Malangizo Owonjezela Kwa Makolo
Monga mwaonela, malangizo ali m’magazini ino ni ozikidwa pa mfundo za m’Baibo. Baibo imapeleka malangizo opindulitsa kwambili kwa aliyense m’banja. Ndipo mfundo zake zimathandiza munthu kukhala woganiza bwino, komanso kupanga zosankha zanzelu.—Miyambo 1:1-4.
BAIBO IMAYANKHANSO MAFUNSO OFUNIKA KWAMBILI MU UMOYO, MONGA AKUTI:
Tikupemphani kuti mudziŵelengele mwekha Baibo, kuti mupeze mayankho pa mafunso aya na enanso. Tambani vidiyo yakuti, N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? yendani pa www. jw.org.