Buku Lakale-kale, Koma Lothandiza Masiku Ano
Anthu ambili amaona kuti Baibo ni buku lopatulika. N’zoona kuti Baibo ni buku lopatulika limene limatiuza mmene tingalambilile Mulungu. Koma lilinso na malangizo othandiza mu umoyo wathu wa tsiku na tsiku.
Mwacitsanzo, onani zimene ena anakamba zoonetsa mmene anapindulila cifukwa coŵelenga Baibo, na kuseŵenzetsa malangizo ake.
“Umoyo wanga uli bwino tsopano. Maganizo na mtima wanga zili m’malo. Lomba nili na umoyo wacimwemwe kwambili.”—Fiona.
“Mwa kuŵelenga Baibo, moyo wanga wakhala wopindulitsa komanso wa colinga.”—Gnitko.
“Umoyo wanga wasintha kwambili kukhala wabwino. Manje nili na umoyo wosalila zambili, ndipo nimapeza nthawi yokwanila yoceza na banja langa.”—Andrew.
Palinso zitsanzo zina zambili monga zimenezi. Zungulile dziko lonse, ambili apeza kuti Baibo imapeleka malangizo othandiza mu umoyo wa tsiku na tsiku.
Tiyeni tione mmene Baibo ingathandizile anthu m’mbali zotsatilazi:
Thanzi labwino
Kudziŵa kulamulila mtima wathu
Umoyo wa banja komanso mabwenzi
Moseŵenzetsela ndalama
Umoyo wauzimu
Baibo ni buku locokela kwa Mulungu, ndipo ingakuthandizeni mu umoyo wanu wa tsiku na tsiku.