Mwacionekere, mungamvetse cifukwa cake ndinali ndi mantha opita ku dziko laconco. Koma Sukulu ya Giliyadi inatikonzekeretsa kudalira Yehova. Conco tinabvomera kupita.

M’dziko la Uganda munali cipwirikiti cokha-cokha. Boma silinali kukwanitsa kupereka madzi, magetsi, ndi zina zofunikira kwa nzika zake. Mafoni sanali kugwira nchito. Anthu anali kuomberana ndi kuberana zinthu maka-maka usiku. Kukada, aliyense anali kukhala panyumba pake n’kumapemphera kuti kusabwere munthu kudzawatengera katundu wao kapena kudzawapha. Ngakhale kuti panali zobvuta zonsezi, abale a kumeneko anali kupita patsogolo kuuzimu!

Tikuphika cakudya ku nyumba ya m’bale Waiswa

Mu 1982, ine ndi Heinz tinafika mu mzinda wa Kampala, womwe ndi mzinda waukulu wa dziko la Uganda. M’miyezi 5 yoyambirira, tinali kukhala ndi Sam Waiswa ndi mkazi wake Christina pamodzi ndi ana awo 5 komanso acibale awo anai. Nthawi zambiri, banja la M’bale ndi Mlongo Waiswa inali kudya kamodzi pa tsiku cifukwa ca kusowekera kwa cakudya. Koma iwo anali osangalala kugawana zocepa zimene anali nazo ndi ife. Izi zinacititsa kuti kucereza kwao kukhale kosaiwalika. Nthawi yonse imene tinali kukhala ndi banjali tinaphunzira zinthu zambiri zimene zinatithandiza pa umoyo wathu waumishonale. Mwacitsanzo, tinaphunzira kusamba pogwiritsa nchito madzi ocepa ndi kugwiritsa nchito madzi amodzi-modziwo m’zimbudzi za m’nyumba. Mu 1983, ine ndi Heinz tinasamukira m’nyumba ina ku Kampala komwe kunaliko kotetezeka.

Zinali zosangalatsa kwambiri kulalikira mu mzinda wa Kampala. Ndikumbukira kuti m’mwezi wina, tinagawira magazini oposa 4,000! Koma cosangalatsa kwambiri ndi mmene anthu analandirira coonadi. Iwo anali kulemekeza kwambiri Mulungu ndipo anali ofunitsitsa kukambirana nao nkhani za m’Baibo. Ine ndi Heinz, aliyense anali ndi maphunziro a Baibo pakati pa 10 ndi 15. Ndipo tinaphunzira zambiri kwa maphunziro athu amenewa. Mwacitsanzo, ngakhale kuti anali kufunika kufika pa misonkhano mlungu ulionse, sanali kudandaula koma anali kukhalabe acimwemwe.

Mu Uganda munacitikanso nkhondo zina ziwiri mu 1985 ndi mu 1986. Nthawi zambiri tinali kuona ana atanyamula zida zankhondo. Iwo anali kugwiritsidwa nchito monga asilikali ndipo ndiwo anali kuimirira pa malodibuloko. Pa nthawi ngati zimenezo, tinali kupemphera kwa Yehova kuti atithandize kukhala ozindikira komanso odekha pamene tinali kusakira anthu acidwi mu ulaliki. Ndipo iye anayankha mapemphero athu. Nthawi zambiri tinali kuiwala nkhawa zathu tikapeza munthu amene afuna kumvetsera uthenga wa Ufumu.

Ndili ndi Heinz komanso Tatjana (ali pakati)

Tinali kusangalalanso kulalikira anthu ocokera m’maiko ena. Mwacitsanzo, tinaphunzira ndi Murat Ibatullin ndi mkazi wake Dilbar omwe anacokera mu mzinda wa Tatarstan ku Russia. Murat anali kugwira nchito zacipatala. Onse awiri anakhala Mboni ndipo anakhala okangalika kuyambira nthawiyo. Pambuyo pake, ndinakumana ndi Tatjana Vileyska, mzimai wa ku Ukraine amene anali ndi maganizo ofuna kudzipha. Iye atabatizika, anabwerera ku Ukraine ndipo pambuyo pake anayamba kugwira nchito yomasulira zofalitsa zathu.a

KUKATUMIKIRA KU DZIKO LINA

Mu 1991 ine ndi Heinz tili ku chuti ku Austria, ofesi ya nthambi ya kumeneko inatiuza kuti utumiki wathu wasintha ndi kuti tidzayamba kutumikira ku Bulgaria. Ulamuliro wa Cikomyunizimu utatha ku Eastern Europe, nchito ya Mboni za Yehova inabvomerezedwanso mwalamulo ku Bulgaria. Monga ndafotokozera kale, ine ndi Heinz tinalowetsapo mwakabisira zofalitsa zathu m’dzikolo pomwe nchito yathu inali yoletsedwa. Koma tsopano, abale anatitumiza kumeneko kukalalikira.

Abale anatiuza kuti tisabwererenso ku Uganda. Conco sitinapitenso ku nyumba ya amishonale ku Uganda kuti tikatenge katundu wathu kapena kukalairana ndi abale kumeneko. M’malomwake, tinapita ku Beteli ya ku Germany, ndipo tinakwera galimoto n’kupita ku Bulgaria. Anatitumiza kukatumikira limodzi ndi kagulu ka ofalitsa ngati 20 komwe kanali mu mzinda wa Sofia.

Ku Bulgaria tinakumana ndi mabvuto ambiri atsopano. Coyamba, sitinali kudziwa kulankhula cinenero ca kumeneko. Kuonjezera apo, zofalitsa zokhazo zimene zinaliko m’cinenero ca ci Bulgaria ndi buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndi Buku Langa la Nkhani za m’Baibo. Ndipo zinali zobvuta kuyambitsa maphunziro a Baibo. Komabe, kagulu kathu kanali kulalikira mokangalika komanso mwakhama. Acipembedzo ca Orthodox ataona zimenezi, anayamba kutizunza.

Mu 1994, boma linaleka kuona Mboni za Yehova monga cipembedzo cobvomerezeka mwalamulo ndipo anthu ambiri anayamba kutiona monga gulu loopsya lacipembedzo. Ena mwa abale athu anamangidwa. Oulutsa nkhani anali kufalitsa nkhani zabodza zokhudza Mboni. Iwo anali kunena kuti a Mboni amapha ana ao cifukwa salola kuikidwa magazi. Anali kunenanso kuti a Mboni amalimbikitsa a Mboni anzao kuti adziphe. Izi zinacititsa kuti zikhale zobvuta kwa ine ndi Heinz kulalikira. Nthawi zambiri tikamalalikira, tinali kukumana ndi anthu amene anali kutilalatira, kutiitanira apolisi, komanso kutiponya ndi zinthu. Zinalinso zobvuta kulandira zofalitsa zathu m’dzikolo kucokera kunja, ndipo kucita lenti nyumba zocitiramo misonkhano kunali kobvuta. Pa nthawi ina, apolisi anafika ngakhale posokoneza ndi kuimitsa umodzi mwa misonkhano yathu yacigawo. Kwa ine ndi Heinz zinali zacilendo kucitidwa cidani ca mtundu umenewu. Izi zinali zosiyana kwambiri ndi gawo la ku Uganda lomwe anthu ake anali acidwi komanso aubwenzi. Koma n’ciani cinatithandiza kupirira zobvuta zonsezi?

Kuceza ndi abale ndi alongo a kumeneko kunatithandiza kukhalabe acimwemwe. Iwo anali kucikonda kwambiri coonadi ndipo anali kuyamikira thandizo limene tinali kuwapatsa. Tonse tinali kucitira zinthu limodzi ndi kuthandizana wina ndi mnzake. Zimene zinaticitikirazi zinatiphunzitsa kuti tingakhalebe acimwemwe mu utumiki ulionse tikapitiriza kukonda anthu.

Marianne ndi Heinz Wertholz.

Tili pa ofesi ya nthambi ya ku Bulgaria mu 2007

M’kupita kwa nthawi, zinthu zinayamba kusinthira kwabwino. Mu 1998, gulu lathu linabvomerezedwanso mwalamulo ndipo zofalitsa zathu zambiri zinayamba kupezeka mu ci Bulgarian. Mu 2004, ofesi ya nthambi yatsopano inapatulidwa kwa Yehova. Tsopano ku Bulgaria kuli mipingo 57, ndi ofalitsa 2,953. M’caka cautumiki capita, anthu 6,475 anapezeka pa Cikumbutso. Pa nthawi ina, mu mzinda wa Sofia munali alongo 5 cabe, koma tsopano muli mipingo 9! Taonadi ‘wamng’ono akusanduka anthu 1,000.’​—Yes. 60:22.

KULIMBANA NDI MABVUTO A PA UMOYO

Pa umoyo wanga ndakhalapo ndi mabvuto osiyana-siyana okhudza thanzi. Pa zaka zapitazi, ndakhalapo ndi zotupa zingapo, ndipo pa nthawi ina madokotala anandipeza ndi cotupa ku ubongo. Ndinalandirapo thandizo lamphamvu la mankhwala, ndipo pa nthawi ina anandicita opaleshoni kwa maola 12 ku India kuti acotse mbali yaikulu ya cotupaco. Pambuyo pocitidwa opaleshoni, kwa kanthawi tinakhala pa Beteli ya ku India kuti ndipezeko bwino. Kenako tinabwerera ku Bulgaria kukapitiriza utumiki wathu.

Tili ku Bulgaria, Heinz anayamba kudwala matenda enaake a kumtundu ochedwa Huntington. Matendawa anam’pangitsa kuti azibvutika kuyenda, kukamba, komanso kugwira nchito. Pamene matendawa anali kukulira-kulira, iye anali kudalira thandizo langa kuti akwanitse kucita zinthu. Nthawi zina ndinali kukhala wamantha komanso wankhawa ndikaganizira mmene zinthu zidzakhalire. Komabe, m’bale wina wacinyamata dzina lake Bobi, nthawi zambiri anali kubwera kudzatenga Heinz ndi kupita naye mu ulaliki. Bobi sanali kudera nkhawa za mmene anthu anali kumuonera cifukwa cokhala ndi Heinz amene anali kubvutika kulankhula, kugwiritsa nchito bwino manja ake, komanso amene anali kubvutika kuyenda. Ndikalephera kuthandiza Heinz, nthawi zonse Bobi anali wokonzeka kumuthandiza. Ngakhale kuti ine ndi Heinz tinasankha kusakhala ndi ana m’dongosolo lino, tinaona kuti Yehova anatipatsa Bobi monga mwana wathu wamwamuna!​—Maliko 10:​29, 30.

Heinz anam’pezanso ndi matenda a khansa. N’zacisoni kuti mwamuna wanga wokondedwa anamwalira mu 2015. Ndinakhala ndi nkhawa kwambiri ndipo zinali ngati maloto kuti iye wamwaliradi. Koma ndikamaganizira kwambiri za zinthu zimene tinacitira pamodzi, zimakhala ngati kuti iye akali moyo! (Luka 20:38) Nthawi zambiri kukaca, ndimakumbukira mau ake okoma mtima komanso malangizo acikondi amene iye anali kundipatsa. Ndimayamikira kwambiri kuti ndinatumikira naye limodzi mokhulupirika kwa zaka zambiri.

NDIYAMIKIRA YEHOVA CIFUKWA CA THANDIZO LAKE

Yehova wakhala akundithandiza kupirira mabvuto osiyana-siyana mu umoyo wanga. Iye anandithandiza kuthetsa manyazi ndipo anandithandizanso kukhala mmishonale. (2 Tim. 1:7) Cifukwa ca thandizo lake, ine ndi mng’ono wanga tsopano tili mu utumiki wa nthawi zonse. Iye ndi mwamuna wake ali m’nchito ya m’dera ku Europe, m’dera la ci Serbian. Yehova wayankha mapemphero amene atate anapereka zaka zingapo zapitazo!

Kuwerenga Baibo kumandithandiza kukhala ndi mtendere wa mu mtima. M’nthawi zobvuta, ndaphunzira kufunika kopemphera “ndi mtima wonse” monga anacitira Yesu. (Luka 22:44) Njira imodzi imene Yehova amayankhira mapemphero anga ndi kudzera mwa mabwenzi a mu mpingo wathu wa Nadezhda mu mzinda wa Sofia amene amacita nane mokoma mtima komanso mwacikondi. Nthawi zambiri iwo amandiitanira ku maceza komanso kundiyamikira. Ndipo izi zimandipatsa cimwemwe coculuka.

Nthawi zambiri ndimasinkhasinkha za kuuka kwa akufa. M’maganizo mwanga ndimaona makolo anga ataimirira patsogolo pa nyumba yathu akuoneka okongola komanso athanzi monga analili atangokwatirana. Ndimaonanso m’bale wanga akukonza cakudya. Ndipo ndimaonanso Heinz ataimirira pafupi ndi hachi yake. Kusinkhasinkha kwa conco kumandithandiza kucepetsako nkhawa zanga ndipo kumandithandizanso kuti ndizimuyamikira Yehova.

Ndikamaganizira zimene zandicitikira pa umoyo wanga komanso za tsogolo langa, ndimabvomereza ndi mtima wonse mau amene Davide anakamba pa Salimo 27:​13, 14 akuti: “Kodi ndikanakhala ndili kuti ndikanapanda kukhala ndi cikhulupiriro coti ndidzaona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu a moyo? Yembekezera Yehova. Limba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu. Inde, yembekezera Yehova.”

a Onani mbiri ya moyo ya Tatjana Vileyska mu Galamukani! ya Cingelezi ya December 22, 2000, mas. 20-24.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani